Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kuvutika
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kuthekera kwina: ‘Mwachiwonekere inu mumakhulupirira Mulungu. Kodi mumakhulupirira kuti Mulungu ndiye chikondi? . . . Kodi mumakhulupirira kuti iye ngwanzeru ndi kuti ngwamphamvu yonse? . . . Pamenepa ayenera kukhala ndi zifukwa zabwino zololera kuvutika. Baibulo limasonyeza chimene zifukwa zimenezo ziri. (Wonani tsamba 222-225.)’

  • Madeti
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Madeti

      Tanthauzo: Madeti amasonyeza nthaŵi pa imene zinthu zimachitika. Baibulo limatchula madeti mowagwirizanitsa ndi nthaŵi yamoyo wa anthu ena, nyengo mu imene olamulira akutiakuti anali kulamulira, kapena zochitika zina zodziŵika. Ali ndi kaŵerengedwe kokha kokwanira kubwerera mmbuyo mpaka ku nthaŵi ya kulengedwa kwa Adamu. Kuŵerenga zaka kwa Baibulo kunatchulanso molunjika pasadakhale nthaŵi pamene zochitika zina zofunika m’kukwaniritsidwa kwa chifuno cha Mulungu zikakhalapo. Kalendala ya Gregory, imene tsopano iri yotchuka m’mbali yaikulu ya dziko, sinayambe kugwiritsiridwa ntchito kufikira 1582. M’magwero audziko muli kusagwirizana pamadeti otchulidwa a zochitika m’mbiri yakale. Komabe, madeti ena ovomerezeka , monga 539 B.C.E. kukhala kugwa kwa Babulo, ndipo chifukwa chake 537 B.C.E. kukhala chaka cha kubwerera kwa Ayuda kuchokera ku ukapolo, ngotsimikiziridwa bwino. (Ezra 1:1-3) Kugwiritsira ntchito madeti otero monga poyambira, kumakhozetsa kufotokoza pamakalendala amakono madeti a zochitika zakale za Baibulo.

      Kodi asayansi atsimikizira kuti anthu akhala ali padziko lapansi kwa zaka mamiliyoni ambiri, osati zaka zikwi zingapo zokha monga momwe Baibulo likusonyezera?

      Njira zogwiritsiridwa ntchito ndi asayansi kudziŵira madeti zazikidwa pa kuyerekezera kumene kungakhale kothandiza koma kaŵirikaŵiri kungachititse zotulukapo zotsutsana kwambiri. Chotero, madeti amene iwo amapereka amakonzedwa mosalekeza.

      Lipoti lina mu New Scientist ya March 18, 1982, limati: “‘Ndikuzizwa kukhulupirira kuti nthaŵi yochepa yonga chaka chimodzi chapita ndinalankhula mawu omwe ndinanenawo.’ Anatero Richard Leakey, pamaso pa omvetsera abwinobwino ku Royal Institution pankhani yamadzulo Lachisanu latha. Anali atafika kudzaulula kuti chidziŵitso chovomeredwa, chimene anali atachirikiza posachedwapa m’mipambo yake ya nkhani za televizhoni za BBC The Making of Mankind, chinali mwinamwake cholakwa m’mbali zingapo zazikulu.’ Kwakukulukulu, iye tsopano akuwona kholo lakale koposa lamunthu kukhala la zaka zocheperapo pang’ono kuposa zaka mamiliyoni 15-20 zonenedwa motsimikizira pa televizhoni.”—P. 695.

      Panthaŵi ndi nthaŵi, njira zatsopano za kuŵerengera zaka zimatulukiridwa. Kodi zimenezi nzodalirika motani? Ponena za imodzi ya njirazo yodziŵika monga thermoluminescence (kuŵerengedwa mwanthaŵi ya kutentha kochititsidwa ndi rediyeshoni), The New Encyclopædia Britannica (1976, Macropædia, Vol. 5, p. 509) imati: “Kuyembekezera osati kutsimikizirika ndizo zimene kwakulukulu zaphatikizidwa ndi mpangidwe wa kuŵerengera zaka wa thermoluminescence panthaŵi ino.” Ndiponso, Science (August 28, 1981, p. 1003) ikusimba kuti mafupa osonyeza msinkhu wa zaka 70 000 wa mpangidwe wa kusintha kwa amino acid anapereka kokha zaka 8 300 kapena 9 000 mwa kuŵerengera ndi radioactive.

      Popular Science (November 1979, p. 81) ikusimba kuti katswiri wophunzira zinthu zowoneka Robert Gentry “amakhulupirira kuti zaka zonse zotulukiridwa ndi kuvunda kochititsidwa ndi radioactive zingakhale zolakwa—osati kokha ndi zaka zoŵerengeka, koma ndi zambirimbiri.” Nkhaniyo ikusonyeza kuti zimene anatulukira zingachititse kunena kuti “mmalo mwakuti munthu akhale atayamba kuyenda padziko lapansi kwa zaka mamiliyoni 3.6, angakhale atakhalako kwa zaka zikwi zoŵerengeka zokha.”

      Komabe, kuyenera kudziŵika kuti asayansi amakhulupirira kuti zaka zimene dziko lenilenilo lakhala liriko nzochuluka kwambiri kuposa zaka zakukhalako kwa munthu. Baibulo silimatsutsa zimenezo.

      Kodi zaka zakubadwa za anthu Chigumula chisanafike monga momwe zafotokozedwera m’Baibulo, zinapimidwa mogwirizana ndi zaka zimodzimodzizo zimene timagwiritsira ntchito?

      Ngati kunalingaliridwa kuti “zaka” ziyenera kukhala zinali zofanana ndi miyezi yathu, pamenepo Enoshi anabala mwana pamene anali ndi zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo Kenani anali ndi zaka zisanu zokha pamene anabala mwana wamwamuna. (Gen. 5:9, 12) Mwachiwonekere, zimenezo, nzosatheka.

      Kuŵerenga zaka kwatsatanetsatane koperekedwa ponena za Chigumula kumasonyeza utali wa miyezi ndi zaka zogwiritsiridwa ntchito panthaŵiyo. Kuyerekezera Genesis 7:11, 24 ndi 8:3, 4 kumasonyeza kuti miyezi isanu (kuchokera pa 17 pa mwezi wa 2 kufikira pa 17 pa mwezi wa 7) anali amasiku okwanira 150,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena