Mawu a M'munsi
a Anthu a ku Babulo ndi amene anayambitsa chikhulupiriro chakuti munthu akamwalira mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo, komanso chakuti munthu akafa amakabadwanso kwinakwake. Kenako, akatswiri a nzeru za anthu a ku India anayambitsa chiphunzitso chotchedwa Karma. Buku lina linanena kuti Karma ndi “lamulo lomwe limanena kuti zimene munthu akuchita m’moyo uno, zimadzakhala ndi zotsatira zake m’moyo wotsatira.”—Britannica Encyclopedia of World Religions, tsamba 913.