MUTU 102
Zimene Yohane Anaona M’masomphenya
Pamene mtumwi Yohane anali mkaidi pachilumba cha Patimo, Yesu anamuonetsa masomphenya okwana 16. Masomphenyawa anasonyeza zimene zidzachitike kuti dzina la Mulungu lidzayeretsedwe, Ufumu wake ubwere komanso kuti zimene Mulungu amafuna zichitike padzikoli ngati mmene zilili kumwamba.
M’masomphenya ena, Yohane anaona Yehova ali kumwamba pampando waulemerero, atazunguliridwa ndi akulu 24 amene anavala zovala zoyera komanso zipewa zagolide. Yohane anamva kulira kwa mabingu ndipo panalinso kuwala kwa mphenzi. Akulu 24 aja anagwada n’kumalambira Yehova. M’masomphenya enanso Yohane anaona anthu ambirimbiri ochokera m’mitundu komanso zilankhulo zosiyanasiyana akulambira Yehova. Mwanawankhosa, yemwe ndi Yesu, ankawatsogolera kumadzi a moyo. Kenako anaonanso masomphenya ena. Anaona Yesu atayamba kulamulira monga Mfumu yakumwamba ndi akulu 24 aja. M’masomphenya ena Yohane anaona Yesu akumenyana ndi chinjoka, chomwe ndi Satana, ndipo chinjokacho chinali ndi ziwanda zake. Yesu anathamangitsa Satana ndi ziwandazo kumwamba n’kuwaponyera padzikoli.
Kenako Yohane anaona masomphenya a Mwanawankhosa ndi anthu 144,000 ataima paphiri la Ziyoni. Anaonanso mngelo akuuluka mumlengalenga n’kumauza anthu kuti aziopa Mulungu komanso azimupatsa ulemerero.
Yohane anaonanso masomphenya ena osonyeza nkhondo ya Aramagedo. Pa nkhondoyi, Yesu ndi gulu lake anagonjetsa Satana ndi dziko loipali. Kenako Yohane anaona masomphenya omaliza osonyeza onse akumwamba komanso apadziko lapansi akukhala mogwirizana. Anaona Yehova atawononga Satana ndi onse omutsatira ndipo aliyense kumwamba ndi padzikoli ankalambira Mulungu komanso kulemekeza dzina lake.
“Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, komanso pakati pa mbadwa yako ndi mbadwa yake. Mbadwa ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene”—Genesis 3:15