Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Moyo (Life)
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • kuphunzira kosalekeza, analinganizidwiradi kukhala ndi moyo kosatha?)

      Kodi pali moyo pa maplaneti ena?

      The New York Times ikusimba kuti: “Kufunafuna zolengedwa za luntha kumalo ena m’chilengedwe chonse . . . kunayamba zaka 25 zapitazo . . . Ntchito yochititsa mantha, imene imaphatikizapo kupenda kosamalitsa nyenyezi mabiliyoni mazana ambiri, kufikira panopa sikunatulutse umboni wowoneka bwino wakuti moyo ungapezeke kutali ndi Dziko Lapansi.”—July 2, 1984, p. A1.

      The Encyclopedia Americana imati: “Palibe maplaneti ena [kunja kwa maplaneti athu ozungulira dzuŵa] amene atumbidwa motsimikizirika. Koma paplaneti lirilonse limene lingakhaleko kunja kwa maplaneti ozungulira dzuŵa, pali kuthekera kwakuti moyo unayamba ndipo unasinthika kukhala kutsungula kwapamwamba.” (1977, Vol. 22, p. 176) (Monga momwe kwasonyezedwera m’mawu ameneŵa, kodi kungakhale kuli kwakuti chisonkhezero chachikulu m’kufunafuna moyo kutali m’mlengalenga kodya ndalama kopambanako ndiko chikhumbo cha kupeza umboni wina wanthanthi ya chisinthiko, umboni wina wakuti munthu sanalengedwe ndi Mulungu ndipo chotero saali ndi mangaŵa kwa Iye?)

      Baibulo limavumbula kuti moyo padziko lino lapansi sindiwo wokha moyo umene ulipo. Pali zolengedwa zauzimu—Mulungu ndi angelo—amene ali apamwamba kwambiri kuposa munthu mu nzeru ndi m’mphamvu. Iwo alankhulana kale ndi anthu, kufotokoza chiyambi cha moyo ndi imene iri njira yothetsera mavuto othetsa nzeru amene amayang’anizana ndi dziko. (Wonani mutu waukulu wakuti “Baibulo” ndi wakuti “Mulungu.”)

  • Moyo (Soul)
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Moyo (Soul)

      Tanthauzo: M’Baibulo, “moyo” watembenuzidwa kuchokera ku liwu Lachihebri neʹphesh ndi Lachigiriki psy·kheʹ. Baibulo limasonyeza moyo kukhala munthu kapena nyama kapena moyo umene munthu kapena nyama iri nawo. Komabe, kwa anthu ambiri “moyo” umatanthauza kanthu kena kolekana ndi thupi kapena mbali yauzimu ya munthu imene imapulumuka pa imfa ya thupi la munthu. Ena amauzindikira kukhala magwero a moyo. Koma malingaliro otsirizira ameneŵa saali ziphunzitso za Baibulo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena