Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm tsamba 31
  • Onani Uthenga wa M’Baibulo—Mwachidule

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Onani Uthenga wa M’Baibulo—Mwachidule
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm tsamba 31
Anthu akusangalala ndi ulamuliro wa Ufumu m’dziko latsopano la paradaiso

Onani Uthenga wa M’Baibulo

  1. Yehova analenga Adamu ndi Hava kuti akhale ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Satana anaipitsa dzina la Mulungu ndipo anasonyeza kuti Mulungu siwoyenera kulamulira. Adamu ndi Hava anagwirizana ndi Satana pogalukira Mulungu ndipo zimenezi zinachititsa kuti iwowo ndiponso ana amene anabereka akhale ochimwa ndiponso ayambe kufa

  2. Yehova anaweruza ochimwawo ndipo analonjeza kuti kudzabwera Mpulumutsi, kapena kuti Mbewu, amene adzaphwanya Satana ndi kuchotsa mavuto onse amene anabwera chifukwa cha kugalukira ndi kuchimwa kumene kunachitikako

  3. Yehova analonjeza Abulahamu ndi Davide kuti adzakhala makolo a Mbewu kapena kuti Mesiya, amene adzalamulire monga Mfumu kwamuyaya

  4. Yehova anauza aneneri kuti alosere zoti Mesiya adzathetsa uchimo ndi imfa. Monga Mfumu, Mesiyayo limodzi ndi olamulira anzake, adzalamulira mu Ufumu wa Mulungu umene udzathetse nkhondo, matenda ngakhalenso imfa

  5. Yehova anatumiza Mwana wake padziko lapansi ndipo anam’dziwikitsa kuti ndi Mesiya. Yesu analalikira za Ufumu wa Mulungu ndipo anapereka moyo wake monga nsembe. Kenako Yehova anamuukitsa monga mzimu

  6. Yehova anaika Mwana wake kukhala Mfumu kumwamba ndipo chimenechi chinali chiyambi cha masiku otsiriza a dziko loipali. Yesu amatsogolera otsatira ake akamalalikira za Ufumu wa Mulungu padziko lonse lapansi

  7. Yehova adzalamula Mwana wake kuti Ufumu wake uyambenso kulamulira padziko lapansi. Ufumuwu udzaphwanya maboma onse oipa, udzabweretsa Paradaiso, komanso mu ufumuwu, anthu onse okhulupirika adzakhala angwiro. Pa nthawiyi, zidzadziwika kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndipo dzina lake lidzayeretsedwa mpaka muyaya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena