-
Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Munthu Zikumuyenderadi?Galamukani!—2014 | October
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO
Kodi Mumaonera Chiyani Kuti Munthu Zikumuyendera?
PALIBE munthu amene amasangalala zinthu zikakhala kuti sizikumuyendera. Koma zimakhalanso zopanda phindu ngati munthu akungoganiza kuti zinthu zikumuyendera pomwe sizikumuyendera. Chifukwatu munthu akazindikira kuti zinthu sizikumuyendera, akhoza kuganizira zimene angachite komanso kuphunzira pa zimene akulakwitsa kuti zinthu ziyambe kumuyenderadi.
Koma n’zosiyana ndi zimene zimachitika ngati munthu akungoganiza kuti zinthu zikumuyendera bwino. Chifukwatu akhoza kumaganiza kuti zonse zili bwino koma zisali bwino, ndipo akamadzazindikira kuti akufunika kusintha, zimakhala zitaipiratu.
Taganizirani zimene Yesu ananena. Iye anati: “Kodi munthu angapindulenji ngati atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?” (Mateyu 16:26) Anthu amene amangokhalira kugwira ntchito n’cholinga choti apeze ndalama zambiri komanso zinthu zapamwamba, angachite bwino kuganizira mawu a Yesuwa. Anthu oterewa angaganize kuti zinthu zikuwayendera bwino, koma zisali choncho. Munthu wina wolangiza anthu za ntchito, dzina lake Tom Denham, anati: “Munthu amene amangoganizira za kukwezedwa pa ntchito, kupeza ndalama zambiri kapena kukhala ndi antchito ochuluka, sakhala wosangalala. Munthu akamaganiza kuti zinthu zikumuyendera poona kuchuluka kwa ndalama zimene ali nazo, amakhala akungodzinamiza. Zili choncho chifukwa chakuti pakapita nthawi amaona kuti ndalama zakezo sizikumuthandiza kukhala wosangalala.”
Anthu ambiri masiku ano amaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Mwachitsanzo, pa kafukufuku wina amene anachitika ku United States, anthu anauzidwa kuti alembe “zinthu 22 zimene zimasonyeza kuti munthu zikumuyendera bwino.” Ambiri anaika “kukhala ndi ndalama zambiri” pa nambala 20. Zinthu zimene anthu ambiri ananena kuti n’zofunika kwambiri zinali, kukhala ndi thanzi labwino, kukhala bwino ndi anthu komanso kugwira ntchito imene umaikonda.
Apa n’zoonekeratu kuti anthu ambiri akafunsidwa amatha kusiyanitsa pakati pa munthu amene akungoganiza kuti zinthu zikumuyendera bwino, ndi amene zikumuyenderadi. Komabe anthu ambiri zimawavuta kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhaniyi.
-
-
Ndani Amene Mungati Zinthu Zikumuyenderadi?Galamukani!—2014 | October
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMAONERA CHIYANI KUTI MUNTHU ZIKUMUYENDERA?
Ndani Amene Mungati Zinthu Zikumuyenderadi?
Kuti muone ngati mumadziwadi munthu amene zikumuyendera bwino kapena ayi, taganizirani zitsanzo zotsatirazi.
Pa anthu otsatirawa ndi ndani amene mungati zinthu zikumuyenderadi?
ALEX
Alex ali ndi bizinezi yaikulu, ndi wolimbikira ntchito, amachita zinthu moona mtima komanso ndi waulemu. Bizinezi yake ikuyenda bwino ndipo iye ndi banja lake amakhala mosangalala.
CAL
Cal nayenso ali ndi bizinezi yaikulu ndipo amapeza ndalama zambiri kuposa Alex. Kuti azipeza phindu lochuluka amangokhalira kugwira ntchito ndipo zimenezi zimam’pangitsa kuti azidwala matenda osiyanasiyana.
JANET
Janet amalimbikira kwambiri sukulu komanso amakonda kuphunzira zinthu. Chifukwa cha zimenezi iye amakhoza bwino m’kalasi.
ELLEN
Ellen nayenso ali pa sukulu ndipo amakhoza bwino kuposa Janet moti amaonedwa kuti ali m’gulu la ana anzeru kwambiri ku sukulu yawo. Koma Ellen amaonera mayeso ndipo sakonda kwenikweni maphunziro.
Kodi mukuona kuti Cal ndi Ellen ndi omwe zikuwayendera? Kapena mukuona kuti anthu 4 onsewa zikuwayendera bwino? Ngati mukuona choncho, ndiye kuti mumaona kuti munthu zikumuyendera pongoona zimene akukwanitsa kuchita osaganizira zomwe akuchita kuti akwanitse zinthuzo.
Koma ngati mukuona kuti Alex ndi Janet ndi omwe zikuwayendera bwino, ndiye kuti mumaona kuti munthu zikumuyendera poona khalidwe lake, ngati amachita zinthu molimbikira komanso ngati amachita zinthu moyenera. Ndipotu zimenezi n’zomveka. Mwachitsanzo taganizirani izi:
Kodi n’chiyani chimene chingadzamuthandize Janet? Kodi ndi kukhoza kwambiri m’kalasi kapena mtima wokonda kuphunzira zinthu?
• Kodi n’chiyani chingathandize kuti ana a Alex azikhaladi osangalala? Zinthu zodula zimene bambo awo angawagulire kapena kukhala ndi bambo amene amapeza nthawi yocheza nawo komanso kuchita nawo zinthu zina?
Mfundo yofunika kwambiri ndi yoti: Si bwino kuganiza kuti munthu zikumuyendera pongoona zimene akukwanitsa kuchita. Tingadziwe kuti munthu zikumuyendera poona khalidwe lake, ngati amachita zinthu molimbikira komanso ngati amachita zinthu moyenera.
-
-
Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?Galamukani!—2014 | October
-
-
NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMAONERA CHIYANI KUTI MUNTHU ZIKUMUYENDERA?
Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?
Baibulo limatithandiza kudziwa zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino. Siliphunzitsa kuti anthu ochepa okha amwayi ndi amene zinthu zimawayendera bwino. Silinenanso kuti munthu zinthu zikhoza kuyamba kumuyendera bwino ngati atayesetsa kupeza zinthu zonse zimene amalakalaka. Anthu ambiri amakhala ndi maganizo amenewa chifukwa choti ali mwana anaphunzitsidwa zimenezi. Koma pambuyo pake amazindikira kuti zimenezi si zoona ndipo amagwiritsidwa fuwa lamoto.
Koma zoona ndi zoti munthu aliyense zinthu zikhoza kumamuyendera bwino, kungoti pamafunika khama. Taonani mfundo zotsatirazi.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
“Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.”—Mlaliki 5:10.
ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Kukhala ndi katundu wambiri sikuchititsa kuti munthu akhale wosangalala. Anthu amene ali ndi zinthu zambiri ndi amenenso amakhala osasangalala. Wolemba mabuku wina, dzina lake Jean M. Twenge, analemba m’buku lake lina kuti: “Anthu amene cholinga chawo chachikulu n’kufuna kulemera, nthawi zambiri amakhala ndi nkhawa ndipo amadwala matenda amaganizo kuposa anthu amene amaona kuti chofunika kwambiri n’kukhala bwino ndi ena.” Ananenanso kuti: “Kafukufuku amasonyeza kuti kukhala ndi ndalama zambiri sikuchititsa munthu kukhala wosangalala. Ngakhale munthu amene ali ndi zinthu zochepa pa moyo wake, akhoza kukhala wosangalala.”—Generation Me.
ZIMENE MUNGACHITE. Musamangokhalira kufunafuna ndalama kapena katundu wambiri. M’malomwake, ganizirani zinthu zimene zingakuthandizeni kukhala wosangalala ndipo muzichita zimenezo. Yesu anati: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”—Luka 12:15.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
“Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.”—Miyambo 16:18.
ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Kunyada komanso kuchita zinthu modzionetsera sikungakuthandizeni kukhala wosangalala. Buku lina linanena kuti makampani omwe amayenda bwino, mabwana ake “amakhala odzichepetsa komanso sachita zinthu modzionetsera. Pomwe makampani omwe mabwana ake ndi odzikuza komanso onyada, sayenda bwino mwinanso amatha kumene.” (Good to Great) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Munthu akakhala wodzikuza kapena wonyada, zinthu sizimuyendera bwino.
ZIMENE MUNGACHITE. M’malo mofuna kutchuka, yesetsani kukhala wodzichepetsa. Baibulo limati: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero, akudzinyenga.” (Agalatiya 6:3) Izi zikusonyeza kuti kutchuka si chizindikiro choti munthu zikumuyendera bwino.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
“Kwa munthu, palibe chabwino kuposa . . . kusangalatsa mtima wake chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.”—Mlaliki 2:24.
ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Mukakhala ndi chizolowezi chogwira ntchito mwakhama, mumasangalala ndi ntchito yanu. Wolemba mabuku wina, dzina lake Madeline Levine, analemba m’buku lake lina kuti: “Munthu amene zinthu zimamuyendera bwino pa ntchito ndi amene amagwira bwino ntchito yakeyo. Ndipo kuti munthu azigwira bwino ntchito yake, amafunika kukhala wakhama komanso wolimbikira.” (Teach Your Children Well) Munthu wotereyu amathanso kupirira akakumana ndi mavuto pa ntchito yakeyo.
ZIMENE MUNGACHITE. Yesetsani kuidziwa bwino ntchito yanu ndipo mukakumana ndi mavuto musamafooke. Ngati muli ndi ana, aphunzitseni kudziwa zimene angachite akakumana ndi mavuto. Muzichita zimenezi mogwirizana ndi msinkhu wa anawo. Akakhala ndi vuto, musathamangire kuwathandiza. Asiyeni kuti ayese kuthana nalo okha. Ana akadziwa mmene angathetsere mavuto, amakhala osangalala komanso amaphunzira kuchita zinthu zomwe zingadzawathandize m’tsogolo.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
“Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.”—Mlaliki 9:4.
ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Ngati mumagwira ntchito yolembedwa, muziiona kuti ndi yofunika pa moyo wanu koma sikuti maganizo anu onse azingokhala pa ntchitoyo. N’kutheka kuti ku ntchito kwanu muli ndi udindo waukulu komanso amakudalirani. Koma mwina mumadzipanikiza kwambiri ndi ntchitoyo ndipo izi zikuchititsa kuti muzidwala matenda osiyanasiyana komanso kuti musamapeze nthawi yochita zinthu zina ndi banja lanu. Kodi pamenepa munganene kuti zinthu zikukuyenderanidi bwino? Munthu amafunika kuti azikhala ndi nthawi yogwira ntchito, yosamalira thanzi lake komanso yochita zinthu zina ndi banja lake. Munthu yemwe akukwanitsa kuchita zimenezi ndi amene tingati zinthu zikumuyenderadi bwino.
ZIMENE MUNGACHITE. Muzisamalira thanzi lanu ndipo muzipuma mokwanira. Palibe chimene munthu angapindule ngati amangokhalira kugwira ntchito n’kumalephera kupeza nthawi yosamalira thanzi lake, yochita zinthu zina ndi banja lake komanso yocheza ndi anzake. Munthu amene amangokhalira kugwira ntchito, angaoneke ngati zinthu zikumuyendera, koma zimenezi si zoona.
ZIMENE BAIBULO LIMANENA:
“Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.
ZIMENE LEMBALI LIKUTANTHAUZA. Kuphunzira Baibulo komanso kutsatira mfundo zake kungakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino. A Mboni za Yehova amaona kuti kupeza nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu kumawathandiza kuchepetsa nkhawa kusiyana ndi kufuna kupeza zinthu zambirimbiri.—Mateyu 6:31-33.
ZIMENE MUNGACHITE. Phunzirani Baibulo kuti mudziwe mmene lingakuthandizireni kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Kuti mudziwe zambiri, funsani a Mboni za Yehova a kudera lanulo, kapena pitani pa webusaiti yathu ya www.pr418.com.
-