NYIMBO 8
Yehova Ndi Pothawirapo Pathu
Losindikizidwa
1. Yehova m’pothawira,
Timamudalira.
Tikhalebe mumthunzi
Womwe watipatsa.
Iye adzatiteteza
Tikhulupirire ndithu.
Yehova mphamvu yathu,
Adzateteza ofatsa.
2. Kaya ambiri agwe
Pafupi ndi ife,
Yehova satisiya
Adzatiteteza.
Choncho tisachite mantha,
Tsoka silidzatigwera.
Yehova M’lungu wathu
Adzatibisa m’mapiko.
3. Ku misampha yambiri
Adzatiteteza.
Zoopsa zilizonse
Sitidzaziopa.
Zoopsa zonse zidzatha.
Tidzapita kulikonse.
Yehova m’pothawira,
Adzatiteteza ndithu.
(Onaninso Sal. 97:10; 121:3, 5; Yes. 52:12.)