Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Ndine . . . Wodzichepetsa”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • MUTU 3

      “Ndine . . . Wodzichepetsa”

      Yesu wakwera bulu wamng’ono ndipo anthu amene aima m’mbali mwa msewu akufuula n’kumagwedeza nthambi za kanjedza. Ena akuyala zovala zawo komanso nthambi za kanjedza mumsewu.

      “Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe”

      1-3. Kodi Yesu analowa bwanji mu Yerusalemu, nanga n’chifukwa chiyani anthu ena amene anaona zimenezi anadabwa?

      MUMZINDA wa Yerusalemu munali chisangalalo chokhachokha chifukwa anthu ankayembekezera munthu wofunika kwambiri amene anali atatsala pang’ono kulowa mumzindawo. Anthu ena anali atasonkhana m’mbali mwa msewu, kunja kwa mzindawo. Anthuwo ankayembekezera mwachidwi kulandira munthu ameneyu chifukwa anthu ena ankanena kuti iye ndi wolowa ufumu wa Davide ndipo ndi woyenera kukhala Mfumu ya Isiraeli. Ndipo ena mwa anthuwo ananyamula masamba a kanjedza n’kumawakupiza m’mwamba posonyeza kumulandira ndipo ena anayala zovala zawo ndiponso nthambi za mitengo mumsewu kuti iye adutsemo bwino. (Mateyu 21:7, 8; Yohane 12:12, 13) Komabe, anthu ambiri ayenera kuti ankadzifunsa kuti, kodi munthu ameneyu alowa bwanji mumzindawu?

      2 Ena mwina ankaganiza kuti iye alowa mumzindawo modzionetsera chifukwa ayenera kuti ankadziwa anthu ena olemekezeka amene anachitapo zimenezi. Mwachitsanzo, Abisalomu mwana wa Davide, atadziika yekha kukhala mfumu, anasankha anthu 50 kuti azithamanga patsogolo pa galeta limene iye anakwera. (2 Samueli 15:1, 10) Komanso Juliasi Kaisara, yemwe anali wolamulira wa Chiroma, anachita zinthu mokokomeza kwambiri. Pa nthawi ina iye anayenda ulendo wachionetsero chosonyeza kuti wapambana pa nkhondo, mpaka kukafika kunyumba ya chifumu ya ku Roma. Ndipo pa ulendo wakewo anali ndi njovu zokwana 40 zimene anazimangirira nyale. Njovuzo zinkayenda kudzanja lake lamanja ndipo zina zinkayenda kudzanja lake lamanzere. Koma pa nthawiyi, anthu a ku Yerusalemu ankayembekezera munthu wofunika kwambiri kuposa anthu onsewa. Kaya gulu la anthulo limadziwa kapena ayi, munthu ameneyu anali Mesiya, munthu wofunika kwambiri kuposa onse amene anakhalapo. Komabe mwina anthu ena anadabwa ndi mmene munthu yemwe ankayembekezera kudzakhala Mfumu ameneyu analowera mumzindawo.

      3 Panalibe magaleta, anthu othamanga pansi, mahatchi ndiponso panalibe njovu. Yesu anakwera pabulu, nyama yomwe ndi yonyozeka kwambiri.a Iye sanavale zovala zapadera zosonyeza ulemerero wake ndiponso pabulu amene anakwerapo sanaikepo chokhalira chamtengo wapatali. M’malomwake, otsatira ake amene ankamukonda kwambiri, anayala zovala zawo pamsana pa buluyo kuti iye akhalepo. N’chifukwa chiyani Yesu analowa mumzinda wa Yerusalemu modzichepetsa chonchi, pamene anthu amene anali ndi udindo wotsika kwambiri poyerekezera ndi iyeyo anasankha kuchita zinthu modzionetsera kwambiri?

      4. Kodi Baibulo linalosera kuti Mfumu yemwenso ndi Mesiya adzalowa bwanji mumzinda wa Yerusalemu?

      4 Yesu anakwaniritsa ulosi wakuti: “Sangalala kwambiri. Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu. Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe. Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso. Ndi yodzichepetsa ndipo ikubwera itakwera bulu. Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.” (Zekariya 9:9) Ulosi umenewu ukusonyeza kuti Wodzozedwa wa Mulungu, kapena kuti Mesiya, tsiku lina adzadziulula kwa anthu a ku Yerusalemu kuti ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu. Ndipo mmene anadziululira komanso nyama imene anasankha kukwera, zinasonyeza kuti anali ndi khalidwe labwino kwambiri lodzichepetsa.

      5. N’chifukwa chiyani timakhudzidwa mtima kwambiri tikamaphunzira za kudzichepetsa kwa Yesu, nanga n’chifukwa chiyani n’zofunika kuti tizimutsanzira?

      5 Kudzichepetsa ndi limodzi mwa makhalidwe abwino kwambiri amene Yesu ali nawo ndipo timakhudzidwa mtima kwambiri tikamaphunzira za khalidwe limeneli. Monga mmene tinaonera m’mutu wapita uja, Yesu yekha ndi amene ali “njira, choonadi ndi moyo.” (Yohane 14:6) N’zoonekeratu kuti pa anthu mabiliyoni ambirimbiri amene anakhalapo padzikoli, palibe munthu amene angafanane ndi Mwana wa Mulungu. Ngakhale zili choncho, Yesu sanasonyeze m’pang’ono pomwe kuti anali wonyada kapena wodzikuza. Koma anthu ambirimbiri omwenso si angwiro amakhala odzikuza. Kuti tikhale otsatira a Khristu, tiyenera kuyesetsa kupewa kudzikuza. (Yakobo 4:6) Kumbukirani kuti Yehova amadana ndi kudzikuza. Choncho n’zofunika kuti tiphunzire komanso kutsanzira kudzichepetsa kwa Yesu.

      Yesu Ndi Wodzichepetsa Kuyambira Kalekale

      6. Kodi kudzichepetsa n’kutani, nanga Yehova anadziwa bwanji kuti Mesiya adzakhala wodzichepetsa?

      6 Kudzichepetsa kumatanthauza kusadzikuza, kusanyada komanso kudziona kuti ndiwe wotsika. Khalidwe limeneli limayambira mumtima ndipo munthu amadziwika kuti ndi wodzichepetsa chifukwa cha zolankhula zake, zochita zake ndiponso mmene amachitira zinthu ndi anthu ena. Kodi Yehova anadziwa bwanji kuti Mesiya adzakhala wodzichepetsa? Yehova ankadziwa kuti Mwana wake anatengera chitsanzo chake changwiro cha kudzichepetsa. (Yohane 10:15) Komanso ankaona mmene Mwana wakeyo ankachitira zinthu modzichepetsa. Kodi anachita zinthu ziti?

      7-9. (a) Kodi Mikayeli anasonyeza bwanji kuti ndi wodzichepetsa atasemphana maganizo ndi Satana? (b) Kodi Akhristu angatsanzire bwanji Mikayeli posonyeza kudzichepetsa?

      7 M’buku la Yuda muli chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti Yesu ndi wodzichepetsa. M’bukuli muli mawu akuti: “Koma pamene Mikayeli, mkulu wa angelo, anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose, sanayese n’komwe kumuweruza komanso kumunyoza, m’malomwake anati: ‘Yehova akudzudzule.’” (Yuda 9) Mikayeli ndi dzina limene Yesu ankadziwika nalo asanabwere padziko lapansi komanso limene amadziwika nalo atabwerera kumwamba. Iye anapatsidwa dzinali chifukwa cha udindo wake monga mkulu wa angelo, kapena kuti mkulu wa gulu lankhondo la angelo a Yehova kumwamba.b (1 Atesalonika 4:16) Ndiyeno tiyeni tione zimene Mikayeli anachita, atasemphana maganizo ndi Satana.

      8 Nkhani imene ili m’buku la Yuda sifotokoza zimene Satana ankafuna kuchita ndi mtembo wa Mose, koma sitikukayikira kuti Mdyerekezi anali ndi zolinga zoipa mumtima mwake. Mwina ankafuna kulimbikitsa anthu kuti azilambira mafano pogwiritsira ntchito mtembo wa munthu wokhulupirikayo. Pamene Mikayeli ankaletsa Satana kuti asachite zolinga zake zoipazo, anasonyeza khalidwe labwino kwambiri lodziletsa. N’zoona kuti Satana ankafunika kudzudzulidwa, koma Mikayeli, amene pa nthawiyi ankakangana ndi Satana, anali asanapatsidwe “udindo wonse woweruza” umene ali nawo panopa. Choncho iye anazindikira kuti Yehova Mulungu yekha ndi amene anayenera kudzudzula Mdyerekeziyo. (Yohane 5:22) Pa angelo onse, Mikayeli ndi amene ali ndi udindo waukulu chifukwa ndi mkulu wa angelo. Komabe, m’malo mofuna kukhala ndi udindo winanso, iye modzichepetsa anasiyira Yehova udindo wodzudzula Mdyerekezi. Kuwonjezera pa khalidwe lodzichepetsa, Yesu anasonyezanso kuti ankadziwa kuti pali zinthu zina zimene ayenera kuchita ndiponso zimene sayenera kuchita.

      9 Pali chifukwa chimene chinachititsa kuti Yuda alembe nkhani imeneyi mouziridwa ndi Mulungu. N’zomvetsa chisoni kuti Akhristu ena munthawi ya Yuda sanali odzichepetsa. Iwo anali odzikweza ndipo ‘ankalankhula monyoza zinthu zonse zimene sankazimvetsa n’komwe.’ (Yuda 10) Zimakhala zosavuta kuti anthu omwe si angwirofe tiyambe kunyada. Ngati sitikumvetsa bwino zinthu zinazake zimene zikuchitika mumpingo wa Chikhristu, mwina ingakhale mfundo inayake imene akulu asankha kuti mpingo utsatire, kodi timachita chiyani? Ngati titayamba kudandaula n’kumalankhula zinthu zosonyeza kuti sitikugwirizana ndi zimene asankhazo, ngakhale kuti sitikudziwa zinthu zonse zimene zachititsa kuti asankhe zimenezo, kodi pamenepa sitingakhale kuti tikusonyeza kuti ndife odzikuza? Choncho, tiyeni tizitsanzira Mikayeli kapena kuti Yesu, popewa kuweruza pa zinthu zimene Mulungu sanatipatse udindo wochita zimenezo.

      10, 11. (a) Kodi Mwana wa Mulungu anasonyeza bwanji khalidwe lodzichepetsa pamene anavomera kubwera padziko lapansi? (b) Kodi tingatsanzire bwanji khalidwe la Yesu la kudzichepetsa?

      10 Mwana wa Mulungu anasonyezanso kuti ndi wodzichepetsa chifukwa anavomera kubwera pano padziko lapansi. Taganizirani zinthu zimene anafunika kusiya. Iye anali mkulu wa angelo. Analinso “Mawu,” kapena kuti wolankhula m’malo mwa Yehova. (Yohane 1:1-3) Yesu ankakhala kumwamba, komwe ndi malo okhala a Yehova “apamwamba, oyera ndi aulemerero.” (Yesaya 63:15) Komabe, Mwanayo “anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo ndipo anakhala munthu.” (Afilipi 2:7) Taganizirani zimene zinachitika kuti abwere padziko lapansi. Moyo wake anausamutsira m’mimba mwa namwali wa Chiyuda ndipo anafunika akhale m’mimba mwa namwaliyo n’kumakula pang’onopang’ono kwa miyezi 9. Kenako anabadwa ngati khanda losadziwa kanthu m’nyumba ya kalipentala yemwenso anali wosauka. Anakula n’kukhala kamnyamata kenako n’kukhala mnyamata wamkulu. Ngakhale kuti anali wangwiro, pa nthawi yonse imene anali mnyamata, ankamvera makolo ake amene sanali angwiro. (Luka 2:40, 51, 52) Pamenepatu iye anasonyeza kudzichepetsa kwambiri.

      11 Tiyeni tiziyesetsa kutsanzira kudzichepetsa kwa Yesu pochita utumiki umene nthawi zina ungaoneke ngati wonyozeka. Mwachitsanzo, ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ingaoneke ngati yonyozeka makamaka ngati anthu sakusonyeza chidwi, akutinyoza kapena kutilankhula mwachipongwe. (Mateyu 28:19, 20) Komabe, ngati titapirira n’kupitirizabe kugwira ntchitoyi, tingathandize kuti anthu ambiri adzapulumuke. Ndipotu tidzaphunzira kukhala odzichepetsa kwambiri komanso tidzatsatira bwino Mbuye wathu, Yesu Khristu.

      Kodi Yesu Anasonyeza Bwanji Kudzichepetsa Ali Padzikoli?

      12-14. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kudzichepetsa pamene anthu ankamutamanda? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa pamene ankachita zinthu ndi anthu? (c) N’chiyani chikusonyeza kuti kudzichepetsa kwa Yesu sikunali kongodzionetsera kapena kongotsatira miyambo?

      12 Yesu anali wodzichepetsa pa nthawi yonse imene ankachita utumiki wake padziko lapansi. Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa poonetsetsa kuti ulemu ndi ulemerero wonse ukupita kwa Atate ake. Nthawi zina anthu ankatamanda Yesu chifukwa cholankhula mawu anzeru, kuchita zozizwitsa komanso chifukwa cha khalidwe lake labwino. Nthawi zonse Yesu ankakana kulandira ulemu umenewo ndipo ankanena kuti Yehova ndi amene ali woyenera kupatsidwa ulemuwo osati iyeyo.​—Maliko 10:17, 18; Yohane 7:15, 16.

      13 Njira ina imene Yesu anasonyezera kuti anali wodzichepetsa ndi mmene ankachitira zinthu ndi anthu. Ndipo iye ananena momveka bwino kuti sanabwere padziko lapansili kudzatumikiridwa koma kudzatumikira ena. (Mateyu 20:28) Iye anasonyeza kuti anali wodzichepetsa chifukwa anali wokoma mtima komanso wodekha akamachita zinthu ndi anthu. Mwachitsanzo, otsatira ake akamukhumudwitsa sankawadzudzula mwaukali, koma ankayesetsa kuwalangiza modekha. (Mateyu 26:39-41) Gulu la anthu litamutsatira pamene ankafunafuna malo opanda anthu komanso phokoso kuti apumule, sanawathamangitse koma anapitiriza kuwaphunzitsa “zinthu zambiri” modzipereka. (Maliko 6:30-34) Pamene mayi wina amene sanali Mwisiraeli ankamuchonderera kuti amuchiritsire mwana wake wamkazi, poyamba Yesu anakana. Komabe iye sanakane mwaukali komanso popeza mayiyo anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chachikulu, Yesu anamuchitira zimene anapemphazo. Tikambirana nkhani imeneyi m’Mutu 14.​—Mateyu 15:22-28.

      14 Yesu anakwaniritsa mawu amene analankhula onena za iye m’njira zina zambiri. Iye anati: “Ndine wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mateyu 11:29) Sikuti iye ankasonyeza kudzichepetsa pongofuna kudzionetsera kapena kungotsatira miyambo yachikhalidwe. Koma kudzichepetsa kwake kunali kochokera pansi pa mtima. N’chifukwa chake Yesu ankaona kuti ntchito yophunzitsa otsatira ake kuti akhale odzichepetsa inali yofunika kwambiri.

      Yesu Ankaphunzitsa Otsatira Ake Kuti Akhale Odzichepetsa

      15, 16. Kodi Yesu ananena kuti pali kusiyana kotani pakati pa khalidwe la olamulira a dzikoli ndi khalidwe limene otsatira ake amafunika kukhala nalo?

      15 Atumwi a Yesu zinawatengera nthawi kuti aphunzire kukhala odzichepetsa. Choncho Yesu anayesetsa kuwaphunzitsa mobwerezabwereza kuti akhale odzichepetsa. Mwachitsanzo, pa nthawi ina Yakobo ndi Yohane anatuma mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wa Mulungu. Modzichepetsa, Yesu anayankha kuti: “Si ine woyenera kusankha amene adzakhale kudzanja langa lamanja kapena lamanzere. Atate wanga adzapereka mwayi umenewo kwa amene anawakonzera.” Atumwi ena 10 aja “anakwiya kwambiri” ndi zimene Yakobo ndi Yohane anachitazi. (Mateyu 20:20-24) Kodi Yesu anathetsa bwanji vuto limeneli?

      16 Yesu anawadzudzula onse mwachifundo kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu. Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.” (Mateyu 20:25-27) N’zodziwikiratu kuti atumwiwo ankaona kuti “olamulira a anthu a mitundu ina” amakhala onyada, odzikuza ndiponso odzikonda. Koma Yesu anasonyeza kuti otsatira ake ayenera kukhala osiyana ndi atsogoleri ankhanza ndiponso okonda kulamulira ena amenewo. Otsatira akewo ankafunika kukhala odzichepetsa. Kodi atumwiwo anamvetsa mfundoyi?

      17-19. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa bwanji atumwi ake phunziro losaiwalika la kudzichepetsa atatsala pang’ono kuphedwa? (b) Kodi ndi phunziro lalikulu komanso losaiwalika liti la kudzichepetsa limene Yesu anapereka pamene anali padziko lapansi?

      17 Ophunzirawo ankavutika kwambiri kuti asonyeze khalidwe lodzichepetsa. Aka sikanali koyamba kapena komaliza kuti Yesu awaphunzitse kufunika koti akhale anthu odzichepetsa. M’mbuyomu, ophunzirawo atakangana pa nkhani yakuti wamkulu kwambiri ndi ndani pakati pawo, Yesu anabweretsa mwana wamng’ono pakati pawo n’kuwauza kuti azikhala ngati ana amene sanyada, sadzikuza komanso safuna udindo ngati mmene anthu akuluakulu amachitira. (Mateyu 18:1-4) Komabe, usiku womaliza Yesu asanaphedwe, anaona kuti atumwi akewo anali asanasiyebe kunyada. Choncho iye anawapatsa phunziro losaiwalika. Anamanga thaulo m’chiuno mwake n’kuyamba kugwira ntchito yonyozeka kwambiri imene pa nthawi imeneyo inkagwiridwa ndi antchito a pakhomo kukabwera alendo. Yesu anasambitsa mapazi a atumwi ake onse, kuphatikizapo Yudasi amene anali atatsala pang’ono kumupereka.​—Yohane 13:1-11.

      18 Yesu anathandiza atumwiwo kumvetsa nkhani ya kudzichepetsa pamene anawauza kuti: “Ndakupatsani chitsanzo.” (Yohane 13:15) Kodi ophunzirawo anamvetsa bwino tanthauzo la zimene Yesu anachitazo? Taganizirani izi. Usiku wa tsiku lomwelo atumwiwo anakangananso pa nkhani yakuti wamkulu kwambiri ndi ndani pakati pawo. (Luka 22:24-27) Koma Yesu anapitiriza kuwalezera mtima ndipo ankawaphunzitsa modzichepetsa. Kenako anawaphunzitsa kudzichepetsa m’njira ina yapadera kwambiri. Iye “anadzichepetsa ndipo anakhala womvera mpaka imfa, inde imfa yapamtengo wozunzikirapo.” (Afilipi 2:8) Ngakhale kuti Yesu sananyozepo Mulungu, iye analolera kuphedwa mochititsa manyazi ngati chigawenga. Pamenepatu Mwana wa Mulungu anasonyeza kuti ndi wapadera, chifukwa anadzichepetsa kwambiri kuposa chilichonse chimene Yehova analenga.

      19 N’kutheka kuti phunziro lomalizira la kudzichepetsali, limene Yesu anawapatsa ali padziko lapansi, ndi limene linathandiza atumwi okhulupirikawo kuti azikumbukirabe phunziro losaiwalika limene Yesu anapereka. Baibulo limatiuza kuti amuna amenewa anagwira ntchito limodzi modzichepetsa kwa zaka zambirimbiri. Nanga bwanji ifeyo?

      Kodi Inuyo Mutsanzira Chitsanzo Chimene Yesu Anatipatsachi?

      20. Kodi tingadziwe bwanji ngati ndife odzichepetsa?

      20 Paulo akulimbikitsa aliyense wa ife kuti: “Khalani ndi maganizo amenenso Khristu Yesu anali nawo.” (Afilipi 2:5) Tiyenera kukhala odzichepetsa ngati mmene Yesu analili. Kodi tingadziwe bwanji ngati tili odzichepetsa? Paulo akutikumbutsa kuti, “Musamachite chilichonse ndi mtima wokonda mikangano kapena chifukwa chodzikuza, koma modzichepetsa, muziona kuti ena amakuposani.” (Afilipi 2:3) Choncho tingadziwe kuti ndife odzichepetsa kapena ayi tikaganizira mmene timaonera anthu ena poyerekezera ndi mmene timadzionera tokha. Tiyenera kumaona kuti anthu ena amatiposa komanso kuti ndi ofunika kwambiri kuposa ifeyo. Kodi inuyo mumvera malangizo a Paulowa?

      21, 22. (a) N’chifukwa chiyani oyang’anira a Chikhristu ayenera kukhala odzichepetsa? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzichepetsa?

      21 Patapita zaka zambiri Yesu atamwalira, mtumwi Petulo ankaganizabe za kufunika kokhala munthu wodzichepetsa. Petulo anaphunzitsa oyang’anira a Chikhristu kuti azigwira ntchito yawo modzichepetsa, osati kumachita zinthu ngati mafumu pakati pa nkhosa za Yehova. (1 Petulo 5:2, 3) Udindo si chifukwa choti munthu akhalire wonyada. M’malomwake, munthu amene ali ndi udindo ayenera kuyesetsa kuti akhale wodzichepetsa kwambiri. (Luka 12:48) Sikuti khalidweli ndi lofunika kwa oyang’anira okha koma kwa Mkhristu aliyense.

      22 N’zoonekeratu kuti Petulo sanaiwale usiku umene Yesu anasambitsa mapazi ake, ngakhale kuti iyeyo ankakana. (Yohane 13:6-10) Petulo analembera Akhristu kuti: “Nonsenu muzichita zinthu modzichepetsa.” (1 Petulo 5:5) Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “muzichita zinthu” amatanthauzanso “kuvala,” ndipo amanena zimene wantchito ankachita. Iye ankavala epuloni kuti agwire ntchito yonyozeka. Mawu amenewa akutikumbutsa zimene Yesu anachita pomanga thaulo m’chiuno mwake n’kugwada kuti agwire ntchito yosambitsa mapazi a ophunzira ake. Ngati ndife odzichepetsa mofanana ndi Yesu, sitidzakana ntchito iliyonse imene Mulungu angatipatse ngakhale itaoneka ngati yonyozeka. Choncho tikhale odzichepetsa ndipo anthu onse aziona kudzichepetsa kwathu ngati mmene amaonera zovala zimene tavala.

      23, 24. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kuchita chilichonse chosonyeza kudzikuza? (b) Kodi mutu wotsatira utithandiza kupewa maganizo abodza ati okhudza kudzichepetsa?

      23 Kudzikuza kuli ngati poizoni ndipo kumawononga zinthu kwambiri. Munthu amene ali ndi luso lochita bwino zinthu zosiyanasiyana angakhale wachabechabe pamaso pa Mulungu ngati wayamba kudzikuza. Koma munthu wodzichepetsa, ngakhale atakhala wooneka ngati wonyozeka, amakhala wamtengo wapatali kwa Yehova. Tikamasonyeza khalidwe lofunika kwambiri limeneli tsiku ndi tsiku, poyesetsa kutsatira Khristu modzichepetsa, tidzalandira mphoto yamtengo wapatali kwambiri. Petulo analemba kuti: “Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.” (1 Petulo 5:6) Yehova anakwezadi Yesu chifukwa anali wodzichepetsa kwambiri. Inunso Mulungu wathu adzasangalala kukupatsani mphoto chifukwa cha kudzichepetsa kwanu.

      24 Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ena amaganiza kuti munthu akakhala wodzichepetsa ndiye kuti ndi wopusa. Chitsanzo cha Yesu chatithandiza kuona kuti maganizo amenewo ndi abodza, chifukwa iye anali munthu wodzichepetsa kwambiri kuposa aliyense komanso anali wolimba mtima kwambiri kuposa wina aliyense. M’mutu wotsatira tidzakambirana nkhani imeneyi.

      a Pofotokoza za nyama zimenezi, buku lina limanena kuti, nyama zimenezi “zimayenda pang’onopang’ono, n’zosamvera, n’zosaoneka bwino ndipo kawirikawiri amene amakhala nazo ndiponso kuzigwiritsa ntchito ndi anthu osauka.”

      b Kuti mupeze umboni wina wosonyeza kuti Yesu ndi Mikayeli, onani nkhani yakuti “Kodi Mikayeli Mkulu wa Angelo Ndi Ndani?” yomwe ikupezeka pambali yakuti, “Kuyankha Mafunso a M’baibulo” pa webusaiti ya Mboni za Yehova ya jw.org.

      Kodi Mungatani Kuti Muzitsatira Yesu?

      • Ngati mwayamba kunyada chifukwa cha zimene mwakwanitsa kuchita, kodi chitsanzo cha Yesu chingakuthandizeni bwanji?​—Mateyu 12:15-19; Maliko 7:35-37.

      • Kodi mungatsanzire bwanji Yesu pogwira ntchito zooneka ngati zonyozeka zothandiza abale ndi alongo anu auzimu?​—Yohane 21:1-13.

      • Kodi mungapindule bwanji ndi chitsanzo cha Yesu ngati mwayamba kufunitsitsa kuti zinthu zizikuyenderani bwino m’dzikoli komanso kuti mukhale wotchuka?​—Yohane 6:14, 15.

  • “Taona! Mkango wa Fuko la Yuda”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • MUTU 4

      “Taona! Mkango wa Fuko la Yuda”

      Molimba mtima, Yesu akuuza gulu la anthu okwiya komanso asilikali amene abwera kuti adzamugwire kuti munthu amene akumufunayo ndi iyeyo. Atumwi ake okhulupirika akuonerera chapatali.

      “Ndi ineyo”

      1-3. Kodi Yesu anakumana ndi zinthu zoopsa ziti, nanga iye anatani?

      PA NTHAWI ina, gulu la anthu linapita kukafunafuna Yesu kuti limugwire. Pagululi panali amuna amene ananyamula malupanga ndi zibonga komanso panali asilikali. Popeza gulu la anthuwo linali ndi cholinga choipa, linayenda usiku m’misewu ya mu Yerusalemu kuwoloka chigwa cha Kidironi kupita kuphiri la Maolivi. Ngakhale kuti kunja kunali mwezi, anthuwo ananyamula zounikira. Kodi anthuwo ananyamula zounikirazo chifukwa chakuti mitambo inkaphimba mweziwo? Kapena kodi ankaganiza kuti munthu amene akufuna kumugwirayo angabisale? Sitikudziwa, koma chimene tikudziwa n’chakuti amene angaganize kuti Yesu ankachita mantha, ndiye kuti sakumudziwa bwino.

      2 Yesu ankadziwa kuti anthu akubwera kudzamugwira, koma iye sanathawe. Anthuwo anafika ndipo Yudasi, yemwe poyamba anali mnzake weniweni wa Yesu, ndi amene ankawatsogolera. Mopanda manyazi Yudasi anapereka Yesu, amene kale anali mbuye wake, pomupatsa moni wachiphamaso ndiponso kumukisa. Komabe, Yesu sanachite mantha ndipo anapita kukakumana ndi anthuwo. Iye anawafunsa kuti: “Mukufuna ndani?” Ndipo iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.”

      3 Ambirife tingachite mantha gulu la anthu onyamula zida ngati amenewa litabwera kudzatigwira. Mwina anthuwa ankaganizanso kuti Yesu achita mantha kwambiri. Koma iye sanaope, sanathawe ndiponso sananame kuti adzipulumutse. M’malomwake iye anangonena kuti: “Ndi ineyo.” Iye ananena zimenezi mtima uli m’malo komanso mopanda mantha ndipo anthuwo anadabwa kwambiri, moti anabwerera m’mbuyo n’kugwa pansi.​—Yohane 18:1-6; Mateyu 26:45-50; Maliko 14:41-46.

      4-6. (a) Kodi Mwana wa Mulungu amuyerekezera ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi Yesu anachita zinthu zitatu ziti zimene zimasonyeza kuti anali wolimba mtima?

      4 N’chifukwa chiyani Yesu sanachite mantha kapena kunjenjemera gulu loopsali litabwera kudzamugwira? Kuyankha mwachidule tinganene kuti anali wolimba mtima. Kulimba mtima ndi limodzi mwa makhalidwe ofunika kwambiri ndiponso osiririka amene mtsogoleri aliyense ayenera kukhala nawo. Ndipo palibe munthu amene angafanane ndi Yesu kapena kum’posa pa nkhani ya kulimba mtima. M’mutu wapita uja, tinaphunzira kuti Yesu anali wodzichepetsa komanso wofatsa kwambiri. N’chifukwa chake ankatchedwa kuti “Mwanawankhosa.” (Yohane 1:29) Koma chifukwa choti Yesu anali wolimba mtima, Baibulo limatchula Mwana wa Mulungu ameneyu ndi dzina lapadera. Limati: “Taona! Mkango wa fuko la Yuda.”​—Chivumbulutso 5:5.

      5 Mkango ndi nyama yolimba mtima kwambiri. Kodi munayamba mwaonapo maso ndi maso mkango waukulu waumuna? Ngati munauona, mwina mkangowo unali m’malo osungirako nyama zakutchire otetezedwa ndi mpanda. Komabe kuona mkango maso ndi maso, ngakhale uli mumpanda, n’kochititsa mantha. Mukamayang’anizana maso ndi maso ndi nyama yaikulu komanso yamphamvu imeneyi, simungaganize kuti mkangowo ungathawe chilichonse chifukwa cha mantha. Baibulo limanena kuti ‘mkango ndi wamphamvu kwambiri pa nyama zonse zakutchire ndiponso suopa chilichonse n’kubwerera m’mbuyo.’ (Miyambo 30:30) Khristu ndi wolimbanso mtima ngati mkango.

      6 Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene Yesu anachita zimene zimasonyeza kuti anali wolimba mtima ngati mkango. Tiona zimene anachita poteteza choonadi, potsatira chilungamo ndiponso pamene ankatsutsidwa. Tionanso kuti tonsefe, kaya ndife olimba mtima mwachibadwa kapena ayi, tingathe kutsanzira Yesu posonyeza kulimba mtima.

      Yesu Anateteza Choonadi Molimba Mtima

      7-9. (a) Kodi chinachitika n’chiyani Yesu ali ndi zaka 12, nanga n’chifukwa n’chiyani mukuona kuti zimene anachitazo zinali zochititsa mantha? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima pokambirana ndi aphunzitsi pakachisi?

      7 M’dziko lolamuliridwa ndi Satanali, yemwe ndi “tate wake wa bodza,” pamafunika kulimba mtima kuti munthu ateteze choonadi. (Yohane 8:44; 14:30) Yesu ankateteza choonadi molimba mtima kuyambira ali wamng’ono. Mwachitsanzo, ali ndi zaka 12 anasiyana ndi makolo ake pambuyo pa chikondwerero cha Pasika ku Yerusalemu. Kwa masiku atatu, Mariya ndi Yosefe anamufufuza ali ndi nkhawa kwambiri. Kenako anamupeza m’kachisi. Kodi ankachita chiyani m’kachisimo? Anamupeza “atakhala pakati pa aphunzitsi ndipo ankawamvetsera n’kumawafunsa mafunso.” (Luka 2:41-50) Ndiye taganizirani mmene zinthu zinalili pamene ankakambirana ndi aphunzitsiwo.

      8 Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti atsogoleri ena achipembedzo olemekezeka ankakonda kutsalira pakachisi pambuyo pa zikondwerero ndipo ankaphunzitsa anthu pakhonde lina lalikulu la kachisiyo. Anthu ankakhala pansi n’kumawamvetsera komanso kuwafunsa mafunso. Aphunzitsi amenewa anali ophunzira kwambiri moti ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose. Ankadziwanso bwino miyambo yawo yambirimbiri komanso malamulo ambirimbiri opanga okha amene anali ovuta kuwamvetsa. Kodi mukanamva bwanji ngati mukanakhala pakati pa anthu ngati amenewo? N’zosakayikitsa kuti mukanachita mantha ndipo zimenezo sizikanakhala zodabwitsa. Nanga bwanji mukanakhala kuti muli ndi zaka 12 zokha? N’zodziwikiratu kuti mukanaopa kwambiri chifukwa ana ambiri amachita mantha ndiponso manyazi. (Yeremiya 1:6) Ana ena akakhala m’kalasi amayesetsa kuchita zinthu zoti aphunzitsi awo asawatchule kuti ayankhe funso chifukwa amaopa kuti angachite manyazi kapena anzawo angawaseke.

      9 Koma Yesu anali wolimba mtima chifukwa anakhala pakati pa anthu ophunzira kwambiri ndipo ankawafunsa mafunso okhwima molimba mtima. Ndipo si zokhazi zimene anachita. Nkhani ya m’Baibuloyi imati: “Onse amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:47) Baibulo silinena zimene iye ananena pa nthawiyo, komabe tikukhulupirira kuti sankanena zinthu zabodza zimene aphunzitsi achipembedzowo ankakonda kuphunzitsa. (1 Petulo 2:22) Iye anateteza choonadi cha m’Mawu a Mulungu, ndipo anthu amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri kuti mwana wa zaka 12 akulankhula zinthu zanzeru molimba mtima.

      Mlongo wachitsikana akukambirana ndi aphunzitsi ake pogwiritsa ntchito bulu lakuti “Is There a Creator Who Cares About You?”.

      Akhristu ambiri achinyamata amauza anzawo molimba mtima zimene amakhulupirira

      10. Kodi Akhristu achinyamata masiku ano amatsanzira bwanji kulimba mtima kwa Yesu?

      10 Masiku ano, achinyamata ambiri a Chikhristu akutsanzira Yesu. N’zoona kuti iwo ndi osiyana ndi Yesu chifukwa si angwiro. Komabe mofanana ndi Yesu, iwo sayembekeza kuti akule kaye kuti adzateteze choonadi. Mwachitsanzo, kusukulu kapena m’madera amene akukhala, iwo amafunsa anthu mafunso mwanzeru, amawamvetsera ndipo amawauza choonadi mwaulemu. (1 Petulo 3:15) Achinyamata amenewa athandiza ana asukulu anzawo, aphunzitsi awo komanso anthu amene amakhala moyandikana nawo kukhala otsatira a Khristu. Iwo amasangalatsa kwambiri Yehova chifukwa cha kulimba mtima kwawo. Mawu a Mulungu anayerekezera achinyamata amenewa ndi mame chifukwa amakhala otsitsimula, osangalatsa ndiponso ochuluka.​—Salimo 110:3.

      11, 12. Kodi Yesu atakula anasonyeza bwanji kulimba mtima poteteza choonadi?

      11 Yesu atakula anasonyezanso kulimba mtima mobwerezabwereza poteteza choonadi. Ndipotu anthu ambiri angavomereze kuti zimene zinachitika pamene ankayamba utumiki wake zinali zoopsa. Yesu anafunika kulimbana ndi Satana, amene ndi mdani wa Yehova wamphamvu komanso woopsa kwambiri pa adani ake onse. Komatu pa nthawiyi Yesu anali munthu wamba, sanali mkulu wa angelo wamphamvu ayi. Komabe iye anatsutsa Satana ndipo anakana kuchita zimene anamupempha, Satanayo atagwiritsa ntchito Malemba molakwika. Pamapeto pake, Yesu anathetsa zokambiranazo pokalipira Satana kuti: “Choka Satana!”​—Mateyu 4:2-11.

      12 Choncho Yesu anasonyeza kuti pa utumiki wake, adziteteza Mawu a Atate ake molimba mtima kuti asapotozedwe kapena kugwiritsidwa ntchito molakwika. Mofanana ndi masiku ano, pa nthawiyo atsogoleri ambiri achipembedzo anali osaona mtima. N’chifukwa chake Yesu anauza atsogoleri achipembedzo a nthawi imeneyo kuti: “Mumapangitsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu imene munaipereka kwa anthu.” (Maliko 7:13) Anthu ankalemekeza kwambiri atsogoleri amenewo, koma Yesu anawadzudzula mopanda mantha ndipo anawanena kuti ndi atsogoleri akhungu komanso anthu achinyengo.a (Mateyu 23:13, 16) Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yesu kumeneku?

      13. Tikamatsanzira Yesu, kodi tizikumbukira chiyani, nanga tili ndi mwayi wapadera uti?

      13 N’zoona kuti tilibe mphamvu yodziwa za mumtima mwa munthu kapena yoweruza anthu ngati mmene Yesu ankachitira. Komabe tingateteze choonadi molimba mtima ngati mmene iye ankachitira. Mwachitsanzo, tikamatsutsa mabodza amene zipembedzo zimaphunzitsa, monga onena za Mulungu, cholinga chake komanso Mawu ake, timathandiza anthu kuti aone kuwala kwa choonadi m’dziko limene Satana walichititsa mdima ndi ziphunzitso zake zabodza. (Mateyu 5:14; Chivumbulutso 12:9, 10) Timathandiza anthu kuti amasuke ku ziphunzitso zabodza zimene zimawachititsa kuti aziopa zinthu zomwe sizingachitike ndiponso zimene zimawononga ubwenzi wawo ndi Mulungu. Tilitu ndi mwayi wapadera kwambiri kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.

      Molimba Mtima, Yesu Ankaonetsetsa Kuti Zinthu Zikuchitika Mwachilungamo

      14, 15. (a) Kodi ndi njira imodzi iti imene Yesu anasonyezera bwinobwino “chilungamo chenicheni”? (b) Kodi Yesu anapewa maganizo a tsankho ati kuti athe kulankhula ndi mkazi wa Chisamariya?

      14 Ulosi wa m’Baibulo unaneneratu kuti Mesiya adzasonyeza bwinobwino anthu a mitundu ina “chilungamo chenicheni.” (Mateyu 12:18; Yesaya 42:1) Yesu anayamba kuchita zimenezi ali padziko lapansi pano. Yesu anali wolimba mtima ndipo nthawi zonse ankachita zinthu mwachilungamo komanso mopanda tsankho. Mwachitsanzo, ngakhale kuti anthu ambiri ankachita zinthu mwatsankho ndiponso mokondera, Yesu anakana kuchita nawo zimenezi chifukwa zinali zosagwirizana ndi malemba.

      15 Pamene Yesu ankalankhula ndi mayi wa Chisamariya pachitsime cha ku Sukari, ophunzira ake anadabwa kwambiri. N’chifukwa chiyani anadabwa? Pa nthawi imeneyo, Ayuda ankadana kwambiri ndi Asamariya ndipo chidani chimenechi chinayamba kale kwambiri Yesu asanabwere padziko lapansi. (Ezara 4:4) Komanso arabi ena ankakhulupirira kuti akazi ndi otsika poyerekezera ndi amuna. Iwo anafika polemba malamulo oletsa amuna kuti asamalankhule ndi akazi. Ankaonanso kuti akazi si oyenera kuwaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu ndipo akazi a Chisamariya ankawaona kuti ndi odetsedwa. Koma Yesu sanatengere maganizo a tsankho amenewo. Mosabisa, Yesu anaphunzitsa mkazi wa Chisamariya (amene anali wachiwerewere) ndipo anauza mkaziyo kuti iye ndi Mesiya.​—Yohane 4:5-27.

      16. N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala olimba mtima kuti apewe tsankho?

      16 Kodi munayamba mwakhalapo ndi anthu atsankho? Mwina iwo amanena nthabwala zonyoza anthu a mtundu kapena fuko lina, amalankhula zinthu zonyoza anthu amene si amuna kapena akazi anzawo, kapenanso amanyoza anthu ooneka ngati onyozeka kapena osauka. Otsatira a Khristu amapewa khalidwe limeneli ndipo amachita khama kuti achotse maganizo alionse atsankho mumtima mwawo. (Machitidwe 10:34) Aliyense wa ife ayenera kukhala wolimba mtima kuti apewe tsankho.

      17. Kodi Yesu anachita chiyani m’kachisi, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezo?

      17 Popeza anali wolimba mtima, Yesu analimbikitsa anthu a Mulungu kuti akhale oyera ndiponso kuti kulambira kwawo kukhale kosadetsedwa. Kumayambiriro kwa utumiki wake, iye analowa m’kachisi wa ku Yerusalemu ndipo ananyansidwa kwambiri ataona anthu akugulitsa malonda ndi kusintha ndalama m’kachisimo. M’pomveka kuti Yesu anakwiya ndipo anathamangitsa anthu adyerawo n’kutulutsa malonda awo m’kachisimo. (Yohane 2:13-17) Kenako, atatsala pang’ono kutsiriza utumiki wake padzikoli, Yesu anachitanso chimodzimodzi. (Maliko 11:15-18) Anthu ena anayamba kudana naye kwambiri chifukwa cha zimenezi, komabe iye anapitiriza kutsatira chilungamo. Chifukwa chiyani? Kuyambira ali wamng’ono, ankanena kuti kachisiyo ndi nyumba ya Atate ake ndipo zinali zoona. (Luka 2:49) Kuchita zinthu zodetsa kulambira koyera kumene kunkachitika pakachisiyo kunali kupanda chilungamo ndipo iye sakanalekerera zimenezo. Chifukwa chakuti anali wodzipereka kwambiri, iye analimba mtima n’kuchita zimene zinali zoyenera.

      18. Kodi Akhristu masiku ano angasonyeze bwanji kulimba mtima kuti mpingo ukhalebe woyera?

      18 Mofanana ndi Yesu, otsatira a Khristu masiku ano amafunitsitsa kuti aliyense m’gulu la atumiki a Mulungu akhale woyera komanso kuti apitirize kulambira Mulungu m’njira yoyenera. Iwo salekerera akadziwa kuti Mkhristu mnzawo wachita tchimo lalikulu, koma molimba mtima amalankhula naye. (1 Akorinto 1:11) Amaonetsetsa kuti akulu mumpingo adziwa za nkhaniyo. Akulu amathandiza anthu amene akudwala mwauzimu ndipo amayesetsa kuteteza nkhosa za Yehova kuti zisadetsedwe.​—Yakobo 5:14, 15.

      19, 20. (a) Kodi ndi zinthu ziti zopanda chilungamo zimene zinkachitika m’masiku a Yesu, nanga ndi mavuto otani amene Yesu anakumana nawo? (b) N’chifukwa chiyani otsatira Khristu amakana kulowerera ndale komanso kuchita zachiwawa, nanga amapeza madalitso otani chifukwa cha zimenezi?

      19 Kodi tinganene kuti Yesu ankafuna kuthetsa zinthu zonse zopanda chilungamo? Ayi. Zinthu zambiri zopanda chilungamo zinkachitika paliponse. Mwachitsanzo, dziko limene iye anabadwira linkalamuliridwa ndi Aroma. Iwo ankagwiritsira ntchito asilikali awo pozunza Ayudawo ndipo ankawalamula kuti azipereka ndalama zambiri za msonkho komanso ankasokoneza miyambo ya chipembedzo chawo. N’chifukwa chake Ayuda ambiri ankafuna kuti Yesu azichita nawo ndale kuti akhale mtsogoleri wawo. (Yohane 6:14, 15) Apanso, Yesu ankafunika kusonyeza kulimba mtima.

      20 Yesu anafotokoza kuti Ufumu wake sunali wa padziko lapansi. Iye anaphunzitsa otsatira ake kuti asamalowerere m’mikangano ya ndale za nthawi imeneyo ndipo anachita zimenezi powasonyeza chitsanzo chabwino. Komanso anawalimbikitsa kuti azilalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Yohane 17:16; 18:36) Iye anawapatsa phunziro labwino pankhani yopewa chiwawa, pamene gulu la anthu linabwera kuti lidzamugwire. Mwamsanga Petulo anasolola lupanga lake n’kuvulaza munthu wina pagululo. Anthu angaganize kuti Petulo sanalakwitse kugwiritsa ntchito lupanga pamene anthu anabwera kudzagwira Mwana wa Mulungu yemwe anali wosalakwa. Koma pa nthawiyo Yesu anapereka phunziro limene likugwirabe ntchito kwa otsatira ake mpaka lero. Iye anati: “Bwezera lupanga lako m’chimake, chifukwa onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyu 26:51-54) Otsatira a Khristu ankafunika kukhala olimba mtima kuti athe kuchita zinthu mwamtendere pa nthawi imeneyo ndipo masiku anonso timafunika kulimba mtima. Anthu a Mulungu masiku ano ali ndi mbiri yabwino yoti samenya nawo nkhondo, sachita ziwawa ndi zina zotero chifukwa chakuti salowerera ndale. Amenewatu ndi madalitso amene amapeza chifukwa cha kulimba mtima kwawo.

      Yesu Analimba Mtima Pamene Ankatsutsidwa

      21, 22. (a) Kodi Yesu analimbikitsidwa bwanji asanayambe kukumana ndi mayesero aakulu? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kulimba mtima mpaka imfa?

      21 Mwana wa Yehova ankadziwa bwino kuti akadzabwera padziko lapansi adzatsutsidwa kwambiri. (Yesaya 50:4-7) Anthu osiyanasiyana ankafuna kumupha ndipo zolinga zawozo zinakwaniritsidwadi monga mmene tafotokozera kumayambiriro kwa nkhani ino. Kodi Yesu anatani kuti akhalebe wolimba mtima pa nthawi yovutayo? Kumbukirani zimene Yesu ankachita gulu la anthu lija lisanafike kudzamugwira. Iye ankapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Ndipo Yehova anamuyankha chifukwa Baibulo limanena kuti “anamumvera.” (Aheberi 5:7) Yehova anatumiza mngelo kuchokera kumwamba kuti adzalimbikitse Mwana wake wolimba mtimayo.​—Luka 22:42, 43.

      22 Patangopita nthawi yochepa mngeloyo atamulimbikitsa, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita.” (Mateyu 26:46) Mawu amenewatu akusonyeza kuti Yesu anali wolimba mtima kwambiri. Ngakhale ananena kuti “nyamukani, tiyeni tizipita,” Yesu ankadziwa kuti auza gulu la anthu odzamugwirawo kuti asavulaze anzakewo. Ankadziwanso kuti anzakewo amusiya n’kuthawa komanso kuti akhala yekhayekha akamazunzidwa mwankhanza kwambiri. Iye analidi yekhayekha pamene ankamuimba mlandu womunamizira ndi kumuweruza mopanda chilungamo, kumunyoza, kumuzunza komanso kumupha mwankhanza. Pa nthawi yonse imene ankazunzikayo, Yesu anakhalabe wolimba mtima.

      23. Fotokozani chifukwa chake tikunena kuti zimene Yesu anachita pamene anthu ankafuna kumupha sizikusonyeza kuti sankasamala za moyo wake.

      23 Kodi Yesu anasonyeza kuti sankasamala za moyo wake? Ayi si choncho, chifukwa kulimba mtima n’kosiyana ndi kuchita zinthu mosasamala. Ndipotu polimbikitsa otsatira ake kuti apitirize kutumikira Mulungu, Yesu anawauza kuti azikhala osamala komanso kuti azichoka pamalo akaona kuti china chake choopsa chichitika. (Mateyu 4:12; 10:16) Koma pa nthawiyi, Yesu ankadziwa kuti palibe chilichonse chimene akanachita kuti apewe mayeserowo. Ankadziwa zimene Mulungu akufuna kuti iyeyo achite. Yesu anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupirika, choncho sakanachitira mwina koma kulola kuti akumane ndi mayeserowo basi.

      Abale atatu avala mayunifolomu akundende ndipo mofunitsitsa akupirira pamene ankazunzidwa ndi chipani cha Nazi ku Germany.

      A Mboni za Yehova amasonyeza kulimba mtima akamazunzidwa

      24. N’chifukwa chiyani sitikukayikira kuti tingakhalebe olimba mtima pamene takumana ndi mayesero alionse?

      24 N’zosangalatsa kuti otsatira a Yesu mobwerezabwereza atengera chitsanzo cha Mbuye wawo molimba mtima. Ambiri asonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro cholimba akamanyozedwa, kuzunzidwa, kumangidwa, kumenyedwa mwankhanza ngakhale kulolera kuphedwa kumene. Kodi zimatheka bwanji kuti anthu omwe si angwiro akhale olimba mtima choncho? Sikuti zimangochitika mwamwayi. Mulungu ndi amene anathandiza Yesu ndipo amathandizanso otsatira ake. (Afilipi 4:13) Choncho musamaope zimene zingadzakuchitikireni m’tsogolo. Koma tsimikizani mtima kuti mukhalabe okhulupirika ndipo Yehova adzakuthandizani kuti mukhale olimba mtima. Chitsanzo cha Mtsogoleri wathu Yesu chizikulimbitsani mtima, chifukwa iye anati: “Limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”​—Yohane 16:33.

      a Akatswiri a mbiri yakale amanena kuti anthu ankalemekeza kwambiri manda a atsogoleri a chipembedzo ngati mmene ankalemekezera manda a aneneri ndi makolo akale.

      Kodi Mungatani Kuti Muzitsatira Yesu?

      • Kodi chitsanzo cha Yesu chingatithandize bwanji kulankhula molimba mtima ngakhale pamene anthu akudana ndi choonadi chimene tikuwauza?​—Yohane 8:31-59.

      • N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kuthandiza ena chifukwa choopa Satana ndi ziwanda zake?​—Mateyu 8:28-34; Maliko 1:23-28.

      • N’chifukwa chiyani tiyenera kulolera kuzunzika kuti tisonyeze chifundo kwa anthu amene akuponderezedwa?​—Yohane 9:1, 6, 7, 22-41.

      • Kodi chiyembekezo chinathandiza bwanji Yesu atakumana ndi mayesero, nanga inuyo chingakuthandizeni bwanji kuti mukhale wolimba mtima?​—Yohane 16:28; 17:5; Aheberi 12:2.

  • “Chuma Chonse Chokhudzana ndi Nzeru”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • MUTU 5

      “Chuma Chonse Chokhudzana ndi Nzeru”

      1-3. Kodi Yesu analalikira pamalo ati mu 31 C.E. ndipo zinthu zinali bwanji pa nthawiyo, nanga n’chifukwa chiyani omvera ake anadabwa kwambiri?

      CHINALI chaka cha 31 C.E. ndipo Yesu Khristu anali paphiri linalake lomwe lili pafupi ndi mzinda wa Kaperenao. Mzindawu unali kumpoto chakumadzulo kwa nyanja ya Galileya ndipo unali wotchuka kwambiri. Yesu anali yekhayekha kuphiri limeneli ndipo anapemphera usiku wonse. Kunja kutacha, anaitana ophunzira ake n’kusankhapo anthu 12 omwe anawatchula kuti atumwi. Pa nthawiyi, anthu ambiri, ena mwa iwo ochokera m’madera a kutali, anatsatira Yesu kumalo amene iye anali ndipo anasonkhana pamalo afulati paphiripo. Iwo ankayembekezera mwachidwi kuti amvetsere Yesu akamaphunzitsa komanso kuti awachiritse matenda awo osiyanasiyana. Ndipo Yesu anachitadi zimene anthuwo ankayembekezera.​—Luka 6:12-19.

      2 Yesu anapita pamene panali anthuwo n’kuchiritsa aliyense amene ankadwala. Kenako iye anakhala pansi n’kuyamba kuwaphunzitsa.a Anthuwo ayenera kuti anadabwa ndi mmene iye ankaphunzitsira chifukwa anali asanamvepo munthu wina aliyense akuphunzitsa ngati mmene Yesu anachitira. Pofuna kusonyeza kuti zimene ankaphunzitsazo n’zofunika kwambiri, Yesu sanaikemo miyambo ya Ayuda kapena zinthu zimene arabi otchuka a Chiyuda ankaphunzitsa. Koma mobwerezabwereza, iye ankagwira mawu Malemba a Chiheberi ouziridwa. Uthenga wake unali wosapita m’mbali komanso unali womveka bwino ndipo iye ankagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva. Atamaliza kuphunzitsa, anthuwo anadabwa kwambiri. Mpake kuti iwo anadabwa chifukwa anali atamvetsera ulaliki wa munthu wanzeru kwambiri kuposa aliyense padziko lapansi.​—Mateyu 7:28, 29.

      Yesu akulankhula ndi gulu lalikulu la anthu pa ulaliki wake wapaphiri.

      “Gulu la anthulo . . . linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake”

      3 Ulaliki umenewu limodzi ndi zinthu zina zambiri zimene Yesu ananena ndi kuchita, zinalembedwa m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Tingachite bwino kufufuza mozama Mawu a Mulungu kuti tidziwe mfundo zina zokhudza Yesu, chifukwa “chuma chonse chokhudzana ndi nzeru” chili mwa iye. (Akolose 2:3) Yesu anali ndi nzeru ndipo zochita zake zinkasonyeza kuti ankadziwa zinthu zambiri komanso anali wozindikira. Kodi nzeru zimenezo anazitenga kuti? Kodi iye anasonyeza bwanji kuti anali ndi nzeru, nanga ifeyo tingamutsanzire bwanji?

      “Kodi Munthu Ameneyu Anazitenga Kuti . . . Nzeru Zimenezi?”

      4. Kodi anthu amene ankamvetsera Yesu ku Nazareti anafunsa funso lotani, nanga n’chifukwa chiyani?

      4 Pa nthawi ina Yesu ali pa ulendo wolalikira m’madera osiyanasiyana, anafika ku Nazareti, mzinda umene iye anakulira, n’kuyamba kuphunzitsa m’sunagoge. Ambiri mwa anthu amene ankamumvetsera anadabwa ndipo anafunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti . . . nzeru zimenezi?” Iwo ankawadziwa bwino makolo ake komanso abale ake ndipo ankadziwanso kuti anachokera m’banja losauka. (Mateyu 13:54-56; Maliko 6:1-3) Anthuwo ayenera kuti ankadziwanso kuti kalipentala wodziwa kuphunzitsa Mawu a Mulungu ameneyu sanaphunzire m’sukulu zotchuka za arabi. (Yohane 7:15) Choncho m’pomveka kuti iwo anafunsa funso limeneli.

      5. Kodi Yesu anaulula kuti nzeru zake zinachokera kwa ndani?

      5 Ngakhale kuti Yesu anali wangwiro, nzeru zimene anasonyeza pophunzitsa sizinkachokera m’mutu mwake. Pa nthawi ina Yesu akuphunzitsa m’kachisi, anaulula kuti nzeru zake n’zochokera kwa winawake wanzeru kwambiri kuposa iyeyo. Iye anati: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga, koma ndi za amene anandituma.” (Yohane 7:16) Choncho, nzeru za Yesu zinachokera kwa Atate wake amene anamutuma. (Yohane 12:49) Komabe, kodi Yesu analandira bwanji nzeru zochokera kwa Yehova?

      6, 7. Kodi Yesu analandira nzeru zochokera kwa Atate ake m’njira ziti?

      6 Mzimu woyera wa Yehova unakhazikika mumtima ndi m’maganizo a Yesu. Polosera za Mesiya wolonjezedwa, amene ndi Yesu, Yesaya ananena kuti: “Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye, mzimu wanzeru ndi womvetsa zinthu, mzimu wopereka malangizo abwino ndi wamphamvu, mzimu wodziwa zinthu ndi woopa Yehova.” (Yesaya 11:2) Choncho, n’zosadabwitsa kuti mawu komanso zochita za Yesu zinasonyeza kuti anali ndi nzeru zakuya chifukwa mzimu woyera wa Yehova unali pa iye ndipo unkatsogolera maganizo ake ndiponso zinthu zimene ankasankha kuchita.

      7 Yesu analandira nzeru kuchokera kwa Atate ake m’njira inanso yapadera kwambiri. Mogwirizana ndi zimene tinaona m’mutu wachiwiri, iye anakhala zaka zosawerengeka ndi Atate ake kumwamba asanabwere padziko lapansi. Pa nthawiyi, Yesu anali ndi mwayi wodziwa maganizo a Atate ake pa nkhani zosiyanasiyana. Sitingathe n’komwe kudziwa kuya kwa nzeru zimene Mwanayu anatengera kwa Atate ake. Iye anatengera nzeruzi kwa Mulungu pamene ankagwira ntchito yolenga zinthu zonse, zamoyo komanso zopanda moyo, monga ‘mmisiri wake waluso.’ Choncho, n’zomveka kuti Baibulo limafotokoza kuti Mwanayu asanabwere padziko lapansi anali ngati nzeru. (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:15, 16) Pa utumiki wake wonse, Yesu ankagwiritsa ntchito nzeru zimene anatengera kwa Atate ake pa nthawi imene anali kumwamba.b (Yohane 8:26, 28, 38) Choncho, sitiyenera kudabwa kuti pa mawu aliwonse ndiponso pa chilichonse chimene ankachita, Yesu anasonyeza nzeru zakuya komanso kumvetsa zinthu.

      8. Monga otsatira a Yesu, kodi tingatani kuti tipeze nzeru?

      8 Monga otsatira a Yesu, nafenso tiyenera kudalira Yehova kuti azitipatsa nzeru. (Miyambo 2:6) Komabe, Yehova sangatipatse nzeru mozizwitsa. M’malomwake iye amayankha mapemphero athu ochokera pansi pa mtima opempha nzeru zimene zingatithandize kuti tizilimbana ndi mavuto pa moyo wathu. (Yakobo 1:5) Pamafunika khama kuti tipeze nzeru zimenezi, choncho tiyenera kupitiriza kuzifunafuna “ngati chuma chobisika.” (Miyambo 2:1-6) Ndithudi, tikuyenera kupitiriza kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu kuti tipeze nzeru zimenezi ndipo tizichita zinthu mogwirizana ndi zimene taphunzirazo. Njira imodzi yabwino kwambiri imene ingatithandize kupeza nzeru ndi kuganizira chitsanzo cha Yesu, amene ndi Mwana wa Yehova. Tiyeni tione mbali zingapo zimene Yesu anasonyezera nzeru ndipo tiphunzira zimene tingachite kuti timutsanzire.

      Mawu a Nzeru

      M’bale akuwerenga Baibulo. Ndipo padesiki yake pali mabuku otsegula othandiza pophunzira Baibulo.

      Baibulo limasonyeza nzeru zimene Mulungu ali nazo

      9. N’chiyani chinachititsa kuti zinthu zimene Yesu ankaphunzitsa zikhale za nzeru?

      9 Anthu ambirimbiri ankapita kwa Yesu kukamumvetsera akamaphunzitsa. (Maliko 6:31-34; Luka 5:1-3) Ndipo zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Yesu ankati akayamba kulankhula, mawu ake ankakhala a nzeru zosaneneka. Zinthu zimene ankaphunzitsa zinasonyeza kuti ankadziwa bwino kwambiri Mawu a Mulungu komanso ankawadziwa bwino anthu. Zimene ankaphunzitsa zikugwirabe ntchito mpaka lero ndipo n’zothandiza kwa munthu aliyense. Taonani zina mwa zitsanzo zosonyeza nzeru za Yesu, “Mlangizi Wodabwitsa,” amene Yesaya anamulosera.​—Yesaya 9:6.

      10. Kodi Yesu anatilimbikitsa kuti tikhale ndi makhalidwe abwino ati, nanga n’chifukwa chiyani?

      10 Ulaliki wa paphiri, umene tautchula kumayambiriro kwa nkhani ino, ndi ulaliki wautali kwambiri pa maulaliki onse a Yesu amene analembedwa m’Baibulo. Mu ulalikiwu mulibe mawu ofotokozera kapena mawu a anthu ena. Sikuti Yesu anangopereka malangizo okhudza kulankhula mwaulemu komanso kukhala ndi khalidwe labwino, koma ananenanso zimene zingatithandize kuchita zimenezi. Chifukwa choti Yesu ankadziwa kuti anthufe timalankhula komanso kuchita zinthu zimene zili mumtima ndi m’maganizo mwathu, iye anatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino, amene amayambira mumtima ndi m’maganizo. Ena mwa makhalidwe amenewa ndi kufatsa, chilungamo, chifundo, mtendere ndiponso kukonda anthu ena. (Mateyu 5:5-9, 43-48) Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe amenewa mumtima mwathu, khalidwe lathu ndiponso zolankhula zathu zimasangalatsa Yehova komanso timakhala pa ubwenzi wabwino ndi anthu ena.​—Mateyu 5:16.

      11. Popereka malangizo amene amatithandiza kupewa makhalidwe oipa, kodi Yesu anasonyeza bwanji kufunika kolimbana ndi chimene chimayambitsa vuto?

      11 Pamene ankapereka malangizo othandiza kuti tizipewa makhalidwe oipa, Yesu anatchula zimene zimayambitsa makhalidwe oipawo. Mwachitsanzo, iye sanangotiuza kuti tizipewa kuchita zachiwawa. M’malomwake, anatichenjeza kuti tizipewa kusunga mkwiyo mumtima mwathu. (Mateyu 5:21, 22; 1 Yohane 3:15) Kuwonjezera pa kuletsa kuchita chigololo, iye anatichenjeza kuti tizipewa maganizo oipa amene amayambira mumtima omwe amachititsa kuti munthu achite tchimoli. Komanso anatichenjeza kuti tisamalole kuti maso athu azitichititsa kukhala ndi chilakolako choipa chogonana. (Mateyu 5:27-30) Yesu anatiphunzitsa kufunika kolimbana ndi chimene chimayambitsa vuto, osati kungolimbana ndi vuto lokhalo. Iye anapereka malangizo amene amatithandiza kuthana ndi makhalidwe ndiponso mtima umene ungatilimbikitse kuchita tchimo.​—Salimo 7:14.

      12. Kodi otsatira a Yesu amaona bwanji malangizo amene iye anapereka, ndipo n’chifukwa chiyani?

      12 Mawu a Yesu anasonyeza nzeru zakuya kwambiri. Choncho n’zosadabwitsa kuti “gulu la anthulo . . . linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake.” (Mateyu 7:28) Monga otsatira ake, timagwiritsa ntchito malangizo akewo kuti azitithandiza pa moyo wathu. Timayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino amene iye analimbikitsa, monga chifundo, mtendere ndiponso chikondi. Timadziwa kuti kukhala ndi makhalidwe amenewa n’kofunika kwambiri kuti tizisangalatsa Yehova. Timayesetsa kuchotsa mumtima mwathu khalidwe lililonse loipa limene Yesu anachenjeza kuti tizilipewa, monga kupsa mtima. Komanso timapewa maganizo aliwonse oipa, monga okhudza chiwerewere. Timayesetsa kuchita zimenezi chifukwa timadziwa kuti zingatithandize kupewa kuchita tchimo.​—Yakobo 1:14, 15.

      Zimene Yesu Ankachita Zinasonyeza Kuti Anali Wanzeru

      13, 14. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anasankha kugwiritsira ntchito moyo wake mwanzeru?

      13 Yesu anasonyeza kuti anali wanzeru pa zimene ankalankhula komanso zimene ankachita. Chilichonse pa moyo wake, monga zimene ankasankha kuchita, mmene ankadzionera ndiponso mmene ankachitira zinthu ndi anthu ena, zimasonyeza bwino kwambiri kuti nzeru zake ankazigwiritsa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Tiyeni tione zitsanzo zimene zikusonyeza kuti Yesu anali ndi ‘nzeru zopindulitsa ndiponso ankaganiza bwino.’​—Miyambo 3:21.

      14 Munthu angasonyeze kuti ndi wanzeru ngati amachita zinthu mozindikira pa moyo wake. Zimene Yesu anasankha kuchita pa moyo wake zimasonyeza kuti ndi wozindikira kwambiri. Iye akanatha kusankha kuti akhale ndi moyo wapamwamba ndiponso kuti akhale ndi zinthu zabwino kwambiri. Mwachitsanzo, akanatha kumanga nyumba yabwino kwambiri, kukhala ndi bizinezi yaikulu kapenanso kukhala wolamulira wotchuka. Koma Yesu ankadziwa kuti kufunitsitsa kukhala ndi zinthu zimenezi ‘n’kwachabechabe ndipo kuli ngati kuthamangitsa mphepo.’ (Mlaliki 4:4; 5:10) Kukhala ndi moyo wofunitsitsa zinthu zimenezi n’kupusa ndiponso kupanda nzeru. Yesu anasankha kuti akhale ndi moyo wosafuna zambiri. Iye analibe cholinga choti akhale ndi ndalama zambiri kapena katundu wambiri. (Mateyu 8:20) Mogwirizana ndi zimene ankaphunzitsa, iye anali ndi diso loyang’ana pa chinthu chimodzi, chomwe chinali kuchita chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 6:22) Yesu anasonyeza nzeru pogwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zake pa zinthu zokhudzana ndi Ufumu, zomwe ndi zofunika kwambiri poyerekezera ndi zinthu zakuthupi. (Mateyu 6:19-21) Choncho iye anatisiyira chitsanzo chabwino choti titsatire.

      15. Kodi otsatira a Yesu angasonyeze bwanji kuti ali ndi diso loyang’ana pa Ufumu wa Mulungu wokha, nanga n’chifukwa chiyani ndi nzeru kuchita zimenezi?

      15 Otsatira a Yesu masiku ano amaonanso kuti n’chinthu chanzeru kukhala ndi diso loyang’ana pa chinthu chimodzi chomwe ndi Ufumu wa Mulungu. Choncho, iwo amapewa kutenga ngongole zosafunikira zimene zingawabweretsere mavuto. Amapewanso kuda nkhawa kwambiri ndi zinthu zatsiku ndi tsiku zimene zingawawonongere nthawi ndiponso mphamvu zawo. (1 Timoteyo 6:9, 10) Ndipotu ambiri asintha zina ndi zina pa moyo wawo kuti azikhala moyo wosafuna zambiri n’cholinga choti azithera nthawi yambiri mu utumiki wa Chikhristu, ngakhalenso kuyamba utumiki wanthawi zonse. Palibe chinthu chanzeru kwambiri kuposa kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’moyo wathu, zimenezi zimatithandiza kuti tikhale osangalala komanso kuti tilandire madalitso ambiri.​—Mateyu 6:33.

      16, 17. (a) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa komanso kuti ankadziwa kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife odzichepetsa komanso kuti tikudziwa kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kuchita?

      16 Baibulo limasonyeza kuti munthu wanzeru amakhalanso wodzichepetsa. Zimenezi zikutanthauza kuti amazindikira zimene sangakwanitse kuchita. (Miyambo 11:2) Yesu anasonyeza kuti anali wodzichepetsa chifukwa ankadziwa kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse. Iye ankadziwa kuti sakanapangitsa kuti aliyense amene wamva uthenga wake akhale wotsatira wake. (Mateyu 10:32-39) Ankadziwanso kuti anthu amene angakwanitse kuwalalikira ndi ochepa kwambiri. N’chifukwa chake anachita zinthu mwanzeru n’kusiyira otsatira ake ntchito yothandiza anthu kuti akhale ophunzira ake. (Mateyu 28:18-20) Modzichepetsa, Yesu ananena kuti otsatira akewo “adzachita ntchito zazikulu kuposa” zimene iye anachita, chifukwa iwo adzalalikira kwa anthu ambiri, m’madera ambiri ndiponso adzalalikira kwa nthawi yaitali. (Yohane 14:12) Komanso, Yesu sankadziona kuti ndi wapamwamba moti sangathandizidwe ndi wina aliyense. Mwachitsanzo, iye anavomera kuthandizidwa ndi angelo amene anabwera kudzamutumikira pamene anali m’chipululu ndiponso anavomera kuthandizidwa ndi mngelo amene anabwera kudzamulimbikitsa m’munda wa Getsemane. Pa nthawi imene anafunikira kuthandizidwa kwambiri, Mwana wa Mulungu anapemphera mofuula kuti Atate ake amuthandize.​—Mateyu 4:11; Luka 22:43; Aheberi 5:7.

      17 Ifenso tiyenera kukhala odzichepetsa ndipo tizidziwa kuti pali zinthu zina zomwe sitingakwanitse. Komabe, tizigwira ndi mtima wonse ntchito yolalikira ndi kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira a Yesu ndipo tizichita zimenezi mwakhama kwambiri. (Luka 13:24; Akolose 3:23) Ngakhale zili choncho, tisaiwale kuti Yehova satiyerekezera ndi munthu wina ndipo ifenso tisamachite zimenezi. (Agalatiya 6:4) Nzeru zidzatithandiza kudziikira zolinga zimene tingakwanitsedi zogwirizana ndi mphamvu zathu ndiponso mmene zinthu zilili pa moyo wathu. Komanso, nzeru zingathandize anthu amene ali ndi udindo kuzindikira kuti pali zinthu zina zimene sangakwanitse kuchita pawokha, ndipo angafunike kuthandizidwa ndiponso kulimbikitsidwa nthawi ndi nthawi. Kudzichepetsa kungawathandize kuvomera mwaulemu wina akafuna kuwathandiza ndipo iwo angazindikire kuti Yehova akhoza kugwiritsira ntchito Mkhristu mnzawo kuti ‘awalimbikitse kwambiri.’​—Akolose 4:11.

      18, 19. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu anali wololera ndiponso wokoma mtima pochita zinthu ndi ophunzira ake? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okoma mtima komanso ololera pochita zinthu ndi ena, nanga tingachite bwanji zimenezi?

      18 Lemba la Yakobo 3:17 limati: ‘Nzeru yochokera kumwamba ndi yololera.’ Yesu anali wololera ndiponso wokoma mtima pochita zinthu ndi ophunzira ake. Ngakhale kuti ankadziwa zimene ophunzirawo ankalakwitsa, iye ankayang’ana zabwino zimene iwo ankachita. (Yohane 1:47) Yesu ankadziwa kuti ophunzira akewo adzamuthawa usiku umene adzamangidwe, komabe sanakayikire zoti iwo anali okhulupirika. (Mateyu 26:31-35; Luka 22:28-30) Mwachitsanzo, Petulo anakana katatu zoti amamudziwa Yesu. Komabe, Yesu anapempherera Petulo ndipo anasonyeza kuti akudziwa kuti anali wokhulupirika. (Luka 22:31-34) Ndipo usiku womaliza atatsala pang’ono kupita kumwamba, pamene ankapemphera kwa Atate ake, Yesu sanatchule zinthu zimene ophunzira akewo ankalakwitsa. M’malomwake, ananena zinthu zabwino zimene iwo ankachita mpaka usiku umenewu. Yesu anati: “Iwo amvera mawu anu.” (Yohane 17:6) Ngakhale kuti ophunzirawo sanali angwiro, iye anawasiyira ntchito yolalikira za Ufumu wake komanso kuthandiza anthu kuti akhale ophunzira ake. (Mateyu 28:19, 20) Chifukwa chakuti Yesu anasonyeza kuti ankawadalira komanso kuwakhulupirira, n’zosakayikitsa kuti zimenezi zinawalimbikitsa kuti akwanitse kugwira ntchito imene iye anawalamula.

      19 Otsatira a Yesu ali ndi zifukwa zomveka zotsanzirira chitsanzo chakechi. Ngati Mwana wa Mulungu yemwe ndi wangwiro, anali woleza mtima pochita zinthu ndi ophunzira ake amene si angwiro, ndiye kuti ifenso omwe ndi anthu ochimwa, tiyenera kukhala oleza mtima pochita zinthu ndi anzathu. (Afilipi 4:5) M’malo momaganizira kwambiri zolakwa za Akhristu anzathu, tingachite bwino kumaona zabwino zimene amachita. Ndipo tizikumbukira kuti Yehova ndi amene anawakoka. (Yohane 6:44) Izitu zikusonyeza kuti Mulungu amaona zabwino zimene iwo amachita ndipo ifenso tizitengera chitsanzo chake. Zimenezi zingatithandize kuti ‘tizinyalanyaza zolakwa’ zawo komanso kuti tizifufuza zabwino zimene abale athuwo amachita n’kumawayamikira. (Miyambo 19:11) Tikamasonyeza kuti abale ndi alongo athu a Chikhristu timawadalira, zimawalimbikitsa kuti azitumikira Yehova ndipo amasangalala ndi utumiki wawo.​—1 Atesalonika 5:11.

      20. Kodi tiyenera kuchita chiyani ndi nzeru zakuya zopezeka m’Mauthenga Abwino, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezo?

      20 Munkhani za m’Mauthenga Abwino, zomwe zimafotokoza za moyo ndi utumiki wa Yesu, timapezamo nzeru zakuya. Kodi tizichita chiyani ndi nzeru zimenezi, zomwe ndi mphatso yamtengo wapatali? Pomaliza ulaliki wake wa paphiri, Yesu analimbikitsa anthu amene ankamvetsera mawu ake anzeruwo kuti azichita kapena kutsatira zimene amvazo, osati kungomvetsera chabe. (Mateyu 7:24-27) Maganizo athu, zolinga zathu komanso zochita zathu zikamagwirizana ndi mawu ndiponso zochita za Yesu zomwe ndi zanzeru, tidzakhala ndi moyo wabwino panopa ndipo tidzapitiriza kuyenda m’njira ya kumoyo wosatha. (Mateyu 7:13, 14) Ndithudi kuchita zimenezi ndi chinthu chabwino kwambiri komanso chanzeru kuposa chilichonse.

      a Nkhani imene Yesu anakamba tsiku limenelo ndi imene imadziwika kuti ulaliki wa paphiri. M’Baibulo, nkhaniyi ili pa Mateyu 5:3 mpaka 7:27, ndipo ili ndi mavesi 107. N’kutheka kuti Yesu anakamba nkhaniyi maminitsi pafupifupi 20 okha basi.

      b Zikuoneka kuti ‘kumwamba kutatseguka’ pa nthawi ya ubatizo wake, Yesu anakumbukira moyo umene anali nawo kumwambako asanabwere padziko lapansi.​—Mateyu 3:13-17.

      Kodi Mungatani Kuti Muzitsatira Yesu?

      • Kodi muyenera kuchita chiyani ngati mwazindikira kuti mwakhumudwitsa Mkhristu mnzanu?​—Mateyu 5:23, 24.

      • Kodi mawu anzeru a Yesu angakuthandizeni bwanji kuchita zinthu mwanzeru ngati ena akukhumudwitsani kapena kukunenerani mawu achipongwe?​—Mateyu 5:38-42.

      • Kodi kuganizira mozama mawu a Yesu kungakuthandizeni bwanji kuti muziona ndalama ndi chuma moyenera?​—Mateyu 6:24-34.

      • Kodi kutsatira chitsanzo cha Yesu kungakuthandizeni bwanji kuti muzisankha zinthu mwanzeru pa moyo wanu?​—Luka 4:43; Yohane 4:34

  • “Anaphunzira Kumvera”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • MUTU 6

      “Anaphunzira Kumvera”

      1, 2. N’chifukwa chiyani bambo wachikondi angasangalale kuona mwana wake akumumvera, ndipo kodi zimenezi zikusonyeza bwanji mmene Yehova amamvera?

      TAYEREKEZERANI kuti mukuona bambo akusuzumira pawindo n’kumaonerera mwana wake wamwamuna akusewera mpira ndi anzake. Kenako mpirawo ukugwera mumsewu. Koma mwanayo wangoima n’kumauyang’ana mwachidwi. Ndiyeno mnzake wina akumuuza kuti apite kukautola, koma iye akukana n’kunena kuti: “Bambo anga anandiletsa kusewera mumsewu.” Atamva zimenezi bambowo akumwetulira.

      2 N’chifukwa chiyani bambowo akusangalala? Chifukwa chakuti anamuuza mwana wawoyo kuti asamasewere mumsewu. Mwanayo wamvera malangizowo ngakhale kuti sakudziwa kuti bambo akewo akumuona. Bambowo akudziwa kuti mwana wawo akuphunzira kukhala womvera komanso kuti zimenezi zidzamuthandiza kwambiri. Mmene bambowo akumvera mumtima ndi mmenenso Yehova, Atate wathu wakumwamba amamvera. Mulungu akudziwa kuti tiyenera kumukhulupirira komanso kumumvera kuti tikhalebe okhulupirika ndiponso kuti tidzalandire madalitso amene watisungira m’tsogolo. (Miyambo 3:5, 6) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, iye anatitumizira mphunzitsi wabwino kwambiri kuposa munthu aliyense.

      3, 4. Kodi mfundo yakuti Yesu “anaphunzira kumvera” ndiponso ‘anakhala wangwiro’ ikutanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

      3 Baibulo limatchula mfundo inayake yosangalatsa yokhudza Yesu. Limati: “Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo. Ndipo atakhala wangwiro, anali ndi udindo wopulumutsa kwamuyaya anthu onse amene amamumvera.” (Aheberi 5:8, 9) Mwana woyamba kubadwayu anakhalapo kumwamba kwa zaka zambirimbiri ndipo anaona Satana komanso angelo ena akugalukira Mulungu koma iye sanagwirizane nawo. Ponena za iye, ulosi wouziridwa umati: “Ine sindinamupandukire.” (Yesaya 50:5) Ndiye ngati nthawi zonse Yesu amamvera Atate ake n’chifukwa chiyani tikunena kuti “anaphunzira kumvera”? Ngati Yesu anali kale wangwiro n’chifukwa chiyani tikunena kuti ‘anakhala wangwiro’ atabwera padzikoli?

      4 Kuti timvetse mfundoyi, tiyerekezere ndi mmisiri womanga nyumba amene akufuna kugula chipangizo chomangira. Iye wagula chipangizo chatsopano chabwino kwambiri. Koma kodi angadziwe bwanji ngati chipangizocho n’cholimba? Ngakhale kuti chipangizocho chikuoneka kuti n’chabwino kwambiri, mmisiriyo angadziwe kuti n’cholimbadi akayamba kuchigwiritsa ntchito kwambiri. N’chimodzimodzi ndi Yesu. Asanabwere padziko lapansi, ankamvera Yehova mokhulupirika. Koma atabwera padziko lapansili anali ndi mwayi woti asonyeze m’njira ina yapadera kuti ndi womvera kwambiri. Iye anakumana ndi mayesero amene sakanakumana nawo akanakhala kumwamba, koma anakhalabe womvera.

      5. N’chifukwa chiyani zinali zofunika kwambiri kuti Yesu azimvera Atate wake, nanga kodi m’mutu uno tikambirana chiyani?

      5 Yesu anafunikadi kukhala womvera kuti akwaniritse cholinga chimene anabwerera padziko lapansi. Monga “Adamu womalizira,” Yesu anabwera padziko lapansi kudzachita zimene kholo lathu loyamba linalephera kuchita. Iye anamvera Yehova Mulungu ngakhale pamene ankayesedwa. (1 Akorinto 15:45) Komabe sikuti Yesu ankangomvera mokakamizika. Iye ankamvera Mulungu ndi maganizo ake onse, mtima wake wonse komanso moyo wake wonse ndipo ankachita zimenezi mosangalala. Kwa iye, kuchita zimene Atate wake ankafuna chinali chinthu chofunika kwambiri kuposa chakudya. (Yohane 4:34) Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tikhale omvera ngati Yesu? Choyamba, tiyeni tione zifukwa zimene zinachititsa Yesu kuti akhale womvera. Ndipo tikakhala ndi zifukwa zofanana ndi za Yesu, tidzatha kupewa mayesero komanso tidzatha kuchita chifuniro cha Mulungu. Tionanso madalitso amene tingapeze tikakhala omvera ngati Khristu.

      N’chifukwa Chiyani Yesu Anali Womvera?

      6, 7. Kodi zina mwa zifukwa zimene zinachititsa kuti Yesu azimvera Yehova ndi ziti?

      6 Yesu anali womvera chifukwa choti anali ndi makhalidwe abwino. Monga mmene tinaonera m’mutu wachitatu, Yesu anali wodzichepetsa. Munthu akakhala wodzikuza safuna kumvera, koma akakhala wodzichepetsa amamvera Yehova ndi mtima wonse. (Ekisodo 5:1, 2; 1 Petulo 5:5, 6) Komanso zinthu zimene Yesu ankakonda ndiponso kudana nazo ndi zimene zinamuthandiza kuti akhale womvera.

      7 Chifukwa chachikulu n’chakuti Yesu ankakonda kwambiri Yehova, Atate wake wakumwamba. M’Mutu 13, tidzakambirana za chikondi chimenecho mwatsatanetsane. Chikondi chimenecho n’chimene chinachititsa Yesu kuti aziopa Mulungu. Iye ankaopa kuchita zinthu zimene zingakhumudwitse Yehova, chifukwa chakuti amamukonda komanso kumulemekeza kwambiri. Yesu amaopa Mulungu ndipo zimenezi zinachititsa kuti Mulungu azimva mapemphero ake. (Aheberi 5:7) Panopa Yesu akulamulira monga Mfumu komanso Mesiya ndipo amalamulira mosonyeza kuti amalemekeza Yehova kwambiri ndipo nthawi zonse amafuna kumusangalatsa.​—Yesaya 11:3.

      Abale awiri aima patsogolo pa posita imene ikunena za filimu yachiwawa. M’bale mmodzi akuyang’ana monyansidwa ndipo winayo wakweza dzanja n’kuyang’ana kumbali.

      Kodi zosangalatsa zimene mumakonda zimasonyeza kuti mumadana ndi zinthu zoipa?

      8, 9. Malinga n’kunena kwa ulosi, kodi Yesu ankaona bwanji chilungamo ndiponso zinthu zoipa, nanga anasonyeza bwanji zimenezo?

      8 Munthu amene amakonda Yehova ayeneranso kudana ndi zinthu zimene Yehova amadana nazo. Mwachitsanzo, taonani mawu aulosi otsatirawa okhudza Mesiya yemwenso ndi Mfumu. Mawu ake ndi akuti: “Unkakonda chilungamo ndipo unkadana ndi zoipa. N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, wakudzoza ndi mafuta achisangalalo chachikulu kuposa mafumu anzako.” (Salimo 45:7) “Mafumu” ena amene akutchulidwa pa lembali anali ochokera m’banja lachifumu la Mfumu Davide. Pa nthawi imene anadzozedwa, Yesu anali ndi zifukwa zambiri zimene zinamuchititsa kuti asangalale kapena kukondwera kuposa mafumu onsewo. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mphoto imene analandira inali yaikulu kuposa mafumu enawo ndipo ufumu wakewo udzabweretsa madalitso ambiri. Yesu analandira mphoto chifukwa chakuti ankamvera Mulungu pa chilichonse. Iye ankamvera Mulungu chifukwa ankakonda chilungamo komanso ankadana ndi zinthu zoipa.

      9 Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda chilungamo ndiponso amadana ndi zoipa? Mwachitsanzo, kodi Yesu anatani otsatira ake atadalitsidwa chifukwa chomvera malangizo ake pa ntchito yolalikira? Iye anasangalala kwambiri. (Luka 10:1, 17, 21) Nanga Yesu anamva bwanji pamene anthu a ku Yerusalemu anasonyeza mobwerezabwereza mtima wosamvera n’kukana zimene iye ankachita pofuna kuwathandiza? Analira chifukwa cha kusamvera kwa anthuwo. (Luka 19:41, 42) Yesu ankakhudzidwa kwambiri ndi zinthu zabwino komanso zoipa zimene anthu ankachita.

      10. Kodi timafunika kukhala ndi mtima wotani pa nkhani yokhudza zinthu zabwino ndiponso zoipa, nanga n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezo?

      10 Tikamaganizira mozama mmene Yesu ankaonera zinthu, zingatithandize kuonanso zimene zimachititsa kuti ifeyo tizimvera Yehova. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, n’zotheka kuti tizikonda kwambiri zinthu zabwino n’kumadana kwambiri ndi makhalidwe oipa. Tiyenera kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kuona zinthu mmene iye ndiponso Mwana wake amaonera. (Salimo 51:10) Komanso tiyenera kupewa zinthu zimene zingatilepheretse kuona zinthu mmene Yehova ndi Mwana wake amazionera. N’zofunika kuti tizisamala kwambiri posankha zinthu zimene timasangalala nazo komanso anthu ocheza nawo. (Miyambo 13:20; Afilipi 4:8) Tikakhala ndi mtima womvera ngati wa Khristu, ndiye kuti sitidzakhala omvera n’cholinga choti anthu atione. Tidzachita zinthu zoyenera chifukwa chakuti timakonda kuchita zinthuzo. Tidzapewa kuchita zinthu zoipa, osati chifukwa choopa kugwidwa, koma chifukwa choti timadana ndi zoipazo.

      “Iye Sanachite Tchimo”

      11, 12. (a) Kodi n’chiyani chinachitikira Yesu atangoyamba kumene utumiki wake? (b) Kodi poyamba Satana anamuyesa bwanji Yesu, nanga ndi njira ziti zaukathyali zimene anagwiritsa ntchito?

      11 Yesu atangoyamba kumene utumiki wake anayesedwa ndipo anasonyeza kuti amadana ndi tchimo. Yesu atabatizidwa anakhala m’chipululu osadya kwa masiku 40, masana ndi usiku. Masiku 40 amenewo atatha Satana anabwera kudzamuyesa. Taonani mmene Mdyerekezi ananenera zinthu mwaukathyali.​—Mateyu 4:1-11.

      12 Choyamba Satana ananena kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.” (Mateyu 4:3) Kodi Yesu anamva bwanji atasala kudya nthawi yaitali? Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Anamva njala.” (Mateyu 4:2) Choncho Satana anapezerapo mwayi ndipo mosakayikira anayembekezera mpaka Yesu atafooka ndi njala. Onaninso mawu a mtopola amene Satana ananena. Iye anati: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu.” Satana ananena zimenezi ngakhale kuti ankadziwa zoti Yesu ndi “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Komabe, Yesu sanalole kuti Satana amuchititse kuti asamvere Mulungu. Yesu ankadziwa kuti si cholinga cha Mulungu kuti iye agwiritse ntchito mphamvu zake ndi zolinga zolakwika. Iye anakana kuchita zofuna za Satana ndipo anasonyeza kuti ankadalira kwambiri Yehova kuti amupatse chakudya komanso kumutsogolera.​—Mateyu 4:4.

      13-15. (a) Kodi Satana anamuyesa bwanji Yesu kachiwiri ndi kachitatu, nanga Yesu anachita chiyani? (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu ankakhala tcheru nthawi zonse polimbana ndi Satana?

      13 Pamene Satana ankayesa Yesu kachiwiri, anamutenga n’kupita naye pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi. Mochenjera kwambiri, Satana anapotoza Mawu a Mulungu poyesa Yesu kuti achite zinthu modzionetsera. Iye anamuuza kuti adziponye pansi kuti angelo amupulumutse. Gulu la anthu amene anali pakachisipo akanaona zodabwitsazo, kodi pakanapezeka aliyense wokayikira zoti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa? Ngati anthuwo akanavomereza kuti iye ndi Mesiya chifukwa cha zodabwitsazo, kodi zimenezi sizikanachititsa kuti Yesu asakumane ndi mavuto ambiri? Mwina zikanaterodi. Koma Yesu ankadziwa kuti Yehova akufuna kuti Mesiya agwire ntchito yake modzichepetsa, osati kuchita zinthu zodabwitsa modzionetsera kuti anthu amukhulupirire. (Yesaya 42:1, 2) Choncho Yesu anakananso kuchita zinthu zosonyeza kusamvera Yehova ndipo sanakodwe ndi msampha wofuna kutchuka.

      14 Koma kodi Yesu anakodwa ndi msampha woti akhale wolamulira? Pamene ankamuyesa kachitatu, Satana anauza Yesu kuti amupatsa maufumu onse a padziko lapansi ngati atamulambira kamodzi kokha. Kodi iye anayamba waganizira kaye zimene Satana anamuuzazo? Ayi, chifukwa nthawi yomweyo anamuyankha kuti: “Choka Satana! Chifukwa Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’” (Mateyu 4:10) Palibe chimene chikanakopa Yesu kuti alambire mulungu wina, n’kuchita zinthu zosonyeza kusamvera Yehova chifukwa chofuna kukhala wolamulira kapena wotchuka m’dzikoli.

      15 Kodi Satana analekera pomwepo? N’zoona kuti Yesu atamulamula kuti achoke, anachokadi. Koma Uthenga Wabwino wa Luka umanena kuti Mdyerekezi “anamusiya mpaka nthawi ina yabwino.” (Luka 4:13) Ndithudi, pa nthawi yonse imene Yesu anali padziko lapansi, Satana anapitiriza kumuyesa pa mpata uliwonse umene anapeza. Baibulo limanena kuti Yesu “anayesedwa pa zinthu zonse.” (Aheberi 4:15) Izi zikusonyeza kuti Yesu ankakhala tcheru nthawi zonse ndipo ifenso tizichita chimodzimodzi.

      16. Kodi Satana amayesa bwanji atumiki a Mulungu masiku ano, nanga tingapewe bwanji misampha yake?

      16 Masiku ano Satana akupitiriza kuyesa atumiki a Mulungu. N’zomvetsa chisoni kuti iye amatipezerera chifukwa chakuti si ife angwiro. Mwachibadwa, anthufe timakhala ndi mtima wodzikonda, wodzikuza ndiponso wofuna kulamulira ena ndipo Satana amapezerapo mwayi n’kumatiyesa. Iye angagwiritse ntchito makhalidwe onsewa nthawi imodzi kuti atikole mumsampha wokonda chuma. Choncho m’pofunika kuti nthawi ndi nthawi tizidzifufuza moona mtima. Tiyenera kumaganizira mozama mawu opezeka pa 1 Yohane 2:15-17. Tikamachita zimenezi, tingachite bwino kudzifufuza kuti tione ngati kufuna kuchita zinthu za m’dzikoli, kufunitsitsa kukhala ndi chuma, kapena kufunitsitsa kuchita zinthu zogometsa anthu, zikuchititsa kuti tisiye kukonda kwambiri Atate wathu wakumwamba. Tizikumbukira kuti dzikoli likupita limodzi ndi Satana amene ndi wolamulira wake. Choncho tisalole kuti atikope kuti tichite tchimo. Tiyeni tizitsanzira Ambuye wathu amene “sanachite tchimo.”​—1 Petulo 2:22.

      “Ndimachita Zinthu Zimene Zimamusangalatsa Nthawi Zonse”

      17. Kodi Yesu ankaona bwanji nkhani yomvera Atate ake, nanga anthu ena anganene kuti chiyani?

      17 Pali zambiri zimene munthu ayenera kuchita posonyeza kuti ndi womvera osati kungopewa tchimo lokha. Mwachitsanzo, Khristu ankachita ndi mtima wonse zinthu zonse zimene Atate ake ankamulamula. Iye anati: “Ndimachita zinthu zimene zimamusangalatsa nthawi zonse.” (Yohane 8:29) Yesu ankakhala wosangalala kwambiri chifukwa choti anali womvera. Anthu ena anganene kuti zinali zosavuta kuti Yesu asonyeze kuti ndi womvera tikayerekezera ndi ife. Iwo anganene kuti Yesu ankangofunikira kumvera Yehova yekha, yemwe ndi wangwiro, pamene anthufe timafunikira kumvera anthu anzathu omwe si angwiro amene ali ndi udindo. Koma zoona zake n’zakuti Yesu ankamveranso anthu omwe si angwiro amene anali ndi maudindo.

      18. Pamene anali wachinyamata, kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yomvera?

      18 Yesu anakulira m’banja la Yosefe ndi Mariya, amene anali makolo omwe si angwiro. Ndipo kuposa mwana aliyense, iye ankaona kwambiri zimene makolo akewo ankalakwitsa. Kodi iye anasiya kumvera makolo akewo n’kuyamba kuwalangiza mmene angayendetsere banjalo? Taonani zimene lemba la Luka 2:51 limanena zokhudza Yesu ali ndi zaka 12. Lembali limati: “Anapitiriza kuwamvera.” Pamenepa Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwa achinyamata a Chikhristu, amene amayesetsa kumvera makolo awo ndiponso kuwalemekeza.​—Aefeso 6:1, 2.

      19, 20. (a) Kodi Yesu anakumana ndi mavuto otani pa nkhani yomvera anthu omwe si angwiro? (b) N’chifukwa chiyani Akhristu masiku ano ayenera kumvera anthu amene akuwatsogolera?

      19 Pa nkhani yomvera anthu omwe si angwiro, Yesu anakumana ndi mavuto amene Akhristu oona masiku ano sangakumane nawo. Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Kwa nthawi yaitali, Yehova ankasangalala ndi chipembedzo cha Ayuda. Iwo anali ndi kachisi ku Yerusalemu ndipo ansembe ankatumikira m’kachisimo. Koma tsopano Yehova anali atatsala pang’ono kuchotsa chipembedzo chimenecho kuti akhazikitse mpingo wa Chikhristu. (Mateyu 23:33-38) Pa nthawiyi atsogoleri ambiri achipembedzo ankaphunzitsa zinthu zabodza zimene Agiriki ankakhulupirira. Anthu ankachita zinthu zambiri zachinyengo m’kachisi moti Yesu anatchula kachisiyo kuti ndi “phanga la achifwamba.” (Maliko 11:17) Kodi Yesu anasiya kupita kukachisiko ndi kumasunagoge? Ayi, chifukwa chakuti Yehova ankagwiritsabe ntchito zinthu zimenezo. Yesu anasonyeza kuti ndi womvera ndipo ankapitabe ku zikondwerero za kukachisi komanso ankapita kusunagoge mpaka pamene Mulungu anasintha zinthu.​—Luka 4:16; Yohane 5:1.

      20 Popeza kuti Yesu anakhalabe womvera ngakhale kuti zinthu zinali choncho, nawonso Akhristu oona masiku ano ayenera kukhala omvera. Ndipotu zinthu masiku ano n’zosiyana ndi mmene zinalili m’nthawi ya Yesu. Mogwirizana ndi ulosi, ife tikukhala m’nthawi imene kulambira koyera kwabwezeretsedwa. Mulungu akutilonjeza kuti sadzalola kuti Satana asokoneze anthu amene akumulambira m’njira yovomerezeka. (Yesaya 2:1, 2; 54:17) N’zoona kuti mumpingo wa Chikhristu nthawi zina anthu amachimwa komanso kuchita zinthu zosayenera chifukwa choti si angwiro. Koma kodi tizisiya kumvera Yehova, mwina mpaka kusiya kupita kumisonkhano ya Chikhristu kapena kuyamba kunyoza akulu chifukwa cha zolakwa za anthu ena? Ayi ndithu. M’malomwake, timamvera ndi mtima wonse abale amene akutitsogolera mumpingo. Timasonyeza kuti ndife omvera tikamapita kumisonkhano ya Chikhristu ndiponso tikamagwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba zimene timaphunzira kumisonkhanoko.​—Aheberi 10:24, 25; 13:17.

      Abale ndi alongo akucheza mosangalala panja pa Nyumba ya Ufumu.

      Timasonyeza kumvera tikamagwiritsa ntchito zimene timaphunzira kumisonkhano ya Chikhristu

      21. Kodi Yesu anatani anthu atamulimbikitsa kuti achite zinthu zosonyeza kusamvera Mulungu, ndipo anatipatsa chitsanzo chotani?

      21 Yesu sanalole anthu ena, ngakhale anzake amene anali ndi zolinga zabwino, kuti amulepheretse kumvera Yehova. Mwachitsanzo, mtumwi Petulo anayesa kulimbikitsa Ambuye wake kuti asalole kuti avutike ndiponso kufa. Ngakhale kuti Petulo anali ndi zolinga zabwino pamene ankalankhula zimenezi, Yesu anakana malangizo olakwika akuti adzikomere mtima. (Mateyu 16:21-23) Masiku ano, otsatira a Yesu kawirikawiri amapewa kukopedwa ndi achibale amene akuwalimbikitsa kuti asiye kumvera malamulo ndi mfundo za Mulungu. Mofanana ndi otsatira a Yesu oyambirira, ifenso timatsatira mfundo yakuti “tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Machitidwe 5:29.

      Tikakhala Omvera Ngati Khristu Tidzapeza Madalitso

      22. Kodi Yesu anapereka yankho la funso liti, nanga analipereka bwanji?

      22 Sizinali zophweka kuti Yesu akhalebe womvera pamene anamugwira kuti akamuphe. Koma pa tsiku lovutali, “anaphunzira kumvera” kwambiri. Iye anachita zimene Atate wake ankafuna osati zofuna zake. (Luka 22:42) Pochita zimenezi, anasonyeza mwapadera kwambiri kuti n’zotheka kutumikira Mulungu mokhulupirika. (1 Timoteyo 3:16) Iye anapereka yankho la funso limene lakhalapo kwa nthawi yaitali lakuti: Kodi munthu wangwiro angakhalebe womvera kwa Yehova ngakhale pamene akuyesedwa? Adamu ndi Hava analephera kukhalabe omvera. Koma kenako Yesu anabwera ndipo anasonyeza kuti n’zotheka munthu kukhalabe wokhulupirika mpaka imfa. Mwana wa Mulungu, yemwe ndi munthu wapamwamba kwambiri kuposa zolengedwa zonse za Yehova, anapereka yankho lamphamvu kwambiri. Iye anakhalabe womvera ngakhale kuti anavutika mpaka imfa.

      23-25. (a) Kodi kumvera n’kogwirizana bwanji ndi kukhala wokhulupirika? Perekani chitsanzo. (b) Kodi m’mutu wotsatira tikambirana chiyani?

      23 Tikakhala omvera timasonyeza kuti ndife odzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse ndiponso kuti tikumutumikira mokhulupirika. Chifukwa chokhalabe womvera, Yesu anasonyeza kuti amatumikira Mulungu mokhulupirika ndipo zimenezi zinathandiza anthu onse. (Aroma 5:19) Yehova anadalitsa kwambiri Yesu ndipo ifenso adzatidalitsa tikamamvera Khristu, Ambuye wathu. Tikamamvera Khristu ‘tidzapulumutsidwa kwamuyaya.’​—Aheberi 5:9.

      24 Kuwonjezera pamenepo, anthu amene amatumikira Mulungu mokhulupirika amadalitsidwa. Lemba la Miyambo 10:9 limati: “Munthu wochita zinthu mokhulupirika adzakhala wotetezeka.” Kukhala wokhulupirika tingakuyerekezere ndi nyumba yaikulu imene anaimanga ndi njerwa ndipo chilichonse chimene tachita posonyeza kuti ndife omvera tingachiyerekezere ndi njerwa imodzi. Njerwa imodzi ingaoneke ngati yopanda ntchito, koma kwenikweni njerwa iliyonse ndi yofunika. Ndipo tikasanja njerwa zambirimbiri pomanga nyumba, pamapeto pake imakhala nyumba yokongola kwambiri. N’chimodzimodzinso ndi kutumikira Mulungu mokhulupirika. Tikamachita zinthu zosiyanasiyana zosonyeza kumvera tsiku ndi tsiku komanso chaka ndi chaka, zinthu zonsezo kuziphatikiza pamodzi zimatithandiza kuti tikhale anthu okhulupirika.

      25 Munthu akakhala womvera kwa nthawi yaitali ndiye kuti ali ndi khalidwe lina labwino lomwe ndi kupirira. M’mutu wotsatira tikambirana mmene Yesu anasonyezera khalidwe limeneli.

      Kodi Mungatani Kuti Muzitsatira Yesu?

      • Kodi ena mwa malamulo a Khristu ndi ati ndipo tingawatsatire bwanji, nanga tingapeze madalitso otani?​—Yohane 15:8-19.

      • Yesu atangoyamba kumene utumiki wake, kodi abale ake ankauona bwanji utumiki wakewo, nanga tingaphunzire chiyani tikaona mmene Yesu anawathandizira?​—Maliko 3:21, 31-35.

      • N’chifukwa chiyani sitiyenera kuda nkhawa kuti tidzakhala osasangalala pa moyo wathu tikamamvera Yehova?​—Luka 11:27, 28.

      • Kodi tikuphunzira chiyani pa mtima wa Yesu wofunitsitsa kumvera lamulo limene kwenikweni silinkagwira ntchito kwa iye?​—Mateyu 17:24-27.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena