-
HeloKukambitsirana za m’Malemba
-
-
zenizeni kapena chinali kokha fanizo la kanthu kena? The Jerusalem Bible, m’mawu amtsinde, limavomereza kuti iri ndilo “fanizo mumpangidwe wanthano popanda kutchula munthu aliyense wa m’mbiri. “Ngati angatengedwe mmene mawuwo aliri, kukanatanthauza kuti awo okhala ndi chiyanjo cha Mulungu akanakwana onse pa chifuwa cha munthu mmodzi, Abrahamu; kuti madzi pansonga ya chala chamunthuyo sakanaumikidwa ndi moto wa m’Hade; kuti dontho lokha likanabweretsa mpumulo kwa munthu wovutika mmenemo. Kodi zimenezo zikumvekera kukhala zomveka? Ngati zinali chonchodi, zikanasiyana ndi mbali zina za Baibulo. Chotero ngati Baibulo linali lodzitsutsa motero, kodi wokonda chowonadi akanaligwiritsira ntchito monga maziko achikhulupiriro chake? Komatu Baibulo silimadzitsutsa.
Kodi fanizolo limatanthauzanji? “Wachuma” amaimira Afarisi. (Wonani vesi 14.) Lazaro wopemphapempha amaimira anthu wamba Achiyuda amene anali onyozedwa ndi Afarisi koma amene analapa nakhala otsatira Yesu. (Wonani Luka 18:11; Yohane 7:49; Mateyu 21:31, 32.) Imfa zawo zinalinso zophiphiritsira, zikumaimira kusintha m’mikhalidwe. Chotero, awo amene poyamba anali oluluzika anafikira kukhala mmalo oyanjidwa ndi Mulungu, ndipo amene poyamba anawonekera kukhala oyanjidwa anakanidwa ndi Mulungu, pamene anazunzidwa ndi mauthenga achiweruzo operekedwa ndi anthu amene iwo anawanyoza.—Mac. 5:33; 7:54.
Kodi ndiati amene ali magwero a chiphunzitso cha helo wamoto?
Mu zikhulupiriro za Babulo ndi Suriya wakale “dziko lapansi pa nthaka . . . likuchitiridwa chinthunzi ndi malo odzala ndi zonyansa, ndipo likuyang’aniridwa ndi milungu ndi ziwanda zanyonga ndi zochititsa mantha.” (The Religion of Babylonia and Assyria, Boston, 1898, Morris Jastrow, Jr., p. 581) Umboni woyamba wa mbali yamoto wa helo Wadziko Lachikristu ukupezedwa m’chipembedzo cha Igupto wakale. (The Book of the Dead, New Hyde Park, N.Y., 1960, limene mawu ake oyambirira analembedwa ndi E. A. Wallis Budge, pp. 144, 149, 151, 153, 161) Chibuddha, chimene chinayambira kalekale m’zaka za zana la 6 B.C.E., m’nthaŵi yokwanira chinasonyeza mwapadera ponse paŵiri helo wotentha ndi helo wozizira. (The Encyclopedia Americana, 1977, Vol. 14, p. 68) Zithunzi za helo wosonyezedwa m’matchalitchi a Katolika mu Italiya ziri ndi magwero akalekale a Etruria.—La civiltà etrusca (Milan, 1979), Werner Keller, p. 389.
Koma magwero enieni a chiphunzitso chochitira chipongwe Mulungu chimenechi ngwozama kwambiri. Malingaliro auchiwanda ogwirizanitsidwa ndi helo wozunza amasinjirira Mulungu ndipo magwero ake ndiye wosinjirira wamkulu wa Mulungu (Mdyerekezi, dzina limene limatanthauza “Wosinjirira”), iye amene Yesu Kristu anamutcha “Atate wabodza.”—Yoh. 8:44.
-
-
ImfaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Imfa
Tanthauzo: Kulekeka kwa kugwira ntchito konse kwa moyo. Pamene kupuma, kugunda kwamtima, ndi kugwira ntchito kwa ubongo zileka, mphamvu ya moyo pang’ono ndi pang’ono imaleka kugwira ntchito m’maselo athupi. Imfa ndiyo kusiyana ndi moyo.
Kodi munthu analengedwa ndi Mulungu kuti afe?
Mosemphana ndi zimenezi, Yehova anachenjeza Adamu kusakhala wosamvera, kumene kukanatsogolera ku imfa. (Gen. 2:17) Pambuyo pake, Mulungu anachenjeza Aisrayeli motsutsana ndi kudzisungira kumene kukanatsogolera ngakhale ku imfa yamwamsanga kwa iwo. (Ezek. 18:31) M’nthaŵi yokwanira anatumiza Mwana wake kukafera anthu kotero kuti awo amene akakhulupirira m’kakonzedwe kameneka akakhale nawo moyo wosatha.—Yoh. 3:16, 36.
Salmo 90:10 limanena kuti nthaŵi yozoloŵereka ya moyo wamunthu ndiyo zaka 70 kapena 80. Zimenezo zinali zowona pamene Mose analemba, koma sizinali choncho kuyambira pachiyambi. (Yerekezerani ndi Genesis 5:3-32.) Ahebri 9:27 amati: “Popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi.” Izinso, zinali zowona pamene zinalembedwa. Koma sizinali choncho Mulungu asanapereke chiŵeruzo pa Adamu wochimwayo.
Kodi nchifukwa ninji timakalamba ndi kufa?
Yehova analenga anthu aŵiri oyamba ali angwiro, okhala ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha. Anapatsidwa ufulu wakudzisankhira. Kodi akamvera Mlengi wawo mwachikondi ndi chiyamikiro kaamba ka zonse zimene anali atawachitira? Iwo anali oti nkukhoza kotheratu kuchita choncho. Mulungu anauza Adamu kuti: “Koma mtengo wakudziŵitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadye umenewo udzafa ndithu.” Mogwiritsira ntchito njoka monga
-