Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?
    Galamukani!—2015 | July
    • Munthu ali kuntchito koma akuganizira mavuto ake

      NKHANI YA PACHIKUTO

      Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?

      KODI muli wachinyamata munali ndi zolinga ziti? Mwina munkafuna kukhala pa banja, kukhala ndi luso linalake kapena kugwira ntchito inayake. Koma nthawi zina zinthu siziyenda mmene tinkaganizira. Mavuto ena angasokoneze kwambiri moyo wathu. Izi n’zimene zinachitikira anthu atatu amene akuoneka m’munsimu.

      Anja, Delina, ndi Gregory
      • Woyamba ndi mayi wina wa ku Germany dzina lake Anja. Iye anapezeka ndi khansa ali ndi zaka 21 ndipo panopa amangokhala pakhomo.

      • Wachiwiri ndi mayi wina wa ku United States dzina lake Delina. Iye amadwaladwala komanso amasamalira azichimwene ake atatu olumala. Wachitatu ndi bambo wina wa ku Canada dzina lake Gregory. Iye amavutika kwambiri ndi nkhawa.

      • Koma onsewa amadziwa zochita ndi mavuto awo. Kodi iwo amatani?

      Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miyambo 24:10) Choncho nkhani yagona pa mmene timaonera mavuto athu. Anthu ena akakumana ndi mavuto amangogwa ulesi. Koma anthu amene amaona mavuto awo moyenera savutika kudziwa zochita.

      Tiyeni tione zimene Anja, Delina ndi Gregory amachita.

  • Vuto Limene Limakhalapo: Zinthu Zina Simungazisinthe
    Galamukani!—2015 | July
    • Anja akucheza ndi anzake pa tabuleti

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?

      Vuto Limene Limakhalapo: Zinthu Zina Simungazisinthe

      KODI panopa mukuvutika chifukwa cha matenda aakulu, kutha kwa banja kapena kuferedwa? Munthu akakumana ndi mavuto ngati amenewa amasowa chochita koma amafuna zinthu zitasintha. Ndiye kodi mungatani?

      CHITSANZO CHA M’BAIBULO: PAULO

      Mtumwi Paulo anali mmishonale wakhama ndipo ankayenda m’madera osiyanasiyana. Koma zinthu zinasintha pamene anamangidwa n’kumalonderedwa ndi asilikali kwa zaka ziwiri. M’malo motaya mtima, Paulo anaganizira zimene angathe kuchita. Iye ankaphunzitsa ndiponso kulimbikitsa anthu amene ankabwera kudzamuona. Analembanso makalata angapo amene ali m’Baibulo.—Machitidwe 28:30, 31.

      ZIMENE ANJA AMACHITA

      Paja tanena kale kuti Anja amangokhala pakhomo. Ndiyeno iye anati: “Matenda a khansa asokoneza kwambiri moyo wanga. Ngati nditayenda ndikhoza kudwala kwambiri, choncho sindipita kuntchito kapena kocheza.” Kodi Anja amatani ndi vuto lakeli? Iye anati: “Ndinangosintha zochita pa moyo wanga. Ndinaganizira zofunika kwambiri n’kulemba ndandanda ya zimene ndingakwanitse kuchita. Zimenezi zandithandiza kwambiri.”

      “Ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo.”—Izi n’zimene Paulo ananena pa Afilipi 4:11

      ZIMENE MUNGACHITE

      Ngati vuto lanu ndi loti simungalisinthe, yesani kuchita izi:

      • Ganizirani zimene mungathe kuchita. Mwachitsanzo, ngati muli ndi matenda, mwina mungathe kumachitabe masewera olimbitsa thupi, kudya chakudya chabwino komanso kupuma mokwanira

      • Khalani ndi zolinga pa moyo wanu. Zolingazo muziike m’zigawo zing’onozing’ono. Ndiyeno tsiku lililonse muzichita zochepa mpaka mudzazikwaniritse.

      • Muziyesetsa kuchita zinazake ngakhale zing’onozing’ono kuti mumtima muzimva kuti mwapanga kenakake. Mwachitsanzo, mungayeretse tebulo, kutsuka mbale kapena kudzisamalira bwinobwino. Muziyesetsa kuchita zinthu zofunika kwambiri chakum’mawa.

      • Ganizirani zabwino zimene mungachite chifukwa cha mavuto anuwo. Mwachitsanzo, panopa mukhoza kumvetsa ndiponso kuthandiza anthu amene akukumana ndi mavuto ngati anuwo.

      Mfundo Yofunika: Mavuto ena simungawasinthe koma mukhoza kusintha zimene mumachita mukakumana ndi mavutowo.

  • Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika
    Galamukani!—2015 | July
    • Delina akusamalira maluwa

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?

      Vuto Limene Limakhalapo: Kupanikizika

      MWINA simunkayembekezera kuti moyo wanu udzakhala mmene ulili panopa. N’kutheka kuti mumapanikizika chifukwa chosamalira banja, kugwira ntchito ndiponso kusamalira makolo amene akudwala. Koma mukuonanso kuti si bwino kuchita zonse zimene anthu ena angafune ndipo mwina simungakwanitse. Ndiyeno kodi mungatani?

      CHITSANZO CHA M’BAIBULO: MOSE

      Poyamba Mose ankaweruza yekha Aisiraeli ndipo mwina ankaona kuti ndi udindo wake. Koma apongozi ake anamuuza kuti: ‘Imene ukutsatirayi si njira yabwino. Ndithu utopa nazo zimenezi.’ Apongozi akewo anamuuza kuti apeze amuna oyenerera amene angathandize kuti nkhani zovuta kwambiri zokha zizibwera kwa Mose. Ndiyeno anamutsimikizira kuti: “Udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kumahema awo mu mtendere.”—Ekisodo 18:17-23.

      ZIMENE DELINA AMACHITA

      Monga tanenera m’nkhani yoyamba ija, Delina amadwaladwala komanso amasamalira azichimwene ake atatu olumala. Iye anati: “Sindidera nkhawa za mawa ndipo sindizengereza kuchita zinthu. Izi zimandithandiza kuti ndisamapanikizike. Ndimauzanso anthu momasuka zimene ndikuvutika nazo. Choncho mwamuna wanga komanso anthu ena amandithandiza. Tsiku lililonse ndimapezanso nthawi yochepa yosamalira maluwa chifukwa zimandisangalatsa.”

      “Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1

      ZIMENE MUNGACHITE

      Ngati mumapanikizika kwambiri, yesani izi:

      • Mungapemphe ena kuti azikuthandizani. Mwachitsanzo, mungapemphe ana anu, achibale kapena anzanu amene amakhala pafupi.

      • Muziuza anthu ena mavuto anu. Mwachitsanzo, mungakambirane ndi abwana anu ngati akukupanikizani. Mwina mukawafotokozera mavuto anu, akhoza kukuchepetserani ntchito.

      • Lembani zinthu zonse zimene muyenera kuchita mlungu uliwonse. Kodi pali zinthu zina zimene anthu ena angakuchitireni?

      • Mukaitanidwa kocheza ganizani bwino musanavomere. Ngati mulibe nthawi yokwanira kapena mwatopa, mungokana mwaulemu.

      Mfundo Yofunika: Mukamayesa kuchita zonse nokha mukhoza kulephera kuchita chilichonse.

  • Vuto Limene Limakhalapo: Kukhala Wosasangalala
    Galamukani!—2015 | July
    • Gregory akuona zinthu zosangalatsa m’chilengedwe

      NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?

      Vuto Limene Limakhalapo: Kukhala Wosasangalala

      KODI nthawi zambiri mumakhala okhumudwa kapena okwiya? Ngati ndi choncho, mukhoza kulephera kuchita zinthu zofunika kwambiri. Ndiyeno kodi mungatani?a

      CHITSANZO CHA M’BAIBULO: DAVIDE

      Nthawi zina Mfumu Davide ankada nkhawa kapena kumva chisoni. Kodi n’chiyani chinkamuthandiza? Iye ankasiya mavuto ake m’manja mwa Mulungu. (1 Samueli 24:12, 15) Davide ankalembanso mmene ankamvera mumtima mwake. Iye anali ndi chikhulupiriro ndipo ankakonda kupemphera.b

      ZIMENE GREGORY AMACHITA

      M’nkhani yoyamba ija tanena kuti Gregory amavutika kwambiri ndi nkhawa. Iye anati: “Vuto langa loda nkhawa linafika poipa kwambiri.” Kodi n’chiyani chinamuthandiza pa vuto lake? Gregory anati: “Ndinalola kuthandizidwa ndi mkazi wanga komanso anzanga. Ndinapitanso kuchipatala ndipo anandithandiza kumvetsa bwino vuto langali. Ndiyeno nditasintha zochita pa moyo wanga, ndinayamba kupezako bwino. Nthawi zina ndimavutikabe koma ndimazindikira chimene chayambitsa ndipo ndimadziwa zimene zingandithandize.”

      “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa.”—Miyambo 17:22

      ZIMENE MUNGACHITE

      Ngati mumakhala osasangalala, yesani izi:

      • Muzilemba mmene mukumvera mumtima mwanu.

      • Muzifotokozera m’bale wanu kapena mnzanu zimene zikukuvutani.

      • Muzikhala pansi n’kuona ngati palidi chifukwa chokhalira osasangalala. Mwachitsanzo, ngati mukudziona kuti ndinu wolephera, mungadzifunse kuti: ‘Kodi pali umboni wakuti ndinedi wolephera?’

      • c

      Mfundo Yofunika: Nthawi zambiri timakhumudwa kapena kuda nkhawa chifukwa cha mmene tikuonera vuto lathu osati chifukwa cha vuto lenilenilo.

      a Nthawi zina mavuto amene tatchulawa amabwera chifukwa cha matenda moti mungafunike kupita kuchipatala. Koma Galamukani! siuza anthu zochita pa nkhani zoterezi. Aliyense ayenera kusankha yekha zochita pambuyo poganizira bwino nkhanizi.

      b Masalimo ambiri a m’Baibulo anali mapemphero amene Davide analemba.

      c Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani zoyambirira mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 2015 ya mutu wakuti “N’chiyani Chingatithandize Tikakhala ndi Nkhawa?”

  • Kodi Mumatani Mukakumana ndi Mavuto?
    Galamukani!—2015 | July
    • NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUMATANI MUKAKUMANA NDI MAVUTO?

      Musataye Mtima Mukakumana ndi Mavuto

      Munthu akuyendetsa boti mtima uli m’malo

      ANTHU ambiri amakonda kunena kuti, Pendapenda si kugwa. Choncho tisamataye mtima ngati penapake sizikutiyendera bwino. Masiku ano aliyense amakumana ndi mavuto. Koma chofunika n’kuvomereza mavutowo kenako n’kuona zimene tingakwanitse kuchita. N’zoona kuti mavuto ena akhoza kusintha koma kusintha kwenikweni kudzachitika m’dziko latsopano.

      Baibulo limasonyeza kuti ikubwera nthawi pamene moyo wathu uzidzayenda bwinobwino. Tidzatha kuchita zonse zimene tikufuna popanda mavuto, kupanikizika kapena kukhumudwa. (Yesaya 65:21, 22) Baibulo limati umenewu udzakhala “moyo weniweniwo.”—1 Timoteyo 6:19.

      “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya. Pakuti masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo, ndipo anthu anga osankhidwa mwapadera adzapindula mokwanira ndi ntchito ya manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena