Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chipembedzo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Mboni za Yehova zimadzipereka kuchezera anthu m’nyumba zawo kwa ora limodzi kapena chapompo mlungu uliwonse, kwaulere, kudzakambitsirana Baibulo. Ndiloleni nditenge mphindi zochepa zokha kukusonyezani mmene timachitira?’

      Wonaninso tsamba 89.

      ‘Ndiganiza kuti chipembedzo chiri nkhani yaumwini’

      Mungayankhe kuti: ‘Limenelo liri lingaliro lofala masiku ano, ndipo ngati anthu alidi osakondwerera uthenga wa Baibulo, mokondwera timamka kunyumba zina. Koma kodi munazindikira kuti chifukwa chimene ndadzakuwonerani chiri chakuti ichi ndicho chimene Yesu analangiza otsatira ake kuchita? . . . (Mat. 24:14; 28:19, 20; 10:40)’

  • Chipulumutso
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Chipulumutso

      Tanthauzo: Kutetezeredwa kapena kulanditsidwa kuupandu kapena chiwonongeko. Uku kungakhale kulanditsidwa kwa otsendereza kapena ozunza. Kwa Akristu onse owona, Yehova amapereka kupyolera mwa Mwana wake chilanditso kudongosolo loipa liripoli la zinthu kudzanso chipulumutso ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. Kwa khamu lalikulu la atumiki okhulupirika a Yehova kukhala ndi moyo mkati mwa “masiku otsiriza,” chipulumutso chidzaphatikizapo kutetezeredwa pa chisautso chachikulu.

      Kodi Mulungu, mwa chifundo chake chachikulu, potsirizira pake adzapulumutsa anthu onse?

      Kodi 2 Petro 3:9 amasonyeza kuti padzakhala chipulumutso cha anthu onse? Iye amati: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke [“samafuna kuti aliyense awonongedwe,” TEV], koma kuti onse afike kukulapa.” (RS) Chiri chikhumbo cha kukoma mtima kwa Mulungu kuti ana onse a Adamu alape, ndipo mokoma mtima iye wapanga makonzedwe a kupezera chikhululukiro cha machimo kwa awo amene amatero. Koma iye samakakamiza munthu aliyense kuvomereza makonzedwewo. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 30:15-20.) Ambiri amawakana. Iwo ali ngati munthu womira amene amakankhira kutali chopulumutsira moyo pamene chiponyeredwa kwa iye ndi munthu amene afuna kuthandiza. Komabe, kuyenera kudziŵika, kuti choloŵa mmalo mwa kulapa sindicho helo wamuyaya m’moto. Monga momwe 2 Petro 3:9 amasonyezera, osalapa adzawonongeka, kapena “kuwonongedwa.” Vesi 7 (RS) imasonyanso ku “chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Panopa palibe lingaliro la chipulumutso cha anthu onse.—Wonaninso mutu wankhani waukulu wakuti “Helo.”

      Kodi 1 Akorinto 15:22 amatsimikizira kuti anthu onse potsirizira pake adzapulumutsidwa? Amati: “Monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Kristu onse adzakhalitsidwa ndi moyo.” (RS) Monga momwe kwasonyezedwera m’mavesi ozungulira, chimene chikukambitsiridwa panopa ndicho chiukiriro. Kodi adzaukitsidwa ndani? Onse amene imfa yawo inachititsidwa ndi tchimo la Adamu (wonani vesi 21) koma amene mwa iwo okha sanachite machimo adala olembedwa pa Ahebri 10:26-29. Monga momwe Yesu anaukitsidwira ku Hade (Mac. 2:31), motero ena onse amene ali m’Hade ‘adzakhalitsidwa amoyo’ mwa chiukiriro. (Chiv. 1:18; 20:13) Kodi onse amenewa adzapeza chipulumutso chamuyaya? Mwaŵi umenewo udzakhala wowatsegukira, koma siyense amene adzapindula nawo, monga momwe kwasonyezedwera pa Yohane 5:28, 29, amene amasonyeza kuti chotulukapo kwa ena chidzakhala “chiweruzo” chotsutsa.

      Bwanji za malemba onga Tito 2:11, limene linatchula “chipulumutso cha anthu onse,” mogwirizana ndi kumasulira kwa RS? Malemba ena, monga ngati Yohane 12:32, Aroma 5:18, ndi 1 Timoteo 2:3, 4, amapereka lingaliro lofanana mu RS, KJ, NE, TEV, ndi ena otero. Mawu Achigiriki omasuliridwa “onse” ndi “aliyense” m’mavesi amenewa ali m’mipangidwe ya kusiyanitsidwa kwa liwu lakuti pas. Monga momwe kwasonyezedwera mu Expository Dictionary of New Testament Words ya Vine (London, 1962, Vol. I, p. 46), pas angatanthauzenso “mtundu uliwonse kapena kusiyanasiyana.” Chotero, m’mavesi apamwamba, mmalo mwa “onse,” mawu akutiwo “mtundu uliwonse wa” angagwiritsiridwe ntchito; kapena “mitundu yonse ya,” monga momwe kwachitidwira mu NW. Kodi nkati kamene kali kolungama—“onse” kapena lingaliro loperekedwa ndi “mitundu yonse ya”? Eya, kodi ndikumasulira kuti kumene kulinso kogwirizana ndi mbali yotsala ya Baibulo? Yotsirizirayi ndiyo. Talingalirani Machitidwe 10:34, 35; Chivumbulutso 7:9, 10; 2 Atesalonika 1:9. (Tamverani: otembenuza ena amavomerezanso ganizo iri la liwu Lachigiriki, monga momwe kwasonyezedwera ndi kulimasulira kwawo pa Mateyu 5:11—“mitundu yonse ya,” RS, TEV; “mtundu uliwonse wa,” NE; “mkhalidwe wonse wa,” KJ.)

      Kodi pali malemba amene amasonyeza motsimikizirika kuti ena sadzapulumutsidwa konse?

      2 Ates. 1:9: “Adzamva chilango, ndicho chiwonongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake.” (Akanyenye awonjezeredwa.)

      Chiv. 21:8: “Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse amabodza, cholandira chawo chidzakhala nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiŵiri.”

      Mat. 7:13, 14: “Loŵani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira ya kumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo ya kumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenechi ali oŵerengeka.”

      Pamene munthu apulumutsidwa, kodi iye wapulumutsidwa nthaŵi yonse?

      Yuda 5: “Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale mumadziŵa zonse kale, kuti Ambuye atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwatulutsa m’dziko la Aigupto, anawononganso iwo osakhulupirira.” (Kanyenye wawonjezeredwa.)

      Mat. 24:13: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Chotero, chipulumutso chotsirizira chamunthu sichimatsimikiziridwa panyengo imene iye ayamba kukhulupirira Yesu.)

      Afil. 2:12: “Monga momwe mumvera nthaŵi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.” (Mawuŵa anaperekedwa kwa “asante,” kapena oyera mtima, ku Filipi, monga momwe kwalongosoledwera mu Afilipi 1:1. Paulo anawalimbikitsa kusakhala ndi chidaliro chopambanitsa koma kuzindikira kuti chipulumutso chawo chotsirizira chinali chisanatsimikiziridwebe.)

      Aheb. 10:26, 27, RS: “Ngati tichimwa dala pambuyo pa kulandira chidziŵitso cha chowonadi, sipatsalanso nsembe ya machimo, koma chiyembekezo chochititsa mantha cha chiŵeruzo, ndi mkwiyo wa moto umene udzanyeketsa adani.” (Motero Baibulo silimayenderana ndi lingaliro lakuti ziribe kanthu ndi machimo amene munthu angachite pambuyo pa “kupulumutsidwa” kwake iye sadzatayikiridwa ndi chipulumutso chake. Limalimbikitsa kukhulupirika. Wonaninso Ahebri 6:4-6, kumene limasonyeza kuti ngakhale kumene munthuyo ali wodzozedwa ndi mzimu woyera angathe kutayikiridwa ndi chiyembekezo chake cha chipulumutso.)

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena