-
MwaziKukambitsirana za m’Malemba
-
-
mwa kuswa lamulo lake kukakhala chosankha choipa? Ine ndiridi ndi chikhulupiriro kwa Mulungu. Kodi inu muli nacho? Mawu ake amalonjeza chiukiriro cha awo amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wake. Kodi mumakhulupirira zimenezo? (Yoh. 11:25)’
Kapena munganene kuti: ‘Kungatanthauze kuti sing’angayo sadziŵa mmene angaperekere mankhwala popanda kugwiritsira ntchito mwazi. Ngati kuli kotheka, timayesa kumchititsa kuwonana ndi dokotala amene anali ndi chidziŵitso chofunikacho, kapena timakafunafuna mautumiki a dokotala wina.’
-
-
MzimuKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Mzimu
Tanthauzo: Liwu Lachihebri ruʹach ndi Lachigiriki pneuʹma, amene kaŵirikaŵiri amatembenuzidwa “mzimu,” ali ndi matanthauzo angapo. Iwo onse amasonya kuchinthu chosawoneka ndi maso aumunthu ndi chimene chimapereka umboni wa mphamvu mwa kuyenda. Mawu Achihebri ndi Achigiriki amagwiritsidwa ntchito kutanthauza (1) mphepo, (2) mphamvu yogwira ntchito ya moyo m’zolengedwa za padziko lapansi, (3) mphamvu yosonkhezera imene imatuluka mu mtima wophiphiritsira wa munthu ndi imene imamchititsa kunena ndi kuchita zinthu mwanjira ina yake, (4) mawu ouziridwa ochokera m’magwero osawoneka, (5) anthu auzimu, ndi (6) mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, kapena mzimu woyera wa Mulungu. Kugwiritsiridwa ntchito kungapo kwa zimenezi kwakambitsiridwa panopa mogwirizana ndi mitu yankhani imene ingabuke muuminisitala wakumunda.
Kodi mzimu woyera nchiyani?
Kuyerekezera malemba a Baibulo amene amatchula mzimu woyera kumasonyeza kuti umanenedwa kunakhala ‘ukudzaza’ anthu; iwo angakhoze ‘kubatizidwa’ nawo; ndipo angakhoze “kudzozedwa” nawo. (Luka 1:41; Mat. 3:11; Mac. 10:38) Palibe alionse a mawu ameneŵa akakhala oyenerera ngati mzimu woyera unali munthu.
Yesu anatchulanso mzimu woyera kukhala “nkhoswe” (Chigiriki, pa·raʹkle·tos), ndipo ananena kuti nkhoswe imeneyi ikakhoza ‘kuphunzitsa,’ “kuchitira umboni,” “kulankhula,” ndi ‘kumva.’ (Yoh. 14:16, 17, 26; 15:26; 16:13) Sikuli kwachilendo m’Malemba kuti kanthu kena kanenedwe monga munthu. Mwachitsanzo, nzeru ikunenedwa kukhala iri ndi “ana.” (Luka 7:35) Uchimo ndi imfa zimanenedwa kukhala monga mafumu. (Aroma 5:14, 21) Pamene kuli kwakuti malemba ena amanena kuti mzimu “unalankhula,” malemba ena amanena momvekera bwino kuti zimenezi zinachitidwa kudzera mwa angelo kapena anthu. (Mac. 4:24, 25; 28:25; Mat. 10:19, 20; yerekezerani ndi Machitidwe 20:23 ndi 21:10, 11.) Pa 1 Yohane 5:6-8, simzimu wokha umene wanenedwa kukhala “ukuchitira umboni” komanso “madzi ndi mwazi.” Chotero, palibe alionse a mawu opezedwa m’malemba ameneŵa amene mwa iwo okha amatsimikizira kuti mzimu woyera ndimunthu.
Tanthauzo lolungama la mzimu woyera liyenera kuyenerana ndi malemba onse amene amatchula mzimuwo. Tiri ndi lingaliro limeneli, kuli koyenera kunena kuti mzimu woyera ndiwo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Suli munthu, koma ndiyo nyonga yamphamvu imene Mulungu amachititsa kutuluka mwa iye kukwaniritsa chifuniro chake.—Sal. 104:30; 2 Pet. 1:21; Mac. 4:31.
Wonaninso tsamba 393, 394, pamutu wakuti “Utatu.”
Kodi nchiyani chimene chimapereka umboni wakuti munthu alidi ndi mzimu woyera, kapena “Mzukwa Woyera” (KJ)?
Luka 4:18, 31-35: “[Yesu anaŵerenga m’mpukutu wa mneneri Yesaya:] ‘Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka uthenga wabwino . . . Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mudzi wa ku Galileya. Ndipo anali kuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake; chifukwa mawu ake anali ndi ulamuliro. Ndipo munali m’sunagoge munthu, wokhala nacho chiŵanda chonyansa; nafuula ndi mawu olimba, . . . Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiŵandacho mmene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.” (Kodi nchiyani chimene chinatsimikizira kuti Yesu anali ndi mzimu wa Mulungu? Cholembedwacho sichimanena kuti iye anathunthumira kapena anafuula kapena kuyendayenda mokangalika. Mmalo mwake, chimanena kuti analankhula mwaukumu. Komabe, kuli kokondweretsa kuwona, kuti panthaŵiyo mzimu wachiŵanda unachititsa munthuyo kufuula ndi kumgwetsera pansi.)
Mac. 1:8 amanena kuti pamene otsatira a Yesu analandira mzimu woyera akakhala mboni zake. Mogwirizana ndi kunena kwa Machitidwe 2:1-11, pamene analandira mzimu umenewo, openyerera anachita chidwi ndi chenicheni chakuti, ngakhale
-