MUTU 10
Kumbukirani Mkazi wa Loti
Loti ankakhala ndi Abulahamu ku Kanani. Lotiyu anali mwana wa mng’ono wake wa Abulahamu. Kenako onse anakhala ndi ziweto zambiri moti malo odyetsera ziwetozo anawachepera. Ndiyeno Abulahamu anauza Loti kuti: ‘N’zosatheka kuti tizikhalabe limodzi. Yamba iweyo kusankha kumene ukufuna kukakhala ndipo ine ndipita kwinako.’ Apatu Abulahamu anasonyeza kuti sanali wodzikonda.
Loti anaona dera lapafupi ndi mzinda wa Sodomu limene linali lokongola. Iye anakopeka ndi derali chifukwa linali ndi madzi ambiri komanso udzu wobiriwira. Choncho anasankha dera limeneli ndipo anasamukira kumeneku ndi banja lake.
Anthu a mumzinda wa Sodomu komanso mzinda wina wapafupi wotchedwa Gomora anali ndi makhalidwe oipa kwambiri. Choncho Yehova anaona kuti ndi bwino kungowononga mizindayo. Koma Mulungu anaganiza zoti apulumutse Loti ndi banja lake. Iye anatumiza angelo awiri kukawauza kuti: “Fulumirani! Tulukani mumzinda uno, chifukwa Yehova auwononga.”
Koma Loti ndi banja lake ankangochedwachedwa moti angelowo anachita kuwagwira manja n’kuwatulutsa mumzindawo. Iwo anawauza kuti: ‘Thawani mupulumutse moyo wanu! Musayangʼane kumbuyo chifukwa mukangoyang’ana mufa.’
Iwo atafika mumzinda wa Zowari, Yehova anagwetsa moto ndi sulufule ngati mvula mumzinda wa Sodomu ndi Gomora. Mizinda yonseyi inapseratu. Koma mkazi wa Loti sanamvere Yehova ndipo anayang’ana m’mbuyo. Atangotero anasanduka chipilala chamchere. Komabe Loti ndi ana ake aakazi anapulumuka chifukwa choti anamvera Yehova. Onse ayenera kuti anamva chisoni ataona kuti mayi afa chifukwa chosamvera. Koma anasangalala kuti iwowo anamvera malangizo a Yehova.
“Kumbukirani mkazi wa Loti.”—Luka 17:32