Yerusalemu ndi Kachisi wa Solomo
ANKATCHEDWA ‘wokongola mwangwiro’ komanso ‘mudzi wa Mfumu yaikulu.’ (Sal. 48:2; 50:2; Maliro 2:15) Yerusalemu anali likulu la mtundu wa Mulungu. (Sal. 76:2) Davide ataulanda kwa Ayebusi n’kuikako likulu lake, mudziwu unayamba kutchedwa “mudzi wa Davide,” kapena kungoti “Ziyoni.”—2 Sam. 5:7.
Ngakhale kuti sanali pamalo abwino kwenikweni, Yerusalemu anatchuka chifukwa chakuti Mulungu anaikako dzina lake. (Deut. 26:2) Anali likulu la chipembedzo ndiponso likulu la boma la mtundu wa Israyeli.
Yerusalemu ali pamalo okwera mamita 750 m’katikati mwa mapiri a Yudeya. Baibulo limafotokoza za “phiri” lake ndipo limati olambira ankachita ‘kukwera’ kuti akafikepo. (Sal. 48:2; 122:3, 4) Mudzi wakalewu unazunguliridwa ndi zigwa: kumadzulo ndi kum’mwera kwake kunali Chigwa cha Hinomu ndipo kum’maŵa kwake kunali chigwa cha Kidroni. (2 Maf. 23:10; Yer. 31:40) Mudziwu unkapeza madzi abwino pa akasupe a Gihonia m’Chigwa cha Kidroni ndi Eni-rogeli kumadzulo kwake, ndipo akasupeŵa anali ofunika kwambiri makamaka adani akauukira mudziwu.—2 Sam. 17:17.
Pachithunzi chomwe chili patsamba 21, Mudzi wa Davide ndi wofiirawo. Mu ulamuliro wa Davide ndi Solomo, mudziwu unakula kuloŵera kumpoto n’kukaphatikiza Ofeli (dera lagirini) ndi Phiri la Moriya (dera labluu). (2 Sam. 5:7-9; 24:16-25) Solomo anamangira Yehova kachisi wokongola kwambiri pamalo okwera a paphiri limeneli. Tayerekezerani kuti mukuona anthu miyandamiyanda akukhamukira ku “phiri la Yehova” kudzachita mapwando apachaka! (Zek. 8:3) Maulendo oterowo anali osavuta chifukwa cha misewu yomwe yasonyezedwa patsamba 17.
Kachisi wa Solomo, yemwe anam’kongoletsa ndi golide ndiponso miyala ina yamtengo wapatali, anali imodzi mwa nyumba zomwe zamangidwa ndi ndalama zambiri. Yehova ndiye anakonza mapulani ake, ndipo zimenezi zili ndi tanthauzo kwambiri. Monga momwe mukuonera pachithunzipa, kachisiyu anali ndi mabwalo akuluakulu ndiponso nyumba zaboma zikuluzikulu kumbali yake inayo. Ndi bwino kuphunzira zinthu zosiyanasiyana zokhudza kachisiyu.—1 Maf. 6:1–7:51; 1 Mbiri 28:11-19; Aheb. 9:23, 24.
[Mawu a M’munsi]
a Mfumu Hezekiya anatseka kasupeyu n’kukumba ngalande yokafika kudziŵe la kumadzulo kwa mudziwu.—2 Mbiri 32:4, 30.
[Bokosi patsamba 21]
M’kupita kwa nthaŵi, Yerusalemu anakula kuloŵera kumadzulo ndi kumpoto. Mafumu a Yuda olamulira pambuyo pa Solomo anawonjezera malinga ake ndi zipata zake. Kufukula za m’mabwinja komwe kuli m’kati kungathandize kudziŵa malo ake enieni a mbali zina za malingawo ndi kumene anadutsa. Mzindawu unawonongedwa mu 607 B.C.E. ndipo unakhala bwinja zaka 70. Patatha zaka pafupifupi 80 Ayuda atabwerera kwawo, Nehemiya anayamba ntchito yaikulu yomanganso malinga a Yerusalemu.
[Chithunzi patsamba 21]
(Onani m’kabuku kenikeni kuti mumvetse izi)
Yerusalemu/Kachisi wa Solomo
MALO A KACHISI M’NTHAŴI YA SOLOMO
Mbali za Kachisi
1. Malo Opatulikitsa
2. Malo Opatulika
3. Likole
4. Boazi
5. Yakini
6. Guwa la Nsembe Lamkuwa
7. Thaŵale Lamkuwa
8. Maphaka
9. Zipinda za M’mbali
10. Zipinda Zodyera
11. Bwalo Lamkati
MALO A KACHISI
Phiri la Moriya
Zipinda Zodyera
Maphaka
Zipinda za M’mbali
Malo Boazi
Opatulikitsa Malo Opatulika Guwa la Nsembe Bwalo
Yakini Lamkuwa Lamkati
Maphaka Thaŵale
Lamkuwa
Ofeli
Bwalo la Kuchipata?
Chipata cha Kumadzi?
MUDZI WA DAVIDE
Phiri la Ziyoni
Nyumba Yachifumu ya Davide
Chipata cha Chitsime
Linga la Manase?
Nsanja ya Hananeeli
Nsanja ya Mea
Chipata cha Nkhosa
Chipata cha Kaidi
Chipata cha Hamifikadi
Chipata cha Akavalo
CHIGWA CHA KIDRONI
Linga la Kunsi?
Gihoni
Ngalande yomwe anadzakumba
CHIGWA CHA TYROPOEON
Chipata cha Kudzala (Mapale) (Ndowe)
Eni-rogeli
Chipata cha Kuchigwa
CHIGWA CHA HINOMU
Chipata cha Kungondya
Nsanja ya Ng’anjo
Linga Lachitando
Chipata cha Efraimu
Bwalo la Kuchipata
Chipata cha Mudzi Wakale
Linga Lakale Lakumpoto
DERA LACHIŴIRI
Chipata cha Nsomba
[Chithunzi]
Ofeli
Nyumba ya Mwana Wamkazi wa Farao
Nyumba Yachifumu ya Solomo
Nyumba ya Nkhalango ya Lebano
Khumbi la Nsanamira
Khumbi la Mpando Wachifumu
Phiri la Moriya
Bwalo Lalikulu
Kachisi
[Chithunzi patsamba 20]
Pachithunzipa, “Mudzi wa Davide” unali chakuno. Kachisi anali pamalo afulati (kutsogoloko)
[Chithunzi patsamba 20]
Chithunzi chopanga pakompyuta cha “Mudzi wa Davide” wakale ndi kachisi wa Solomo