Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Anagwidwa ndi Chifundo”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • MUTU 15

      ‘Anagwidwa ndi Chifundo’

      Yesu akuchiritsa anthu awiri osaona.

      “Ambuye, tithandizeni kuti tiyambe kuona”

      1-3. (a) Kodi Yesu anachita chiyani opemphetsa awiri amene anali ndi vuto losaona atamupempha kuti awathandize? (b) Kodi mawu akuti “atagwidwa ndi chifundo” akutanthauza chiyani? (Onani mawu am’munsi.)

      ANTHU awiri amene anali ndi vuto losaona anali m’mphepete mwa msewu pafupi ndi mzinda wa Yeriko. Tsiku lililonse ankabwera pamalowo ndipo ankakhala pamalo abwino pamene ankadziwa kuti pamadutsa anthu ambiri n’kumapempha ndalama. Koma tsiku lina anakumana ndi zinthu zina zimene zinasintha kwambiri moyo wawo.

      2 Mwadzidzidzi, opemphetsawo anamva phokoso la anthu. Popeza kuti anali osaona, sankadziwa chimene chinkachitika ndipo mmodzi wa iwo anafunsa kuti adziwe. Iye anauzidwa kuti: “Yesu Mnazareti akudutsa!” Yesu anali pa ulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu ndipo gulu la anthu linkamutsatira. Anthu opemphetsawo atamva kuti Yesu akudutsa, anayamba kufuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” Gulu la anthulo linakwiya ndipo linawauza kuti akhale chete, koma sanamvere chifukwa iwo ankafunitsitsa kuti awathandize.

      3 Yesu anamva kufuula kwawo ngakhale kuti gulu la anthulo linkasokosa kwambiri. Ndiye kodi iye anatani? Pa nthawiyi, anali ndi zinthu zambiri zimene zinkamudetsa nkhawa mumtima mwake. Panali patangotsala mlungu umodzi wokha kuti aphedwe ndipo ankadziwa kuti posachedwa, azunzidwa komanso kuphedwa mwankhanza ku Yerusalemu. Komabe, iye sananyalanyaze anthu osaona omwe ankafuulawo. Choncho, iye anaima n’kulamula kuti anthu osaonawo awabweretse kwa iye. Iwo anamupempha kuti: “Ambuye, tithandizeni kuti tiyambe kuona.” Yesu “atagwidwa ndi chifundo,” anagwira maso awo ndipo anayamba kuona.a Nthawi yomweyo, iwo anayamba kumutsatira.​—Luka 18:35-43; Mateyu 20:29-34.

      4. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi wakuti iye “adzamvera chisoni munthu wonyozeka”?

      4 Si nthawi yokhayi imene Yesu anachitira ena chifundo. Iye anasonyeza kambirimbiri ndiponso nthawi zosiyanasiyana kuti wagwidwa ndi chifundo ndipo ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu. Ulosi wa m’Baibulo umati iye “adzamvera chisoni munthu wonyozeka.” (Salimo 72:13) Mogwirizana ndi mawu amenewa, Yesu ankazindikira mwamsanga mavuto a anthu ndipo sankadikira kuti achite kumupempha kuti awathandize. Chifundo ndi chimene chinkamuchititsa kuti azilalikira. Tsopano tiyeni tione mmene mabuku a Uthenga Wabwino amasonyezera kuti Yesu anali wachifundo. Tiona zimenezi kuchokera pa zimene ankalankhula komanso kuchita. Tionanso mmene ifeyo tingasonyezere chifundo ngati mmene Yesu anachitira.

      Yesu Ankamvera Chisoni Anthu Ena

      5, 6. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yesu anali munthu wachifundo?

      5 Yesu ankamva chisoni kwambiri akaona anthu akuvutika. Iye ankamvetsa mmene anthu ovutikawo akumvera ndipo ankawamvera chisoni. Ngakhale kuti iye anali asanakumanepo ndi mavuto ngati amenewo, zinkamukhudza kwambiri moti ankamva ululu ngati mmene anthuwo ankamvera. (Aheberi 4:15) Mwachitsanzo, pamene ankachiritsa mayi amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, Yesu anafotokoza kuti ‘matendawo anali aakulu.’ Zimenezi zikusonyeza kuti iye ankadziwa kuti mayiwo akuvutika kwambiri. (Maliko 5:25-34) Ataona Mariya ndi anthu ena akulira chifukwa cha imfa ya Lazaro, anakhudzidwa kwambiri ndi chisoni chawo ndipo anavutika kwambiri mumtima mwake. Ngakhale ankadziwa kuti watsala pang’ono kuukitsa Lazaro, Yesu anamva chisoni kwambiri mpaka anagwetsa misozi.​—Yohane 11:33, 35.

      6 Pa nthawi ina, munthu wakhate anapita kwa Yesu n’kumudandaulira kuti: “Ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.” Kodi Yesu, amene anali munthu wangwiro yemwe sanadwalepo, anatani? Anamumvera chisoni kwambiri munthu wakhateyo, ndipo mpake kuti Baibulo limanena kuti, “anagwidwa chifundo.” (Maliko 1:40-42) Kenako anachita chinthu chodabwitsa kwambiri. Iye ankadziwa bwino kuti mogwirizana ndi Chilamulo, anthu akhate anali odetsedwa ndipo sankayenera kukhala pafupi ndi anthu ena. (Levitiko 13:45, 46) Yesu akanatha kuchiritsa munthuyo ngakhale osamukhudza. (Mateyu 8:5-13) Koma iye anasankha kukhudza munthu wakhateyo ndi kumuuza kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.” Nthawi yomweyo, khatelo linatheratu. Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti ndi munthu wachifundo kwambiri.

      Mlongo akulimbikitsa mlongo mnzake.

      “Muzimverana chisoni”

      7. N’chiyani chingatithandize kuti tizimvera ena chisoni, nanga tingasonyeze bwanji zimenezi?

      7 Monga Akhristu tikulimbikitsidwa kuti tizimvera ena chifundo ngati mmene Yesu ankachitira. Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tizimverana chisoni.’b (1 Petulo 3:8) Zingakhale zovuta kuti timvetse mavuto ndiponso ululu wa anthu amene akudwala matenda aakulu kapena amene akuvutika maganizo, makamaka ngati ifeyo sitinakumanepo ndi mavuto ngati amenewo. Koma kumbukirani kuti sizidalira kuti tikumane ndi mavuto amene mnzathu akukumana nawo kuti timvetse mmene akuvutikira. Mwachitsanzo, Yesu ankamvetsa mmene odwala akuvutikira ngakhale kuti iyeyo sanadwalepo. Nanga tingatani kuti tizimvetsa mavuto amene anthu akukumana nawo? Anthu amene akuvutikawo akamatiuza mavuto awo tizimvetsera modekha ndiponso tiziyerekezera kuti nafenso tili ndi mavuto ngati awowo. Tingachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndikanamva bwanji ndikanakhala kuti ndakumana ndi mavuto ngati amenewa?’ (1 Akorinto 12:26) Ena akamavutika, tiziyesetsa kuwamvera chisoni mwamsanga, tikatero tidzatha ‘kulankhula molimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa.’ (1 Atesalonika 5:14) Nthawi zina tingagwetse misozi posonyeza kuti tili ndi chisoni chifukwa cha mavuto amene mnzathu akukumana nawo, osati kungomuuza kuti nafenso zatikhudza. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Muzilira ndi anthu amene akulira.”​—Aroma 12:15.

      8, 9. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amaganizira ena?

      8 Yesu anali wokoma mtima ndipo akamachita zinthu ankaganizira mavuto amene anthu ankakumana nawo. Mwachitsanzo, kumbukirani nthawi imene anthu anamubweretsera munthu amene anali ndi vuto losamva komanso losalankhula. Mwina ataona kuti munthuyo akuchita manyazi, Yesu anachita chinthu chapadera chimene sanachite pamene ankachiritsa anthu ena. Iye “anatenga munthuyo n’kuchoka naye pagulu la anthulo kupita naye pambali.” Kenako anamuchiritsa popanda anthu oonerera.​—Maliko 7:31-35.

      9 Yesu anachitanso zinthu zosonyeza kuganizira ena pamene anthu anamubweretsera munthu amene anali ndi vuto losaona n’kumupempha kuti amuchiritse. Iye “anagwira dzanja la munthu wosaonayo, n’kupita naye kunja kwa mudzi,” ndipo kumeneko anamuchiritsa mwapang’onopang’ono. Mwina zimenezi zinathandiza munthuyu kuti azolowere pang’onopang’ono kuona kuwala ndi zinthu zosiyanasiyana zimene anali asanazionepo. (Maliko 8:22-26) Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti amaganizira kwambiri anthu ena.

      10. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhudzidwa ndi mmene ena akumvera?

      10 Popeza ndife otsatira a Yesu, tizisonyeza kuti timakhudzidwa ndi mmene ena akumvera. Choncho tiyenera kusamala ndi zimene timalankhula, chifukwa tikudziwa kuti kulankhula mosaganiza bwino kumakhumudwitsa ena. (Miyambo 12:18; 18:21) Akhristu amene amaganizira ena amapeweratu kulankhula mawu a mwano, onyoza ndiponso okhadzula. (Aefeso 4:31) Akulu, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhudzidwa ndi mmene ena akumvera? Mukamapereka malangizo, muzilankhula mokoma mtima kuti anthuwo aone kuti mumawalemekeza. (Agalatiya 6:1) Makolo, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhudzidwa ndi mmene ana anu amamvera? Mukamalangiza ana anu kapena kuwapatsa chilango, muziyesetsa kuchita zimenezi m’njira yoti musawachititse manyazi.​—Akolose 3:21.

      Yesu Ankathandiza Anthu Ngakhale Asanamupemphe

      11, 12. Kodi ndi nkhani ziti za m’Baibulo zimene zikusonyeza kuti Yesu sankadikira kupemphedwa kuti athandize anthu?

      11 Sikuti nthawi zonse Yesu ankadikira kuti anthu amupemphe kuti awachitire chifundo. Ndipotu munthu wachifundo amathandiza anthu mwa kufuna kwake ndipo sadikira kuti achite kupemphedwa. Choncho, n’zosadabwitsa kuti Yesu ankathandiza ena chifukwa anali wachifundo. Mwachitsanzo, gulu la anthu litakhala naye masiku atatu osadya, Yesu sanadikire kuti wina achite kumuuza kuti anthuwo ali ndi njala, kapena kumupempha kuti awathandize. Nkhaniyi imati: “Yesu anaitana ophunzira ake n’kuwauza kuti: ‘Gulu la anthuli likundimvetsa chisoni, chifukwa anthuwa akhala ndi ine kwa masiku atatu ndipo alibe chakudya. Sindikufuna kuwauza kuti azipita ndi njala chifukwa angalenguke panjira.’” Kenako mwa kufuna kwake, Yesu anadyetsa gulu la anthulo mozizwitsa.​—Mateyu 15:32-38.

      12 Tiyeni tione nkhani ina imene inachitika mu 31 C.E. Yesu ali pafupi ndi mzinda wa Naini, anakumana ndi anthu akulira. Anthuwo ankatuluka mumzindawo atanyamula maliro a ‘mwana wamwamuna yekhayo wa mkazi wa masiye,’ ndipo mwina ankapita kumanda apafupi amene anali m’mbali mwa phiri. N’zodziwikiratu kuti mayiyo anali ndi chisoni kwambiri mumtima mwake. Iye ankapita kukaika maliro a mwana wake wamwamuna yekhayo, ndipo analibe mwamuna amene akanamuthandiza kulira. Pagulu la anthu lonselo, Yesu ‘anaona mayiwo,’ amene tsopano anali mkazi wamasiye ndiponso wopanda mwana. Zimene anaonazo zinamukhudza kwambiri ndipo ‘anawamvera chisoni’ mayiwo. Palibe amene anapempha Yesu kuti athandize mayiwo, koma anawathandiza chifukwa cha chifundo chake. Choncho, “anayandikira n’kugwira chithathacho” ndipo anaukitsa mnyamatayo. Kodi kenako chinachitika n’chiyani? Yesu sanauze mnyamatayo kuti akhale m’gulu la anthu amene ankamutsatira koma “anamupereka kwa mayi ake.” Iye anachita zimenezi pofuna kuonetsetsa kuti pakhale munthu wosamalira mkazi wamasiyeyo.​—Luka 7:11-15.

      Mlongo wachitsikana akuthandiza mlongo wachikulire kudzala maluwa.

      Muzithandiza anthu amene akufunikira thandizo ngakhale asanakupempheni

      13. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu, amene sankadikira kuti anthu achite kumupempha kuti awathandize?

      13 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu? N’zoona kuti sitingadyetse anthu mozizwitsa kapena kuukitsa akufa. Komabe, tingatsanzire Yesu pothandiza anthu amene akuvutika ngakhale kuti sanatipemphe. Mwachitsanzo, Mkhristu mnzathu angakhale ndi vuto lalikulu la zachuma kapena ntchito ingamuthere. (1 Yohane 3:17) Komanso nyumba ya mkazi wamasiye ingafunike kukonzedwa mwamsanga. (Yakobo 1:27) Mwinanso tingadziwe banja limene laferedwa ndipo likufunika kulimbikitsidwa kapena kuthandizidwa m’njira ina yake. (1 Atesalonika 5:11) Tikaona anthu ena amene akufunikiradi kuthandizidwa, tisamadikire kuti achite kutipempha kuti tiwathandize. (Miyambo 3:27) Chifundo chidzatichititsa kuti tiwathandize ngati tingakwanitse kutero. Tisaiwale kuti zinthu zochepa zimene tingachite mokoma mtima kapena mawu olimbikitsa amene tingalankhule kuchokera pansi pa mtima angasonyeze kuti ndife achifundo.​—Akolose 3:12.

      Chifundo Chinkachititsa Kuti Yesu Azilalikira

      14. N’chifukwa chiyani Yesu ankaona kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi yofunika kwambiri?

      14 Monga mmene taonera m’gawo lachiwiri la buku lino, Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yolalikira uthenga wabwino. Iye anati: “Ndikuyenera kukalengezanso uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda ina, chifukwa ndi zimene Mulungu anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) N’chifukwa chiyani ankaona kuti ntchito imeneyi ndi yofunika kwambiri? Chifukwa chachikulu n’chakuti amakonda Mulungu. Koma panalinso chifukwa china: Chifundo chimene Yesu anali nacho chinamuchititsa kuona kuti anthu ena anali ndi njala yauzimu ndipo anawathandiza. Pa njira zonse zimene iye anasonyezera chifundo, panalibe njira yofunika kwambiri kuposa kuthetsa njala yauzimu ya anthu ena. Tiyeni tione zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene Yesu ankaonera anthu amene ankawalalikira. Kuchita zimenezi kutithandiza kuti tionenso bwino zifukwa zimene zimatichititsa kugwira nawo ntchito yolalikira.

      15, 16. Fotokozani zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene Yesu ankaonera anthu amene ankawalalikira.

      15 Mu 31 C.E., patatha zaka pafupifupi ziwiri akuchita mwakhama utumiki wake, Yesu anawonjezera utumikiwu poyamba “ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse” ya ku Galileya. Zimene anaona zinamukhudza kwambiri. Mtumwi Mateyu anafotokoza kuti: “Ataona chigulu cha anthu, iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” (Mateyu 9:35, 36) Yesu ankamvera chisoni anthu wamba ndipo ankadziwa bwino kwambiri kuti sankasamalidwa mwauzimu. Yesu ankadziwanso kuti atsogoleri achipembedzo, amene anayenera kuweta anthuwa, sankawasamalira n’komwe koma ankangowazunza. Choncho Yesu anagwidwa ndi chifundo ndipo ankayesetsa mwakhama kuti alalikire anthuwo uthenga wopatsa chiyembekezo. Panalibe chinthu chabwino chimene anthuwo ankafunikira kuposa kumva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

      16 Zinthu zina zofanana ndi zimenezi zinachitika patapita miyezi ingapo, mu 32 C.E., nthawi ya Pasika itatsala pang’ono kufika. Pa nthawiyi, Yesu ndi atumwi ake anakwera ngalawa kupita tsidya lina la nyanja ya Galileya kuti akapume kwaokha. Koma gulu la anthu linathamanga m’mbali mwa nyanja ndipo linakafika ngalawa ija isanafike. Kodi Yesu ataona anthuwo anachita chiyani? Nkhaniyi imati: “Atatsika anaona gulu lalikulu la anthu ndipo anawamvera chisoni, chifukwa anali ngati nkhosa zimene zilibe m’busa. Ndiye anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:31-34) Apanso Yesu “anawamvera chisoni” poona kuti anali ndi njala yauzimu. Mofanana ndi “nkhosa zimene zilibe m’busa,” anthuwo anali ndi njala yauzimu chifukwa atsogoleri achipembedzo anangowasiya kuti azizisamalira okha. Yesu sankangolalikira kuti akwaniritse udindo wake, koma ankalalikira chifukwa chakuti anali wachifundo.

      Mlongo akulankhula mwachifundo ndi mzimayi amene wakumana naye mu utumiki.

      Muzisonyeza chifundo mukamalalikira

      17, 18. (a) N’chiyani chimatichititsa kuti tizigwira nawo ntchito yolalikira? (b) Kodi tingatani kuti tizimvera ena chifundo?

      17 Popeza ndife otsatira a Yesu, kodi n’chiyani chimene chimatichititsa kugwira nawo ntchito yolalikira? Monga mmene tinaonera m’Mutu 9 wa buku lino, tinapatsidwa ntchito yolalikira komanso kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira a Yesu. (Mateyu 28:19, 20; 1 Akorinto 9:16) Koma tisamagwire ntchito imeneyi pofuna kungokwaniritsa udindo umene tapatsidwa. Chofunika kwambiri n’chakuti tizigwira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu chifukwa choti timakonda Yehova. Timalalikiranso chifukwa timachitira chifundo anthu amene sadziwa zimene ife timakhulupirira. (Maliko 12:28-31) Choncho, kodi tingatani kuti tizimvera ena chifundo?

      18 Tiziona anthu ngati mmene Yesu ankawaonera. Iye ankawaona kuti anali “onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe m’busa.” Mwachitsanzo, yerekezerani kuti mwapeza kamwana kankhosa katasochera. Kamwana kankhosako kali ndi njala komanso ludzu chifukwa palibe m’busa woti akatsogolere kumene kuli msipu ndi madzi. Kodi simungakamvere chisoni? Kodi simungayesetse kuchita zonse zimene mungathe kuti mukapatse chakudya ndi madzi? Kamwana kankhosako kali ngati anthu ambiri amene sanamvebe uthenga wabwino. Abusa a zipembedzo zonyenga sakuthandiza anthu awo ndipo anthuwo ali ndi njala komanso ludzu lauzimu moti alibe chiyembekezo chilichonse cha m’tsogolo. Koma ifeyo tili ndi chilichonse chimene iwo angafune. Tili ndi chakudya chauzimu chopatsa thanzi ndiponso madzi otsitsimula a choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. (Yesaya 55:1, 2) Tikamaganizira njala yauzimu imene anthu amenewa ali nayo, timawamvera chisoni kwambiri. Mofanana ndi Yesu tikamamvera anthu chisoni tidzayesetsa kuwauza uthenga wa Ufumu wopatsa chiyembekezo.

      19. Kodi tingathandize bwanji munthu yemwe tikuphunzira naye Baibulo, amene tikuona kuti wakwanitsa zonse zofunikira kuti ayambe kugwira nawo ntchito yolalikira?

      19 Kodi tingathandize bwanji ena kuti azitsanzira Yesu? Tiyerekezere kuti mukufuna kulimbikitsa munthu yemwe mumaphunzira naye Baibulo amene wakwanitsa zonse zofunikira kuti ayambe kugwira nawo ntchito yolalikira. Kapenanso mwina mukufuna kuthandiza munthu amene anasiya kulalikira kuti ayambenso kugwira nawo ntchitoyi. Kodi anthu amenewa tingawathandize bwanji? Tiyenera kuyesetsa kuwathandiza kuti azifunitsitsa kugwira nawo ntchitoyi. Kumbukirani kuti choyamba, Yesu “anawamvera chisoni” anthu kenako anayamba kuwaphunzitsa. (Maliko 6:34) Choncho, tikathandiza wophunzira Baibulo wathu komanso anthu amene anasiya kulalikira kuti azimvera ena chisoni, adzakhala ofunitsitsa kuchokera pansi pa mtima kuti akhale ngati Yesu ndipo adzayamba kugwira nawo ntchito youza ena uthenga wabwino. Mwina tingawafunse kuti: “Kodi uthenga wa Ufumu unasintha bwanji moyo wanu kuti ukhale wabwino? Nanga bwanji anthu amene sanamvebe uthenga umenewu, kodi nawonso sakufunika kuuzidwa? Ndiye inuyo mungatani kuti muthandize anthu amenewo?” Komabe, chifukwa chachikulu chimene chimalimbikitsa munthu kugwira nawo ntchitoyi ndi kukonda Mulungu ndiponso mtima wofunitsitsa kumutumikira.

      20. (a) Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu akhale wotsatira wa Yesu? (b) Kodi tikambirana chiyani m’mutu wotsatira?

      20 Kuti munthu akhale wotsatira wa Yesu amafunika kuchita zambiri, osati kumangotsanzira zimene iye ankanena komanso kuchita. Tiyenera kukhala ndi “maganizo” ngati amene iye anali nawo. (Afilipi 2:5) Ndipo tili ndi mwayi chifukwa Baibulo limasonyeza maganizo ndiponso mtima umene Yesu anali nawo, womwe unkamuchititsa kulankhula komanso kuchita zinthu zosiyanasiyana. Tikadziwa “maganizo a Khristu,” tidzaphunzira kukhala anthu achifundo ndipo tidzachitira ena zinthu ngati mmene Yesu ankachitira. (1 Akorinto 2:16) M’mutu wotsatira, tikambirana njira zosiyanasiyana zimene Yesu anasonyezera chikondi makamaka kwa otsatira ake.

      a Anthu ena amati mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “atagwidwa ndi chifundo,” ndi ena mwa mawu amphamvu kwambiri m’Chigiriki osonyeza kumvera ena chisoni. Buku lina limati mawu amenewa “samangosonyeza kumva chisoni kokha ukaona anthu amene akuvutika, koma amatanthauzanso kukhala ndi mtima wofunitsitsa kuwathandiza komanso kuthetsa mavuto awo.”

      b Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti ‘tizimverana chisoni,’ kwenikweni amatanthauza kuti “tizivutikira limodzi.”

      Kodi Mungatani Kuti Muzitsatira Yesu?

      • Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo pogwiritsa ntchito ulamuliro umene anali nawo, nanga tingamutsanzire bwanji?​—Mateyu 11:28-30.

      • N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tizitsanzira Yesu pa nkhani yochitira ena chifundo?​—Mateyu 9:9-13; 23:23.

      • Kodi Yesu anachita zinthu ziti zosonyeza kuti ankaganizira mmene ena akumvera, nanga tingamutsanzire bwanji?​—Luka 7:36-50.

      • Kodi fanizo la Msamariya wachifundo likusonyeza bwanji kuti chifundo ndi khalidwe lofunika kwambiri, nanga ifeyo tingagwiritse ntchito bwanji mfundo ya mufanizoli?​—Luka 10:29-37.

  • “Yesu . . . Anawakonda Mpaka pa Mapeto a Moyo Wake”
    ‘Bwera Ukhale Wotsatira Wanga’
    • MUTU 16

      “Yesu . . . Anawakonda Mpaka pa Mapeto a Moyo Wake”

      1, 2. Kodi Yesu anatani usiku womaliza pamene anali ndi atumwi ake, ndipo n’chifukwa chiyani maola amenewo anali ofunika kwa iye?

      YESU anasonkhanitsa atumwi ake m’chipinda chapamwamba m’nyumba ina ku Yerusalemu, ndipo ankadziwa kuti usiku umenewo unali womaliza kukhala nawo. Nthawi yoti abwerere kwa Atate wake inali itayandikira. Panali patangotsala maola ochepa kuti amangidwe komanso kuti akumane ndi mayesero aakulu amene anali asanakumanepo nawo. Koma ngakhale kuti ankayembekezera kuphedwa, iye anapitiriza kuganizira zinthu zimene atumwi ake ankafunikira.

      2 Yesu anali atauza kale ophunzira ake kuti watsala pang’ono kubwerera kumwamba, koma panali zinanso zoti awauze kuti awathandize kukhala olimba mtima pa nthawi yovutayi. Choncho pa nthawiyi anawaphunzitsa zinthu zofunika kwambiri zimene zikanawathandiza kukhalabe okhulupirika. Mawu amene anawauza anali achikondi ndiponso olimbikitsa kwambiri kuposa mawu ena aliwonse amene anawauzapo. Koma kodi n’chifukwa chiyani Yesu ankadera nkhawa kwambiri atumwi akewo m’malo modzidera nkhawa yekha? N’chifukwa chiyani maola omalizirawo amene Yesu anakhala ndi atumwi ake anali ofunika kwambiri kwa iye? Yankho la mafunso onsewa ndi lakuti iye ankawakonda kwambiri atumwiwo.

      3. Tikudziwa bwanji kuti Yesu sanadikire kuti usiku womaliza ufike kuti ayambe kusonyeza chikondi kwa otsatira ake?

      3 Patapita zaka zambiri, polemba mouziridwa zimene zinachitika usiku umenewo, mtumwi Yohane anayamba ndi mawu akuti: “Yesu anadziwiratu chikondwerero cha Pasika chisanafike kuti nthawi yake yochoka m’dzikoli kupita kwa Atate yakwana. Ndipo popeza kuti ankakonda otsatira akewo amene anali m’dzikoli, anawakonda mpaka pamapeto a moyo wake.” (Yohane 13:1) Yesu sanadikire kuti usiku umenewu ufike kuti ayambe kusonyeza chikondi kwa atumwi “akewo.” Pa utumiki wake wonse, anasonyeza m’njira zambiri kuti ankakonda atumwi akewo. Choncho tingachite bwino kuti tione zina mwa njira zimene iye anasonyezera chikondi ndiponso mmene tingamutsanzirire, chifukwa tikamamutsanzira timasonyeza kuti ndife ophunzira ake enieni.

      Yesu Anali Woleza Mtima

      4, 5. (a) N’chifukwa chiyani Yesu ankafunika kukhala woleza mtima pochita zinthu ndi ophunzira ake? (b) Kodi Yesu anachita chiyani atumwi ake atatu atalephera kukhala maso m’munda wa Getsemane?

      4 Chikondi ndi kuleza mtima zimayendera limodzi. Lemba la 1 Akorinto 13:4 limanena kuti: “Chikondi n’choleza mtima.” Munthu woleza mtima amakhala wopirira ndiponso wosakwiya msanga. Kodi Yesu ankafunika kukhala woleza mtima pochita zinthu ndi ophunzira ake? Inde, chifukwa monga tinaonera m’Mutu 3, atumwiwo zinkawavuta kukhala odzichepetsa. Kangapo konse, iwo ankakangana pa nkhani yoti wamkulu ndi ndani pakati pawo. Kodi Yesu anachita chiyani? Kodi anakwiya n’kuwakalipira mopsa mtima? Ayi sanatero, koma anakambirana nawo moleza mtima, ngakhale pamene “anayamba kukangana kwambiri” za nkhaniyi usiku womalizira weniweni pamene iye anali nawo.​—Luka 22:24-30; Mateyu 20:20-28; Maliko 9:33-37.

      5 Pa nthawi ina usiku womwewo, Yesu ndi atumwi ake 11 okhulupirika atapita kumunda wa Getsemane, iye anayesedwanso ndipo ankafunika kusonyeza kuleza mtima. Yesu anasiya atumwi 8, ndipo anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane n’kupita nawo mkati mwa mundawo. Ndiyeno anawauza kuti: “Ine ndikumva chisoni chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso.” Kenako iye anayenda kupita patsogolo pang’ono n’kuyamba kupemphera mochokera pansi pa mtima. Atapemphera kwa nthawi yaitali, anabwerera kwa atumwi atatu aja. Kodi anawapeza akuchita chiyani? Iye anawapeza akugona pa nthawi yovuta kwambiri ngati imeneyi. Kodi iye anayamba kuwanyoza chifukwa cholephera kukhala maso? Ayi, koma anawalimbikitsa moleza mtima. Mawu okoma mtima amene iye anawauza anasonyeza kuti ankamvetsa kuti iwo anali ndi nkhawa komanso anali atafooka.a Iye ananena kuti: “Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.” Yesu anakhalabe woleza mtima usiku umenewo, ngakhale kuti anapeza ophunzirawo akugona, osati kamodzi kokha, koma katatu konse.​—Mateyu 26:36-46.

      6. Kodi tingatsanzire bwanji Yesu tikamachita zinthu ndi anthu ena?

      6 N’zolimbikitsa kuona kuti Yesu sanataye mtima n’kuyamba kuganiza kuti atumwi akewo sangasinthe. Kuleza mtima kwake kunathandiza chifukwa amuna okhulupirika amenewa anaphunzira kufunika kokhalabe maso ndiponso kukhala odzichepetsa. (1 Petulo 3:8; 4:7) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pochita zinthu ndi anthu ena? Makamaka akulu ayenera kukhala oleza mtima. Zili choncho chifukwa Mkhristu angapite kwa mkulu kukamuuza mavuto ake pa nthawi imene mkuluyo watopa kapena wasokonezeka ndi mavuto ake. Nthawi zina, anthu amene apatsidwa uphungu angamazengereze kuutsatira. Komabe, akulu oleza mtima amapereka malangizo “mofatsa” ndiponso ‘amasamalira gulu la nkhosa mwachikondi.’ (2 Timoteyo 2:24, 25; Machitidwe 20:28, 29) Makolo nawonso angachite bwino kutsanzira Yesu pokhala oleza mtima chifukwa nthawi zina ana angachedwe kuyamba kutsatira malangizo amene awapatsa. Ngati makolo ali achikondi komanso oleza mtima, sadzafooka koma adzapitirizabe kuphunzitsa ana awo. Ndithudi makolo akapitiriza kuchita zimenezi moleza mtima, adzapeza madalitso ochuluka.​—Salimo 127:3.

      Yesu Ankasamalira Ophunzira Ake

      7. Kodi Yesu anachita zinthu ziti zosonyeza kuti ankasamalira ophunzira ake m’njira zosiyanasiyana?

      7 Munthu amasonyeza chikondi akamachita zinthu mosadzikonda. (1 Yohane 3:17, 18) Chikondi “sichisamala zofuna zake zokha.” (1 Akorinto 13:5) Yesu ankasamalira ophunzira ake m’njira zosiyanasiyana chifukwa anali wachikondi. Kawirikawiri ankawathandiza ngakhale asanamuuze zimene akufuna. Mwachitsanzo, ataona kuti iwo atopa, Yesu anawauza kuti: “Tipite kwatokha kopanda anthu kuti mukapume pang’ono.” (Maliko 6:31) Ataona kuti ophunzira akewo ali ndi njala, sanadikire kuti achite kumuuza, koma anawapatsa chakudya limodzi ndi anthu ambirimbiri amene anabwera kudzamumvetsera pamene ankaphunzitsa.​—Mateyu 14:19, 20; 15:35-37.

      8, 9. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu ankazindikira zosowa zauzimu za ophunzira ake ndipo ankawathandiza? (b) Yesu atapachikidwa pamtengo, kodi anasonyeza bwanji kuti ankadera nkhawa kwambiri mayi ake?

      8 Yesu ankazindikira zosowa zauzimu za ophunzira ake ndipo ankawathandiza. (Mateyu 4:4; 5:3) Nthawi zambiri akamaphunzitsa, ankaganizira mwapadera ophunzira ake. Mwachitsanzo, cholinga cha ulaliki wa paphiri kwenikweni chinali kufotokoza mfundo zimene zingathandize ophunzira ake. (Mateyu 5:1, 2, 13-16) Iye ankagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa, koma “kumbali ankafotokoza zinthu zonse kwa ophunzira ake.” (Maliko 4:34) Yesu ananeneratu kuti adzaika “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” kuti azidzapereka chakudya chauzimu kwa otsatira ake m’masiku otsiriza. Kuyambira m’chaka cha 1919 C.E., gulu la kapololi, lomwe lapangidwa ndi abale a Yesu odzozedwa ndi mzimu padziko lapansi, lakhala likupereka mokhulupirika ‘chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera.’​—Mateyu 24:45.

      9 Pa tsiku limene anaphedwa, Yesu anasonyeza m’njira yapadera kwambiri kuti amadera nkhawa moyo wauzimu wa otsatira ake. Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Yesu anali atapachikidwa pamtengo ndipo ankamva ululu wosaneneka. Kuti athe kupuma bwinobwino, ayenera kuti ankafunika kudziwongola. N’zoonekeratu kuti zimenezi zinachititsa kuti amve ululu kwambiri chifukwa chakuti kulemera kwa thupi lake kunkachititsa kuti mabala a misomali m’mapazi ake aziwonjezeka kukula. Ankamvanso ululu chifukwa msana wake, womwe unali ndi mabala okhaokha, unkakhula mtengowo. Choncho ziyenera kuti zinali zovuta ndi zopweteka kwambiri kuti alankhule chifukwa ankafunika kukoka mpweya wambiri. Komabe Yesu asanafe, ananena mawu osonyeza kuti ankawakonda kwambiri mayi ake, Mariya. Yesu ataona Mariya ndi mtumwi Yohane ataima chapafupi, analankhula ndi mayi akewo momveka bwino moti anthu amene anaima pafupi anamva. Iye anati: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” Kenako anauza Yohane kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.” (Yohane 19:26, 27) Yesu ankadziwa kuti mtumwi wokhulupirikayu adzasamalira Mariya mwauzimu komanso adzamupatsa zinthu zina zofunikira pa moyo wake.b

      Collage: 1. Abambo akuchita kulambira kwa pabanja ndi mkazi komanso ana awo atatu. 2. Bambo, mayi ndi ana akuyendetsa ndege yachipepala. 3. Banja likudyera limodzi chakudya.

      Makolo achikondi amasonyeza kuleza mtima ndiponso amasamalira ana awo powapatsa zinthu zimene akufunikira

      10. Kodi makolo angatsanzire bwanji Yesu pamene akusamalira ana awo?

      10 Makolo achikondi amaona kuti ndi bwino kuganizira chitsanzo cha Yesu. Bambo amene amakondadi banja lake amapatsa banjalo zinthu zofunika pa moyo. (1 Timoteyo 5:8) Bambo, yemwe ndi mutu wa banja amafuna kuti banja lake lizisangalala ndipo amayesetsa kuti banjalo lizipeza nthawi yopuma komanso yopita kokasangalala. Kuwonjezera pamenepo, makolo a Chikhristu amathandiza ana awo mwauzimu ndipo zimenezi n’zofunika kwambiri. Kodi amachita bwanji zimenezi? Makolowo amayesetsa kuti nthawi zonse banja lonse liziphunzira Baibulo limodzi. Komanso amayesetsa kuti ana awo azisangalala ndiponso azilimbikitsidwa akamaphunzira. (Deuteronomo 6:6, 7) Makolo amaphunzitsanso ana awo kuti aziona kuti kulalikira komanso kukonzekera ndi kukapezeka pamisonkhano ndi zinthu zofunika kwambiri polambira Yehova. Makolo amayesetsanso kuwaphunzitsa zimenezi powasonyeza chitsanzo chabwino.​—Aheberi 10:24, 25.

      Yesu Ankakhululukira Ena Mofunitsitsa

      11. Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani otsatira ake pa nkhani ya kukhululukira ena?

      11 Munthu amene amakhululukira ena amasonyeza kuti ali ndi chikondi. (Akolose 3:13, 14) Lemba la 1 Akorinto 13:5 limanena kuti chikondi “sichisunga zifukwa.” Nthawi zambiri Yesu ankaphunzitsa otsatira ake kufunika kokhululukira ena. Iye anawalimbikitsa kuti azikhululukira ena, “osati maulendo 7 okha ayi, koma mpaka maulendo 77,” kutanthauza mopanda malire. (Mateyu 18:21, 22) Komanso anawaphunzitsa kuti azikhululukira munthu wochimwa yemwe walapa pambuyo podzudzulidwa. (Luka 17:3, 4) Yesu ankachita zimene ankaphunzitsa. Iye sanali ngati Afarisi omwe anali achinyengo amene ankangophunzitsa ndi pakamwa pokha. (Mateyu 23:2-4) Tiyeni tione mmene Yesu anasonyezera kuti ankakhululukira ena mofunitsitsa ngakhale pamene mnzake amene ankamudalira anamukhumudwitsa.

      Yesu amene ali pakhonde akuyang’ana Petulo amene ali m’bwalo ndipo akukana kuti sakumudziwa Yesu.

      12, 13. (a) Kodi Petulo anakhumudwitsa bwanji Yesu usiku umene anagwidwa? (b) Kodi zimene Yesu anachita ataukitsidwa zikusonyeza bwanji kuti sankangolalikira zoti tizikhululukira ena?

      12 Yesu ankagwirizana kwambiri ndi mtumwi Petulo, amene anali wokoma mtima, koma nthawi zina ankachita zinthu mopupuluma. Yesu anaona makhalidwe abwino a Petulo ndipo anamupatsa maudindo ambiri. Petulo, Yakobo ndi Yohane, anali atumwi okhawo amene anaona zozizwitsa zina zimene atumwi ena aja sanazione. (Mateyu 17:1, 2; Luka 8:49-55) Monga taonera kale, Petulo anali mmodzi wa atumwi amene anapita ndi Yesu mkati mwa munda wa Getsemane usiku umene Yesuyo anagwidwa. Koma usiku womwewo, pamene Yesu anaperekedwa n’kugwidwa ndi adani ake, Petulo ndi atumwi ena aja anathawa n’kumusiya yekha. Patapita nthawi, Petulo anasonyeza kulimba mtima ndipo anaima panja pa nthawi imene Yesu ankaimbidwa mlandu womunamizira. Kenako Petulo anachita mantha ndipo anachita chinthu chimene sankayenera kuchita. Katatu konse, iye anakanitsitsa kwa mtu wagalu kuti samudziwa Yesu. (Mateyu 26:69-75) Kodi Yesu anatani? Kodi inuyo mukanatani mnzanu wapamtima atakukhumudwitsani mwanjira imeneyi?

      13 Yesu anali wokonzeka kukhululukira Petulo. Iye ankadziwa kuti Petulo anali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha tchimo lakelo. Ndipotu mtumwiyu analapa chifukwa “anamva chisoni n’kuyamba kulira.” (Maliko 14:72) Pa tsiku limene Yesu anaukitsidwa, anaonekera kwa Petulo. N’zosakayikitsa kuti anachita zimenezi pofuna kulimbikitsa mtumwiyu ndiponso kumutsimikizira kuti amamukonda. (Luka 24:34; 1 Akorinto 15:5) Pasanathe miyezi iwiri, Yesu analemekeza Petulo pomulola kuti atsogolere ena pochitira umboni ku gulu la anthu amene anasonkhana ku Yerusalemu pa tsiku la Pentekosite. (Machitidwe 2:14-40) Koma tikumbukirenso kuti Yesu sanasungire chakukhosi atumwi onsewo ngakhale kuti anamuthawa n’kumusiya yekha, chifukwa ataukitsidwa, ankawatchulabe kuti “abale anga.” (Mateyu 28:10) Apatu n’zoonekeratu kuti Yesu sankangolalikira zoti tizikhululukira ena, koma anasonyeza mmene tingachitire zimenezi.

      14. N’chifukwa chiyani tiyenera kuphunzira kukhululukira ena, nanga tingasonyeze bwanji kuti ndife okonzeka kukhululuka?

      14 Popeza ndife ophunzira a Khristu, tiyenera kuphunzira kukhululukira ena. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti mosiyana ndi Yesu ifeyo komanso anthu amene angatilakwirewo si angwiro. Nthawi zambiri tonsefe timapunthwa m’mawu ndi zochita zathu. (Aroma 3:23; Yakobo 3:2) Tikamakhululukira ena pakakhala zifukwa zomveka zowasonyezera chifundo, zimathandiza kuti ifenso Mulungu atikhululukire machimo athu. (Maliko 11:25) Koma kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okonzeka kukhululukira anthu amene atilakwira? Nthawi zambiri, chikondi chimatithandiza kunyalanyaza machimo ndiponso zolakwa zing’onozing’ono za ena. (1 Petulo 4:8) Munthu amene watichimwira akalapa moona mtima ngati mmene Petulo anachitira, tiyenera kumukhululukira mofunitsitsa ngati mmene Yesu ankachitira. M’malo mosunga chakukhosi, timachita zinthu mwanzeru posankha kukhululukira ena. (Aefeso 4:32) Tikamachita zimenezi timalimbikitsa mtendere mumpingo komanso zimatithandiza kuti tikhale ndi mtendere mumtima.​—1 Petulo 3:11.

      Yesu Anasonyeza Kuti Amakhulupirira Ena

      15. N’chifukwa chiyani Yesu ankakhulupirira ophunzira ake ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu?

      15 Chikondi chimayendera limodzi ndi kukhulupirira ena. Ndipo Malemba amati chikondi “chimakhulupirira zinthu zonse.”c (1 Akorinto 13:7) Chifukwa cha chikondi chimene anali nacho, Yesu anasonyeza kuti ankakhulupirira ophunzira ake ngakhale kuti ankalakwitsa zinthu zina. Iye ankawadalira ndipo ankakhulupirira kuti amakonda Yehova ndi mtima wonse ndipo amafunadi kuchita zimene Mulungu amafuna. Ophunzirawo akalakwitsa zinthu, Yesu sankawakayikira n’kumaganiza kuti ali ndi zolinga zoipa. Mwachitsanzo, mtumwi Yakobo ndi Yohane atatuma mayi awo kuti akapemphe Yesu kuti adzakhale naye pafupi mu Ufumu wake, Yesu sanayambe kuwakayikira n’kumawaona ngati anthu osakhulupirika ndiponso sanawachotse m’gulu la atumwi ake.​—Mateyu 20:20-28.

      16, 17. Kodi Yesu anapereka maudindo otani kwa ophunzira ake?

      16 Posonyeza kuti ankakhulupirira ena, Yesu anagawirako ophunzira ake ntchito zosiyanasiyana. Mwachitsanzo maulendo awiri, pamene anachulukitsa chakudya mozizwitsa n’kudyetsa gulu la anthu, anapereka kwa ophunzira ake udindo wogawa chakudyacho. (Mateyu 14:19; 15:36) Pokonzekera mwambo wake womaliza wa Pasika, iye anatuma Petulo ndi Yohane kuti apite ku Yerusalemu kukachita zonse zokonzekera mwambo umenewu. Iwo anaonetsetsa kuti apeza mwana wa nkhosa, vinyo, mikate yopanda zofufumitsa, masamba owawa ndiponso chilichonse chimene chinkafunika pa mwambowu. Imeneyi sinali ntchito yaing’ono chifukwa chakuti Chilamulo cha Mose chinkafuna kuti mwambo wa Pasika uzichitika m’njira yonenera, ndipo Yesu anafunika kuchita zinthu zogwirizana ndi Chilamulocho. Komanso usiku womwewo, poyambitsa Chikumbutso cha imfa yake, Yesu anagwiritsa ntchito vinyo ndi mikate yopanda zofufumitsa monga zizindikiro zofunika.​—Mateyu 26:17-19; Luka 22:8, 13.

      17 Yesu anaona kuti n’koyenera kupatsa ophunzira ake ntchito zina zofunika kwambiri. Kumbukirani kuti Yesu anapereka kwa ophunzira ake ntchito yaikulu yolalikira ndi kuphunzitsa anthu ena kuti nawonso akhale ophunzira ake. (Mateyu 28:18-20) Monga mmene taonera kale, iye ananeneratu kuti adzapatsa kagulu kakang’ono ka otsatira ake odzozedwa padziko lapansi ntchito yofunika kwambiri yopereka chakudya chauzimu. (Luka 12:42-44) Panopa, ngakhale kuti Yesu sitingamuone ndipo akulamulira kumwamba, wapereka udindo wosamalira mpingo wake padziko lapansi kwa amuna oyenerera amene ‘anawapereka kuti akhale mphatso.’​—Aefeso 4:8, 11, 12.

      18-20. (a) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira ndiponso kudalira Akhristu anzathu? (b) Kodi tingatsanzire bwanji Yesu amene ankakonda kugawira ena ntchito? (c) Kodi m’mutu wotsatira tidzakambirana chiyani?

      18 Kodi tingatsanzire bwanji Yesu pamene tikuchita zinthu ndi ena? Tikamakhulupirira Akhristu anzathu ndi kuwadalira timasonyeza kuti timawakonda. Tizikumbukira kuti munthu wachikondi amaona zabwino zimene ena akuchita, osati zimene akulakwitsa. Tikudziwa kuti nthawi zina anthu ena akhoza kutikhumudwitsa, koma ngati tili ndi chikondi sitidzafulumira kuganiza kuti ali ndi zolinga zoipa. (Mateyu 7:1, 2) Tikamaona Akhristu anzathu moyenera, tidzachita zinthu zowalimbikitsa osati zowafooketsa.​—1 Atesalonika 5:11.

      19 Tiyenera kutsanzira Yesu amene ankakonda kugawira ena ntchito. N’zothandiza kwambiri ngati abale amene ali ndi maudindo mumpingo amapatsako ena ntchito zoyenerera komanso zimene angakwanitse n’kumakhulupirira kuti zonse ziyenda bwino. Pochita zimenezi, akulu amene akhala m’maudindo amenewa kwa nthawi yaitali angathandize achinyamata amene “akuyesetsa kuti akhale” pa udindo mumpingo. Iwo angawaphunzitse zinthu zofunika ndiponso zothandiza kwambiri kuti adzathe kugwira bwino ntchito za mumpingo. (1 Timoteyo 3:1; 2 Timoteyo 2:2) Kuphunzitsa achinyamata mwanjira imeneyi n’kofunika kwambiri. Pamene Yehova akupitiriza kutithandiza kuti ntchito yokhudza Ufumu wake ipite patsogolo, m’pofunika kuphunzitsa abale kuti akhale oyenerera kusamalira mipingo imene ikupitiriza kuwonjezeka.​—Yesaya 60:22.

      20 Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza ena chikondi. Pa njira zonse zimene tingamutsanzirire, palibe njira yofunika kwambiri kuposa kukonda ena. M’mutu wotsatira, tidzakambirana zimene anachita popereka moyo wake mofunitsitsa. Imeneyi ndi njira yaikulu imene Yesu anasonyezera kuti amatikonda kwambiri.

      a Kuwonjezera pa kutopa, panali chinthu chinanso chimene chinachititsa atumwiwo kuti agone. Lemba la Luka 22:45 limene limafotokozanso za nkhaniyi, limanena kuti Yesu “anawapeza atagona chifukwa anali atafooka ndi chisoni.”

      b Zikuoneka kuti pa nthawiyi, Mariya anali wamasiye ndipo ana ake ena anali asanakhale ophunzira a Yesu.​—Yohane 7:5.

      c Zimenezi sizikutanthauza kuti munthu wachikondi amangokhulupirira zilizonse, koma zikutanthauza kuti sapezera ena zifukwa kapena kukayikira zolinga zawo. Munthu wachikondi amapewa kuweruza ena mopupuluma asanamvetse zinthu ndipo amapewa kuwaganizira zoipa.

      Kodi Mungatani Kuti Muzitsatira Yesu?

      • N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti tizitsatira malangizo a Yesu onena za kukhululukira ena?​—Mateyu 6:14, 15.

      • Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundo yaikulu ya mufanizo la Yesu lonena za kufunika kokhululukira ena?​—Mateyu 18:23-35.

      • Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankaganizira ophunzira ake, nanga tingamutsanzire bwanji?​—Mateyu 20:17-19; Yohane 16:12.

      • Kodi Yesu anamusonyeza bwanji Petulo kuti ankamudalira, nanga ifeyo tingasonyeze bwanji ena kuti timawadalira?​—Luka 22:31, 32.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena