Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/12 tsamba 28
  • Zimene Mungachite Kuti Muzilimvetsa Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Mungachite Kuti Muzilimvetsa Baibulo
  • Galamukani!—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chimachitika ndi Chiyani Tikamwalira?
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Chimachitika Nchiyani pa Imfa?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Munthu Amene Anali Wakufa Masiku Anai
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 11/12 tsamba 28

Zimene Mungachite Kuti Muzilimvetsa Baibulo

“Palibe amene anganene kuti ife ndi amene timatanthauzira Baibulo molondola chifukwa pali njira zosiyanasiyana zotanthauzira Baibulo.”

Anthu ambiri amakonda kunena mawu amenewa. Koma kodi mumadziwa kuti n’zotheka kulimvetsa Baibulo pogwiritsira ntchito Baibulo lomwelo? Chinsinsi chake ndi ichi: Ngati mavesi ena apambuyo kapena apatsogolo pa vesi lomwe simukulimvetsalo sakufotokoza bwino lembalo, mungachite bwino kuyerekezera ndi mavesi ena m’Baibulo omwe amafotokoza za nkhaniyo. Zimenezi zimathandiza kuti tizitanthauzira Baibulo pogwiritsa ntchito Baibulo lomwelo osati nzeru zathu.

Mwachitsanzo, taganizirani zimene Baibulo limanena pa nkhani yoti chimachitika n’chiyani munthu akamwalira. Taonani mmene malemba 6 ali m’munsimu akugwirizanirana pa mfundo yofotokoza mmene akufa alili.

  • “Akufa salemekeza Yehova, kapena ali yense wakutsikira kuli chete.”​—Salimo 115:17.a

  • “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye. Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”​—Salimo 146:3, 4.

  • “Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi.”​—Mlaliki 9:5.

  • “Kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni.  . . Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero.”​—Yesaya 38:18, 19.

  • “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.”​—Ezekieli 18:4.

  • Ponena za Lazaro, yemwe anali atangomwalira kumene, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take. Chifukwa chake akuphunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, ngati ali m’tulo adzachira. . . . Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, Lazaro wamwalira.”​—Yohane 11:11-14.

Kodi mwaona mfundo yaikulu imene malemba onsewa akusonyeza? Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amakhulupirira, Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akafa ndiye kuti wafa basi. Sakhalanso ndi moyo kumwamba kapena kwinakwake koma amakhala ngati ali mtulo tofa nato ndipo sadziwa chilichonse. Komanso sangathe kulemekeza Mulungu kapena kuganiza chilichonse.b

Mfundo ndi yakuti: Tikafuna kumvetsa zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani inayake, njira yabwino ndi kufufuza mavesi ena omwe amafotokoza bwino nkhaniyo. Njira imeneyi ndi imene Mboni za Yehova zimatsatira, koma imafunika khama. (Miyambo 2:1-5) Ndipotu munthu amachita khama pa zinthu zimene akuziona kuti n’zofunika kwambiri.

a Malembawa achokera m’Baibulo la Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

b Baibulo limaphunzitsa kuti anthu amene anamwalira, omwe Mulungu akuwakumbukira, adzaukitsidwa m’tsogolo pa nthawi imene Mulungu wakonza.​—Werengani Yobu 14:14, 15; Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena