Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chizunzo Chisonkhezera Kuwonjezeka mu Antiokeya
    Nsanja ya Olonda—2000 | July 15
    • kaŵirikaŵiri wotembenuzidwa kuti “anatchedwa,” nthaŵi zonse amagwirizanitsidwa ndi chinthu chokhala ndi mphamvu ya mizimu, chonenedwa ndi mlauli, kapena chaumulungu. Motero akatswiri a Baibulo amatembenuza mneniyu kuti “kulosera,” “kulengeza mwaumulungu,” kapena “kupereka lamulo kaya chilimbikitso chaumulungu, kuphunzitsa kuchokera kumwamba.” Popeza kuti otsatira Yesu anatchedwa kuti Akristu “motsogozedwa ndi Mulungu,” n’zotheka kuti Yehova anatsogolera Saulo ndi Barnaba kupereka dzinali.

      Dzina latsopanoli linapitirira kugwiritsidwa ntchito. Ophunzira a Yesu tsopano sanalingaliridwenso kukhala kagulu kopatuka m’Chiyuda, chomwe anali kusiyana nacho kotheratu. Pofika mu 58 C.E., akuluakulu a boma la Roma anali kudziŵa bwino kuti Akristu anali ayani. (Machitidwe 26:28) Malinga n’kunena kwa wolemba mbiri Tasitasi, pofika mu 64 C.E., dzinali linali lodziŵikanso kwambiri pakati pa anthu wamba ku Roma.

      Yehova Amagwiritsa Ntchito Anthu Ake Okhulupirika

      Uthenga wabwino unapita patsogolo kwambiri mu Antiokeya. Modalitsidwa ndi Yehova ndiponso kutsimikiza mtima kwa otsatira a Yesu kuti apitirizebe kulalikira, Antiokeya anakhala pachimake pa Chikristu m’zaka za zana loyamba. Mulungu anagwiritsa ntchito mpingo wa mu mzindawo monga ponyamukira pokafalitsa uthenga wabwino ku mayiko akutali. Mwachitsanzo, Antiokeya anali malo amene mtumwi Paulo anali kunyamukirapo popita ku uliwonse wa maulendo oyambirira aumishonale.

      M’nthaŵi zamakono changu komanso kutsimikiza mtima pokumana ndi chitsutso nazonso zathandiza kufalikira kwa Chikristu choona, zatheketsa anthu ambiri kumva uthenga wabwino ndi kuuyamikira.b Motero ngati mukumana ndi chitsutso chifukwa chakuti mumachirikiza kulambira koyera, kumbukirani kuti Yehova ali ndi zifukwa zololera zimenezo. Monganso m’zaka za zana loyamba, anthu lerolino ayenera kupatsidwa mwayi wa kumva za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuti athe kuima ku mbali ya Ufumuwo. Mwina mukungofunika kutsimikiza mtima kupitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika kuti munthu wina athandizidwe kukhala ndi chidziŵitso cholondola cha choonadi.

  • Msonkhano wa Pachaka pa October 7, 2000
    Nsanja ya Olonda—2000 | July 15
    • Msonkhano wa Pachaka pa October 7, 2000

      MSONKHANO WA PACHAKA wa mamembala a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania udzachitika pa October 7, 2000, pa Nyumba ya Msonkhano ya Mboni za Yehova, pa 2932 Kennedy Boulevard, Jersey City, ku New Jersey. Kukumana koyambirira kwa mamembala okhaokha kudzakhalako pa 9:15 a.m., motsatiridwa ndi msonkhano wa onse wa pachaka pa 10:00 a.m.

      Mamembala a bungweli ayenera kudziŵitsa Ofesi ya Mlembi tsopano lino za kusintha kulikonse kwa makeyala awo a makalata m’kati mwa chaka chapita kotero kuti iwo adzathe kulandira makalata odziŵitsira anthaŵi zonse ndi mapepala opangira voti m’July.

      Mapepala opangira voti, amene adzatumizidwa kwa mamembalawo limodzi ndi chidziŵitso cha msonkhano wa pachaka, ziyenera kubwezedwa kotero kuti zidzafike ku Ofesi ya Mlembi wa Sosaite pasanafike pa August 1. Membala aliyense ayenera kudzaza ndi kutumiza pepala lake lopangira voti mofulumira, akumafotokoza kuti kaya adzapezeka pamsonkhanowo kapena ayi. Chidziŵitso choperekedwa pa pepala lopangira voti lililonse chiyenera kukhala chotsimikizirika pamfundoyi, popeza kuti chidzakhala chodziŵira amene adzapezekapo.

      Pulogalamu yonse, kuphatikizapo msonkhano wa kayendetsedwe ka zinthu ndi malipoti, zikuyembekezeka kudzatha pa 1:00 p.m. kapena kupitirira pang’ono pamenepo. Sipadzakhala pulogalamu yamasana. Chifukwa cha kuchepa kwa malo, okhala ndi matikiti okha ndiwo amene adzaloledwa kuloŵa. Sipadzakhala makonzedwe akugwirizanitsa matelefoni ndi nyumba zina zosonkhanira pamsonkhano wa pachakawu.

Mabuku a Chichewa (1974-2026)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena