Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/14 tsamba 12-13
  • Dziko la Cambodia

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Cambodia
  • Galamukani!—2014
Galamukani!—2014
g 4/14 tsamba 12-13
Minda ya mpunga ku Cambodia

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Cambodia

Mapu a dziko la Cambodia

M’DZIKO la Cambodia muli nyumba, misika komanso misewu yambiri zimene anazimanga pamwamba pa madzi. M’misewuyi mumadzadza njinga zamoto zimene zimanyamula zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo nkhuku komanso mafiriji kuchoka nazo kwina kupita kwina.

Anthu a ku Cambodia amadziwika kuti ndi ansangala, okonda kucheza komanso amakonda kuchitira limodzi zinthu. Amakonda kutchulana kuti achimwene, chemwali, azakhali, amalume kapena agogo, ndipo amachita zimenezi ngakhale kwa munthu amene angokumana naye koyamba.

Nyumba zomangidwa pamathandala m’madzi

Anthu ena a ku Cambodia amakhala m’nyumba zangati maboti ndipo ena amakhala m’nyumba zomwe anazimanga pamathandala akuluakulu. M’dzikoli mumapezekanso sukulu, zipatala, misika komanso malo othirira mafuta, zomangidwa pamathandala

Zipatso zomwe zimapezeka ku Cambodia

Zipatso zimene zimapezeka zambiri ku Cambodia

Anthu a m’dzikoli amakonda mpunga. Nthawi zambiri pa chakudya pamakhala mpunga, ndiwo zamitundu iwiri ndi msuzi. Ndiwo zimene amakonda kwambiri ndi nsomba. Kawirikawiri, amadya zakudya zophikidwa mosiyanasiyana zingapo, pa nthawi imodzi.

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, amalonda a ku India komanso anthu oyendera zachipembedzo ochokera ku China, anayamba kubwera ku Cambodia kudzachita malonda osinthanitsa nsalu komanso zitsulo, ndipo ankazisinthanitsa ndi matabwa, minyanga ya njovu komanso golide. Patapita nthawi, anthu a ku Cambodia anayamba kutengera zikhalidwe za anthu a ku India ndi a ku China. Chifukwa cha zimenezi ambiri anakhala Ahindu ndi Abuda. Masiku ano anthu ambiri a ku Cambodia ndi Abuda.

A Mboni za Yehova amalalikira uthenga wa m’Baibulo kwa anthu a ku Cambodia. Athandiza anthu ambiri pogwiritsa ntchito buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Bukuli likupezeka m’zinenero pafupifupi 250, kuphatikizapo Chikambodiya.

A Mboni za Yehova akuuza munthu wa ku Cambodia uthenga wa m’Baibulo

Anthu oposa 1,500 akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo zimenezi zawathandiza kupeza mayankho a mafunso monga akuti, “Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?” Komanso “Kodi Mulungu analengeranji dzikoli?”

MFUNDO ZACHIDULE

  • Kuli anthu okwana: 14 miliyoni

  • Likulu: Phnom Penh

  • Nyengo yake: N’kotentha ndipo miyezi ina kumatentha kwambiri komanso kumagwa mvula

  • Zinthu zimene amagulitsa kunja: Zovala, matabwa, labala ndi mpunga

Buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? la m’Chikambodiya

Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova likupezekanso m’Chikambodiya ndipo ndi limene likuoneka apali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena