Mawu a M'munsi
a Ndalama yochepa imawonongedwa nthawi iliyonse imene munthu wapanga dawunilodi zinthu pa JW Library. Mwachitsanzo, chaka chatha tinagwiritsa ntchito ndalama zoposa madola 1.5 miliyoni a ku United States polola anthu kupanga dawunilodi zinthu komanso kungoonera kapena kumvetsera zinthu pa jw.org ndi pa JW Library. Komabe ndalama zimene timagwiritsa ntchito kuti zinthu zizipangidwa dawunilodi n’zochepa kwambiri poyerekezera ndi zimene tingagwiritse ntchito popanga ndi kutumiza mabuku, ma CD komanso ma DVD.