NYIMBO 50
Pemphero Langa Losonyeza Kudzipereka
Losindikizidwa
1. Tengani mtima wanga
Kuti ndikukondeni.
Tengani mawu anga
Ndizikuimbirani.
2. Tengani mapaziwa
Ndikutumikireni.
Tengani chuma changa
Sindingakumaneni.
3. Tengani moyo wanga.
Ndikufuna ndichite
Zimene mumafuna.
Ndikusangalatseni.
(Onaninso Sal. 40:8; Yoh. 8:29; 2 Akor. 10:5.)