Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w01 11/15 tsamba 2-4
  • Kodi Chiyembekezo cha Chipulumutso Chilipodi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chiyembekezo cha Chipulumutso Chilipodi?
  • Nsanja ya Olonda—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Khalanibe ndi “Chiyembekezo cha Chipulumutso” Choŵala!
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Chipulumutso Zimene Chimatanthauza Kwenikweni
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Zimene Tiyenera Kuchita Kuti Tipulumuke
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kodi Chipulumutso N’chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2001
w01 11/15 tsamba 2-4

Kodi Chiyembekezo cha Chipulumutso Chilipodi?

Anthu m’zaka za m’ma 1900 aona kukhetsa magazi kwadzaoneni kuposa zaka zina zonse mmbuyomu. Umbanda, nkhondo zikuluzikulu, nkhondo zapachiweniweni, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kusaona mtima, ndiponso chiwawa zakhala zofala kwambiri m’zaka makumi angapo zapitazi. Kuwonjezera pa zimenezi, anthu avutikanso kwambiri ndi matenda, ukalamba, ndiponso imfa. Kodi ndani sakulakalaka kupulumuka ku mavuto ochulukaŵa omwe ali padziko lapansi lerolino? Tikamayang’ana kutsogolo, kodi chiyembekezo cha chipulumutso chilipodi?

TALINGALIRANI masomphenya omwe mtumwi Yohane anaona zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Iye analemba kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Nayenso mneneri Yesaya analosera kuti: “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena.”​—Yesaya 25:8.

Tangoganizirani zimene kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu ameneŵa kudzatanthauza. Anthu adzawomboledwa ku zinthu monga kuponderezedwa, chiwawa, ndiponso zinthu zosautsa ndi zovutitsa maganizo. Inde, ngakhale matenda, ukalamba, ndi imfa sizidzatisautsanso! Mawu a Mulungu, Baibulo, amalonjeza moyo wosatha m’dziko lapansi momwe zinthu zidzakhale zangwiro. (Luka 23:43; Yohane 17:3) Ndipotu moyo wosatha umenewu ulipo kwa onse amene akuufuna. ‘[Mulungu] akufuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.’​—1 Timoteo 2:3, 4.

Komabe, kuti tipindule ndi malonjezo a Mulungu, tifunikira kuzindikira udindo womwe Yesu Kristu ali nawo wotipulumutsa ndiponso tifunikira kumukhulupirira iye. Yesuyo anati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ponena za udindo wofunika kwambiri umene Yesu Kristu ali nawo pa nkhaniyi, mtumwi Petro anati: “Palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Machitidwe 4:12) Mtumwi Paulo ndi mnzake Sila analimbikitsanso munthu wina wofunafuna choonadi kuti: “Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.”​—Machitidwe 16:30, 31.

Inde, Yesu Kristu ndiye “Mkulu wa moyo” ndipo chipulumutso n’chotheka kudzera mwa iye basi. (Machitidwe 3:15) Koma kodi munthu mmodzi angakhale bwanji wofunika zedi populumutsa anthufe? Kuzindikira bwinobwino udindo womwe ali nawo pa nkhaniyi kuyenera kulimbikitsa chiyembekezo chathu cha chipulumutso.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Tsamba 3: Ndege zoponya mabomba: Chithunzi cha USAF; Ana Osoŵa chakudya: UNITED NATIONS/​J. FRAND; sitima ya nkhondo yapamadzi yomwe ikuyaka: Chithunzi cha U.S. Navy

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena