Mutu 17
Kuphunzitsa Nikodemo
PAMENE adakali pa Paskha wa 30 C.E., Yesu akuchita zizindikiro zapadera, kapena zozizwitsa. Monga chotulukapo, anthu ambiri akuika chikhulupiliro mwa iye. Nikodemo, chiŵalo cha Sanhedrin, bwalo lalikulu la milandu Lachiyuda, akuchititsidwa chidwi ndipo akufuna kuphunzira zowonjezereka. Chotero iye akuchezera Yesu mkati mwa mdima wa usiku, mwinamwake kuwopera kuti mbiri yake ndi atsogoleri ena Achiyuda idzawonongeka ngati iye awonedwa.
“Rabi,” iye akutero, “tidziŵa kuti inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.” M’kuyankha, Yesu akuuza Nikodemo kuti, kuti aloŵe Ufumu wa Mulungu, munthu ayenera ‘kubadwanso.’
Komabe, kodi munthu angabadwenso motani? “Kodi akhoza kuloŵanso m’mimba ya amake ndi kubadwa?” Nikodemo akufunsa motero.
Ayi, zimenezo sindizo zimene kubadwanso kumatanthauza. “Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mzimu,” Yesu akufotokoza motero, “sakhoza kuloŵa ufumu wa Mulungu.” Pamene Yesu anabatizidwa ndipo mzimu woyera unatera pa iye, iye motero anabadwa “mwa madzi ndi mzimu.” Ndi chilengezo chotsagana nacho chochokera kumwamba, ‘Uyu ndiye Mwana wanga mwa amene ndikondwera naye,’ Mulungu analengeza kuti iye anali atabala mwana wamwamuna wauzimu wokhala ndi chiyembekezo cha kuloŵa mu Ufumu wakumwamba. Pambuyo pake, pa Pentekoste wa 33 C.E., anthu ena obatizidwa adzalandira mzimu woyera ndipo motero nawonso adzakhala obadwanso monga ana aamuna auzimu a Mulungu.
Koma mbali ya Mwana wapadera waumunthu wa Mulungu ameneyu njofunika kwambiri. “Monga Mose anakweza njoka m’chipululu,” Yesu akuuza Nikodemo, “chotero Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa, kuti yense wakukhulupilira akhale nawo moyo wosatha mwa iye.” Inde, monga momwe Aisrayeli amenewo olumidwa ndi njoka zaululu anafunikira kuyang’ana panjoka yamkuwa kuti apulumutsidwe, chotero anthu onse afunikira kuika chikhulupiliro mwa Mwana wa Mulungu kuti apulumutsidwe kumkhalidwe wawo wa imfa.
Pogogomezera mbali ya chikondi cha Yehova m’zimenezi, kenako Yesu akuuza Nikodemo kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Motero, pano m’Yerusalemu miyezi isanu ndi umodzi yokha atayamba uminisitala wake, Yesu akusonyeza bwino lomwe kuti iye ndiye njira ya Yehova Mulungu ya kupulumutsira mtundu wa anthu.
Yesu akupitirizabe kufotokozera Nikodemo kuti: “Pakuti Mulungu sanatuma Mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi,” ndiko kuti, kukaliweruza moipa, kapena kulitsutsa, kuweruzira mtundu wa anthu kuchiwonongeko. Mmalomwake, monga momwe Yesu akunenera, iye anatumidwa kuti “dziko lapansi likapulumutsidwe ndi iye.”
Nikodemo wafika kwa Yesu mwamantha mumdima. Motero nkokondweretsa kuti Yesu akumaliza naye makambitsirano ake mwa kunena kuti: “Koma chiweruzo ndiichi, kuti kuunika [kumene Yesu anakusonyeza m’moyo wake ndi m’ziphunzitso] kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Koma wochita chowonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake ziwonekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.” Yohane 2:23–3:21; Mateyu 3:16, 17; Machitidwe 2:1-4; Numeri 21:9.
▪ Kodi nchiyani chimene chikusonkhezera ulendo wa Nikodemo, ndipo nchifukwa ninji iye akudza usiku?
▪ Kodi ‘kubadwanso’ kumatanthauzanji?
▪ Kodi Yesu akufotokoza motani mwa fanizo ntchito yake ya chipulumutso chathu?
▪ Kodi kunena kuti Yesu sanadze kudzaweruza dziko kumatanthauzanji?