NYIMBO 100
Alandireni Bwino
Losindikizidwa
1. Yehova ndi M’lungu wopanda tsankho.
Amasamalira mosakondera.
Amatipatsatu
Kuwala ndi mvula,
Amatipatsanso chakudya.
Timatsanzira Yehova Mulungu
Ngati tikuthandiza osauka.
Adzatidalitsa
Tikamasonyeza
Anthu onse kukoma mtima.
2. Pothandiza ena sitingadziwe
Madalitso omwe tingalandire.
Ngakhale ndi oti
Sitikuwadziwa,
Tiwapatse zosowa zawo.
Monga Lidiya wa m’nthawi yakale,
Akabwera kwathu tiwalandire.
M’lungu amaona
Tikamutsanzira
Pochitira anthu chifundo.
(Onaninso Mac. 16:14, 15; Aroma 12:13; 1 Tim. 3:2; Aheb. 13:2; 1 Pet. 4:9.)