Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/13 tsamba 8-9
  • Dziko la Brazil

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Brazil
  • Galamukani!—2013
Galamukani!—2013
g 12/13 tsamba 8-9
[Chithunzi patsamba 8]

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Brazil

[Mapu patsamba 8]
[Chithunzi patsamba 9]

Anthu a ku Brazil amakonda kwambiri chakudya chokoma chotchedwa feijoada

[Chithunzi patsamba 9]

Mbalame yotchedwa toucan

POYAMBA ku Brazil kunkakhala alenje ndi alimi. Kenako Apwitikizi anafika m’dzikoli n’kuyambitsa Chikatolika ndipo patapita nthawi, m’dzikoli munamangidwa matchalitchi ambiri. Ena mwa matchalitchiwa ankawakongoletsa ndi ziboliboli zokutidwa ndi golide.

Cham’katikati mwa zaka za m’ma 1500 mpaka 1800, sitima zapanyanja zinabweretsa akapolo okwana 4 miliyoni kuchokera ku Africa kuti azigwira ntchito m’minda. Anthu amenewa anabwera ndi miyambo yakwawo, zimene zinapangitsa kuti m’dzikoli mukhale zipembedzo zophatikizana monga macumba komanso candomblé. Nyimbo, magule komanso zakudya za m’dzikoli zimasonyeza kuti zinachokera ku chikhalidwe cha ku Africa.

Anthu a m’dzikoli amakonda kudya chakudya china chotchedwa feijoada chimene amachipanga pophatikiza nyama komanso nyemba zakuda ndipo amadyera mpunga wosakaniza ndi masamba. Chakudyachi chinachokera ku Portugal. M’zaka za m’ma 1800 mpaka 1900, m’dzikoli munafikanso anthu ochokera ku Germany, Italy, Poland, Spain, Japan komanso mayiko ena.

Ku Brazil kuli mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 11,000 ndipo muli Mboni zoposa 750,000. A Mboniwa amaphunzira Baibulo ndi anthu oposa 800,000. Pofuna kuti akhale ndi malo abwino oti azisonkhanamo, magulu 31 ogwira ntchito yomanga, amamanga komanso kukonza Nyumba za Ufumu pafupifupi 250 kapena 300 pa chaka. Kuchokera mu March 2000, Nyumba za Ufumu zokwana 3,647 zamangidwa kapena kukonzedwa.

[Chithunzi patsamba 9]

Mbali yaikulu ya mtsinje wa Amazon ili m’nkhalango yaikulu padziko lonse

KODI MUKUDZIWA?

Mtsinje wa Amazon ndi wautali makilomita 6,275 ndipo ndi umene umathira madzi ambiri m’nyanja kuposa mtsinje uliwonse padziko lonse

DZIWANI IZI

  • Chiwerengero cha anthu: 201 miliyoni

  • Likulu lake: Brasília

  • Zilankhulo: Chipwitikizi komanso zilankhulo zina zokwana 180

  • Dzina: Dzina lakuti Brazil linachokera ku mtengo wotchedwa Caesalpinia echinata, umene ndi wofiira ndipo ankaugwiritsa ntchito kupanga utoto

  • Nyengo: Kumpoto kwa dzikoli n’kotentha. Kum’mwera kwake kuli mapiri ndipo nthawi zina kumagwa chipale chofewa m’nyengo yozizira

  • Kukula kwake: Dziko la Brazil ndi lalikulu pafupifupi hafu ya South America. M’dzikoli muli mitsinje yambiri komanso ikuluikulu padziko lonse lapansi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena