Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Davide Anapha Goliyati
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Davide akuponya mwala kuti aphe Goliyati

      MUTU 40

      Davide Anapha Goliyati

      Yehova anauza Samueli kuti: ‘Pita kunyumba ya Jese. Mwana wake wina adzakhala mfumu ya Isiraeli.’ Samueli anapitadi ndipo ataona mwana woyamba wa Jese, anaganiza kuti: ‘Amene adzakhale mfumu uja ndi ameneyu.’ Koma Yehova anauza Samueli kuti si ameneyo. Kenako anamuuzanso kuti: ‘Ine ndimaona mtima wa munthu osati zimene anthu amaona.’

      Samueli akudzoza Davide kuti akhale mfumu

      Jese anabweretsa ana ake ena 6 koma Samueli anati: ‘Apa palibe aliyense amene Yehova wamusankha. Kodi anyamata anu onse ndi omwewa basi?’ Jese anati: ‘Watsala mmodzi wamng’ono kwambiri, dzina lake Davide. Wapita koweta nkhosa.’ Davide atafika, Yehova anauza Samueli kuti: ‘Ndi ameneyu!’ Zitatero Samueli anathira mafuta pamutu pa Davide. Kusonyeza kuti anamudzoza kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli.

      Goliyati

      Pa nthawi ina, Aisiraeli ankamenyana ndi Afilisiti. Ndiyeno kumbali ya Afilisitiwo kunali chimunthu chachikulu komanso champhamvu dzina lake Goliyati. Tsiku lililonse, Goliyati ankanyoza Aisiraeli. Ankanena kuti: ‘Ndipatseni munthu woti ndimenyane naye! Ngati angandigonjetse nʼkundipha, ndiye kuti tidzakhala antchito anu. Koma ngati ndingamugonjetse, inuyo mudzakhala antchito athu.’

      Davide anafika pamalo pamene panali asilikali a Isiraeli n’cholinga choti apereke chakudya kwa azichimwene ake omwe anali asilikali. Davide anamva zimene Goliyati ankanena ndipo anati: ‘Ine ndikamenyana naye ameneyu.’ Mfumu Sauli atamva anati: ‘Iwe ndiwe mwana.’ Davide anayankha kuti: ‘Yehova andithandiza.’

      Sauli anaveka Davide zovala zake zomenyera nkhondo koma iye anati: ‘Sindingathe kumenya nkhondo ndi zovala zimenezi.’ Choncho anangotenga chinthu choponyera miyala chotchedwa gulaye n’kutsetserekera kukamtsinje. Ndiyeno anatola miyala yosalala bwino 5 n’kuika m’kachikwama kake. Kenako Davide anayamba kuthamangira kumene kunali Goliyati. Goliyatiyo atamuona anati: ‘Mwana iwe! Bwera ndikuphe ndipo ukhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakutchire.’ Davide sanachite mantha. M’malomwake anamuyankha kuti: ‘Iwe ukubwera kudzamenyana ndi ine ndi lupanga komanso mkondo, koma ine ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova. Sukumenyana ndi ine ayi koma ndi Mulungu. Ndipo onse amene ali panowa adziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo. Nonsenu akuperekani mʼmanja mwathu.’

      Kenako Davide anaika mwala pagulaye uja n’kuuponya mwamphamvu kwambiri. Yehova anamuthandiza moti mwalawo unathamanga n’kukaboola Goliyati pachipumi. Nthawi yomweyo Goliyati anagwa n’kufa. Afilisiti ataona zimenezi anayamba kuthawa. Kodi iweyo umadalira Yehova ngati mmene Davide ankachitira?

      “Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma sizili choncho kwa Mulungu chifukwa zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”​—Maliko 10:27

      Mafunso: Kodi Yehova anasankha ndani kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli? Kodi Davide anagwiritsa ntchito chiyani pomenyana ndi Goliyati, nanga ndi ndani anamuthandiza kuti amugonjetse?

      1 Samueli 16:1-13; 17:1-54

  • Davide ndi Sauli
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Davide akufuula polankhula ndi anthu amene ali ndi Sauli

      MUTU 41

      Davide ndi Sauli

      Davide atangopha Goliyati, Mfumu Sauli inamusankha kuti akhale mkulu wa asilikali. Davide anapambana nkhondo zambiri ndipo anatchuka kwambiri. Akamabwera kunkhondo, akazi ankavina komanso kuimba kuti: ‘Sauli wapha adani masauzande koma Davide wapha masauzande ambirimbiri.’ Sauli anapsa mtima kwambiri moti anayamba kufuna kupha Davide.

      Davide ankadziwa kuimba zeze. Tsiku lina akuimbira Sauli nyimbo, Sauliyo anaponya mkondo wake kuti amuphe. Davide anazinda ndipo mkondowo unafikira pakhoma. Kungoyambira pamenepo, Sauli ankayesetsa kuti aphe Davide. Kenako Davide anathawira kuchipululu.

      Davide akutenga mkondo wa Sauli pamene Sauliyo ali mtulo

      Sauli anatenga asilikali 3,000 n’kumakasakasaka Davide. Ndiyeno tsiku lina analowa kuphanga limene kunali Davide ndi anzake. Anzake a Davidewo anati: ‘Uwutu ndi mwayi wako kuti uphe Sauli.’ Davide anangoyenda chokwawa n’kukadula kansalu pa chovala cha Sauli koma Sauliyo sanadziwe chilichonse. Zitatero, Davide anadandaula kwambiri kuti sanalemekeze mfumu yodzozedwa ndi Mulungu. Iye sanalole kuti anzakewo aphe Sauli. Kenako Sauli atatuluka m’phangamo, Davide anafuula n’kumuuza kuti anali ndi mwayi woti amuphe koma anangomusiya. Kodi Sauli anasintha maganizo?

      Ayi ndithu. Anapitirizabe kusakasaka Davide. Tsiku lina usiku, Davide ndi m’bale wake dzina lake Abisai anapita pamalo amene Sauli anagona ndi asilikali ake. Anapeza kuti Abineri, amene anali msilikali wolondera mfumu, nayenso anali atagona. Ndiyeno Abisai anati: ‘Mwayitu suposa apa. Bwanji ndimuphe?’ Koma Davide anati: ‘Ayi, ameneyutu adzalangidwa ndi Yehova. Tiye tingotenga mkondo wake ndi jagi yakeyo tizipita.’

      Kenako Davide anakakwera paphiri lina lapafupi n’kufuula kuti: ‘Iwe Abineri! Ukungogona osateteza mfumuyo? Kodi mkondo wa Sauli ndi madzi ake zili kuti?’ Sauli atazindikira mawu a Davide anati: ‘Mpata woti undiphe unaupeza koma wandikomera mtima. Ndazindikira tsopano kuti iwe udzakhaladi mfumu ya Isiraeli.’ Apa tsopano Sauli anabwerera kunyumba kwake. Koma sikuti anthu onse a m’banja la Sauli ankadana ndi Davide.

      “Ngati nʼkotheka, yesetsani mmene mungathere kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu onse. Okondedwa, musamabwezere zoipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.”​—Aroma 12:18, 19

      Mafunso: N’chifukwa chiyani Sauli ankafuna kupha Davide? N’chifukwa chiyani Davide sanafune kupha Sauli?

      1 Samueli 16:14-23; 18:5-16; 19:9-12; 23:19-29; 24:1-15; 26:1-25

  • Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yonatani ndi mtumiki wake amene ankamunyamulira zida

      MUTU 42

      Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika

      Mwana wamkulu wa Mfumu Sauli anali Yonatani ndipo anali msilikali wolimba mtima. Davide ananena kuti Yonatani ankathamanga kuposa chiwombankhanga ndipo anali wamphamvu kuposa mkango. Tsiku lina, Yonatani anaona asilikali 20 a Afilisiti ali paphiri. Iye anauza mtumiki wake amene ankamunyamulira zida kuti: ‘Awotu tikhoza kuwagonjetsa. Tiye tione ngati Yehova angatipatse chizindikiro. Akatiuza kuti tipite ndiye kuti ndi nthawi yabwino ndipo tikawagonjetsa.’ Nthawi yomweyo Afilisitiwo anafuula kuti: ‘Bwerani tikukhaulitseni!’ Yonatani ndi mtumiki wakeyo anakweradi phirilo ndipo anakawagonjetsa.

      Yonatani akupatsa Davide zinthu zake zina

      Popeza Yonatani anali mwana woyamba, anali woyenera kudzalowa ufumu wa Sauli. Koma iye ankadziwa kuti Yehova anasankha Davide ndipo sankamuchitira nsanje. Yonatani ndi Davide ankagwirizana kwambiri ndipo analonjezana kuti azitetezana. Yonatani anapatsa Davide zovala zake zankhondo, lupanga, uta ndi lamba posonyeza kuti ndi mnzake wapamtima.

      Pa nthawi ina, Davide akuthawa Sauli, mnzakeyu anapita kukamuuza kuti: ‘Limba mtima ndipo usaope chilichonse. Yehova wakusankha kuti ukhale mfumu. Ngakhale bambo anga akudziwa zimenezi.’ Kodi iweyo ungafune kukhala ndi mnzako wabwino ngati Yonatani?

      Yonatani ankaika moyo wake pangozi pofuna kuthandiza Davide. Iye ankadziwa zoti Mfumu Sauli akufuna kupha Davide ndiye anauza bambo akewo kuti: ‘Bambo mukudziwa kuti mukulakwa? Kodi Davide wakulakwirani chiyani kuti mumuphe?’ Koma Sauli anamukwiyira kwambiri Yonatani. Patapita zaka, Sauli ndi Yonatani anafera kunkhondo.

      Yonatani atafa, Davide anafufuza mwana wake dzina lake Mefiboseti. Atamupeza anamuuza kuti: ‘Bambo ako tinkagwirizana kwambiri choncho ndikusamalira kwa moyo wako wonse. Uzikhala m’nyumba mwanga ndipo tizidyera limodzi.’ Apatu Davide anasonyeza kuti sanaiwale Yonatani.

      “Muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani. Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.”​—Yohane 15:12, 13

      Mafunso: Kodi Yonatani anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima? Nanga anasonyezanso bwanji kuti anali wokhulupirika?

      1 Samueli 14:1-23; 18:1-4; 19:1-6; 20:32-42; 23:16-18; 31:1-7; 2 Samueli 1:23; 9:1-13

  • Tchimo la Mfumu Davide
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Mneneri Natani akudzudzula Mfumu Davide

      MUTU 43

      Tchimo la Mfumu Davide

      Sauli atafa, Davide anakhala mfumu. Iye anayamba kulamulira ali ndi zaka 30. Tsiku lina ali padenga la nyumba yake anaona mkazi wokongola. Atafufuza anapeza kuti dzina lake anali Bati-seba ndipo anali mkazi wa Uriya,yemwe anali msilikali. Davide anaitanitsa mkaziyo kuti abwere kunyumba kwake. Iye anagona naye ndipo mkaziyo anakhala oyembekezera. Davide anayesa kupeza njira yoti tchimo lakelo lisadziwike. Iye anauza mkulu wa asilikali kuti aike Uriya kutsogolo n’kumusiya kuti aphedwe. Uriya ataphedwa ku nkhondo, Davide anakwatira Bati-seba.

      Mfumu Davide akupempha Mulungu kuti amukhululukire

      Koma Yehova ankaona zoipa zonsezi. Ndiye kodi anatani? Iye anatumiza Natani kuti akakambirane ndi Davide za nkhaniyi. Natani atafika kwa Davide anamuuza kuti: ‘Panali munthu wina wolemera amene anali ndi nkhosa zambiri ndiye panalinso wosauka yemwe anali ndi kankhosa kamodzi kokha. Wosaukayo ankakakonda kwambiri kankhosa kakeko. Ndiyeno munthu wolemera uja analanda kankhosa ka wosaukayo kuti kakhalenso kake.’ Davide atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anati: ‘Munthu ameneyu ayenera kufa basi.’ Natani anauza Davide kuti: ‘Munthu wolemerayo ndi inuyo.’ Davide anazindikira zimene Natani ankatanthauza ndipo anamva chisoni. Ndiyeno anauza Natani kuti: ‘Ndachimwira Yehova.’ Tchimo limeneli linam’bweretsera mavuto Davide limodzi ndi banja lake. Yehova anapereka chilango kwa Davide koma sanamuphe chifukwa anadzichepetsa komanso analapa kuchokera pansi pa mtima.

      Davide ankafuna kumanga nyumba ya Yehova. Koma Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti ndi amene adzamange nyumbayo. Davide anayamba kusonkhanitsa zinthu zoti Solomo adzagwiritse ntchito pomanga. Iye anati: ‘Nyumba ya Yehova ikufunika idzakhale yokongola kwambiri. Popeza Solomo adakali mwana, ndimuthandiza kupeza zipangizo zomangira nyumbayi.’ Choncho Davide anapereka ndalama zambiri zoti zidzathandize pa ntchito yomanga nyumbayo. Anapeza anthu aluso komanso anasonkhanitsa golide ndi siliva wambiri ndiponso anasonkhanitsa matabwa a mtengo wa mkungudza ochokera ku Turo ndi ku Sidoni. Davide atatsala pang’ono kumwalira, anapatsa Solomo pulani ya mmene adzamangire nyumbayo. Anati: ‘Yehova anandiuza kuti ndikulembere pulaniyi. Usachite mantha chifukwa iye akuthandiza. Limba mtima ndipo yamba kugwira ntchitoyi.’

      Davide akukambirana ndi Solomo zokhudza mapulani a kachisi

      “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma amene amawaulula nʼkuwasiya adzachitiridwa chifundo.”​—Miyambo 28:13

      Mafunso: Kodi Davide anachita tchimo lotani? Kodi Davide anathandiza bwanji Solomo kuti amange nyumba ya Yehova?

      2 Samueli 5:3, 4, 10; 7:1-16; 8:1-14; 11:1-27; 12:1-14; 1 Mbiri 22:1-19; 28:11-21; Salimo 51:1-19

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena