Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • kp tsamba 16-19
  • Dziko Latsopano Limene Mulungu Walonjeza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Latsopano Limene Mulungu Walonjeza
  • Dikirani!
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene “Miyamba Yatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano” Zikuyambira
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano—Monga Kunanenedwera
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
    Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
Onani Zambiri
Dikirani!
kp tsamba 16-19

Dziko Latsopano Limene Mulungu Walonjeza

BAIBULO, Mawu a Mulungu olembedwa, limatipatsa chiyembekezo ponena kuti: “Tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.

Kodi “miyamba yatsopano” n’chiyani? Baibulo limagwirizanitsa kumwamba ndi ulamuliro. (Machitidwe 7:49) “Miyamba yatsopano” ndilo boma latsopano limene lidzalamulira dziko lapansi. Ndi latsopano chifukwa lidzaloŵa m’malo maulamuliro amene alipoŵa. Ndi latsopanonso chifukwa ndi chinthu chatsopano pa nkhani ya kukwaniritsidwa kwapang’onopang’ono kwa zolinga za Mulungu. Boma limeneli ndi Ufumu umene Yesu anatiphunzitsa kuti tizipempherera. (Mateyu 6:10) Chifukwa chakuti Mwiniwake ndi Mulungu ndipo amakhala kumwamba, umatchedwa “Ufumu wa Kumwamba.”—Mateyu 7:21.

Kodi “dziko latsopano” n’chiyani? Si dziko lapansi lenilenili latsopano, chifukwa Baibulo limanena momveka bwino kuti anthu adzakhala pa dziko lapansi kosatha. “Dziko latsopano” ndi anthu atsopano. Lidzakhala latsopano chifukwa anthu oipa adzakhala atachotsedwa. (Miyambo 2:21, 22) Anthu onse amene adzakhalepo nthaŵi imeneyo adzalemekeza ndi kumvera Mlengi ndipo azidzatsatira zimene Mlengiyo amafuna. (Salmo 22:27) Anthu ochokera m’mayiko onse akupemphedwa kuti aphunzire zimenezi ndi kuzitsatira pa miyoyo yawo panopa. Kodi inu mukuchita zimenezo?

M’dziko latsopano la Mulungu, aliyense adzalemekeza ulamuliro Wake. Kodi kukonda Mulungu kumakuchititsani kumumvera? (1 Yohane 5:3) Kodi mumaonetsa zimenezi panyumba panu, kuntchito kapena kusukulu kwanu, ndiponso pa zimene mumachita pa moyo wanu?

M’dziko latsopano limenelo, anthu onse adzakhala ogwirizana polambira Mulungu woona. Kodi mumalambira Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi? Kodi kulambira kwanu kumakuchititsani kukhaladi ogwirizana ndi olambira anzanu ochokera m’mayiko, m’mafuko, ndi m’zinenero zonse?—Salmo 86:9, 10; Yesaya 2:2-4; Zefaniya 3:9.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 17]

Mulungu Amene Walonjeza Zimenezi

Mulungu ameneyu ndi Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi. Ndi amene Yesu Kristu anamutchula kuti “Mulungu woona yekha.”—Yohane 17:3.

Anthu ambiri amalemekeza milungu imene anachita kuipanga okha. Ambiri amagwadira mafano opanda moyo. Ena amalemekeza mabungwe a anthu, nzeru za anthu zosemphana ndi Mulungu, kapena zilakolako zawo. Ngakhale anthu amene amanena kuti amagwiritsa ntchito Baibulo si onse amene amalemekeza dzina la amene Baibulolo limamutchula kuti “Mulungu woonayo.”—2 Mbiri 15:3.

Ponena za iye mwini, Mlengi anati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli.” (Yesaya 42:5, 8) Dzina limeneli limapezeka maulendo opitirira 7,000 m’Baibulo m’zinenero zimene Baibulo linalembedwa poyambirira. Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera motere: “Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mateyu 6:9.

Kodi Mulungu woona ali ndi makhalidwe otani? Iye anadzifotokoza kuti ndi Mulungu “wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi” amene salekerera anthu ophwanya malamulo ake mwadala. (Eksodo 34:6, 7) Mmene wakhala akuchitira zinthu ndi anthu zikusonyeza kuti mawu ameneŵa ndi oona.

Zonse ziŵiri, dzina lake, ndi amene dzinalo limaimira, ziyenera kuyeretsedwa kapena kuti kuonedwa kuti n’zoyera. Monga Mlengi ndiponso Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, ndi woyenera kuti tizimumvera ndi kulambira iye yekha basi. Kodi inuyo mumamuchitira zimenezi?

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

Kodi “Miyamba Yatsopano” ndi “Dziko Latsopano” Zidzabweretsa Kusintha Kotani?

Dziko lapansi lidzasinthidwa kukkhala Paradaiso Luka 23:43

Anthu padziko lonse a mitundu, mafuko, ndi Yohane 13:35;

zinenero zonse adzagwirizana chifukwa Chivumbulutso 7:9, 10

cha chikondi

Padziko lonse padzakhala mtendere, Salmo 37:10, 11;

anthu onse adzakhala otetezekadi Mika 4:3, 4

Ntchito yosangalatsa, zakudya zambiri Yesaya 25:6; 65:17,21-23

Matenda, chisoni, imfa zidzatha Yesaya 25:8;

Chivumbulutso 21:1, 4

Anthu onse adzalambira Mulungu woona Chivumbulutso 15:3, 4

mogwirizana

[Bokosi/Chithunzi patsamba 19]

Kodi Mudzakhalamo?

Mulungu sanganame.—Tito 1:2.

Yehova ananena kuti: “Mawu anga . . . sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:11.

Yehova anayamba kale kulenga “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano.” Ufumu wa kumwamba unayamba kale kugwira ntchito. Maziko a “dziko latsopano” ayalidwa kale.

Buku la Chivumbulutso litafotokoza zina mwa zinthu zochititsa chidwi zimene “m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano” zidzabweretse kwa anthu, linagwira mawu a Mulungu mwiniwakeyo, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, akunena kuti: “Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.” Ndipo ananenanso kuti: “Talemba; pakuti mawu aŵa ali okhulupirika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:1, 5.

Funso lofunika kwambiri kudzifunsa n’lakuti, Kodi tikusintha zinthu zimene tiyenera kusintha pamoyo wathu kuti tidzakhale oyenera kukhala nawo mbali ya “dziko latsopano” lolamulidwa ndi “m’mwamba mwatsopano”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena