-
ChiukiriroKukambitsirana za m’Malemba
-
-
dziko lapansi uli pafupifupi masikweya mailo 57 000 000 (147 600 000 sq km). Ngati theka la malowo linapatulidwira zifuno zina, pakakhalabe yochepera pang’ono ekala imodzi (c. 0.37 ha) pamunthu mmodzi, imene ingagaŵire chakudya choposa chokwanira. Choputira kupereŵera kwa chakudya kulipoku sindicho kusakhoza kwa dziko lapansi kutulutsa zokwanira ayi koma, mmalo mwake, mikangano yandale zadziko ndi umbombo wa zamalonda.
-
-
ChoikidwiratuKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Choikidwiratu
Tanthauzo: Chochitika chosapeŵeka ndipo kaŵirikaŵiri chatsoka. Choikidwiratu ndiko kukhulupirira kuti zochitika zonse zimatsimikiziridwa ndi chifuniro cha Mulungu kapena ndi mphamvu ina yaikulu kwambiri koposa munthu, kuti chochitika chiri chonse chiyenera kuchitika monga momwe chimachitikira chifukwa chakuti chinalinganizidwiratu. Sindicho liwu kapena chiphunzitso cha Baibulo.
Kodi munthu aliyense ali ndi “nthaŵi yakufa” yoikidwiratu?
Chikhulupiriro chimenechi chinali chofala pakati pa Agiriki ndi Aroma. Mogwirizana ndi kunena kwa nthanthi yachikunja ya Agiriki, Olinganiza zoikidwiratu anali milungu itatu imene inapota ulusi wamoyo, kutsimikiza kutalika kwake, ndi kuudula.
Mlaliki 3:1, 2 amanena za “mphindi yakumwalira.” Koma, kusonyeza kuti imeneyi siri mphindi yoikika yoikidwiratu yamunthuyo, Mlaliki 7:17 amapereka uphungu wakuti: “Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa, uferenji nthaŵi yako isanafike?” Miyambo 10:27 imati: “Kuwopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.” Ndipo Salmo 55:23 limawonjezera kuti: “Anthu okhetsa mwazi ndi achinyengo masiku awo sadzafikira nusu.” Pamenepa, kodi Mlaliki 3:1, 2 amatanthauza chiyani? Akungofotokoza kuchitika kosalekeza kwa kukhala wamoyo ndi imfa m’dongosolo lopanda ungwiro lino lazinthu. Pali nthaŵi imene anthu amabadwa ndi nthaŵi imene amafa—kaŵirikaŵiri pamsinkhu wosaposa zaka 70 kapena 80, koma nthaŵi zina mofulumilirapo ndipo nthaŵi zina mochedwerapo.—Sal. 90:10; wonaninso Mlaliki 9:11.
Ngati nyengo yamunthu aliyense ndi mmene adzafera zinaikidwiratu
-