-
MankhwalaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
ntchito zina za khalidwe lozoloŵereka la munthu.”—March 1981, p. 104.
Kodi kusuta chamba nkwaupandu kwambiri kuposa kumwa zakumwa zoledzeretsa?
Zakumwa zoledzeretsa nchakudya ndipo zimapukusidwa ndi thupi kuti zipereke nyonga; mbali yake yogwiritsidwa ntchito imatulutsidwa ndi thupi. Komabe, katswiri wa mankhwala ogodomalitsa maganizo anati: “Chamba chiri mankhwala ogodomalitsa maganizo kwambiri ndipo cholakwa chachikulu koposa chimene timapanga ndicho kuchiyerekezera ndi zakumwa zoledzeretsa.” “Kuyerekezera nsanganizo ndi nsanganizo, THC [m’chamba] kumasonyeza kuti chiri champhamvu kwambiri kuŵirikiza nthaŵi 10 000 kuposa zakumwa zoledzeretsa m’kuledzeretsa kwake kodziŵika . . . THC imachotsedwa pang’onopang’ono kuchokera m’thupi, ndipo pamafunikira miyezi yambiri kuti muchire ku ziyambukiro zake.” (Executive Health Report, October 1977, p. 3) Mlengi amadziŵa mmene tinapangidwira, ndipo Mawu ake amaloleza kumwa kwachikatikati zakumwa zoledzeretsa. (Sal. 104:15; 1 Tim. 5:23) Komanso iye amatsutsa mwamphamvu kumwa kopitirira muyezo zakumwa zoledzeretsa, monga momwedi amatsutsira kususuka.—Miy. 23:20, 21; 1 Akor. 6:9, 10.
Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimawona kusuta fodya kukhala cholakwa chachikulu?
Kumasonyeza kusalemekeza mphatso ya moyo
Mac. 17:24, 25: “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo . . . apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.”
“Umboni wakuti ndudu zimachepetsa moyo ngwochuluka; kugwirizana kwake nkotsimikizirika kwambiri monga momwedi kuliri kwa mankhwala alionse.”—Science 80, September/October, p. 42.
Malipoti amasonyeza kuti mu United States chiŵerengero cha akufa chaka ndi chaka chifukwa cha kusuta fodya chawonkhetsedwa kukhala 300 000; m’Britain, 50 000; m’Canada, 50 000. “Anthu oposa miliyoni imodzi amafa chaka chiri chonse ndi nthenda zogwirizanitsidwa ndi kusuta fodya ndipo m’Maiko Osatukuka, amene amasuta 52% ya fodya yense wosutidwa padziko lonse lapansi, akuwonjezera mofulumira ziŵerengero za akufa amenewo.”—The Journal (Toronto), September 1, 1983, p. 16
Amene kale anali Nduna ya U.S., Yazaumoyo wa Anthu, Maphunziro, ndi Makhalidwe Abwino a Anthu, Joseph Califano, anati: “Lerolino sipangakhale kukaikira kuti kusuta fodya kulidi mchitidwe wakudzipha kwapang’onopang’ono.”—Scholastic Science World, March 20, 1980, p. 13.
Sikuli kogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna kuti Akristu apereke kwa iye
Aroma 12:1: “Ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.”
Dokotala wa opareshoni wamkulu wa ku United States, C. Everett Koop, anati: “Kusuta ndudu kuli kogwirizanitsidwa kotheratu ndi chochititsa imfa chachikulu chokhoza kuchinjirizidwa m’dziko lathu.” (The New York Times, February 23, 1982, p. A1) “Mafufuzidwe a zamankhala amasonyeza kuti . . . avereji ya nthaŵi ya moyo ya wosuta fodya njocheperapo ndi zaka zitatu kufikira zinayi kuposa munthu wosasuta. Nthaŵi ya moyo ya wosuta fodya kopambanitsa—munthu amene amasuta mapaketi andudu aŵiri kapena kuposa patsiku—ingakhale yocheperapo ndi zaka zisanu ndi zitatu kuposa munthu wosasuta fodya.” (The World Book Encyclopedia, 1984, Vol. 17, p. 430) Kodi nkoyenerera kwa munthu kupereka moyo wake ku utumiki wa Mulungu ndiyeno kuwononga moyowo pang’onopang’ono?
“Kusuta fodya nkowononga kwambiri, makamaka kumtima ndi mapapu, kotero kuti mbali zina za mankhwala otetezera amakhala opanda ntchito pang’ono ngati munthuyo amasuta fodya.” (University of Southern California News Service, February 18, 1982) “Mwinamwake kusuta fodya ndiko chochititsa nthenda chachikulu koposa m’dziko chimene chingakhoze kuchinjirizidwa.” (Dr. H. Mahler, mtsogoleri wamkulu wa Gulu Lazaumoyo wa Anthu Ladziko Lonse, mu World Health, February/March 1980, p. 3) Kodi nkuchita mogwirizana kuti munthu adzipereke kwa Mulungu kaamba ka utumiki wopatulika ndiyeno kuwononga dala thanzi lake?
Kusuta ndiko kuswa lamulo la Mulungu lakuti tikonde anansi athu
Yak. 2:8: “Uzikonda mmzako monga udzikonda wekha.”—Yerekezerani ndi Mateyu 7:12.
“Mafufuzidwe aposachedwapa . . . anavumbula kuti akazi osasuta amene amuna awo amasuta amafa mofulumirirapo paavareji ya zaka zinayi kuposa akazi amene amuna awo alinso asasuta.” (The New York Times, November 22, 1978, p. C5) “Kusuta fodya m’nthaŵi ya kukhala ndi pakati kungachititse kupunduka kobadwa nako kokulira kwambiri kotero kuti mwinamwake mwana wosabadwayo amafa, kapena khandalo limatero mwamsanga pambuyo pa kubadwa.” (Family Health, May 1979, p. 8) Mchitidwe wopanda chikondi wotero m’ziŵalo zabanja uli umboni wowoneka bwino wakuti munthuyo sakuchita monga Mkristu.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 5:8.
“Mafufuzidwe asonyeza kuti popeza kuti wosuta wachikatikati kwenikweni amasuta ndudu yake mbali yaing’ono pamene ikolezedwa, wosasutayo angakakamizidwedi mosadzifunira kupuma pafupifupi mpweya woipa wochuluka wotchedwa carbon monoxide, tar ndi chikonga pamene wosuta weniweniyo wakhala pafupi naye.” (Today’s Health, April 1972, p. 39) Munthu amene ali wopanda chikondi motero kulinga kwa munthu mnzake samaperekanso umboni wa kukonda Mulungu.—Wonani 1 Yohane 4:20.
Kodi nchifukwa ninji Mulungu anapanga zomera zimene mankhwala oledzeretsa amatengedwako ngati kuli kulakwa kuwagwiritsira ntchito?
Kaŵirikaŵiri zinthu zimene zimagwiritsiridwa ntchito molakwa zingakhoze kugwiritsiridwanso ntchito mopindulitsa. Zimenezo nzowona ponena za mphamvu za munthu za kubala. Nchimodzimodzi ndi vinyo. Chamba chimapangidwa ndi masamba oumikidwa ndi nsonga za maluŵa a chomera cha chamba, chimene chimatulutsa bwazi wothandiza kupangira chingwe ndi nsalu. Masamba a fodya, ogwiritsiridwa ntchito molakwa ndi osuta, angagwiritsiridwenso ntchito kupangira mankhwala otetezera kuvunda ndi mankhwala ophera tizirombo. Ponena za chuma chambiri chadziko lapansi, pakali chikhalirebe zochuluka za kuziphunzira ponena za mmene zingagwiritsiridwire ntchito mopindulitsa. Ngakhale kaufiti ngwopindulitsa m’kutetezera kukokololoka kwa nthaka ndi kugaŵira chonde pamene nthaka sikulimidwa.
Kodi munthu angachitenji ngati wayesa kuwonjoka ku kusuta fodya kapena kugwiritsira ntchito mankhwala ena ogodomalitsa ndipo sanapeze chipambano?
Choyamba, mwa phunziro Labaibulo ndi kusinkhasinkha ndipo mufunikira kukulitsa chikhumbo champhamvu cha kukondweretsa Mulungu ndi cha kukhala ndi moyo m’dongosolo lake latsopano lolungama lazinthu. Ngati muyandikira kwa iye, iye adzayandikira kwa inu, kukukupatsani chithandizo chofunika.—Yak. 4:8.
Nkofunika kukhala wotsimikizira za kuipa kwa zizoloŵezi zimenezi ndi kukulitsa kuzida mowona mtima. (Sal. 97:10) Zimenezi zingachitidwe mwa kupenda maumboni olembedwa m’gawo lino labukhu ndi kusinkhasinkha, osati pa chikondwerero chakanthaŵi chatsopano chimene chingachokere m’zizoloŵezi, koma pa zokondweretsa Mulungu ndi mmene zotulukapo za zizoloŵezi zoipa zingakhalire zonyasa.
Ngati mwamva chilakolako champhamvu cha kufuna kusuta fodya kapena kugwiritsira ntchito amodzi a mankhwala ogodomalitsa enawo, pempherani mwaphamphu kwa Mulungu kaamba ka chithandizo. (Luka 11:9, 13; yerekezerani ndi Afilipi 4:13.) Teroni nthaŵi yomweyo. Ndiponso, tengani Baibulo lanu ndipo ŵerengeni mofuula, kapena wonanani ndi Mkristu wachikulire. Muuzeni zimene zikuchitika ndipo pemphani chithandizo chake.
-
-
Mariya (Amayi ŵa Yesu)Kukambitsirana za m’Malemba
-
-
Mariya (Amayi ŵa Yesu)
Tanthauzo: Mkazi wosankhidwa ndi Mulungu ndi woyanjidwa kwambiri amene anabala Yesu. Pali Amariya ena asanu otchulidwa m’Baibulo. Ameneyu anali mbadwa ya Mfumu Davide, wa fuko la Yuda, ndipo anali mwana wamkazi wa Heli. Pamene akudziŵikitsidwa kwa ife kwa nthaŵi yoyamba m’Malemba, iye ngwopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, amenenso anali wa fuko la Yuda ndi mbadwa ya Davide.
Kodi tingaphunzirenji kuchokera ku cholembedwa cha Baibulo chonena za Mariya?
(1) Phunziro la kufunitsitsa kumvetsera zimene Mulungu amanena kupyolera mwa amithenga ake ngakhale ngati zimene timva poyamba zingativutitse maganizo kapena kuwonekera kukhala zosatheka.—Luka 1:26-37.
(2) Kulimba mtima kuchita mogwirizana ndi zimene munthuwe umva kukhala chifuniro cha Mulungu, kudalira kotheratu mwa iye. (Wonani Luka 1:38. Monga momwe kwasonyezedwera pa Deuteronomo 22:23, 24, pakakhala zotulukapo zowopsa kwa msungwana Wachiyuda wosakwatidwa amene anapezedwa ndi pakati.)
(3) Kufunitsitsa kwa Mulungu kugwiritsira ntchito munthu mosasamala kanthu mkhalidwe wa munthuyo m’moyo.—Yerekezerani ndi Luka 2:22-24 ndi Levitiko 12:1-8.
(4) Kuika chigogomezero pazinthu zauzimu. (Wonani Luka 2:41; Machitidwe 1:14. Sikunali kofunika kuti akazi Achiyuda agwirizane ndi amuna awo paulendo wautali womka ku Yerusalemu panthaŵi ya Paskha chaka chirichonse, koma Mariya anatero.)
-