Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Satana Mdyerekezi
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • 20:3 (KJ) chimanena kuti Satana ‘akuponyedwa . . . m’dzenje lopanda mapeto,’ iye ndithudi sakungosiyidwa pamene iye ali kale—wosawoneka koma wobindikiritsidwira kumalo a dziko lapansi. Iye ali kutali ndi kumeneko, “kuti asanyengenso amitundu, kufikira zikatha zaka chikwi.” Tawonani kuti Chivumbulutso 20:3 chimanena kuti, pamapeto a zaka chikwi, ndiye Satana, osati amitundu, amene amasulidwa kuphompho. Pamene Satana amasulidwa, anthu amene kalelo anapanga mitundu imeneyo adzakhala aliko kale.

      Yesaya 24:1-6 ndi Yeremiya 4:23-29 (KJ) nthaŵi zina amatchulidwa kuchirikiza chiphunzitso chimenechi. Ameneŵa amati: “Tawonani, Yehova apululutsa dziko, nalipasula . . . dziko lidzapululuka konse, ndi kupasulidwa ndithu; pakuti Yehova ananena mawu ameneŵa.” “Ndinawona dziko lapansi, ndipo tawona linali lopasuka lopanda kanthu . . . ndinawona, ndipo tawona panalibe munthu . . . pakuti Yehova atero dziko lonse lidzakhala bwinja . . . midzi yonse idzasiyidwa, ndipo simudzakhala munthu mmenemo.” Kodi nchiyani chimene maulosi ameneŵa amatanthauza? Anali ndi kukwaniritsidwa kwawo koyamba pa Yerusalemu ndi padziko la Yuda. M’kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu, Yehova analola Ababulo kugonjetsa dzikolo. Potsirizira pake linasiyidwa lonse labwinja ndi lapululu. (Wonani Yeremiya 36:29.) Koma Mulungu sanakhalitse labwinja dziko lonse panthaŵiyo, ndiponso iye sadzatero tsopano. (Wonani tsamba 131-133, pamutu wakuti “Dziko Lapansi,” ndiponso mutu waukulu wakuti “Kumwamba.”) Komabe, iye adzapululutsa kotheratu ponse paŵiri mnzake wamakono wa Yerusalemu wosakhulupirika, Dziko Lachikristu, limene limatonza dzina la Mulungu mwa makhalidwe ake oipa, ndi mbali yonse yotsala ya gulu lowoneka la Satana.

      Mmalo mwa kukhala lapululu ndi labwinja, mkati mwa Zaka Chikwi za Kulamulira kwa Kristu, ndipo pamene Satana ali chiponyedwere m’mphompho, dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. (Wonani “Paradaiso.”)

  • Tchimo
    Kukambitsirana za m’Malemba
    • Tchimo

      Tanthauzo: Kwenikweni, kuphonyedwa kwa chizindikiro, mogwirizana ndi kunena kwa malemba apamanja a Baibulo Achihebri ndi Achigiriki. Mulungu mwini amakhazikitsa “chizindikiro” chimene zolengedwa zake zaluntha ziyenera kufikira. Kuphonya chizindikiro chimenecho ndiko tchimo, limenenso liri chisalungamo, kapena kusayeruzika. (Aroma 3:23; 1 Yoh. 5:17; 3:4) Tchimo ndiro

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena