Mawu a M'munsi
a Si nthawi zonse pamene mantha angakhale oipa. Mantha ena angatiteteze pomwe ena angachititse kuti tikumane ndi mavuto. Satana angagwiritse ntchito mantha potichititsa kusankha zolakwika. N’zoonekeratu kuti timafunika kuyesetsa kuti tisamakhale ndi mantha amenewo. Kodi n’chiyani chingatithandize? Monga mmene tionere munkhaniyi, tikamakhulupirira kuti Yehova ali kumbali yathu komanso amatikonda, sitingamaope chilichonse.