Mawu a M'munsi
c Mabuku a Uthenga Wabwino amafotokoza zozizwitsa zoposa 30 zimene Yesu anachita. Kuwonjezera pamenepo, iye anachitanso zozizwitsa zina zambiri zomwe Baibulo silinatchule chilichonse pachokhapachokha. Pa nthawi ina ‘anthu onse a mumzinda’ anabwera kwa iye ndipo “anachiritsa ambiri amene anali kudwala.”—Maliko 1:32-34.