Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g16 No. 4 tsamba 12-13
  • Dziko la Kyrgyzstan

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Kyrgyzstan
  • Galamukani!—2016
Galamukani!—2016
g16 No. 4 tsamba 12-13
Tinyumba ta ku chigwa cha Tash Rabat dziko la Kyrgyzstan

Tinyumba ta ku chigwa cha Tash Rabat

ANTHU NDI MAYIKO

Dziko la Kyrgyzstan

Mapu a Kyrgyzstan

DZIKO la Kyrgyzstan lili ku Central Asia ndipo linayandikana ndi mayiko a Kazakhstan, Uzbekistan, Tajikistan, ndi China. Malo aakulu kwambiri m’dzikoli kuli mapiri okhaokha omwe ndi aatali. Pamwamba pa mapiriwa pamazizira kwambiri moti mpaka pamapezeka madzi oundana. Dzikoli linatenga mbali yaikulu ya mapiri a Tian Shan omwe ndi aalitali mamita 7,439. Ku Kyrgyzstan kulinso nkhalango yaikulu kwambiri ya mitengo inayake yobereka zipatso zokhala ndi mtedza mkati mwake. Mitengoyi ili m’gulu la mitengo ikuluikulu padziko lonse.

Wa Mboni za Yehova akuphunzira Baibulo ndi mzimayi ku Kyrgyzstan

A Mboni za Yehova akuphunzitsa Baibulo anthu ambiri ku Kyrgyzstan

Anthu a ku Kyrgyzstan ndi okonda kuchereza komanso aulemu. Akamayankhula ndi munthu wamkulu amagwiritsa ntchito mawu aulemu akuti “inu.” Ndipo amasiyira akuluakulu malo abwino oti akhale akakwera basi komanso akamadya chakudya.

Mabanja ambiri m’dzikoli amakhala ndi ana atatu kapena kuposerapo. Nthawi zambiri mwana wamwamuna womaliza amakhalabe ndi makolo ake ngakhale atakwatira. Amachita zimenezi kuti azisamalira makolo ake kwa moyo wawo wonse.

Makolo amaphunzitsa ana awo aakazi maluso osiyanasiyana kuyambira ali aang’ono n’cholinga choti akadzakwatiwa adzakhale akazi abwino. Ndipo mwana wamkazi wazaka zapakati pa 14 ndi 16 amakhala atadziwa bwino ntchito zonse zapakhomo. Nthawi zambiri makolo amakonzeratu mphatso zoti adzapereke kwa mwamuna amene adzakwatire mwana wawo. Amapereka mphatso monga zofunda, zovala komanso kapeti yopanga pamanja. Nayenso mwamuna amapereka ndalama kapena ziweto.

Anthu a m’dzikoli amapha nkhosa kapena hatchi pa zisangalalo kapenanso pa maliro. Ndipo chiwalo chilichonse cha nyamayo chimakhala ndi tanthauzo linalake. Ndiyeno mlendo aliyense yemwe wabwera pamwambowo amapatsidwa chiwalo chinachake potengera msinkhu kapena udindo womwe ali nawo. Anthuwa amachita zimenezi chifukwa chakuti amalemekezana kwambiri. Zikatere amapatsa alendowo chakudya chomwe anthu am’dzikoli amadya chotchedwa beshbarmak. Chakudyachi amachidya ndi manja.

mtsikana akuimba nyimbo pogwiritsa ntchito chida chotchedwa komuz

Anthu m’dzikoli amakonda kuimba pogwiritsa ntchito chida chinachake chotchedwa Komuz

MFUNDO ZACHIDULE

Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

Buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? likufalitsidwa m’Chirikigizi ndipo likupezeka pa jw.org

  • Kuli Anthu Okwana: 5,776,000

  • Likulu la Dzikoli: Bishkek

  • Chinenero: Chirikigizi ndi Chirasha

  • Zinthu Zochokera M’dzikoli: Thonje, ubweya wa ziweto, golide, mekyule ndi yureniyamu

  • Chipembedzo: Anthu ambiri m’dzikoli ndi Asilamu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena