Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/15 tsamba 8-9
  • Dziko la Honduras

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Honduras
  • Galamukani!—2015
Galamukani!—2015
g 4/15 tsamba 8-9
Dziko la Honduras lomwe lili m’mbali mwa nyanja

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Honduras

Mapu a dziko la Honduras

DZINA lakuti “Honduras” ndi lachisipanishi ndipo limatanthauza “kuya.” Dziko la Honduras lili m’mphepete mwa nyanja ya Atlantic. Zikuoneka kuti Christopher Columbus ankagwiritsa ntchito mawu akuti “Hondurus” ponena za kuya kwa madzi a m’nyanjayi. Anthu ena amanena kuti apa m’pamene dzina la dzikoli linachokera.

Anthu a ku Honduras amakhala okhulupirika m’banja komanso ogwirizana. Mwamuna ndi mkazi wake asanasankhe zochita, amakambirana kaye n’kugwirizana. Mwachitsanzo amakambirana pa nkhani zokhudza mmene azigwiritsira ntchito ndalama pakhomo pawo komanso sukulu zomwe angatumizeko ana awo.

Anthu ambiri a ku Honduras ndi Amesitizo. Makolo a Amesitizo ndi ochokera ku Europe ndi ku Honduras komweko. M’dzikoli mumapezekanso anthu otchedwa a Chortí ndipo iwowa ndi amene anali oyamba kukhala m’dzikoli. Kulinso anthu ena otchedwa Agarifuna amene makolo awo anali akuda komanso amwenye.

Munthu wachigarifuna akuimba ng’oma

Munthu wachigarifuna akuimba ng’oma

Poyamba makolo a Agarifuna ankakhala pachilumba chotchedwa St. Vincent. Mu 1797, Agarifuna anafika pazilumba za Bay. Kenako anakhazikika m’mbali mwa nyanja kudera lotchedwa Caribbean. Patapita nthawi, Agarifuna anafalikira m’chigawo chapakati ndi kumpoto kwa America.

Agarifuna amavina magule osiyanasiyana ndipo povina magulewa amaimba ng’oma. Amakondanso zovala zowala komanso kufotokozerana nkhani. Amakonda chakudya chotchedwa ereba, chomwe ndi keke yopyapyala yopangidwa ndi ufa wa chinangwa.

Ku Honduras kuli mipingo 400 ya Mboni za Yehova. Misonkhano yawo imachitika m’Chigarifuna, m’Chimandarini cha ku China, m’Chimisikito, m’chinenero chamanja cha ku Honduras, m’Chingelezi ndi m’Chisipanishi.

Chakudya chotchedwa ereba

Chakudya chotchedwa ereba chopangidwa ndi ufa wa chinangwa

MFUNDO ZACHIDULE

  • Chiwerengero cha anthu: 8,111,000

  • Likulu lake: Tegucigalpa

  • Boma: Demokalase

  • Chinenero: Chisipanishi

  • Nyengo: Kumatentha komanso kumagwa mvula yambiri. M’madera a m’mapiri kumakhala nyengo yozizirako

  • Dera lake: Mbali yaikulu ya dzikoli kuli mapiri. M’dzikoli mulinso zigwa ndi zilumba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena