Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/13 tsamba 12-13
  • Dziko la Cameroon

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Cameroon
  • Galamukani!—2013
Galamukani!—2013
g 1/13 tsamba 12-13

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Cameroon

ANTHU oyambirira kukhala ku Cameroon anali amtundu wa Baka omwenso amatchedwa Abathwa. Kenako Apwitikizi anafika m’dzikoli cha m’ma 1500. Patapita zaka zambiri, kunafikanso anthu amtundu wa Fulani, omwe anali Asilamu ndipo anagonjetsa anthu omwe ankakhala kumpoto kwa dziko la Cameroon. Masiku ano ku Cameroon, anthu 40 pa 100 alionse amati ndi Akhristu, 20 pa 100 alionse ndi Asilamu ndipo anthu 40 pa 100 alionse ali m’zipembedzo za makolo.

Anthu a ku midzi ya ku Cameroon amadziwa kuchereza alendo. Mlendo akafika amamulowetsa m’nyumba n’kumpatsa moni. Kenako amamupatsa madzi ndi chakudya. Anthuwa amaona kuti kukana chakudya ndi mwano.

Akamacheza ndi mlendo, amayamba kumufunsa za mmene alili komanso za banja lake. Nthawi zina amatha kufunsanso mmene ziweto zawo zilili. Joseph, yemwe amakhala ku Cameroon, ananena kuti: “Mlendo akatsanzika, timamuperekeza kwinaku tikucheza naye mpaka kukabwerera kunjira, ndipo akapanda kuperekezedwa amaona kuti sanalandiridwe bwino.”

Nthawi zina anthu amadyera chakudya m’mbale imodzi ndi manja. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti anthuwo ndi ogwirizana. Nthawi zina, kudyera chakudya mbale imodzi kumathandiza kuti anthu omwe anasiya kuchezerana ayambirenso kugwirizana. Akamadyera limodzi amakhala ngati akunena kuti, “Basi takhululukirana.”

DZIWANI IZI

  • Kuli anthu okwana: Pafupifupi 20 miliyoni

  • Likulu lake: Yaoundé

  • Nyengo: Kumpoto kwa dzikolo n’kouma komanso kumatentha, ndipo kumadera a m’mphepete mwa nyanja kumakhala kotentha ndi kwa chinyontho

  • Zimene amagulitsa kumayiko ena: Mafuta, Cocoa, Khofi, Thonje, Matabwa ndi Aluminiyamu

  • Zilankhulo: Chingelezi ndi Chifulenchi, komanso kuli zinenero zina pafupifupi 270

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena