Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Paradaiso
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kodi “Chipangano Chatsopano” chimasonya kuparadaiso wamtsogolo wa padziko lapansi kapena kodi iye ali kokha mu “Chipangano Chakale”?

      Kugaŵanitsidwa kwa Baibulo kukhala mbali ziŵiri, kuyamikira kufunika kwa mawuwo pamaziko akuti kaya iwo ali mbali “Yakale” kapena “Yatsopano” sikuli kogwirizana ndi Malemba. Pa 2 Timoteo 3:16 timauzidwa kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pachiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.” Aroma 15:4 amasonya ku Malemba ouziridwa a Chikristu chisanakhale pamene amati: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza.” Motero, yankho labwino lafunsoli liyenera kulingalira Baibulo lathunthu.

      Genesis 2:8 amafotokoza kuti: “Yehova Mulungu anabzala [“paki,” Mo; “paradaiso,” Dy; pa·raʹdei·son, LXX] mu Edene, chakummaŵa; momwemo ndipo adaika munthu [Adamu] adamuumbayo.” Panali zomera ndi zinyama zochuluka zamitundumitundu ndi zochititsa chidwi. Yehova anadalitsa anthu aŵiri oyambirira ndipo anati kwa iwo: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pansomba zamnyanja, ndi pambalame zamlengalenga, ndi pazamoyo zonse zakukwaŵa padziko lapansi.” (Gen. 1:28) Chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba kadziko lonse lapansi cha kukhala paradaiso lokhalidwa ndi awo amene moyamikira anamvera malamulo ake sichidzalephera kukwaniritsidwa. (Yes. 45:18; 55:10, 11) Ndicho chifukwa chake Yesu anati odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Ndicho chifukwa chakenso iye anaphunzitsira ophunzira ake kupemphera kuti: “Atate wathu Wakumwamba dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mat. 5:5; 6:9, 10) Mogwirizana ndi zimenezo, Aefeso 1:9-11 amalongosola chifuno cha Mulungu cha ‘kusonkhanitsa zinthu zonse pamodzi kachiŵirinso mwa Kristu, zinthu za kumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi.’ Ahebri 2:5 amasonya ku “dziko lirinkudza.” Chivumbulutso 5:10 chimatchula awo amene, monga oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu, “achita ufumu padziko.” Chivumbulutso 21:1-5 ndi 22:1, 2 amawonjezera malongosoledwe okongola a mikhalidwe imene idzakhalako mu “dziko lapansi latsopano” ndipo zimenezo zimakumbutsa munthuwe za Paradaiso woyambirira mu Edene limodzi ndi mtengo wake wamoyo.—Gen. 2:9.

      Ndiponso, Yesu anagwiritsira ntchito mawu Achigiriki ochedwa pa·raʹdei·sos ponena za Paradaiso wadziko lapansi wamtsogolo. “Iye anati kwa iye [wochita zoipa amene anapachikidwa pambali pa Yesu ndi amene anasonyeza chikhulupiriro muufumu ulinkudza wa Yesu kuti]: ‘Ndithudi ndikuuza lerolino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43, NW.

      Kodi tingatsimikizire motani zimene Yesu anatanthauza mwa liwulo Paradaiso m’mawu ake kwa wochita zoipa, pa Luka 23:43?

      Kodi anali malo akanthaŵi kaamba ka ‘miyoyo yakufa ya olungama,’ mbali yaHade?

      Kodi nchiyani chimene chiri magwero a lingaliro limenelo? The New International Dictionary of New Testament Theology imafotokoza kuti: “Mwa kubwerera kwa chiphunzitso Cha[chigiri]ki chakusakhoza kufa kwa moyo paradaiso amafikira kukhala malo okhala olungama mkati mwa mkhalidwe wapakati.” (Grand Rapids, Mich.; 1976, lolembedwa ndi Colin Brown, Vol. 2, p. 761) Kodi lingaliro losagwirizana ndi malemba limenelo linali lofala pakati pa Ayuda pamene Yesu anali padziko lapansi? Dictionary of the Bible ya Hastings imasonyeza kuti zimenezi ndizokaikitsa.—(Edinburgh, 1905), Vol. III, pp. 669, 670.

      Ngakhale ngati lingaliro limenelo linali lofala pakati pa Ayuda m’zaka za zana loyamba, kodi Yesu akanalivomereza mwalonjezo lake kwa wochita zoipa wolapa? Yesu anali atatsutsa mwamphamvu Afarisi Achiyuda ndi alembi kaamba ka kuphunzitsa miyambo imene inatsutsana ndi Mawu a Mulungu.—Mat. 15:3-9; wonaninso mutu waukulu wakuti “Moyo (Soul).”

      Yesu anapita ku Hade pamene anafa, monga momwe kwasonyezedwera pa Machitidwe 2:30, 31. (Mtumwi Petro, posonya ku Salmo 16:10, akugwidwa mawu kukhala akugwiritsira ntchito Hade monga chifanefane cha Sheoli.) Koma kulibe kulikonse m’Baibulo kumene limalongosola kuti Sheoli/Hade kapena mbali yake iriyonse ali paradaiso amene amapatsa munthu chikondwerero. Mmalo mwake, Mlaliki 9:5, 10 amanena kuti awo amene ali kumeneko “sadziŵa kanthu bi.”

      Kodi Paradaiso wa pa Luka 23:43 anali kumwamba kapena mbali ina ya kumwamba?

      Baibulo silimavomereza lingaliro lakuti Yesu ndi wochita zoipa anapita kumwamba patsiku limene iye analankhula naye. Yesu anali ataneneratu kuti, pambuyo pakuphedwa kwake, sakaukitsidwa kufikira tsiku la chitatu. (Luka 9:22) Mkati mwa nyengo ya masiku atatu imeneyo sanali kumwamba, chifukwa chakuti pambuyo pa chiukiliro chake anauza Mariya Magadala kuti: “Sindinakwerebe kwa Atate.” (Yoh. 20:17, NW) Anali masiku 40 pambuyo pa chiukiliro cha Yesu pamene ophunzira ake anamuwona akukwezedwa kuchoka padziko lapansi nazimilirika mmaso mwawo pamene anayamba kukwera kwake kumwamba.—Mac. 1:3, 6-11.

      Wochita zoipayo sanakwaniritse ziyeneretso zopitira kumwamba ngakhale nthaŵi ya pambuyo pake. Iye sanali “wobadwa mwatsopano”—kukhala wobatizidwa mmadzi kapena kubadwa ndi mzimu wa Mulungu. Mzimu woyera sunatsanuliridwe pa ophunzira a Yesu kufikira masiku oposa 50 pambuyo pa imfa ya wochita zoipayo. (Yoh. 3:3, 5; Mac. 2:1-4) Patsiku la imfa yake, Yesu anali atachita pangano la ufumu wakumwamba ndi awo amene ‘anali atamamatirana naye mmayesero ake.’ Wochita zoipayo analibe mbiri yotero ya kukhulupirika ndipo sanaphatikizidwe.—Luka 22:28-30.

      Kodi nchiyani chimene chimasonya ku Paradaiso ameneyo kukhala wapadziko lapansi?

      Malemba Achihebri sanachititse konse Ayuda okhulupirira kuyembekezera mphotho ya moyo wakumwamba. Malemba amenewo anasonya kukubwezeretsedwa kwa Paradaiso pano padziko lapansi. Danieli 7:13, 14 anali ataneneratu kuti pamene “ulamuliro, ndi ulemelero, ndi ufumu” zikaperekedwa kwa Mesiya, “anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi amanenedwe onse, amtumikire.” Nzika zimenezo za Ufumu zikakhala pano padziko lapansi. Mwa zimene analankhula ndi Yesu, wochita zoipayo mwachiwonekere anali kusonyeza chiyembekezo chakuti Yesu akamkumbukira pamene nthaŵiyo ikafika.

      Pamenepo, kodi ndimotani, mmene Yesu akanakhalira ndi wochita zoipa? Mwa kumamuukitsa kwa akufa, kuchita kakonzedwe kazosoŵa zake zakuthupi, ndi kumpatsa mwaŵi wa kuphunzira ndi kuchita mogwirizana ndi zofunika za Yehova za moyo wamuyaya. (Yoh. 5:28, 29) Yesu anawona mkhalidwe wolapa ndi wochitira ulemu mwa wochita zoipayo maziko omphatikiza pa mabiliyoni ambiri amene adzaukitsidwira kumoyo wapadziko lapansi ndi kupeza mwaŵi wakutsimikizira kuyenerera kwawo kukhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso.

      Kodi ndiliti pamene wochita zoipa adzakhala m’Paradaiso?

      Kuzindikira Luka 23:43 kwa munthu kumasonkhezeredwa ndi chizindikiro chopuma chogwiritsiridwa ntchito ndi otembenuza. M’zolembedwa zapamanja za Baibulo Lachigiriki loyambirira analibe zizindikiro zopuma. The Encyclopedia Americana (1956, Vol. XXIII, p. 16) imafotokoza kuti: “Palibe kuyesayesa kwa kuika zizindikiro za kupuma kumene kukuwonekera m’zolembedwa zapamanja zoyambirira ndi m’zilemba za Agiriki.” Munali kokha m’zaka za zana la 9 C.E. pamene zizindikiro zopuma zimenezo zinayamba kugwiritsiridwa ntchito. Kodi Luka 23:43 ayenera kunena kuti, “Indetu, ndinena ndi iwe, lerolino udzakhala ndi ine m’Paradaiso” (RS), kapena kodi ayenera kukhala, ‘Ndithudi ndikuuza lerolino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso’? Ziphunzitso za Kristu ndi Baibulo lonse ziyenera kukhala maziko otsimikizirira, ndipo osati koma (comma) woloŵetsedwa m’mlembalo zaka mazana ambiri Yesu atanena mawu amanewo.

      The Emphasised Bible lotembenuzidwa ndi J. B. Rotherham likuvomerezana ndi chizindikiro chopuma cha mu New World Translation. M’mawu amtsinde a Luka 23:43 womasulira Baibulo Wachijeremani L. Reinhardt amati: “Chizindikiro choima chogwiritsidwa ntchito lerolino [ndi omasulira ochuluka] m’vesili chiri mosakaikira chonama ndi chotsutsana ndi njira yonse ya malingaliro a Kristu ndi wochita zoipa. . . . Ndithudi [Kristu] sanazindikire kuti paradaiso anali kachigawo kakang’ono ka malo okhala anthu akufa, koma mmalo mwake kubwezeretsedwa kwa paradaiso wapadziko lapansi.”

      Kodi ndiliti pamene Yesu analoŵa mu ufumu ndi kukwaniritsa chifuno cha Atate wake kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso? Bukhu la Chivumbulutso, lolembedwa pafupifupi zaka 63 pambuyo pakunenedwa kwa mawu olembedwa pa Luka 23:42, 43, limasonyeza kuti zochitika izi zinali chikhalirebe mtsogolo. (Wonani tsamba 231-234, pankhani ya “Madeti,” ndiponso mutu waukulu wakuti “Masiku Otsiriza.”)

  • Pemphero
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Pemphero

      Tanthauzo: Kulankhula kopembedza, kaya mofuula kapena mwakachetechete mmalingaliro a munthu, kwa Mulungu wowona kapena kwa milungu yonyenga.

      Kodi mumalingalira, monga momwe amachitira ambiriwo, kuti simumapeza yankho kumapemphero anu?

      Kodi ndimapemphero ayani amene Mulungu ali wofunitsitsa kumva?

      Sal. 65:2; Mac. 10:34, 35: “Wakumva pemphero inu, zamoyo zonse zizadza kwa inu.” “Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Mtundu wa munthu, mawonekedwe a khungu la munthu, kapena mikhalidwe yazachuma ya munthu sindizo kanthu. Koma zisonkhezero za mtima wa munthu ndi njira ya moyo ya munthuyo zimatero.)

      Luka 11:2: “Pamene mupemphera nenani, Atate, dzina lanu liyeretsedwe.” (Kodi mapemphero anu amalunjikitsidwa kwa Atate, uyo amene dzina lake Baibulo limamutcha Yehova? Kapena, mmalo mwake, mumapereka mapemphero anu kwa “oyera mtima”?)

      Yoh. 14:6, 14: “Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine ngati mudzapempha kanthu mu dzina langa, ndidzachita.” (Kodi mumapemphera m’dzina la Yesu Kristu, mukumavomereza kuti monga munthu wochimwa mufunikira kuti akutetezereni?)

      1 Yoh. 5:14: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera. (Komabe, kuti mukhale ndi chidaliro chotero, muyenera choyamba kudziŵa chifuniro cha Mulungu. Ndiyeno tsimikizirani kuti mapemphero anu ngogwirizana nacho.)

      1 Pet. 3:12: “Maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye iri pa wochita zoipa.” (Kodi inu mwapeza nthaŵi ya kuphunzira zimene Yehova amanena kupyolera mwa Mawu ake ponena za cholungama ndi choipa?)

      1 Yoh. 3:22, NW: “Chirichonse tipempha, tilandira kwa iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zokodweretsa pamaso pake.” (Kodi chiridi chikhumbo chanu kukondweretsa Mulungu, ndi kuyesayesa mwamphamvu kumvera malamulo ake amene mumadziŵa kale?)

      Yes. 55:6, 7: “Funani Yehova popezeka iye, itanani Iye pamene ali pafupi; woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi Mulungu wathu, pakuti adzakhululukira koposa.” (Mwachifundo, Yehova amaitana ngakhale anthu amene anachita zoipa kumfikira m’pemphero. Koma, kuti apeze chiyanjo cha Mulungu, iwo ayenera kulapa mowona mtima njira zawo zochimwa ndi malingaliro ndi kusintha njira yawo.)

      Kodi nchiyani chimene chingapangitse mapemphero a munthu kukhala osavomerezeka pamaso pa Mulungu?

      Mat. 6:5: “Pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m’masinagoge, ndi pamphambano zamakwalala, kuti awonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, iwo alandiriratu mphoto zawo.” (Ndiponso Luka 18:9-14)

      Mat. 6:7: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga momwe amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.”

      Miy. 28:9: “Wopeŵetsa khutu lake kuti asamve chilamulo [cha Mulungu], ngakhale pemphero lake linyasa.”

      Mika 3:4: “Pamenepo adzapfuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthaŵi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe awo.”

      Yak. 4:3: “Mupempha, ndipo simulandila, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.”

      Yes. 42:8, Dy; Mat. 4:10, JB: “Ine, Ambuye [“Yahweh,” JB; “Yehova,” NW]: ndilo dzina langa. Sindidzapatsa munthu aliyense ulemerero wanga kapena chitamando changa kumafano osemedwa.” “Uyenera kulambira Ambuye Mulungu wako [“Yehova Mulungu wako,” NW], ndi kumtumikira iye yekha.” (Ndiponso Salmo 115:4-8, kapena 113:4-8 mpambo wachiŵiri wa chiŵerengero mu Dy) (Pemphero ndilo mpangidwe wa kulambira. Ngati mupemphera pamaso pa zinthu zosemedwa kapena mafano, kodi zimenezo zidzakondweretsa Mulungu?)

      Yes. 8:19: “Pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa alauli, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang’ung’udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wawo? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?”

      Yak. 1:6, 7: “Apemphe ndi chikhulupiriro, osakaika konse; pakuti wokaikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye.”

      Kodi ndiponena za nkhani zoyenerera zotani zimene tingapempherere?

      Mat. 6:9-13: “Pempherani inu chomwechi: ‘[1] Atate wathu Wakumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. [2] Ufumu wanu udze. [3] Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. [4] Mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero. [5] Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu. [6] Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.’” (Tawonani kuti dzina la Mulungu ndi chifuno ziyenera kukhala zoyambirira.)

      Sal. 25:4, 5: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’chowonadi chanu, ndipo mundiphunzitse pakuti inu ndinu Mulungu wachipulumutso changa.”

      Luka 11:13: “Ngati inu okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa mzimu woyera kwa iwo akupempha iye.”

      1 Ates. 5:17, 18: “Pempherani kosaleka; m’zonse yamikani.”

      Mat. 14:19, 20: “[Yesu] anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziŵirizo, ndipo pamene anayang’ana kumwamba anadalitsa, nanyema, napatsa mikateyo kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa makamuwo. Ndipo anadya onse, nakhuta.”

      Yak. 5:16, NW: “Pemphereranani.”

      Mat. 26:41: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa.”

      Afil. 4:6: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”

      Ngati Wina Anena Kuti—

      ‘Yambani mwapemphera nane, ndiyeno ndilalikireni uthenga wanu’

      Mungayankhe kuti: ‘Ndiri wokondwera kudziŵa kuti ndinu munthu woyamikira kufunika kwa pemphero. Mboni za Yehova nazonso zimapemphera nthaŵi zonse. Koma pali kanthu kena kamene Yesu ananena ponena za nthaŵi ndi mmene tingapempherere kamene kangakhale katsopano kwa inu. Kodi munali kudziŵa kuti anauza ophunzira ake kusapereka mapemphero apoyera ndi cholinga chakuti ena awone kuti iwo anali opembedza, anthu opemphera? . . . (Mat. 6:5)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Tamverani zimene iye anapitirizabe kunena kuti ziyenera kukhala nkhaŵa yathu yaikulu ndi zimene tiyenera kuika poyamba m’mapemphero athu. Ndizo zimene ndadzagaŵana nanu. (Mat. 6:9, 10)’

      Kapena munganene kuti: ‘Ndidziŵa kuti oimira magulu ena a zipembedzo amachita zimenezo. Koma Mboni za Yehova sizimatero chifukwa chakuti Yesu adalangiza ophunzira ake kuchita ntchito yawo yolalikira mu mpangidwe wina. Mmalo mwakunena kuti, “poloŵa m’nyumba, yambani mwapemphera,” tamverani zimene ananena monga momwe zikupezekera pa Mateyu 10:12, 13. . . . Ndipo tawonani pano muvesi 7 zimene anayenera kukambitsirana. . . . Kodi ndimotani mmene Ufumuwo ungathandizire anthu onga inu ndi ine? (Chiv. 21:4)’

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena