Zamkatimu
GAWO 1 N’CHIFUKWA CHIYANI MUYENERA KUBWERERA KWA YEHOVA?
Atumiki akale a Yehova ankakumana ndi mavuto ofanana ndi athu. Yehova ankawathandiza ndipo amalonjeza kuti adzatithandizanso masiku ano. Iye ali ngati M’busa wachikondi ndipo amafufuza anthu amene asochera n’kuwathandiza kuti abwerere.
Gawo 1 “Nkhosa Zosochera Ndidzazifunafuna”
GAWO 2 MPAKA 4 MAVUTO AMENE ANGAKULEPHERETSENI KUBWERERA KWA YEHOVA
Pali atumiki ena okhulupirika amene anafooka chifukwa cha nkhawa, kukhumudwa kapena kudziimba mlandu. Werengani kabukuka kuti muone mmene Yehova anawathandizira kuti ayambenso kumutumikira mosangalala.
Gawo 2 “Timapanikizidwa Mwamtundu Uliwonse”
Gawo 3 Tikakhala ndi “Chifukwa Chodandaulira”
Gawo 4 “Ndiyeretseni kuTchimo Langa”
Gawo 5 N’CHIYANI CHINGAKUTHANDIZENI KUBWERERA KWA YEHOVA?
Mu gawo 5 muli umboni wosonyeza kuti Yehova akufuna kuti mubwerere. Muonanso zimene Akhristu ena anachita kuti abwerere, mmene mpingo unawalandirira komanso mmene akulu anawathandizira.