MUTU 1
Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova
PADZIKO lonse, pali magulu ambiri achipembedzo, andale, amalonda ndi enanso ambiri. Magulu amenewa ali ndi zolinga zosiyanasiyana komanso amatsatira mfundo zosiyanasiyana. Koma pali gulu limodzi lomwe limasiyana kwambiri ndi magulu onsewa. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti gulu limeneli ndi la Mboni za Yehova.
2 N’zosangalatsa kuti inuyo muli m’gulu limeneli. Mutadziwa chifuniro cha Mulungu, munayamba kuchichita. (Sal. 143:10; Aroma 12:2) Panopa mumatumikira Mulungu mwakhama limodzi ndi gulu la abale achikondi omwe akupezeka padziko lonse lapansi. (2 Akor. 6:4; 1 Pet. 2:17; 5:9) Mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu analonjeza, kuchita zimenezi kumakubweretserani madalitso ambiri komanso kumakuthandizani kukhala wosangalala. (Miy. 10:22; Maliko 10:30) Mukamachita chifuniro cha Yehova mokhulupirika, mumakhalanso mukukonzekera madalitso abwino kwambiri komanso osatha a m’tsogolo.—1 Tim. 6:18, 19; 1 Yoh. 2:17.
3 Mlengi wathu wamkulu ali ndi gulu lapadziko lonse lomwe ndi losiyana kwambiri ndi magulu ena onse. Gulu limeneli limalamuliridwa ndi Yehova, yemwe ndi Mutu wa zonse. Iye ndi Woweruza wathu, Wotipatsa Malamulo komanso Mfumu yathu ndipo timamudalira kwambiri. (Yes. 33:22) Popeza kuti Mulungu amafuna kuti zinthu zonse zizichitika mwadongosolo, wakonza njira yotithandiza kuti ‘tizigwira naye ntchito limodzi’ pokwaniritsa cholinga chake.—2 Akor. 6:1, 2.
4 Pamene mapeto a dziko loipali akuyandikira kwambiri, ifeyo tikupitirizabe kupita patsogolo motsogoleredwa ndi Mfumu yathu, Khristu Yesu. (Yes. 55:4; Chiv. 6:2; 11:15) Ndipotu Yesu ananeneratu kuti otsatira ake adzachita zinthu zambiri kuposa zimene iyeyo anachita ali padziko lapansi. (Yoh. 14:12) Zimenezi zinali zoti zidzathekadi chifukwa otsatira ake anali oti adzakhalapo ambiri komanso adzagwira ntchito yolalikira kwa zaka zambiri moti adzakwanitsa kulalikira m’madera ambiri. Adzalengeza uthenga wabwino wa Ufumu mpaka kumalekezero a dziko lapansi.—Mat. 24:14; 28:19, 20; Mac. 1:8.
5 Pali umboni wosonyeza kuti zimenezi zikuchitikadi panopa. Komabe, mmene Yesu anafotokozera, ntchito yolalikira uthenga wabwino idzatha pa nthawi imene Yehova anaika. Zinthu zimene zikuchitika zikusonyeza kuti tsiku lalikulu la Yehova lochititsa mantha limene linatchulidwa m’Mawu a Mulungu layandikira.—Yow. 2:31; Zef. 1:14-18; 2:2, 3; 1 Pet. 4:7.
Tiyenera kuchita khama kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. Kuti tichite zimenezi, tifunika kudziwa bwino mmene gulu la Mulungu limachitira zinthu
6 Pamene tikudziwa zambiri zokhudza chifuniro cha Yehova, tiyenera kuyesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Kuti zimenezi zitheke, tifunika kudziwa bwino mmene gulu la Yehova limayendera ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi gululo. Gulu la Yehova limatsatira mfundo za m’Malemba, komanso malamulo ndi ziphunzitso zopezeka m’Mawu a Mulungu.—Sal. 19:7-9.
7 Anthu a Yehova akamatsatira malangizo a m’Baibulo, amakhala mwamtendere komanso amagwira ntchito mogwirizana. (Sal. 133:1; Yes. 60:17; Aroma 14:19) Chikondi n’chimene chimathandiza abale padziko lonse kukhala ogwirizana. Monga Akhristu, timayesetsa kukonda anzathu. (Yoh. 13:34, 35; Akol. 3:14) Zimenezi zimasangalatsa Mulungu ndipo zimathandiza kuti tiziyendera limodzi ndi mbali yakumwamba ya gulu la Yehova.
MBALI YAKUMWAMBA YA GULU LA YEHOVA
8 Mneneri Yesaya, Ezekieli ndi Danieli anaona masomphenya a mbali yakumwamba ya gulu la Yehova. (Yes., chap. 6; Ezek., chap. 1; Dan. 7:9, 10) Nayenso mtumwi Yohane anaona masomphenya a mmene zinthu zimachitikira kumwamba ndipo zimene analemba m’buku la Chivumbulutso zimatithandiza nafenso kudziwa mmene zinthu zimayendera kumwamba. Anaona Yehova ali pampando wake wachifumu ndipo panalinso angelo omwe ankaimba kuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene analipo, amene alipo, ndi amene akubwera.” (Chiv. 4:8) Yohane anaonanso “Mwanawankhosa wa Mulungu,” yemwe ndi Yesu Khristu, “ataimirira pafupi ndi mpando wachifumu.”—Chiv. 5:6, 13, 14; Yoh. 1:29.
9 Masomphenya osonyeza Yehova atakhala pampando wachifumu akutithandiza kudziwa kuti iye ndi amene amatsogolera gulu lake. Pofuna kusonyeza udindo wake wapamwamba, lemba la 1 Mbiri 29:11, 12 limati: “Inu Yehova, ukulu, mphamvu, kukongola, ulemerero, ndi ulemu ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu. Ufumu ndi wanu, inu Yehova, ndinunso Wokwezeka monga mutu pa onse. Chuma ndi ulemerero zimachokera kwa inu. Inu mumalamulira chilichonse. M’dzanja lanu muli mphamvu ndi nyonga, ndipo dzanja lanu limatha kukweza ndiponso kupereka mphamvu kwa onse.”
10 Yesu Khristu yemwe amagwira ntchito ndi Yehova nayenso ali ndi udindo wofunika kwambiri kumwamba ndipo anapatsidwa mphamvu zambiri. Ndipotu, “Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi a iyeyo, ndipo anamuika mutu wa zinthu zonse chifukwa cha mpingo.” (Aef. 1:22) Ponena za Yesu, mtumwi Paulo anati: “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse akumwamba, apadziko lapansi, ndi apansi pa nthaka apinde mawondo awo. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.” (Afil. 2:9-11) Choncho, tingakhulupirire ndi mtima wonse kuti Yesu Khristu ndi wolamulira wachilungamo.
11 Mneneri Danieli anaona masomphenya osonyeza Wamasiku Ambiri atakhala pampando wake wachifumu ndipo panali angelo “okwana miliyoni imodzi amene anali kumutumikira nthawi zonse, ndi atumiki enanso mamiliyoni 100 amene anali kuimirira pamaso pake.” (Dan. 7:10) Baibulo limanena za angelo amenewa kuti ndi “mizimu yotumikira ena, yotumidwa kukatumikira amene adzalandire chipulumutso monga cholowa chawo.” (Aheb. 1:14) Angelo amenewa anapatsidwa ‘mipando yachifumu, maboma, maulamuliro ndipo ena ndi ambuye.’—Akol. 1:16.
12 Tikamaganizira zinthu zokhudza mbali yakumwamba ya gulu la Yehova zimenezi, tingamvetse mmene Yesaya anamvera ataona masomphenya osonyeza “Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka,” komanso ‘pamwamba pake pali aserafi.’ Ataona zimenezi, Yesaya anati: “Tsoka kwa ine! Popeza maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu. Nditsikira kuli chete pakuti ndine munthu wa milomo yodetsedwa, ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.” Yesaya anachita mantha ndipo anadabwa kwambiri ataona mbali yakumwambayi ya gulu la Yehova. Zimenezi zinamulimbikitsa kwambiri moti Yehova atafunsa kuti angatume ndani kuti agwire ntchito yolengeza za chiweruzo chake, iye anayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”—Yes. 6:1-5, 8.
13 Anthu a Yehova amalimbikitsidwanso ngati mmene anachitira Yesaya chifukwa chozindikira ndi kumvetsa mmene gulu la Yehova limayendera. Choncho pamene gulu la Yehova likupita patsogolo, nafenso tiyenera kuyendera nalo limodzi komanso kulikhulupirira.
GULU LA YEHOVA LIKUPITA PATSOGOLO
14 Chaputala 1 cha ulosi wa Ezekieli, chili ndi masomphenya osonyeza Yehova atakwera galeta lakumwamba lalikulu kwambiri. Galeta laulemerero limeneli likuimira mbali yosaoneka ya gulu la Yehova. Ponena kuti Yehova wakwera galeta zikutanthauza kuti iye ndi amene akutsogolera gulu lake kuti lizichita zinthu mogwirizana ndi zimene akufuna.—Sal. 103:20.
15 Galetali lili ndi mawilo okhala ndi mawilo ena opingasa mkati mwawo. N’chifukwa chake mawilowa amatha “kulowera kumbali zonse zinayi.” (Ezek. 1:17) Mawilowa amathanso kusintha mwamsanga kumene akulowera. Komabe sikuti galetali limangodziyendera lokha popanda woliwongolera. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova samangosiya gulu lake kuti lizipita kulikonse kumene likufuna. Lemba la Ezekieli 1:20 limati: “Kulikonse kumene mzimu ukufuna kupita, zamoyozo zinali kupita kumeneko.” Choncho ndi Yehova amene amachititsa kuti gulu lake lipite kulikonse kumene akufuna pogwiritsa ntchito mzimu wake. Ndiye tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimayendera limodzi ndi gululi?’
16 Kuyendera limodzi ndi gulu la Yehova sikumangotanthauza kupita kumisonkhano komanso kulalikira. M’malomwake, kumaphatikizapo kupita kwathu patsogolo mwauzimu komanso zimene timachita kuti tikhalebe olimba mwauzimu. Nthawi zonse tikamachita zinthu, tiyenera ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti,’ komanso tiyenera kudya chakudya chauzimu chimene chikuperekedwa m’gulu lake. (Afil. 1:10; 4:8, 9; Yoh. 17:3) Tizikumbukiranso kuti, kuti zinthu zichitike mwadongosolo pamafunika kuyendetsa zinthu bwino komanso kuchita zinthu mogwirizana. Choncho tiyenera kugwiritsa ntchito bwino chuma chauzimu komanso zinthu zimene Yehova watipatsa n’cholinga choti tikwaniritse ntchito yake. Tikamayendera limodzi ndi galeta la Yehova, zochita zathu zimagwirizana ndi uthenga umene timalalikira.
17 Gulu la Yehova likutithandiza kuti tizipita patsogolo pochita chifuniro cha Mulungu. Kumbukirani kuti amene akuyendetsa galeta lakumwambali ndi Yehova. Choncho tikamayendera limodzi ndi galeta lake, timasonyeza kuti timamulemekeza ndiponso timamukhulupirira monga Thanthwe lathu. (Sal. 18:31) Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu. Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.” (Sal. 29:11) Popeza tili m’gulu la Yehova, timalandira nawo mphamvu imene amapereka ndiponso timakhala ndi mtendere umene amapereka kwa anthu ake. Sitikukayikira kuti Yehova adzapitiriza kutidalitsa pamene tikuchita chifuniro chake panopa komanso mpaka kalekale.