-
Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Sabata?Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 29
Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Tsiku la Sabata?
YESU ANALALIKIRA KU YUDEYA
ANACHIRITSA MUNTHU WODWALA AMENE ANALI PAFUPI NDI DZIWE
Pamene Yesu anali ku Galileya anachita zambiri pa ntchito yake yolalikira. Komabe pamene ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso,” anasonyeza kuti ankaganizira zokalalikira kumadera enanso, osati ku Galileya kokha. Choncho anapita “n’kumalalikira m’masunagoge a mu Yudeya.” (Luka 4:43, 44) Zinali zomveka kuti achite zimenezi chifukwa pa nthawiyi mwambo wa Pasika, womwe unkachitikira ku Yerusalemu, unali utayandikira.
Mauthenga Abwino safotokoza zambiri zokhudza zimene Yesu anachita ku Yudeya poyerekeza ndi zimene anachita ku Galileya. Ngakhale kuti anthu ambiri a ku Yudeya sankamvetsera uthenga wake, Yesu sanasiye kulalikira mwakhama komanso kuchitira anthu ena zinthu zabwino kulikonse kumene ankapita.
Kenako Yesu anayamba ulendo wopita ku mzinda wa Yerusalemu, womwe unali likulu la chigawo cha Yudeya, kuti akachite nawo mwambo wa Pasika wa mu 31 C.E. Polowa mumzindawu anadzera ku Chipata cha Nkhosa ndipo pafupi ndi chipatachi panali dziwe lomwe linkadziwika kuti Betesida. Anthu ambiri odwala, akhungu komanso olumala ankabwera ku dziwe limeneli chifukwa ankakhulupirira kuti atha kuchira ngati atalowa m’dziwelo pa nthawi imene madziwo awinduka.
Yesu atafika ku dziweli anaona munthu wina yemwe anatha zaka 38 akudwala, koma tsikuli linali la Sabata. Kenako Yesu anamufunsa munthuyo kuti: “Kodi ukufuna kuchira?” Munthuyo anayankha kuti: “Bambo, ndilibe munthu wondiviika m’dziwemu madzi akawinduka, ndipo ndikati ndikalowemo wina amandipitirira n’kulowamo.”—Yohane 5:6, 7.
Kenako Yesu ananena mawu amene anadabwitsa munthuyo komanso aliyense amene anamumva akulankhula. Iye anamuuza kuti: “Nyamuka, nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.” (Yohane 5:8) Munthuyo anachitadi zimene anauzidwazo. Nthawi yomweyo anachira ndipo ananyamula machira ake n’kuyamba kuyenda.
M’malo mosangalala ndi zinthu zabwino zimene zinachitikazo, Ayuda ataona munthuyo anayamba kulankhula momuweruza kuti: “Lero ndi Sabata, n’kosaloleka kuti unyamule machirawa.” Koma munthuyo anawayankha kuti: “Amene wandichiritsayo wandiuza kuti, ‘Nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.’” (Yohane 5:10, 11) Ayudawo ankafuna kupezera zifukwa munthu amene anachiritsa wodwala pa tsiku la Sabata.
Pofuna kudziwa munthu amene anachita zimenezi, anafunsa wodwalayo kuti: “Ndiye ndani amene wakuuza kuti, ‘Nyamula machira ndi kuyamba kuyenda’?” Iwo anamufunsa funsoli chifukwa pa nthawiyi Yesu anali “atalowa m’chikhamu cha anthu” komanso munthu amene anachiritsidwa uja sankadziwa dzina la munthu amene anamuchiritsayo. (Yohane 5:12, 13) Komabe munthuyo anakumananso ndi Yesu m’kachisi ndipo tsopano anadziwa bwino munthu amene anamuchiritsa pa dziwe paja.
Munthu uja atakumananso ndi Ayuda omwe anamufunsa za munthu amene anamuchiritsa, anawauza kuti anachiritsidwa ndi Yesu. Ayudawo atamva zimenezo anapita kwa Yesu. Koma sanapite kwa Yesu kuti akadziwe chimene chinkamuchititsa kuti azitha kuchita zinthu zodabwitsazo. M’malomwake, anapita kuti akangomupezera zifukwa chifukwa choti anachita zinthu zabwino pa tsiku la Sabata. Ndipo anayamba kumuvutitsa chifukwa cha nkhaniyi.
-
-
Kodi Pali Ubale Wotani Pakati pa Yesu ndi Mulungu?Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 30
Kodi Pali Ubale Wotani Pakati pa Yesu ndi Mulungu?
MULUNGU NDIYE ATATE AKE A YESU
YESU ANALONJEZA KUTI AKUFA ADZAUKA
Yesu atachiritsa munthu pa tsiku la Sabata, Ayuda ena anamuimba mlandu wophwanya Sabata. Poyankha Ayuda amenewa Yesu ananena kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.”—Yohane 5:17.
Zimene Yesu anachita pa tsikuli zinali zosaletsedwa m’Chilamulo cha Mulungu. Yesu ankagwira ntchito yolalikira komanso kuchiritsa anthu potsanzira ntchito zabwino za Mulungu. Choncho Yesu ankachita zinthu zabwino tsiku lililonse, posatengera kuti tsikulo ndi la Sabata kapena ayi. Koma zimene Yesu anayankhazo zinawakwiyitsa kwambiri moti anayamba kufuna kumupha. N’chifukwa chiyani Ayudawo ankafuna kumupha?
Kuwonjezera pa zimene Yesu anachita pochiritsa munthu pa Sabata, Ayudawo anakwiyanso kwambiri atamva Yesu akunena kuti ndi Mwana wa Mulungu. Iwo ankaona ngati Yesu akunyoza Yehova Mulungu ponena kuti ndi Atate ake chifukwa kwa iwowo zinkakhala ngati akunena kuti iyeyo ndi wofanana ndi Mulungu. Komabe Yesu sanachite mantha chifukwa anapitiriza kuwafotokozera zambiri zokhudza ubale wake ndi Mulungu. Yesu ananena kuti: “Atatewo amakonda Mwana wake. Amamuonetsa zonse zimene iwo akuchita.”—Yohane 5:20.
Atate ndi amene amapereka moyo ndipo anasonyezapo zimenezi m’mbuyomo pamene anapereka mphamvu kwa anthu ena kuti aukitse amene anamwalira. Yesu ananenanso kuti: “Pakuti monga Atate amaukitsa akufa ndi kuwapatsa moyo, nayenso Mwana amapereka moyo kwa amene iye wafuna kuwapatsa.” (Yohane 5:21) Zimene Yesu ananenazi n’zolimbikitsa kwambiri tikaganizira zimene zidzachitike m’tsogolo. Ngakhale panopo, Mwanayu akupitirizabe kuukitsa anthu amene anali akufa mwauzimu. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Iye wakumva mawu anga ndi kukhulupirira amene anandituma ine ali nawo moyo wosatha, ndipo salowa m’chiweruzo koma wachoka ku imfa, waolokera ku moyo.”—Yohane 5:24.
Pa nthawiyi Yesu anali asanaukitsepo munthu aliyense, koma anauza anthu amene ankamuimba milanduwo kuti anthu amene anamwalira adzaukitsidwa. Iye ananena kuti: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.
Ngakhale kuti Yesu ali ndi udindo waukulu umenewu, iye ananena momveka bwino kuti amamvera Mulungu. Iye anati: “Ine sindingachite chilichonse chongoganiza ndekha. . . . Sinditsatira chifuniro changa, koma chifuniro cha amene anandituma.” (Yohane 5:30) Koma Yesu anafotokoza za udindo wake pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu, umene pa nthawiyi anali asanauonetsepo pa gulu la anthu. Ndipotu ena mwa anthu amene ankaimba mlandu Yesuwa anali akudziwa kale zinthu zambiri zokhudza Yesu. N’chifukwa chake Yesu anawakumbutsa kuti: “Inu munatumiza anthu kwa Yohane [M’batizi], ndipo iye anachitira umboni choonadi.”—Yohane 5:33.
N’kutheka kuti anthu amene ankaimba milandu Yesu, anali atamvapo zimene zinachitika zaka ziwiri m’mbuyomo. Pa nthawiyo Yohane anauza atsogoleri achipembedzo Achiyuda za Munthu wina amene ankabwera m’mbuyo mwake yemwe ankadziwika ndi dzina lakuti “Mneneri” komanso “Khristu.” (Yohane 1:20-25) Yesu anapitiriza kuwakumbutsa za mmene ankaonera Yohane, yemwe pa nthawiyi anali m’ndende. Iye anati: “Kwa kanthawi kochepa inu munali ofunitsitsa kusangalala m’kuwala kwakeko.” (Yohane 5:35) Koma pa nthawiyi, Yesu anawapatsa umboni wamphamvu kuposa umene Yohane M’batizi anawapatsa.
Kenako Yesu anawauza kuti: “Ntchito zimene ine ndikuchita [kuphatikizapo ntchito yochiritsa imene anali atangoigwira], zikundichitira umboni kuti Atate ananditumadi.” Ananenanso kuti: ‘Atate amene anandituma anandichitira umboni.’ (Yohane 5:36, 37) Mwachitsanzo, Mulungu anachitira umboni za Yesu pa nthawi imene ankabatizidwa.—Mateyu 3:17.
Choncho anthuwa analibe zifukwa zokwanira zokanira Yesu chifukwa Malemba amene ankafufuza ankachitira kale umboni za Yesu. Ndiyeno Yesu anamaliza n’kuwauza kuti: “Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso ine, pakuti iyeyo analemba za ine. Koma ngati simukhulupirira zolemba za ameneyo, mungakhulupirire bwanji mawu anga?”—Yohane 5:46, 47.
-
-
Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la SabataYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 31
Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la Sabata
MATEYU 12:1-8 MALIKO 2:23-28 LUKA 6:1-5
OPHUNZIRA ANABUDULA NGALA ZA TIRIGU PA TSIKU LA SABATA
YESU NDIYE “MBUYE WA SABATA”
Yesu ndi ophunzira ake anayamba ulendo wolowera kumpoto cha ku Galileya. Ayenera kuti anayenda ulendowu m’mwezi wa March kapena April chifukwa pa nthawiyi tirigu anali atacha. Ophunzira a Yesu anali ndi njala ndipo anayamba kubudula tirigu n’kumadya. Koma limeneli linali tsiku la Sabata ndipo Afarisi anaona zimene ophunzira a Yesuwo ankachita.
Kumbukirani kuti Ayuda ena a ku Yerusalemu ankafuna kupha Yesu pomuganizira kuti waphwanya Sabata. Koma pa nthawiyi, Afarisi anayamba kumuimba Yesu mlandu chifukwa cha zimene ophunzira ake anachita. Iwo ananena kuti: “Taona! Ophunzira ako akuchita zosayenera kuzichita pa sabata.”—Mateyu 12:2.
Afarisi ankanena kuti kubudula ngala n’kuzitikita m’manja n’cholinga choti udye, kunali ngati kugwira ntchito yokolola ndi kupuntha. (Ekisodo 34:21) Tsiku la Sabata linakhazikitsidwa kuti likhale tsiku losangalala komanso loti anthu azilimbikitsidwa akamaganizira zinthu zauzimu.Koma tsikuli linali lolemetsa chifukwa cha malamulo okhwima amene Afarisi anakhazikitsa okhudza ntchito zimene anthu ankayenera kugwira. Yesu anatsutsa maganizo awo olakwikawo powafotokozera zitsanzo zosonyeza kuti zimene ankachitazo zinali zosiyana ndi zimene Yehova Mulungu ankafuna kuti anthu azichita potsatira lamulo la Sabata.
Chitsanzo choyamba chimene Yesu anawauza ndi cha Davide ndi anyamata ake. Pa nthawi ina ali ndi njala, Davide ndi anyamata ake anakalowa mu chihema n’kudya mkate wachionetsero. Mikateyo inali itachotsedwa kale pamaso pa Yehova ndipo anali ataikapo ina yatsopano koma amene ankayenera kudya mikate yochotsedwayo anali ansembe okha. Koma chifukwa cha mmene zinthu zinalili, Davide ndi anyamata ake sanaimbidwe mlandu chifukwa chodya mikateyi.—Levitiko 24:5-9; 1 Samueli 21:1-6.
Pofotokoza chitsanzo chachiwiri, Yesu anati: “Kapena simunawerenge m’Chilamulo, kuti pa sabata ansembe m’kachisi anali kuchita zinthu mosalabadira kupatulika kwa tsiku la sabata koma anakhalabe osalakwa?” Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti ansembe ankapha nyama zoti apereke nsembe komanso ankagwira ntchito zina za pakachisi pa tsiku la Sabata. Kenako Yesu ananena kuti: “Koma ndikukuuzani kuti wamkulu kuposa kachisi ali pano.”—Mateyu 12:5, 6; Numeri 28:9.
Pofuna kuwathandiza kumvetsa bwino mfundo yake, Yesu anagwiritsa ntchito Malemba ndipo ananena kuti: “Ngati mukanamvetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe,’ simukanaweruza anthu osalakwa.” Kenako anamaliza ndi kuti: “Pakuti Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa sabata.” Pamenepa Yesu ankanena za Ufumu wake womwe udzalamulire mwamtendere kwa zaka 1000.—Mateyu 12:7, 8; Hoseya 6:6.
Kwa zaka zambiri, anthu akhala akuvutika kwambiri ndi nkhondo komanso zinthu zankhanza zomwe zimachitika chifukwa chakuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli. Zimenezi zidzakhalatu zosiyana kwambiri ndi zimene zidzachitike tikadzalowa mu Sabata lalikulu, lomwe ndi ulamuliro wa Khristu. Pa nthawi imeneyi tidzapumula ku mavuto athu onse. Zimenezi ndi zimene takhala tikuziyembekezera kwa nthawi yaitali.
-
-
Kodi Malamulo Ankalola Munthu Kuchita Chiyani pa Sabata?Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 32
Kodi Malamulo Ankalola Munthu Kuchita Chiyani pa Tsiku la Sabata?
MATEYU 12:9-14 MALIKO 3:1-6 LUKA 6:6-11
YESU ANACHIRITSA MUNTHU WOPUWALA DZANJA PA TSIKU LA SABATA
Pa tsiku lina la Sabata, Yesu anapita ku sunagoge ndipo n’kutheka kuti sunagogeyo anali wa ku Galileya. Ali kumeneko anapeza munthu yemwe anali wopuwala dzanja lamanja. (Luka 6:6) Pa nthawiyi alembi ndi Afarisi ankangoyang’anitsitsa kuti aone zimene Yesu achite. Kodi n’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Zimene ankaganiza zinadziwika bwino atamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka kuchiritsa odwala tsiku la sabata?”—Mateyu 12:10.
Atsogoleri achipembedzo achiyuda ankakhulupirira kuti kuchiritsa pa tsiku la Sabata kunali kovomerezeka pokhapokha ngati moyo unali pangozi. Mwachitsanzo, sikunali kololeka kubwezeretsa fupa limene lachoka m’malo mwake kapena kumanga pamene wabinya, chifukwa sizinali zinthu zoika moyo wa munthu pangozi. Sikuti alembi ndi Afarisi ankamufunsa Yesu chifukwa choti ankadera nkhawa munthu wopuwala dzanja uja, ayi. Iwo ankangofuna kuti amupezere Yesu chifukwa chomuimbira milandu.
Komabe Yesu anadziwa maganizo olakwika amene anthuwa anali nawo. Anadziwanso kuti anthuwa ankakhwimitsa kwambiri malamulo okhudza ntchito zimene anthu ayenera kugwira pa tsiku la Sabata, zomwe zinali zosagwirizana ndi Malemba. (Ekisodo 20:8-10) Pa nthawiyi n’kutinso anthu ena atamuimbapo kale milandu chifukwa cha zinthu zabwino zimene ankachita. Koma nkhaniyo inakula pamene Yesu anauza munthu amene anali wopuwala dzanja uja kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.”—Maliko 3:3.
Kenako Yesu anayang’ana alembi ndi Afarisi aja n’kuwafunsa kuti: “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa imodzi, ndiyeno nkhosayo n’kugwera m’dzenje tsiku la sabata, sangaigwire ndi kuitulutsa?” (Mateyu 12:11) Pa nthawiyo nkhosa inkaonedwa kuti ndi chiweto chobweretsa ndalama. Ndiye ngati nkhosayo yagwera m’dzenje, mwiniwake sakanaisiya m’dzenjemo kufikira tsiku lotsatira chifukwa ikanatha kufa ndipo akanaluza zambiri. Ndipotu Malemba amanena kuti: “Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake.”—Miyambo 12:10.
Pofuna kuthandiza anthuwo kumvetsa mfundo yake, Yesu anawauza kuti: “Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa. Choncho, n’kololeka inde kuchita chinthu chabwino pa tsiku la sabata.” (Mateyu 12:12) Izi zikusonyeza kuti Yesu sanaphwanye Sabata pochiritsa munthu uja pa tsiku la Sabata. Atsogoleri achipembedzowo analephera kutsutsa mfundo yomveka bwino komanso yosonyeza chifundo imene Yesu anafotokozayi, moti anangokhala chete.
Yesu atakwiya komanso atagwidwa ndi chisoni chifukwa chodziwa maganizo awo olakwika, anayang’ana uku ndi uku n’kuuza munthu wopuwala dzanja uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” (Mateyu 12:13) Atangolitambasula, nthawi yomweyo dzanjalo linakhala bwinobwino. Munthuyo anasangalala kwambiri, koma kodi Afarisi aja anatani?
M’malo moti asangalale kuti munthu uja wachira, Afarisi anatuluka m’sunagogemo ndipo nthawi yomweyo “anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi a chipani cha Herode kuti amuphe.” (Maliko 3:6) Anthu ena omwe anali m’chipanichi, anali ochokera m’gulu la chipembedzo la Asaduki. Nthawi zambiri Asaduki ndi Afarisi sankagwirizana koma pa nthawi imeneyi anagwirizana n’cholinga choti atsutsane ndi Yesu.
-