Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/14 tsamba 14-15
  • Dziko la Italy

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Italy
  • Galamukani!—2014
Galamukani!—2014
g 1/14 tsamba 14-15
Chigwa cha dziko la Italy

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Italy

Mapu a dziko la Italy

MBALI ina ya dziko la Italy ndi yamapiri ndipo mbali ina ndi m’mbali mwa nyanja. Kum’mwera kwa dzikoli kumatentha, pamene kumpoto kwake ndi kozizira kwambiri. Mapiri ambiri a m’dzikoli ndi oti akhoza kuphulika n’kutulutsa ziphalaphala zapansi panthaka komabe ochepa okha, monga phiri la Stromboli ndi la Etna, ndi amene nthawi zambiri amaphulika.

Dziko la Italy ndi limodzi mwa mayiko amene kuli anthu ambiri ku Ulaya. M’dzikoli mumapezeka anthu monga Aluya, Agiriki, Afoinike ndi enanso.

M’dzikoli muli zinthu zakale zambiri zochititsa chidwi. M’mizinda ndi m’matauni ambiri mumapezekabe zomangamanga zakale za Agiriki ndi Aroma. Zinthu monga zithunzi, zipilala za mabo komanso akasupe a madzi, ndi zina mwa zimene zimakumbutsa anthu a m’dzikoli za akatswiri ena monga Bernini, Michelangelo ndi Raphael.

Anthu okaona malo akwera mabwato

Anthu okaona malo m’dzikoli amakonda kukwera mabwato akakhala mumzinda wa Venice

Anthu a m’dzikoli amakonda chakudya chosiyanasiyana ndipo chikhalidwe chilichonse chimadziwika ndi kaphikidwe kawo ka chakudya. Anthu ambiri amakonda chakudya chotchedwa pasta ndipo nthawi zambiri amadyera nyama kapena nsomba, ndi masamba. Mafuta a maolivi amagwiritsidwanso ntchito kwambiri chifukwa amapangidwa m’dziko lomweli. Anthu enanso a m’dzikoli amakonda chakudya chotchedwa pizza komanso risotto.

Chakudya chotchedwa pasta

Anthu ambiri a ku Italy amakonda chakudya chotchedwa Pasta

Anthu a ku Italy ndi okonda kuchereza alendo, ansangala komanso okonda kucheza. Anthu a m’dzikoli amakonda kuuza anthu ena nkhani zawo moti si zachilendo kuona anthu akucheza m’malo opezeka anthu ambiri kapena kukambirana nkhani uku akuyenda.

Anthu ambiri a ku Italy amati ndi Akatolika, koma ndi ochepa okha amene amapita kutchalitchi. Anthu ambiri asiya kutsatira zimene tchalitchichi chimaphunzitsa komanso asiya kutsatira mfundo zimene tchalitchichi chakhala chikuyendera kwa zaka zambiri monga zokhudza kuchotsa mimba komanso kuthetsa ukwati.

A Mboni za Yehova akuchuluka ku Italy. A Mboniwa amadziwika ndi kuphunzitsa anthu Baibulo komanso kuti amayesetsa kutsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. M’dzikoli muli mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 3,000, ndipo yambiri ya mipingo imeneyi imalalikira anthu amene amalankhula zinenero zina kuwonjezera pa Chitaliyana. Pa zaka 10 zapitazi, chiwerengero cha anthu ochokera m’mayiko ena kupita ku Italy chawonjezeka kwambiri ndipo izi zikusonyezeratu kuti pakufunikadi kuti anthuwa aziphunzitsidwa Baibulo m’zinenero zawo.

Mapiri a Dolomites

Dera la mapiri a Dolomites, lomwe lili kumpoto chakum’mawa kwa dziko la Italy

KODI MUKUDZIWA?

Ngakhale kuti mzinda wa Vatican uli ku Rome, kuyambira mu 1929 umaonedwa ngati dziko la palokha ndipo anthu a ku Italy amaona kuti anthu a mumzinda umenewu si a m’dziko lawo.

MFUNDO ZACHIDULE

  • Kuli anthu okwana: 61 miliyoni

  • Likulu lake: Rome

  • Nyengo: Kum’mwera kwa dzikoli kuli nyanja ya Mediterranean ndiponso ndi kotentha ndipo nyengo yotenthayi imakhala yaitali. Kumpoto kwa dzikoli kuli mapiri ambiri ndipo nyengo yake ndi yozizira

  • Dera lake: Kuli mapiri ambiri ndipo dera lokwana makilomita 7,500 lili m’mbali mwa nyanja

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena