Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 1/15 tsamba 7
  • Chisa cha Njuchi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chisa cha Njuchi
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2015
  • “Dziko Loyenda Mkaka ndi Uchi”
    Nsanja ya Olonda—2011
Galamukani!—2015
g 1/15 tsamba 7
Njuchi zili pa chisa

KODI ZINANGOCHITIKA ZOKHA?

Chisa cha Njuchi

NJUCHI zimamanga zisa za uchi pogwiritsa ntchito phula lomwe limatuluka pansi pa mimba zawo. Akatswiri amaona kuti zisazi zimapangidwa mwaluso zedi. N’chifukwa chiyani amaona choncho?

Taganizirani izi: Njuchi zimapanga zisa za uchi zomwe zimakhala ndi timabowo ta makona 6. Kwa zaka zambiri, akatswiri a masamu akhala akuona kuti zinthu za makona 6 zikasanjidwa, siziwononga malo ambiri poyerekezera ndi zinthu za makona atatu kapena 4. Akhalanso akuona kuti zinthu za makona 6 zimakhala zolimba komanso siziwononga zipangizo zambiri zomangira. Koma sankafotokoza bwinobwino chimene chimachititsa zimenezi. Mu 1999, pulofesa wina, dzina lake Thomas C. Hales, anachita masamu ndipo anapeza umboni wosonyeza kuti zinthu zokhala ndi makona 6 sizithadi malo komanso zimakhala zolimba.

Popeza njuchi zimapanga zisa za uchi mwanjira imeneyi, zimatha kusunga uchi wambiri pamalo ochepa. Zimathanso kumanga zisa zawo pogwiritsa ntchito phula lochepa. Choncho n’zosadabwitsa kuti akatswiri ambiri amaona kuti chisa cha uchi chimapangidwa mogometsa kwambiri.

Masiku ano, asayansi akutengera mmene njuchi zimamangira zisa zawo. Mwachitsanzo, akufuna kugwiritsa ntchito njirayi popanga ndege zolimba kwambiri koma zopepuka. Akuganiza kuti zimenezi zingapangitse kuti ndegezo zisamawononge mafuta ambiri.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti njuchi zizimanga zisa mwaukatswiri chonchi, kapena pali winawake amene anazilenga kuti zizichita zimenezi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena