Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • anagwiritsira ntchito kuthandiza anthu inali yopindulitsa? . . . Timayesa kutsatira chitsanzo chake.’

      ‘Akristu amayembekezeredwa kukhala Mboni za Yesu, osati za Yehova’

      Mungayankhe kuti: ‘Imeneyo iri mfundo yokondweretsa imene mwadzutsa. Ndipo mwalondola kuti tiri ndi thayo la kukhala mboni za Yesu. Ndicho chifukwa chake ntchito ya Yesu m’chifuno cha Mulungu yagogomezeredwa m’mabukhu athu. (Mungafune kugwiritsira ntchito bukhu latsopano kapena magazine kuchitira chitsanzo zimenezi.) Koma nachi chinthu china chimene chingakhale lingaliro latsopano kwa inu. (Chiv. 1:5) . . . Kodi Yesu anali “Mboni Yokhulupirika” ya yani? (Yoh. 5:43; 17:6) . . . Yesu anapereka chitsanzo chimene tiyenera kutsatira, kodi sanatero? . . . Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kudziŵa onse aŵiri Yesu ndi Atate wake? (Yoh. 17:3)’

  • Misa
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Misa

      Tanthauzo: Monga momwe kwafotokozedwera ndi Mpingo Wopatulika wa Madzoma a Tchalitchi cha Roma Katolika, Misa ndiyo “—nsembe mu imene Nsembe Yamtanda imapitirizidwa;—Chikumbukiro cha imfa ndi chiukiriro za Ambuye, amene anati ‘chitani ichi chikhale chikumbukiro changa’ (Luka 22:19);—Phwando lopatulika limene, Thupi ndi Mwazi za Ambuye zimagwirizanitsidwa, Anthu a Mulungu amapeza mapindu a Nsembe ya Paskha, kuyambiranso Pangano Latsopano limene Mulungu wapangana ndi anthu kamodzi kunthaŵi zonse kupyolera mwa Mwazi wa Kristu, ndipo mwachikhulupiriro ndi chiyembekezo limaphiphiritsira ndipo limakhala kalambule bwalo wa phwando la pambuyo kutha kwadziko mu ufumu wa Atate, kulengeza imfa ya Ambuye ‘kufikira kudza Kwake.’” (Eucharisticum Mysterium, May 25, 1967) Ndiyo njira ya Tchalitchi cha Katolika yochitira zimene amazindikira kuti Yesu Kristu anachita pa Mgonero Womaliza.

      Kodi mkate ndi vinyo zimasandulizidwadi kukhala thupi ndi mwazi za Kristu?

      Mu “Dzoma la Kulengezedwa kwa Chikhulupiriro” pa June 30, 1968, Papa Paul VI anati: “Tikhulupirira kuti monga momwe mkate ndi vinyo zodalitsidwa ndi Ambuye pa Mgonero Womaliza zinasandulizidwira kukhala Thupi Lake ndi Mwazi Wake zimene zinayenera kuperekedwa kaamba ka ife pamtanda,

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena