-
Chiyembekezo Chimathandizadi?Galamukani!—2004 | May 8
-
-
Chiyembekezo Chimathandizadi?
DANIEL anali ndi zaka teni basi, koma anali atatha chaka chathunthu akuvutika ndi matenda a kansa. Madokotala ndiponso achinansi ake anali atataya kale mtima. Koma Daniel sanataye mtima ayi. Iye ankakhulupirira kuti akadzakula adzakhala wofufuza ndipo adzathandiza kupeza mankhwala ochiritsa matenda a kansa. Chinamulimbitsanso mtima makamaka chinali chakuti ankayembekezera kubwera kwa dokotala wodziŵa bwino za kansa yakeyo. Komano tsiku lake litakwana, dokotalayo analephera kubwera chifukwa kunja sikunache bwino. Zimenezi Daniel zinamulefula. Kwa nthaŵi yoyamba, iye anatayiratu mtima. Kenaka patangotha masiku angapo anamwalira.
Amene anasimba nkhani ya Daniel ndi munthu wina wa zaumoyo yemwe anafufuza mmene chiyembekezo ndi kutaya mtima zimakhudzira thanzi lathu. N’kutheka kuti nkhani zoterezi munazimvapo. Mwachitsanzo, mwina munamvapo za agogo enaake amene ankadwala mwakayakaya komano ankafunitsitsa ataona chinthu chinachake chomwe achidikirira kwa nthaŵi yaitali; chinthu monga kufika kwa wokondedwa wawo winawake kapena chabe chikondwerero chinachake cha pachaka. Ndiye chinthucho chitangochitika, basi agogowo anafa. Kodi n’chiyani chimachititsa zoterezi? Kodi kukhala n’chiyembekezo n’kothandizadi kwambiri monga mmene anthu ena amaganizira?
Anthu ambiri ofufuza za matenda amati kusataya mtima, kukhala n’chiyembekezo, komanso maganizo ena otere, kumathandizadi pa moyo ndiponso thanzi la munthu. Komano si onse amagwirizana ndi mfundoyi. Ofufuza ena amati zimenezi n’zikhulupiriro chabe ndipo zilibe umboni wasayansi. Iwoŵa amaona kuti matenda amayambitsidwa ndi zinthu zenizeni osati za m’maganizo chabe ayi.
Inde, kuyambira kale anthu akhala asakukhulupirira kuti chiyembekezo n’chothandizadi. Zaka masauzande zapitazo, Aristotle, yemwe anali wafilosofi wa ku Greece anafunsidwapo kuti anene tanthauzo la chiyembekezo, ndiyeno iye anayankha kuti chiyembekezo “n’kulota uli maso.” Ndipo osati kale kwenikweni, mtsogoleri wa dziko la America, Benjamin Franklin ananena monyoza kuti: “Wodalira chiyembekezo amangotaya nthaŵi pachabe.”
Motero kodi zoona zake zenizeni za chiyembekezo n’zotani? Kodi nthaŵi zonse munthu akakhala n’chiyembekezo amakhala akungodzinamiza yekha kuti akwanitsa kuchita zinthu zomwe kwenikweni zili zosatheka? Kapena kodi pali zifukwa zomveka zoganizira kuti chiyembekezo n’chinthu chofunikiradi kwa tonsefe kuti tikhale athanzi ndi osangalala, komanso kuti chiyembekezo n’chinthu chotsimikizika ndiponso chopindulitsadi?
-
-
Kodi Timafuniranji Chiyembekezo?Galamukani!—2004 | May 8
-
-
Kodi Timafuniranji Chiyembekezo?
KODI Daniel, yemwe ankadwala matenda a kansa, amene tam’tchula m’nkhani yam’mbuyo uja, akanati asatayebe mtima zinthu zikanamuyendera bwanji? Kodi akanachira matenda a kansawo? Kodi bwenzi ali moyobe panopo? Ngakhale anthu ogogomezera kwambiri ubwino wa chiyembekezo sanganene kuti akanatero. Ndipotu pamenepa pagona mfundo yofunika kwambiri; mfundo yakuti sitiyenera kukokomeza ubwino wa chiyembekezo. Chiyembekezo si mankhwala ochiritsa vuto lililonse.
Poyankha mafunso omwe a bungwe lofalitsa nkhani la Columbia Broadcasting System anali kumufunsa, Dr. Nathan Cherney anachenjeza kuti kukokomeza ubwino wa chiyembekezo kungathe kupweteketsa odwala amene matenda awapezeketsa kwambiri. Iye anati: “Taonapo amuna akunena akazi awo kuti akufulumira kutaya mtima.” Dr. Cherney anapitiriza kuti: “Maganizo ameneŵa achititsa anthu kumaona kuti matenda awo angathe kuchepa ngati sakutaya mtima, ndiyeno matendawo akamaipiraipira ena amaganiza kuti ndiye kuti odwalawo akufulumira kutaya mtima, komatu uku n’kulakwa.”
Zoona zake n’zakuti anthu amene akudwala matenda akayakaya amasauka nawo kwambiri matendawo. Motero si bwino kuti pamwamba pa zimenezi, ife owakondafe tiwachititse kuti azidziimba mlandu. Komano kodi tingati chiyembekezo chilibe kanthu?
Ayi sitingatero. Mwachitsanzo, dokotala tam’tchula uja, ndi katswiri wa chithandizo chosalimbana ndi nthenda kapena kutalikitsa moyo wa wodwala, koma chongothandiza kuti moyo wake ukhale wofeŵerapo panthaŵi yonse yomwe akudwalayo. Madokotala otereŵa amaona kuti chithandizo chokhazikitsa pansi maganizo a wodwala, ngakhale amene matenda awapezeketsa kwambiri, n’chothandiza kwabasi. Pali umboni wochuluka wosonyeza kuti chiyembekezo n’chothandiza m’njira imeneyi komanso m’njira zina zambiri.
Kuthandiza Kwake kwa Chiyembekezo
Mtolankhani wina amene amalemba nkhani za matenda, dzina lake Dr. W. Gifford-Jones anati: “Chiyembekezo ndi mankhwala amphamvu kwambiri.” Iyeyu anaŵerenga akafukufuku osiyanasiyana omwe anachitidwa pofuna kudziŵa ubwino wolimbikitsa anthu amene akudwala mwakayakaya. Akuti zimenezi zimawathandiza kuti asamataye mtima. Atafufuza m’chaka cha 1989 anapeza kuti odwala amene anathandizidwa m’njira imeneyi ankakhala ndi moyo wautaliko, komano atafufuza posachedwapa sanapeze mfundo iliyonse yotsimikizira zimenezi. Komabe zina zimene akhala akufufuza zatsimikizira kuti odwala amene amalimbikitsidwa savutika maganizo ndiponso samva kuwawa monga odwala ena.
Taganiziraninso za kafukufuku wina wofuna kudziŵa kuti kutaya mtima ndiponso kusataya mtima kumakhudzana bwanji ndi matenda a mitsempha ya kumtima. Amuna okwana 1,300 anawaonetsetsa kwa nyengo yaitali kuti adziŵe ngati anali okonda kutaya mtima msanga kapena ayi. Patatha zaka teni anadzapeza kuti amuna opitirira 12 pa 100 aliwonse pa gululi anadzadwala matenda a mitsempha ya kumtima. Ndipo pa gulu la odwalawo, amuna amene ankataya mtima msanga anali ochuluka moŵirikiza poyerekezera ndi amene sankataya mtima msanga. Laura Kubzansky, yemwe ndi pulofesa wothandizira wa zaumoyo ndi makhalidwe a anthu ku Harvard School of Public Health anati: “Umboni wambiri wotsimikizira kuti ‘kusataya mtima’ kumathandiza pa thanzi la munthu n’ngosatsimikizirika ndi sayansi. Komano pa kafukufuku amene tachitayu, kwa nthaŵi yoyamba, tapeza umboni weniweni wa sayansi wotsimikizira kuti kusataya mtima n’kothandiza munthu akamadwala matenda a mitsempha ya kumtima.”
Ofufuza ena anapeza kuti anthu amene amadziona kuti alibe thanzi labwino sachira mwamsanga pambuyo powachita opaleshoni kusiyana ndi anthu amene amadziona kuti ali ndi thanzi labwino. Akuti zikuoneka kuti kusataya mtima msanga kumathandizanso kuti munthu akhale ndi moyo wautali. Pa kafukufuku wina anafuna kudziŵa mmene kuona ukalamba ngati chinthu chabwino kapena choipa kumakhudzira anthu achikulire. Anthu ena achikulire atawachititsa kuti aziona mawu ongoonekera kwa kanthaŵi kochepa osonyeza kuti kukalamba kumasonyeza nzeru ndi kukhwima maganizo, achikulirewo anapezeka kuti ayamba kuyenda mwamphamvu. Mphamvu anapezazo n’zofanana ndi zimene akanapeza akanati azichita maseŵera olimbitsa thupi kwa milungu 12!
Kodi n’chifukwa chiyani zinthu ngati chiyembekezo, kusataya mtima, ndiponso maganizo abwino zimaoneka kuti zimatipatsa thanzi labwino? N’kutheka kuti asayansi ndiponso madokotala sangatiuze yankho lotsimikizika la funsoli chifukwa samvetsa bwinobwino mmene maganizo ndiponso thupi la munthu limayendera. Komabe akatswiri otere, amene amafufuza nkhaniyi angathe kunenapo malingaliro awo monga anthu oti akuidziŵa bwino nkhaniyi. Mwachitsanzo, pulofesa wina wa zaubongo anati n’kutheka kuti n’chifukwa choti: “Timamva bwino m’thupimu tikakhala osangalala ndiponso osataya mtima. Tikamamva choncho sitikhala ndi nkhaŵa iliyonse ndipo thupi lathu limasangalala. Chimodzi mwa zinthu zina zimene anthu angachite kuti akhale athanzi n’chimenechi.”
Madokotala, akatswiri a maganizo a anthu, ndiponso asayansi ena zimenezi angazione ngati nzeru zatsopano, komatu izi si zatsopano kwa anthu ophunzira Baibulo. Kwa zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, mfumu yanzeru Solomo inauziridwa kulemba mawu aŵa: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Onani kuti lembali silikukokomeza nkhaniyi. Silikunena kuti mtima wosekerera ungathe kuchiritsa nthenda ina iliyonse koma langoti “uchiritsa bwino.”
Ndipotu, sikungakhale kulakwa kufunsa kuti kodi chiyembekezo chikanakhala kuti ndi mankhwala, alipo dokotala amene akanapanda kulembera odwala ake mankhwalaŵa? Komansotu chiyembekezo chimathandiza m’njira ina yofunika kwambiri kuposa thanzi chabe.
Mmene Kusataya Mtima Ndiponso Kutaya Mtima Kumakhudzira Moyo Wanu
Ofufuza anapeza kuti anthu osakonda kutaya mtima amapindula kwambiri chifukwa cha maganizo otere. Nthaŵi zambiri amachita bwino kusukulu, kuntchito ngakhalenso pa zamaseŵera. Mwachitsanzo, anachita kafukufuku pa timu ina ya atsikana yochita maseŵera osiyanasiyana. Makochi a timuyo anafotokoza zonse zokhudza maluso a atsikanawo pa maseŵerawo. Komanso, mtsikana aliyense anam’funsa bwinobwino payekha n’kudziŵa kuti ali ndi chiyembekezo chachikulu motani. Kunapezeka kuti chinthu chothandiza kwambiri kuti atsikanawo aziseŵera bwino chinali chiyembekezo chawo osati maluso ena onse amene makochi awo anatchula. Kodi n’chifukwa chiyani chiyembekezo chimathandiza kwambiri chonchi?
Pali zambiri zimene zadziŵika pofufuza zimene zimachitika tikataya mtima. Atafufuza nkhaniyi cha m’ma 1960, anatulukira zodabwitsa pa khalidwe la nyama, zomwe zinachititsa kuti pabwere mawu akuti “kutaya mtima kochita kuphunzira.” Kenaka anapeza kuti anthu angathenso kukhala ndi vutoli. Mwachitsanzo, pofuna kutsimikiza zimenezi anatenga anthu n’kuwaika pa malo aphokoso loboola mkutu atawauza kuti angathe kuzimitsa phokosolo podina mabatani enaake. Anthuwo anakwanitsa kuzimitsa phokosolo.
Gulu lina la anthu linauzidwa kuchita chimodzimodzi, komano anthuwo akadina mabataniwo palibe chimene chinkachitika. N’zosadabwitsa kuti ambiri pa gululi anafika pongotaya mtima kuti phokosolo silisiya. Kenaka atawayesanso anthuwo anachita mphwayi moti sanayese n’komwe kuzimitsa phokosolo. Iwowo anali ataona kuti palibe chilichonse chimene angachitepo kuti phokosolo lileke. Koma ngakhale m’gulu lachiŵirili, anthu osataya mtima sanalefuke maganizo n’kusiya kuyesayesa.
Dr. Martin Seligman, amene anathandiza kukonza njira zofufuzira pa akafukufuku ena oyamba aja anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anapeza pa ntchito yofufuza mmene kutaya mtima ndiponso kusataya mtima kumakhudzira anthu moti anaisandutsa ntchito yake yeniyeni. Iyeyu anafufuza mosamala za mmene anthu amene ankakonda kudziona ngati olephera amaganizira. Iye anapeza kuti kutaya mtima motere kumasokoneza anthu kuchita zinthu zambiri m’moyo mwinanso kuwalepheretseratu kuchita zinthu bwinobwino. Ponenapo mwachidule za kutaya mtimaku Seligman anati: “Nditafufuza nkhaniyi kwa zaka 25 ndatsimikiza kuti ngati nthaŵi zambiri maganizo athu ali ofanana ndi maganizo a anthu osachedwa kutaya mtima, pomaganiza kuti zinthu zikangolakwika ndiye kuti olakwa ndi ifeyo, komanso kuti zipitirirabe kutero, ndipo kuti zingathe kusokoneza zochita zathu zonse, chimachitika n’chakuti timakumanadi ndi zovuta zambiri kusiyana ndi zimene tikanakumana nazo.”
Kwa ena, izinso zingaoneke ngati zatsopano, komatu si zachilendo kwenikweni kwa anthu ophunzira Baibulo. Taonani mwambi uwu: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” (Miyambo 24:10) Inde, Baibulo limalongosola momveka bwino kuti mukafooka chifukwa cha maganizo, mumalefuka. Ndiyeno kodi mungatani kuti musamataye mtima msanga koma muzikhala ndi chiyembekezo chachikulu?
[Chithunzi pamasamba 12, 13]
Chiyembekezo chingakuthandizeni kwambiri
-
-
Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya MtimaGalamukani!—2004 | May 8
-
-
Mungathe Kuthetsa Khalidwe Lotaya Mtima
KODI mavuto amene mumakumana nawo mumawaona motani? Akatswiri ambiri amakhulupirira kuti munthu amadziŵika kuti ali ndi khalidwe lotaya mtima kapena losataya mtima malingana ndi yankho lake pa funso limeneli. Tonsefe timakumana ndi zovuta zambiri m’moyo wathu ndipo ena zimawachulukira koposa ena. Komano n’chifukwa chiyani zimaoneka kuti anthu ena sachedwa kuiwalako zovuta zawozo ndipo amayambiranso kuyesayesa, pamene ena sachedwa kugonja ngakhale atakumana ndi zovuta zazing’ono chabe?
Mwachitsanzo, ingoyerekezani kuti mukufunafuna ntchito. Motero mukupita kokafunsidwa mafunso oona ngati muli woyenerera ndiyeno akukukanani pa ntchitoyo. Kodi zimenezi zingakukhudzeni bwanji? Mwina mungakhumudwe nazo kwambiri ndipo mungadzione kuti ndinu munthu wokanika, n’kumaganiza kuti, ‘Palibe amene angalembe ntchito munthu ngati ineyo. Zolembedwa ntchito ndingoiwalako basi.’ Mwinanso chifukwa cha zomwezi mungayambe kuona kuti zochitika zanu zonse n’zolephera, n’kumaganiza kuti, ‘Ndine munthu wachabechabe ine. Palibe amene angandione ngati munthu wofunika.’ Maganizo onse otereŵa amasonyeza kutaya mtima.
Kulimbana ndi Khalidwe Lotaya Mtima
Kodi mungalimbane nawo bwanji maganizoŵa? Chinthu choyamba chofunika ndicho kuzindikira kuti muli ndi maganizo otere. Chachiŵiri ndicho kulimbana nawo. Yesani kuganizira zifukwa zina zomveka zimene zachititsa kuti asakulembeni ntchitoyo. Mwachitsanzo, kodi n’zoonadi kuti sanakulembeni chifukwa chakuti palibe amene akanakonda kukulembani ntchito? Kapena kodi n’zotheka kuti pantchitoyo amafuna munthu wodziŵa zinthu zina zimene inuyo simudziŵa?
Mutaganizira mfundo zinazake bwinobwino mungathe kuona kuti maganizo anuwo n’ngokokomeza chabe zinthu. Kodi kukanidwa ntchito kamodzi kokha kumatanthauza kuti ndinu munthu wokanika, moti n’zoona kuti palibiretu zinthu zina m’moyo wanu zimene mumatha kuziyendetsa bwino? Zinthu monga zauzimu, zinthu zokhudza anthu a m’banja mwanu, kapenanso anzanu? Maganizo osathandiza akakufikirani phunzirani kungowakankhira kunkhongo podziŵa kuti inuyo ndi amene mukungowakulitsa m’maganizo mwanumo. Ndiponso kodi mungadziŵedi kuti simudzapezanso ntchito? Pali zina zambiri zimene mungachite kuti musakhale ndi maganizo olefula.
Kuganiza Kwabwino Kofuna Kukwanitsa Zolinga Zanu
Masiku ano tanthauzo la chiyembekezo limene ofufuza anapanga, n’lochititsa chidwi ngakhale kuti n’lopereŵera mwina ndi mwina. Iwowo amanena kuti chiyembekezo chimatanthauza kukhulupirira kuti ukwaniritsa zolinga zako. Monga mmene nkhani yathu yotsatira isonyezere, kwenikweni chiyembekezo chimatanthauzanso zinthu zina zambiri, komano tanthauzo la ofufuzali likuoneka kuti n’lothandiza m’njira zingapo. Kuganizira kwambiri mbali imeneyi ya chiyembekezo kungatithandize kuti tizikhala ndi maganizo abwino, ofuna kukwanitsa zolinga zathu.
Chimene chingatilimbitse mtima kuti tikwaniritse zolinga zathu za m’tsogolo ndicho kukhala ndi chizoloŵezi chopanga zolinga n’kumazikwanitsa. Ngati mukuona kuti mulibe chizoloŵezi chotere, ndi bwino kuganizapo bwino pa zolinga zimene mumapanga. Poyamba, kodi muli ndi cholinga chilichonse chimene mumafuna mutakwanitsa? M’posavuta kumangotanganidwa ndi zochitika zina popanda kuganizirapo kuti n’chiyani makamaka chimene chili chofunika kwambiri pamoyo wathu. Pa mfundo yothandiza yomaona kaye kuti chinthu chofunika kwambiri n’chiti, timapezanso kuti kalekale Baibulo linalondola ponena kuti tiyenera “kusankha zimene zili zofunika kwenikweni.”—Afilipi 1:10, Chipangano Chatsopano Mu Chicheŵa Cha Lero.
Tikatsimikizira zinthu zimene zili zofunika kwambiri kwa ifeyo, sizikhala zovuta kusankha zinthu zofunika kwambiri pamoyo wathu wauzimu, pabanja lathu, kapena pantchito yathu. Komabe ndi bwino kusakhala ndi zolinga zambirimbiri poyamba ndiponso cholinga chilichonse chimene tapanga chizikhala choti tingathe kuchikwanitsa mosavuta. Ngati cholinga chathu chili chovuta kwambiri kukwanitsa, tingathe kufooka n’kugonja. Motero, nthaŵi zambiri zimathandiza kugaŵa zolinga zanu zikuluzikulu m’magawo a zolinga zing’onozing’ono.
“Kanthu n’khama,” anatero akuluakulu akale, ndipotu mawuŵa n’ngoona ndithu. Tikaganizira zolinga zathu zofunika kwambirizo, timafunika kutsimikiza, kufunitsitsadi kuzikwanitsa. Chimene chingatithandize kuti chikhumbo chathuchi chikule ndicho kuganizira ubwino wa zolinga zathuzo ndi mmene zidzatipindulitsire ngati titazikwanitsa. Inde, tidzapeza zovuta zina, koma tiyenera kuona kuti n’zotheka osati ngati kuti n’zosatheka kuzithetsa.
Komanso, tiyenera kuganizira za njira zina zotithandiza kukwanitsa zolinga zathu. Wolemba mabuku wina, C. R. Snyder, yemwe anafufuza kwambiri za phindu la chiyembekezo, anati ndi bwino kuganizira njira zingapo zokwanitsira cholinga chathu. Motero njira imodzi ikakanika, tingathe kuyesa yachiŵiri, kaya yachitatu, n’kumapita m’tsogolo.
Snyder anatinso ndi bwino kuphunzira kudziŵa nthaŵi yosiyira kulimbana n’cholinga chinachake n’kupeza cholinga china choloŵa m’malo mwake. Ngati kukwanitsa cholinga chinachake kukutivuta kwambiri, kudandaula nazo kwambiri kungangotifooketsa. Komano tikakhala n’cholinga china chotheka choloŵa m’malo mwa cholinga chimenecho tingapeze polimbira mtima.
Pankhaniyi, Baibulo lili ndi chitsanzo chothandiza kwambiri. Mfumu Davide anali ndi cholinga choti adzamange kachisi wa Mulungu wake, Yehova. Koma Mulungu anamuuza Davide kuti mwana wake Solomo ndiye adzakhale ndi mwayi wochita zimenezo. M’malo monyanyala kapena kuchita makani atamva zokhumudwitsazi, Davide anangosintha zolinga zake. Ndi mphamvu zake zonse anasonkhanitsa chuma ndiponso zipangizo zimene mwana wake adzafunikire kuti athe kumanga kachisiyu.—1 Mafumu 8:17-19; 1 Mbiri 29:3-7.
Ngakhale ifeyo patokha titakwanitsa kukhala ndi chiyembekezo poyesetsa kukhala ndi maganizo abwino ofuna kukwanitsa zolinga zathu, chiyembekezo chathu chingakhalebe chopereŵera kwambiri. Kodi zingatheke bwanji? Zingatheke chifukwa chakuti masiku ano zinthu zambiri zimene zimatisoŵetsa chiyembekezo ndi zinthu zoti sitingathe kuchitapo kanthu kuti tizisinthe. Kodi tingakhale bwanji ndi chiyembekezo tikamaganizira za mavuto aakulu amene akusautsa anthu, monga umphaŵi, nkhondo, kupanda chilungamo, kuopsa kwa matenda ndiponso imfa?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi akapanda kukulembani ntchito imene mumafuna, mumangofulumira kuganiza kuti simudzapezanso ntchito?
[Chithunzi patsamba 16]
Mfumu Davide anasonyeza kuti anali munthu wololera kusintha zolinga zake
-
-
Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?Galamukani!—2004 | May 8
-
-
Kodi Chiyembekezo Chodalirika Mungachipeze Kuti?
WOTCHI yanu yaima ndipo ikuoneka kuti yawonongeka. Mukuganiza zoikonzetsa ndipo mukupeza kuti pali njira zambirimbiri zoikonzetsera. Onenerera malonda okonza mawotchi angoti mbwee, ndipo ngakhale kuti onsewo akudzitama kuti ndi akatswiri, zonena zawo zina zikutsutsana. Ndiye kodi mungatani ngati mutadziŵa kuti munthu amene mukukhala moyandikana naye ndiye katswiri amene anapanga wotchi yanuyo zaka zambiri zapitazo? Kuphatikizanso apo, mukumva kuti iyeyo angakukonzereni wotchiyo, kwaulere. Kodi pamenepa mungavutikenso n’kuganiza zopita kwina?
Ndiyeno yerekezani wotchiyo ndi mmene chiyembekezo chanu chilili. Ngati mukuona kuti chiyembekezo chanu chikuchepa, monga mmenenso chikuchitira kwa anthu ambiri m’masiku ovuta ano, kodi mungagwire mtengo wanji? Anthu ambiri amanena kuti angathe kuthetsa vuto lotere, koma zinthu zambirimbiri zimene amanena zimakhala zosokoneza ndipo mwinanso zotsutsana kumene. Motero pachiyambi pomwe, bwanji osangopita kwa Iye amene anapanga anthu m’njira yakuti azikhala ndi chiyembekezo? Baibulo limanena kuti iye “sakhala patali ndi yense wa ife.”—Machitidwe 17:27; 1 Petro 5:7.
Tanthauzo Lenileni la Chiyembekezo
Chiyembekezo chotchulidwa m’Baibulo chili ndi tanthauzo latsatanetsatane ndiponso lokhudza zinthu zambiri kuposa tanthauzo limene madokotala, asayansi, ndiponso akatswiri ambiri a zamaganizo amanena. Mawu a chinenero choyamba cha Baibulo amene amamasuliridwa kuti “chiyembekezo” amatanthauza kudikirira mtima uli m’mwamba ndiponso kuyembekezera zabwino. Kwenikweni, chiyembekezo chili mbali ziŵiri. Chili ndi mbali ya chikhumbo chofuna chinthu chinachake chabwino komanso chifukwa chomveka choganizira kuti chabwinocho chichitika. Chiyembekezo cha zinthu zotchulidwa m’Baibulo si cha zinthu zosatheka zimene timangolakalaka chabe ayi. N’chiyembekezo chokhala ndi zifukwa zotsimikizika ndiponso zokhala ndi umboni.
Pa mbali imeneyi, chiyembekezo n’chofanana ndi chikhulupiriro, chifukwa nacho chimayenera kukhala ndi umboni, osati kungokhulupirira zinthu motengeka maganizo ayi. (Ahebri 11:1) Ngakhale zili choncho, Baibulo limasiyanitsa chikhulupiriro ndi chiyembekezo.—1 Akorinto 13:13.
Mwachitsanzo: Mukafunsa mnzanu wapamtima kuti akuthandizeni penapake, mumakhala ndi chiyembekezo chakuti aterodi. Chiyembekezo chotere chili ndi maziko enieni, pakuti mnzanuyo mumamukhulupirira chifukwa chomudziŵa bwino ndipo mwamuonapo akuchita zinthu mokoma mtima ndiponso mowoloŵa manja. Chikhulupiriro ndi chiyembekezo chanu ndi zinthu zoyenderana kwambiri, komabe n’zosiyana. Kodi mungakhale bwanji ndi chiyembekezo chotere mwa Mulungu?
Chifukwa Chokhalira N’chiyembekezo
Mulungu ndiye mwini wa chiyembekezo chodalirika. M’nthaŵi za m’Baibulo, Mulungu ankatchedwa kuti “chiyembekezo cha Israyeli.” (Yeremiya 14:8) Chiyembekezo chilichonse chodalirika chimene anthu ake anali nacho chinkachokera kwa iyeyo, motero Mulunguyo ndiye anali chiyembekezo chawo. Chiyembekezo chimenechi si chinali kungolakalaka zinthu. Mulungu anawapatsa chifukwa chachikulu chokhalira ndi chiyembekezo. Kwa zaka zochuluka, Mulungu anawaonetsa kuti akalonjeza chinthu amachikwaniritsadi. Mtsogoleri wawo, Yoswa ananena mawu aŵa kwa Aisrayeli: “Mudziŵa . . . kuti pa mawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasoŵapo mawu amodzi.”—Yoswa 23:14.
Patha zaka zambirimbiri mawuŵa atanenedwa ndipo Yehova akusungabe malonjezo ake onse. Baibulo lili ndi malonjezo ambiri a Mulungu ndiponso mbiri yolondola ya mmene anawakwaniritsira. Malonjezo ake aulosi n’ngodalirika kwambiri mwakuti nthaŵi zina amalembedwa ngati kuti anali atakwaniritsidwa kale.
N’chifukwa chake tingathe kunena kuti Baibulo ndi buku la chiyembekezo. Mukamaŵerenga mmene Mulungu wakhala akuchitira ndi anthu, mudzakhala ndi zifukwa zamphamvu zokhalira ndi chiyembekezo mwa Iye. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.”—Aroma 15:4.
Kodi Mulungu Amatipatsa Chiyembekezo Chotani?
Kodi ndi panthaŵi yanji pamene timaona kuti tikufunikira kwambiri chiyembekezo? Kodi si panthaŵi ya imfa? Komabe kwa anthu ambiri, panthaŵi yangati imeneyi, mwachitsanzo panthaŵi imene imfa yawalanda munthu amene amam’konda, m’pamene chiyembekezo chimawathaŵira. Chifukwa amaganiza kuti popeza munthu wafa kale, n’chiyaninso angayembekezere? Imfa sitopa ndipo siyang’ana nkhope. Inde, tingathe kuipeŵa kwa kanthaŵi, koma sitingathe kuigonjetsa. M’pake kuti Baibulo limati imfa ndi “mdani wotsiriza.”—1 Akorinto 15:26.
Motero, kodi tingakhale bwanji ndi chiyembekezo imfa ikationekera? Vesi la m’Baibulo limene limati imfa ndi mdani wotsiriza limanenanso kuti mdaniyu “adzathedwa.” Yehova Mulungu ndi wamphamvu kuposa imfa. Anatsimikiza zimenezi nthaŵi zingapo. Kodi anatero motani? Anatero poukitsa akufa. Baibulo limatchulapo nthaŵi zisanu ndi zinayi zimene Mulungu anaukitsa anthu akufa ndi mphamvu zake.
Modabwitsa, Yehova anapatsa mphamvu Mwana wake Yesu, kuti aukitse Lazaro, mnzake wapamtima amene anali atamwalira kwa masiku anayi. Yesu anachitadi zimenezi ndipo sanazichite mwachinsinsi ayi, koma mwapoyera, pamaso pa anthu ambirimbiri.—Yohane 11:38-48, 53; 12:9, 10.
Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani anaukitsa anthu? Kodi anthuwo sanadzakalambenso n’kufabe ndithu?’ Inde anatero. Komano chifukwa cha nkhani zodalirika za chiukiriro ngati zimenezi, ifeyo sitimangolakalaka chabe komanso tili ndi zifukwa zokhutiritsa zakuti anthu apamtima pathu amene anamwalira adzaukitsidwa. M’chicheŵa china tingati, tili ndi chiyembekezo chenicheni.
Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Iyeyu ndi amene Yehova adzam’patse mphamvu zoukitsa anthu padziko lonse. Yesuyu anati: “Ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu [a Kristu], nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Inde, anthu onse amene akugona m’manda angadzaukitsidwe n’kudzakhala padziko lapansi la paradaiso.
Mneneri Yesaya analemba mawu ochititsa chidwi aŵa osimba za chiukiriro: “Akufa ako ali moyo, matupi awo adzaukanso. Iwo akugona m’nthaka adzauka ndi kusangalala; pakuti mame ako ali mame a kuwala konyezimira, ndipo dziko lidzabalanso iwo amene anafa kalekale.”—Yesaya 26:19, The New English Bible.
Kodi zimenezi si zolimbikitsa? Anthu akufa ali pabwino kwambiri, monga mmene mwana amakhalira m’mimba mwa amayi ake. Inde, iwo amene akupuma m’manda akusungidwa bwinobwino m’maganizo a Mulungu Wamphamvuyonse yemwe alibe malire a zinthu zimene angathe kukumbukira. (Luka 20:37, 38) Ndipo posachedwapa adzaukitsidwanso, n’kufika m’dziko la anthu osangalala, omwe adzawalandire ndi manja aŵiri monga mmene banja limalandirira khanda lobadwa kumene! Motero, ngakhale munthu atafa pamakhala chiyembekezo.
Mmene Chiyembekezo Chingakuthandizireni
Paulo anatiphunzitsa zinthu zambiri zokhudza kufunika kwa chiyembekezo. Ananena kuti chiyembekezo ndi chisoti, chomwe ndi mbali yofunika kwambiri ya zida zathu zauzimu. (1 Atesalonika 5:8) Kodi ankatanthauzanji ponena mawu amenewo? M’nthaŵi za m’Baibulo, msilikali akamapita kunkhondo ankavala chisoti chachitsulo, ndipo nthaŵi zambiri m’kati mwake ankavalamo kansalu kapena kachipewa. Chifukwa cha chisotichi, zida zambiri za adani zinkalephera kufika m’mutu n’kumuvulaza msilikaliyo. Ndiye kodi mfundo ya Paulo inali yotani? Chiyembekezo chimateteza maganizo, monga mmene chisoti chimatetezera mutu. Ngati muli ndi chiyembekezo champhamvu chogwirizana ndi zolinga za Mulungu, simungasokonezeke maganizo chifukwa cha mantha kapena kusoŵa pogwira mukakumana ndi mavuto. Kodi tingati alipo amene safunikira chisoti chotere?
Paulo anatchulanso chitsanzo china chosavuta kukumbukira pofotokoza za chiyembekezo chokhudzana ndi chifuno cha Mulungu. Iye analemba kuti: “[Chiyembekezo] chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso.” (Ahebri 6:19) Paulo ankadziŵa bwino kufunika kwa nangula chifukwa anali atapulumukapo pa ngozi ya chombo cha m’madzi kangapo. Amalinyero akakumana ndi mafunde ankaloŵetsa nangula pansi pa nyanja. Nangulayo akakafika pansi n’kukakola bwinobwino, ndiye kuti chombocho chimatha kupulumuka chimphepocho m’malo mokaponyedwa m’mphepete mwa nyanja n’kukamenyetseka ku miyala.
Chimodzimodzinso, ngati ifeyo timaona kuti malonjezo a Mulungu ndi chiyembekezo ‘chokhazikika ndi cholimba,’ chiyembekezo chimenecho chingatithandize kulimbana ndi chimphepo cha mavuto a masiku anoŵa. Yehova amalonjeza kuti posachedwapa anthu sadzasautsidwanso ndi nkhondo, uchifwamba, chisoni, ngakhalenso imfa. (Onani bokosi patsamba 10.) Kukhala ndi chiyembekezo chimenechi kungatithandize kupeŵa zinthu zotiika m’mavuto, n’kutipangitsa kukhala ndi mtima wofunitsitsa kugwirizana ndi mfundo zimene Mulungu amatipatsa m’malo motsatira mzimu wachisokonezo, komanso wokonda zoipa womwe wafala kwambiri m’dziko muno masiku ano.
Chiyembekezo chimene Yehova akupereka chimakukhudzaninso inuyo panokha. Iye akufuna kuti muzikhala moyo wangati umene iyeyo ankafuna pachiyambi. Iye amafuna kuti “anthu onse apulumuke.” Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Choyamba aliyense wa anthuŵa amayenera kuti ‘afike pozindikira choonadi.’ (1 Timoteo 2:4) Ofalitsa magazini ino akukulimbikitsani kuti muphunzire choonadi chopatsa moyo chimenechi cha Mawu a Mulungu. Chiyembekezo chimene Mulungu adzakupatseni mukatero n’choposa chiyembekezo chilichonse chimene mungachipeze m’dziko lino.
Ndi chiyembekezo chotere, palibe chifukwa chosoŵera pogwira, pakuti Mulungu angathe kukupatsani mphamvu zimene mukufunikira kuti mukwaniritse zolinga zanu zilizonse zomwe zili zogwirizana ndi cholinga chake. (2 Akorinto 4:7; Afilipi 4:13) Kodi ichi sindicho chiyembekezo chimene mukufunikira? Motero ngati mukusoŵa chiyembekezo, ndipo ngati mwakhala mukuchifunafuna, limbani mtima. Chiyembekezo chilipo. Mungathe kuchipeza!
[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]
Zifukwa Zokhalira ndi Chiyembekezo
Malemba aŵa angakuthandizeni kukhala ndi chiyembekezo champhamvu:
◼ Mulungu amalonjeza tsogolo losangalatsa.
Mawu Ake amanena kuti dziko lonse lidzasanduka paradaiso wokhala ndi anthu osangalala ndiponso ogwirizana.—Salmo 37:11, 29; Yesaya 25:8; Chivumbulutso 21:3, 4.
◼ Mulungu sanganame.
Iye amadana ndi bodza la mtundu wina uliwonse. Yehova ndi woyera ndiponso wolungama mopanda malire, motero n’kosatheka kuti aname.—Miyambo 6:16-19; Yesaya 6:2, 3; Tito 1:2; Ahebri 6:18.
◼ Mulungu ali ndi mphamvu zopanda malire.
Yehova yekha ndiye wamphamvuyonse. Palibe chilichonse m’chilengedwe chonse chimene chingamuletse kukwaniritsa malonjezo ake.—Eksodo 15:11; Yesaya 40:25, 26.
◼ Mulungu amafuna kuti mukhale ndi moyo wosatha.
—Yohane 3:16; 1 Timoteo 2:3, 4.
◼ Mulungu ali n’chiyembekezo chakuti tichita bwino.
Safuna kuona zophophonya ndiponso zolakwa zathu, koma makhalidwe ndi zochita zathu zabwino. (Salmo 103:12-14; 130:3; Ahebri 6:10) Iye ali n’chiyembekezo chakuti tichita bwino ndipo amasangalala tikaterodi.—Miyambo 27:11.
◼ Mulungu amalonjeza kuti azikuthandizani kukwanitsa zolinga zanu zaumulungu.
Atumiki ake sayenera kumva kuti akusoŵa pogwira. Mulungu amapereka mzimu wake woyera mowoloŵa manja kuti utithandize, ndipotu mzimu umenewu ndi mphamvu yoposa mphamvu ina iliyonse.—Afilipi 4:13.
◼ Simudzakhumudwapo chifukwa chokhala ndi chiyembekezo mwa Mulungu.
Mulungu n’ngodalirika kwambiri, motero sangakukhumudwitseni ngakhale pang’ono.—Salmo 25:3
[Chithunzi patsamba 20]
Chiyembekezo chimateteza maganizo monga mmene chisoti chimatetezera mutu
[Chithunzi patsamba 20]
Monga nangula, chiyembekezo cholimba chingatipangitse kukhala wokhazikika
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy René Seindal/Su concessione del Museo Archeologico Regionale A. Salinas di Palermo
-