-
Mafanizo Awiri Onena za Munda wa MpesaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 106
Mafanizo Awiri Onena za Munda wa Mpesa
MATEYU 21:28-46 MALIKO 12:1-12 LUKA 20:9-19
FANIZO LONENA ZA ANA AWIRI
FANIZO LA ALIMI OSAMALIRA MUNDA WA MPESA
Ali kukachisi Yesu anasokoneza ansembe aakulu ndi akulu amene anamufunsa kuti awauze kumene ankatenga ulamuliro umene ankachitira zinthu. Zimene anawayankha zinawasowetsa chonena. Kenako Yesu ananena fanizo limene linasonyeza kuti ansembe aakulu ndi akuluwo anali anthu otani.
Iye anati: “Munthu wina anali ndi ana awiri. Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti: ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito m’munda wa mpesa.’ Iye poyankha anati, ‘Ndipita bambo,’ koma sanapite. Kenako anapita kwa mwana wachiwiri uja n’kumuuzanso chimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Ayi sindipita.’ Koma pambuyo pake anamva chisoni ndipo anapita. Ndani mwa ana awiriwa amene anachita chifuniro cha bambo ake?” (Mateyu 21:28-31) Anthuwa sanavutike kupeza yankho la funsoli. Mwana wachiwiri ndi amene pomaliza anachita zimene bambo ake ankafuna.
Ndiyeno Yesu anauza anthu amene ankamutsutsawo kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu ufumu wa Mulungu.” Poyamba okhometsa msonkho komanso mahule sankatumikira Mulungu. Koma kenako anthu amenewa analapa ndipo anayamba kutumikira Mulungu. Zimenezi ndi zofanana ndi zimene mwana wachiwiri uja anachita. Koma atsogoleri achipembedzo anali ngati mwana woyamba uja. Iwo ankaoneka ngati ankatumikira Mulungu koma zoona zake n’zoti sankamutumikira. Yesu ananena kuti: “Pakuti Yohane [M’batizi] anabwera kwa inu m’njira yachilungamo, koma inu simunam’khulupirire. Koma okhometsa msonkho ndi mahule anam’khulupirira, Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve chisoni n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupirire.”—Mateyu 21:31, 32.
Yesu atamaliza kunena fanizo limeneli ananenanso fanizo lina. Ananena fanizo lachiwirili pofuna kusonyeza kuti atsogoleri achipembedzo sankafuna kutumikira Mulungu komanso kuti anali anthu oipa. Iye ananena kuti: “Munthu wina analima munda wa mpesa ndi kumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa, ndi kumanga nsanja. Atatero anausiya m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina. Tsopano nyengo ya zipatso itakwana, iye anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akam’patseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo. Koma iwo anam’gwira, n’kumumenya ndi kum’bweza chimanjamanja. Iye anatumizanso kapolo wina kwa iwo koma ameneyu anamutema m’mutu ndi kumuchitira zachipongwe. Anatumizanso wina, koma ameneyo anamupha. Ndiyeno anatumizanso akapolo ena ambiri. Ena mwa iwo anawamenya ndipo ena anawapha.”—Maliko 12:1-5.
Kodi anthu amene ankamva Yesu akunena fanizo limeneli anamvetsa tanthauzo lake? N’kutheka kuti anthuwo anakumbukira mawu amene Yesaya analemba akuti: “Ine ndine Yehova wa makamu ndipo Isiraeli ndi munda wanga wa mpesa. Amuna a ku Yuda ndiwo mitengo ya mpesa imene ndinali kuikonda. Ine ndinali kuyembekezera chilungamo koma ndinaona anthu akuphwanya malamulo.” (Yesaya 5:7) Anthu komanso zinthu zimene Yesu anatchula m’fanizoli ndi zofanana ndi zimene Yesaya ananena. Tikutero chifukwa mwiniwake wa mundawo ndi Yehova ndipo munda wa mpesa ndi mtundu wa Aisiraeli, womwe unkatetezedwa ndi Chilamulo cha Mulungu. Yehova ankatumiza aneneri kuti azilangiza anthu ake komanso kuwathandiza kuti azibala zipatso zabwino.
Koma ‘alimiwo’ anazunza komanso kupha “akapolo” amene mwinimunda uja anawatuma. Yesu anapitiriza kufotokoza kuti: “Tsopano [mwiniwake wa mundawo] anatsala ndi mmodzi yekha, mwana wake wokondedwa. Anatumizanso mwanayo kwa iwo ngati wotsirizira, n’kunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ Koma alimiwo anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa. Bwerani, tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Choncho anamugwira n’kumupha.”—Maliko 12:6-8.
Kenako Yesu anawafunsa anthuwo kuti: “Kodi mwinimunda wa mpesawo adzachita chiyani?” (Maliko 12:9) Atsogoleri achipembedzowo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angam’patse zipatso m’nyengo yake.”—Mateyu 21:41.
Ponena mawu amenewa, atsogoleri achipembedzowa anadziweruza okha mosadziwa chifukwa iwo anali m’gulu la “alimi” ogwira ntchito ‘m’munda wa mpesa’ wa Yehova, womwe unkaimira mtundu wa Isiraeli. Chimodzi mwa zipatso zimene Yehova ankayembekezera kwa alimiwo chinali choti azikhulupirira Mwana wake, yemwenso ndi Mesiya. Yesu anayang’ana atsogoleri achipembedzowo n’kunena kuti: “Kodi simunawerengepo lemba limene limati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri’? Kodi simunawerenge kuti ‘Umenewu wachokera kwa Yehova, ndipo ndi wodabwitsa m’maso mwathu’?” (Maliko 12:10, 11) Kenako Yesu ananena mfundo imene ankafuna kuti anthuwo amvetse. Iye anati: “Ichi n’chifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.”—Mateyu 21:43.
Alembi komanso ansembe aakulu anazindikira kuti Yesu “anali kunena za iwo mufanizolo.” (Luka 20:19) Pa nthawi imeneyi anthuwo anafunitsitsa kupha Yesu, yemwe anali “wolandira cholowa.” Koma sanamuphe chifukwa ankaopa gulu la anthu, lomwe linkaona kuti Yesu ndi mneneri.
-
-
Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la UkwatiYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 107
Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati
FANIZO LA PHWANDO LA UKWATI
Yesu atatsala pang’ono kumaliza utumiki wake anapitirizabe kugwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuti anthu onse adziwe zimene alembi komanso ansembe aakulu ankachita. Chifukwa cha zimenezi, alembi komanso ansembe aakuluwo ankafuna kumupha. (Luka 20:19) Koma Yesu anafotokozanso fanizo lina. Iye anati:
“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake. Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando laukwati, koma anthuwo sanafune kubwera.” (Mateyu 22:2, 3) Yesu anayamba kufotokoza fanizoli ndi mawu akuti “Ufumu wakumwamba.” Ndiye kuti “mfumu” ya m’fanizoli ndi Yehova Mulungu. Nanga mwana wa mfumuyo komanso anthu amene anaitanidwa ku phwando laukwati ndi ndani? Pamenepanso n’zosavuta kuzindikira kuti mwana wa mfumuyo ndi Mwana wa Yehova, amene ankanena fanizoli ndipo amene anaitanidwawo ndi anthu amene adzalamulire ndi Mwanayo mu Ufumu wakumwamba.
Kodi ndani amene anali oyamba kuitanidwa? Ayenera kuti anali Ayuda chifukwa ndi amene Yesu ndi atumwi ankawalalikira za Ufumu. (Mateyu 10:6, 7; 15:24) Mu 1513 B.C.E., Ayudawo anapanga pangano ndi Mulungu ndipo anavomereza kuti adzatsatira Chilamulo chimene anawapatsa. Choncho Ayuda anali anthu oyambirira kupanga “ufumu wa ansembe.” (Ekisodo 19:5-8) Koma kodi anaitanidwa liti ku “phwando la ukwati?” Anayamba kuitanidwa mu 29 C.E. pamene Yesu anayamba kulalikira za Ufumu wakumwamba.
Kodi Aisiraeli ambiri anatani ataitanidwa? Yesu ananena kuti “anthuwo sanafune kubwera.” Atsogoleri achipembedzo komanso anthu ambiri sanavomereze kuti Yesu anali Mesiya komanso Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu.
Koma Yesu anasonyeza kuti Ayudawo adzapatsidwanso mwayi wina. Iye anati: “Kenako inatumanso akapolo ena kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana, ng’ombe zanga komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani ku phwando laukwati.”’ Koma anthuwo ananyalanyaza ndi kuchoka. Wina anapita kumunda wake, wina kumalonda ake. Koma enawo anagwira akapolo akewo, ndi kuwachitira zachipongwe n’kuwapha.” (Mateyu 22:4-6) Ndipo zimenezi ndi zimene zinachitika mpingo wachikhristu utangokhazikitsidwa kumene. Nthawi imeneyi, Ayuda anali ndi mwayi wolowa nawo mu Ufumu koma ambiri anakana mwayi umenewu mpaka kufika pozunza ‘akapolo a mfumu.’—Machitidwe 4:13-18; 7:54, 58.
Kodi mtunduwu unakumana ndi zotani chifukwa chochita zimenezi? Yesu ananena kuti: “Pamenepo mfumu ija inakwiya kwambiri, ndipo inatumiza asilikali ake kukawononga opha anthu amenewo ndi kutentha mzinda wawo.” (Mateyu 22:7) Zimenezi zinachitika mu 70 C.E. pamene Aroma anawononga “mzinda [wa Ayuda]” wa Yerusalemu.
Chifukwa chakuti Ayuda anakana mfumu itawaitana, ndiye kuti palibe aliyense amene akanaitanidwa? Ayi. Tikutero chifukwa fanizo la Yesu limapitiriza kuti: “Kenako [mfumu] anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa ndithu, koma oitanidwa aja anali osayenera. Chotero pitani m’misewu yotuluka mumzinda, ndipo aliyense amene mukam’peze, mukamuitanire phwando laukwatili.’ Choncho akapolowo anapita m’misewu ndi kusonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe. Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu oyembekezera kulandira chakudya.”—Mateyu 22:8-10.
Izi zinayamba kuchitika pamene mtumwi Petulo anayamba kuthandiza anthu a mitundu ina, omwe sanali Ayuda komanso amene sanatembenukire ku Chiyuda, kuti nawonso akhale Akhristu. Mwachitsanzo mu 36 C.E., Koneliyo, yemwe anali kapitawo wa gulu la asilikali achiroma, ndi anthu a m’banja lake analandira mzimu wa Mulungu. Zimenezi zinawapatsa mwayi wolowa mu Ufumu wakumwamba umene Yesu ananena.—Machitidwe 10:1, 34-48.
Fanizo la Yesu linasonyezanso kuti si onse amene anabwera ku phwandolo omwe “mfumu” inawavomereza. Yesu anati: “Pamene mfumu ija inalowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati. Chotero inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’ Iye anasowa chonena. Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja ndi miyendo ndipo mum’ponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’ “Pakuti oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”—Mateyu 22:11-14.
N’kutheka kuti atsogoleri achipembedzo amene anamva Yesu akunena zimenezi sanamvetse zimene ankatanthauza. Komabe anthuwa anakwiya kwambiri ndipo anatsimikiza kuti athane ndi Yesu chifukwa ankawachititsa manyazi.
-
-
Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti AmugwireYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 108
Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti Amugwire
MATEYU 22:15-40 MALIKO 12:13-34 LUKA 20:20-40
PEREKANI ZA KAISARA KWA KAISARA
KODI ANTHU AMENE ADZAUKITSIDWE ADZAKWATIRA KAPENA KUKWATIWANSO?
MALAMULO AKULUAKULU
Atsogoleri achipembedzo anakwiya kwambiri ndi Yesu chifukwa ananena mafanizo omwe anasonyeza kuti atsogoleriwo anali anthu oipa kwambiri. Afarisi anagwirizana zoti amugwire. Iwo anapangana zoti Yesu akalankhula zinazake amugwire n’kukamupereka kwa wolamulira wachiroma moti anapatsa ndalama ena mwa ophunzira awo kuti akamugwire.—Luka 6:7.
Ophunzira a Afarisiwo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti mumanena ndi kuphunzitsa molondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. Kodi n’kololeka kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” (Luka 20:21, 22) Yesu sanapusitsike ndi funso lawo lachinyengolo. Ngati Yesu akanayankha kuti, ‘Ayi, sikololeka kupereka msonkho,’ akanaimbidwa mlandu woukira boma la Aroma. Komanso ngati akanayankha kuti, ‘Inde, muzikhoma msonkho,’ anthu omwe ankadana ndi ulamuliro wa Aroma akanaganiza kuti Yesu ali ku mbali ya Aroma ndipo akanamuukira. Ndiye kodi Yesu anawayankha bwanji?
Iye ananena kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa? Ndionetseni khobidi la msonkho.” Pamenepo anam’bweretsera khobidi limodzi la dinari. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi ndi mawu akewa n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Pamenepo iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”—Mateyu 22:18-21.
Anthuwo anagoma kwambiri ndi zimene Yesu anawayankha moti anasowa chonena n’kungochokapo. Ichi chinali chiyambi chabe chifukwa anthu aja atalephera kumukola, panabweranso gulu la atsogoleri achipembedzo kudzamuyesa.
Asaduki omwe sankakhulupirira kuti anthu omwe anamwalira adzauka, anafunsa Yesu funso lokhudza za kuuka kwa akufa komanso za ukwati wa pachilamu. Iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, Mose anati, ‘Ngati munthu wamwalira wopanda ana, m’bale wake ayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana.’ Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako n’kumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake. Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja.Pamapeto pake mkaziyo nayenso anamwalira. Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”—Mateyu 22:24-28.
Poyankha Asadukiwo, Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Mose analemba omwenso Asadukiwo ankawakhulupirira. Iye ananena kuti: “Mukulakwitsa. Kodi kulakwitsa kumeneku si chifukwa chakuti simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu? Akadzauka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba. Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’? Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa. Mukulakwitsa kwambiri anthu inu.” (Maliko 12:24-27; Ekisodo 3:1-6) Gulu la anthulo linadabwa kwambiri ndi zimene Yesu anawayankha.
Yesu anasowetsa chonena Afarisi ndi Asaduki, kenako magulu awiriwa anapanga gulu limodzi ndipo anapitanso kwa Yesu kuti akamuyese. Mlembi wina pa gululo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?”—Mateyu 22:36.
Yesu anayankha kuti: “Loyamba n’lakuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu, Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi. Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Kulibe lamulo lina lalikulu kuposa amenewa.”—Maliko 12:29-31.
Mlembiyo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino mogwirizana ndi choonadi, ‘Iye ndi Mmodzi, ndipo palibenso wina, koma Iye yekha.’ Kunena za kukonda Mulungu ndi mtima wonse, maganizo onse, mphamvu zonse, komanso kukonda mnzako mmene umadzikondera wekha, n’zofunika kwambiri kuposa nsembe zonse zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.” Pamenepo Yesu, pozindikira kuti mlembiyo wayankha mwanzeru anamuuza kuti: “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.”—Maliko 12:32-34.
Kwa masiku atatu, kuyambira pa Nisani 9, 10 ndi 11, Yesu anakhala akuphunzitsa m’kachisi. Anthu ena anasangalala kumva zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo m’modzi mwa anthuwo anali mlembiyu. Koma atsogoleri achipembedzo sanasangalale naye moti palibe amene “analimba mtima kumufunsanso.”
-
-
Anadzudzula Atsogoleri Achipembedzo Omwe AnkamutsutsaYesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
-
-
MUTU 109
Anadzudzula Atsogoleri Achipembedzo Omwe Ankamutsutsa
MATEYU 22:41–23:24 MALIKO 12:35-40 LUKA 20:41-47
KODI KHRISTU NDI MWANA WA NDANI?
YESU ANANENA POYERA KUTI ANTHU AMENE ANKAMUTSUTSA ANALI ACHINYENGO
Atsogoleri achipembedzo analephera kuchititsa Yesu manyazi komanso analephera kumugwira kuti akamupereke kwa Aroma. (Luka 20:20) Ndiyeno pa Nisani 11, Yesu ali kukachisi anthu omwe ankamutsutsa anabwera kuti adzamukole mawu koma zinthu zinatembenuka. Yesu ndi amene anayamba kuwapanikiza ndipo ananena poyera kuti iyeyo ndi Mesiya. Iye anawafunsa kuti: “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” (Mateyu 22:42) Anthu ankadziwa kuti Khristu kapena kuti Mesiya adzachokera mumzera wa Davide ndipo ndi zimene anthuwo anayankha Yesu.—Mateyu 9:27; 12:23; Yohane 7:42.
Yesu anawafunsanso kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu, Davide anamutcha ‘Ambuye,’ muja anati, ‘Yehova wauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’? Chotero ngati Davide anamutcha kuti ‘Ambuye,’ akukhala bwanji mwana wake?”—Mateyu 22:43-45.
Afarisiwo sanayankhe chifukwa ankayembekezera kuti munthu wochokera mumzera wa Davide ndi amene adzawalanditse ku ulamuliro wa Aroma. Ndiyeno Yesu anagwiritsa ntchito mawu amene Davide ananena pa Salimo 110:1, 2 pofuna kusonyeza kuti Mesiya sadzakhala wolamulira wamba. Yesu anafotokoza kuti Mesiya ndi Mbuye wa Davide ndipo adzayamba kugwiritsa ntchito mphamvu zake akadzakhala kudzanja lamanja la Mulungu. Zimene Yesu anawayankha zinawasowetsa chonena.
Pa nthawi imene Yesu ankalankhula zimenezi, ophunzira ake komanso anthu ena ankangomvetsera. Ndiyeno Yesu anayamba kulankhula nawo ndipo anawachenjeza za alembi ndi Afarisi. Yesu anawauza kuti anthu amenewa “adzikhazika pampando wa Mose” kuti aziphunzitsa anthu Chilamulo cha Mulungu. Yesu anauza anthuwo kuti: “Muzichita ndi kutsatira zilizonse zimene angakuuzeni, koma musamachite zimene iwo amachita, chifukwa iwo amangonena koma osachita.”—Mateyu 23:2, 3.
Kenako Yesu anafotokoza zinthu zomwe zinasonyeza kuti alembi ndi Afarisi anali achinyengo. Iye anati: “Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba timene amavala monga zodzitetezera.” Ayuda ena ankavala timapukusi tomwe tinkaoneka ngati kabokosi kakang’ono pachipumi kapena padzanja ndipo tinkakhala ndi mawu a m’Chilamulo. Koma Afarisi ankavala timapukusi tatikulu kuposa timeneti pofuna kusonyeza anthu kuti iwo anali odzipereka kwambiri potsatira Chilamulo. Afarisiwa ‘ankakulitsanso ulusi wopota wa m’mphepete mwa zovala zawo.’ Aisiraeli ankafunika kuika ulusi wopota m’mphepete mwa zovala zawo, koma Afarisi ankawonetsetsa kuti ulusi wa zovala zawo uzikhala wautali kwambiri. (Numeri 15:38-40) Ankachita zimenezi “kuti anthu awaone.”—Mateyu 23:5.
Yesu ankadziwanso kuti ophunzira ake akhoza kutengera mtima wofuna kukhala otchuka, choncho anawalangiza kuti: “Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi, wakumwamba Yekhayo. Musamatchedwe ‘atsogoleri,’ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu.” Ndiye ophunzirawo ankayenera kudziona bwanji, nanga ankafunika kuchita bwanji zinthu ndi anthu ena? Yesu anawauza kuti: “Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu. Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.”—Mateyu 23:8-12.
Kenako Yesu ananena zimene zidzachitikire alembi ndi Afarisi achinyengowo. Iye anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mukutseka ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Pakuti inuyo simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe.”—Mateyu 23:13.
Yesu anadzudzula Afarisi chifukwa chakuti sankaona zinthu zofunika ngati mmene Yehova amazionera ndipo zimenezi zinkaonekera pa malamulo osamveka amene iwo ankaika. Mwachitsanzo, iwo ankanena kuti: “Ngati munthu walumbirira kachisi palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira golide wa m’kachisi, asunge lumbiro lake.” Iwo ankasonyeza kuti anali okonda chuma chifukwa ankaganizira kwambiri za golide wa m’kachisi m’malo moganizira kuti kachisiyo ndi malo amene ankalambirirako Yehova. Komanso ‘ankanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika.”—Mateyu 23:16, 23; Luka 11:42.
Yesu ananena kuti Afarisiwa anali ‘atsogoleri akhungu, amene ankasefa zakumwa zawo kuti achotsemo kanyerere koma ankameza ngamila.’ (Mateyu 23:24) Afarisi ankasefa vinyo wawo kuti achotsemo nyerere chifukwa nyerereyo inali m’gulu la tizilombo todetsedwa. Koma chifukwa chakuti ankanyalanyaza zinthu zofunika kwambiri za m’Chilamulo, zinali ngati kuti akumeza ngamila yomwenso inali nyama yodetsedwa.—Levitiko 11:4, 21-24.
-