-
Adamu ndi HavaKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Uchimo wa Adamu unali chifuniro cha Mulungu, kakonzedwe ka Mulungu’
Mungayankhe kuti: ‘Anthu ambiri anena zimenezo. Koma ngati ine ndinafunikira kuchita kanthu kena kamene inu munafuna kuti ndichite, kodi mukanditsutsa nako kanthuko? . . . Pamenepa, ngati uchimo wa Adamu unali chifuniro cha Mulungu, kodi nchifukwa ninji Adamu anathamangitsidwa m’munda wa Edene monga wochimwa? (Gen. 3:17-19, 23, 24)’
Kapena mukanati: ‘Imeneyo iri mfundo yokondweretsa, ndipo yankho limaphatikizapodi mtundu wa munthu amene Mulungu ali. Kodi kukakhala kolungama kapena kwachikondi kutsutsa munthu kaamba ka kuchita chinthu chimene inu mwini mwamlinganizira kuti achite?’ Ndiyeno mwinamwake mungawonjezere: (1) ‘Yehova ali Mulungu wachikondi. (1 Yoh. 4:8) Njira zake zonse ndichiweruzo. (Sal. 37:28; Deut. 32:4) Sichinali chifuniro cha Mulungu kuti Adamu achimwe; iye anachenjeza Adamu kusatero. (Gen. 2:17)’ (2) ‘Mulungu analoleza Adamu, monga momwe amachitira kwa ife, ufulu wa kusankha chimene akachita. Ungwiro sunaletse kugwiritsira ntchito ufulu wa kusankha kusamvera. Adamu anasankha kupandukira Mulungu, mosasamala kanthu za chenjezo lakuti imfa ikakhala chotulukapo.’ (Wonaninso tsamba 118.)
-
-
AkaziKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Akazi
Tanthauzo: Anthu achikulire achikazi. M’Chihebri, liwu lakuti mkazi ndiro ’ish·shahʹ, limene kwenikweni limatanthauza “mwamuna wachikazi.”
Kodi Baibulo limaluluza akazi kapena kuwachitira ngati kuti anali anthu apansi?
Gen. 2:18, NW: “Yehova Mulungu anapitirizabe kunena kuti: ‘Sikuli bwino kuti mwamuna apitirizebe kukhala yekha. Ndidzampangira womthangata, monga womkwaniritsa.’” (Panopa mwamuna sakulongosoledwa ndi Mulungu kukhala munthu wabwino kwambiri kuposa mkazi. Mmalo mwake, Mulungu anasonyeza kuti mkazi akakhala ndi mikhalidwe imene ikwaniritsa ya mwamuna mkati mwa kakonzedwa ka Mulungu. Chokwaniritsa ndicho chimodzi cha zinthu ziŵiri zimene zimapanga chinthu
-