Mawu a M'munsi
a Nkhani ya Hoseyayi ndi yapadera chifukwa masiku ano Yehova sanaike lamulo lakuti munthu akachita chigololo, mnzake wosalakwayo apitirizebe kukhala naye pa banja. Ndipotu Yehova anauza Mwana wake kuti afotokoze kuti wolakwiridwayo angathe kukatenga chikalata chothetsera ukwati ngati akufuna kutero.—Mat. 5:32; 19:9.