Mawu a M'munsi
a Atumiki onse a Yehova amasangalala achinyamata akabatizidwa. Komabe pambuyo pobatizidwa, ophunzira atsopano ayenera kupitirizabe kupita patsogolo mwauzimu. Pofuna kuthandiza onse mumpingo, nkhaniyi ifotokoza zimene achinyamata omwe angobatizidwa kumene angachite kuti apitirizebe kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.