-
ChipulumutsoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
ambiri amene adzasonyeza chikhulupiriro chowona m’makonzedwe amene Mulungu wawapanga kupyolera mwa Yesu. Koma Baibulo limanena kuti ali 144 000 okha amene adzapita kumwamba kukakhala ndi Kristu. Kodi munayamba mwawona zimenezo m’Baibulo? . . . Ziri pano pa Chivumbulutso 14:1, 3.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Kodi iwo adzachitanji kumwamba? (Chiv. 20:6)’ (2) ‘Kuli kwachiwonekere kuti iwo adzakhala akulamulira pa anthu ena. Kodi amenewo angakhale ayani? . . . (Mat. 5:5; Mat. 6:10)’
-
-
ChisinthikoKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Chisinthiko
Tanthauzo: Chisinthiko cha zinthu zamoyo chiri chiphunzitso chakuti zinthu zoyamba zamoyo zinachokera m’kanthu kopanda moyo. Pamenepo, kukunenedwa kuti, pamene kanatulutsanso zinthu zina, kanasinthika kukhala mitundu ina ya zamoyo, potsirizira pake kutulutsa mipangidwe yonse ya zomera ndi nyama zimene zakhalako chiyambire padziko lino lapansi. Zonsezi zikunenedwa kukhala zitakwaniritsidwa popanda kuloŵerera koposa kwaumunthu kwa Mlengi. Anthu ena amayesayesa kugwirizanitsa kukhulupirira Mulungu ndi chisinthiko, akumanena kuti Mulungu analenga kupyolera mwa chisinthiko, kuti iye anachititsa kukhalapo kwa mipangidwe yoyamba yosatsungula ya moyo ndi kuti pambuyo pake mipangidwe yotsungula kwambiri ya moyo, kuphatikizapo munthu, inatulutsidwa kudzera mwa chisinthiko. Sichiri chiphunzitso cha Baibulo.
Kodi chisinthiko chiridi chausayansi?
“Dongosolo la sayansi” liri lotere: Kupenda chimene chimachitika; pamaziko a mapendedwe amenewo, kupanga chiphunzitso cha chimene chingakhale chowona; kuyesa chiphunzitsocho mwa mapendedwe ena ndi kuyesa; ndi kuyang’anitsitsa kuti ziwoneke ngati zonenedweratu zozikidwa pa chiphunzitsocho zikukwaniritsidwa. Kodi iri ndiro dongosolo lotsatiridwa ndi okhulupirira ndi kuphunzitsa chisinthiko?
Katswiri wophunzira zakuthambo Robert Jastrow amati: “Mowachititsa manyazi [asayansi] alibe yankho lachindunji, chifukwa chakuti akatswiri osanganiza mankhwala sanapeze konse chipambano m’kutulutsanso zoyesayesa zachilengedwe pakulengedwa kwa moyo kuchokera m’chinthu chopanda moyo. Asayansi samadziŵa mmene zimenezo zinachitikira.”—The Enchanted Loom: Mind in the Universe (New York, 1981), p. 19.
Wokhulupirira chisinthiko Loren Eiseley anavomereza kuti: “Pambuyo pa kudzudzula wophunzira zaumulungu kaamba ka kudalira kwake panthanthi ndi chozizwitsa, sayansi inadzipeza iri mu mkhalidwe wothetsa nzeru wa kufunikira kudzipangira nthanthi yake: yakuti, kuyerekezera kwakuti, chimene sichikatsimikiziridwa kuchitika lerolino pambuyo pa kuyesayesa kwa nthaŵi yaitali, chinachitika m’nthaŵi yamakedzana.”—The Immense Journey (New York, 1957), p. 199.
Mogwirizana ndi New Scientist: “Chiŵerengero chowonjezereka cha asayansi, makamaka chiŵerengero chomakulakula koposa cha okhulupirira chisinthiko . . . chikutsutsa kuti chiphunzitso cha chisinthiko cha Darwin sichiri konse chiphunzitso cha sayansi yowona. . . . Unyinji wa osuliza uli ndi maumboni anzeru apamwamba koposa.”—June 25, 1981, p. 828.
Katswiri wasayansi yampangidwe (physicist) H. S. Lipson anati: “Kulongosoka kokha kovemerezedwa ndiko chilengedwe. Ndidziŵa kuti aka nkonyansa kwa akatswiri asayansi yampangidwe, monga momwedi kaliridi kwa ine, koma sitiyenera kukana chiphunzitso chimene sitimakonda ngati umboni wa kufufuza uyichirikiza.” (Kanyenye wawonjezeredwa.)—Physics Bulletin, 1980, Vol. 31, p. 138.
Kodi ochirikiza chisinthikowo amavomerezana? Kodi maumboniwa amakupangitsani kulingalira motani ponena za zimene amaphunzitsa?
Mawu oyamba a kope la zana la The Origin of Species ya Darwin (London, 1956) amati: “Monga momwe tikudziŵira, pali malingaliro osiyanasiyana kwambiri pakati pa akatswiri ophunzira za moyo, osati kokha ponena za magwero achisinthiko komanso za mchitidwe weniweniwo. Kusiyanaku kulipo chifukwa chakuti umboni ngwosakhutiritsa ndipo sumapereka mpata wa kunena kotsimikizirika kulikonse. Chifukwa chake kuli kolungama ndi koyenera kusonyeza anthu onse osadziŵa sayansi kusagwirizana kwa chisinthiko.”—Lolembedwa ndi W. R. Thompson, amene kale anali mtsogoleri wa Commonwealth Institute of Biological Control, Ottawa, Canada.
“Zaka zana limodzi pambuyo pa imfa ya Darwin, tikali chikhalirebe opanda ngakhale lingaliro laling’ono koposa lokhoza kusonyezeka kapena ngakhale lachiphamaso ponena za mmene kwenikweni chisinthiko chinachitikira—ndipo m’zaka zaposachedwapa zimenezi zachititsa mipambo yapadera ya mikangano ponena za funso lonselo. . . . Pali mkhalidwe wa pafupifupi nkhondo yapoyera ya kagulu ka achisinthiko eniwo, mtundu uliwonse wa kagulu ka [achisinthiko] ukumasonkhezera masinthidwe atsopano.”—C. Booker (wolemba London Times), The Star, (Johannesburg), April 20, 1982, p. 19.
Magazine asayansi otchedwa Discover anati: “Chisinthiko . . . sichiri kuukiridwa kokha ndi Akristu okhulupirira Baibulo, koma chikukaikiridwanso ndi asayansi otchuka. Pakati pa akatswiri a zokwiriridwa, asayansi amene amaphunzira cholembedwa
-