Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/15 tsamba 12-13
  • Dziko la Nicaragua

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Nicaragua
  • Galamukani!—2015
Galamukani!—2015
g 9/15 tsamba 12-13
Chilumba cha Ometepe chomwe chinapangidwa ndi kuphulika kwa mapiri awiri omwe ali m’nyanja ya Nicaragua

Nyanja ya Nicaragua imadziwika kwambiri chifukwa cha chilumba chokongola cha Ometepe chomwe chili ndi mapiri awiri omwe amaphulika

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Nicaragua

Mapu a dziko la Nicaragua

NICARAGUA ndi dziko lomwe lili ndi nyanja zambiri komanso kumakonda kuphulika mapiri. Dziko la Nicaragua ndi limene lili ndi nyanja yaikulu kwambiri ku Central America konse. Anthu a m’dzikoli amatchula nyanjayo kuti Cocibolca kutanthauza nyanja ya madzi okoma. M’nyanja ya Nicaragua muli zilumba zambiri ndipo ndi nyanja yokhayo imene ndi yopanda mchere yomwe mumapezeka nsomba za m’nyanja zikuluzikulu monga shaki.

Maluwa a ku Nicaragua omwe amawatchula kuti sacuanjoche

Maluwa a ku Nicaragua omwe amawatchula kuti sacuanjoche

Ku Nicaragua kuli dera linalake lakutali kwambiri lomwe amalitchula kuti Mosquito Coast. Derali lili m’mbali mwa nyanja komanso ndi lalikulu makilomita 65 ndipo limakafika ku Honduras, dziko lomwe linachita malire ndi Nicaragua. Ku Mosquito Coast kumakhala anthu amtundu wa Miskito ndipo anthu amenewa anabwera kale kwambiri m’dzikoli moti pamene anthu amitundu ina ankafika m’dzikoli cha m’ma 1500, anachita kuwapeza.

Amiskito ndi anthu ogwirizana kwambiri komanso ali ndi chikhalidwe chosiyana kwambiri ndi ena. M’chinenero cha Chimesikito mulibe mawu ena omwe anthu amatchula pofuna kulemekeza munthu. Mwachitsanzo m’madera a kumidzi, ana amatchula munthu wamwamuna kuti “Ankolo” ndipo wamkazi amangoti “Anti,” kaya anthuwo atakhala achibale awo kapena ayi. Kuyambira kale, azimayi a mtundu wa Miskito amapatsana moni pogunditsana masaya. Akangogunditsana masayawo, mzimayi amene anayamba kupereka moniyo amapuma mokoka mpweya.

Anthu a ku Nicaragua

Anthu a ku Nicaragua

Mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo olembedwa mu chinenero cha Chimayanya ndi Chimesikito

Mabuku a Mboni za Yehova ofotokoza nkhani za m’Baibulo olembedwa m’chinenero cha Chimayanya ndi Chimesikito

MFUNDO ZACHIDULE

  • Chiwerengero cha anthu: 6,176,000

  • Chinenero chachikulu: Chisipanishi. Komabe kumadera ena akutali amalankhula zinenero monga Chimesikito, Chimayanya, Chirama ndi Chingelezi cha Chikiliyo

  • Boma: Demokalase

  • Likulu: Managua

  • Nyengo: N’kotentha, koma kumadera okwera kumakhala kozizira

  • Dera lake: Madera a m’mbali mwa nyanja ndi otsika, koma mkatikati mwa dzikoli muli mapiri

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi ndi ziti zomwe zili zoona ponena za dziko la Nicaragua?

  1. Dzina la dzikoli linachokera kwa munthu wina dzina lake Nicarao. Munthuyu anali mtsogoleri wa fuko linalake zaka zambiri m’mbuyomo.

  2. Dzikoli ndi lokhalo m’chigawo cha Latin America, lomwe linalamuliridwapo ndi dziko la Spain ndi Britain.

  3. Zaka zambiri zapitazo, zigawenga zapanyanja zochokera ku Caribbean zinkabwera kudzabera anthu omwe ankakhala m’mizinda yomwe inali m’mbali mwa nyanja ya Nicaragua.

  4. Ku Nicaragua n’kumene kuli anthu ochepa kwambiri poyerekeza ndi madera ena a ku Central America.

Mayankho: Zonsezi ndi zolondola.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena