Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kudziimira
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • maŵa tidzapita kuloŵa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nawo; inu amene simudziŵa chimene chidzagwa maŵa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuwonekera kanthaŵi, ndi pamenepo ukanganuka. Mukadanena inu, Akalola Mulungu, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.”

      Pamene chikhumbo cha munthu cha kudzimiira chimtsogolera ku kutsanzira dziko lokhala kunja kwa Mpingo Wachikristu, kodi amaloŵa mu ulamuliro wayani? Ndipo kodi Mulungu amawona motani zimenezi?

      1 Yoh. 2:15; 5:19: “Musakonde dziko lapansi kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye.” “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”

      Yak. 4:4: “Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi ladziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.”

  • Kudziveka Thupi Lanyama
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Kudziveka Thupi Lanyama

      Tanthauzo: Chikhulupiriro chakuti munthu amabadwa kachiŵiri m’kukhalapo kumodzi kapena kuposa kotsatizanatsatizana, kumene kungakhale mwa munthu kapena nyama. Kaŵirikaŵiri ndiwo “moyo” wosawonekawo umene umakhulupiriridwa kubadwanso m’thupi lina. Sichiri chiphunzitso cha Baibulo.

      Kodi lingaliro lachilendo la kukhala ozoloŵerana ndi mabwenzi ndi malo atsopano kotheratu limatsimikizira kudzviveka thupi lanyama kukhala kotsimikizirika?

      Kodi munayamba mwafanizirapo mwamuna wina kapena mkazi wamoyo ndi munthu wina amenenso ali moyo tsopano? Ochuluka akhala ndi chokumana nacho chotero. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti anthu ena ali ndi zizoloŵezi zofanana kapena angawonekere kukhala pafupifupi ofanana. Chotero lingaliro lakuti mumadziŵa munthuyo ngakhale kuli kwakuti simunakumanepo naye kale silimatsimikiziradi kuti munali wozoloŵerana naye m’moyo wapapitapo, kodi sichoncho?

      Kodi nchifukwa ninji nyumba kapena tauni ingawonekere kukhala yozoloŵereka kwa inu ngati simunakhale kumeneko konse? Kodi chiri chifukwa chakuti munakhala kumeneko m’nthaŵi ya moyo wanu woyamba? Nyumba zambiri zimamangidwa motsatira mapangidwe ofanana. Mipando yogwiritsiridwa ntchito m’mizinda yotalikirana ingakhale yopangidwa kuchokera ku zitsanzo zofanana. Ndipo kodi sizowona kuti malo okongola m’zigawo zotalikirana kwambiri amawonekera kukhala ofanana kwambiri? Motero, popanda kufunikira kuvekedwa thupi lanyama, malingaliro anu a kufanana kwa malo ali ndi chifukwa chabwino kwambiri.

      Kodi zikumbukiro za moyo panthaŵi ina pamalo ena, monga momwe zimatulutsidwira ndi munthu atatsirikidwa, zimatsimikizira kudziveka thupi?

      Pamene munthu atsirikidwa unyinji wa chidziŵitso chosungidwa muubongo wake ungakhoze kutulutsidwa. Otsirikawo amagwira kuganiza kwa munthuyo. Koma kodi zinthu zokumbukiridwa zimenezo zinafikamo motani? Mwinamwake munaŵerenga bukhu, munawona chithunzi chakanema, kapena kuphunzira za anthu ena patelevizheni. Ngati inu mudziika mmalo a anthu ponena za amene munali kuphunzira, kungakhale kutachititsa kukhomerezeka kwakukulu, pafupifupi ngati kuti chochitikacho chinali cha inu mwini. Zimene kwenikweni inu munachita zingakhale zakalekale kotero kuti mwaziiŵala, koma mutatsirikidwa chochitikacho chingakumbukike monga ngati kuti munali kukumbukira “moyo.” Komabe, ngati zimenezo zinali zowona, kodi aliyense sakanakhala ndi zikumbukiro zotero? Koma siyense amene amatero. Nkokondweretsa kuwona kuti chiŵerengero chowonjezereka cha makhothi apamwamba a zigawo m’United States sichimavomereza umboni woperekedwa munthu atatsirikidwa. Mu 1980 Khothi Lapamwamba la m’Minnesota linalengeza kuti “umboni wabwino koposa wa katswiri umasonyeza kuti palibe katswiri amene angatsimikizire kuti kaya chikumbukiro chochititsidwa ndi kutsirikidwa, kapena mbali iriyonse ya chikumbukirocho, uli wowona, wonama, kapena nthano—kungodzadza malingaliro ndi nthano. Zotulukapo zotero siziri zodalirika moyenerera kukhala zolondola.” (State v. Mack, 292 N.W.2d 764) Chisonkhezero cha malingaliro opangidwa ndi otsirika kwa munthu wotsirikidwayo ndicho chochititsa kusadalirika kumeneku.

      Kodi Baibulo liri ndi umboni wa kukhulupirira kudziveka thupi lanyama?

      Kodi Mateyu 17:12, 13 akupereka maziko a kukhulupirira kudziveka thupi lanyama?

      Mat. 17:12, 13: “[Yesu anati,] Eliya anadza kale, ndipo iwo

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena