Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 96 tsamba 224-tsamba 225 ndime 2
  • Yesu Anasankha Saulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anasankha Saulo
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Wozunza Aona Kuunika Kwakukulu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Pa Njira ya ku Damasiko
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mpingo “Unayamba Kukhala Pamtendere”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Kulalikira kwa Saulo Kunamudanitsa ndi Anthu
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 96 tsamba 224-tsamba 225 ndime 2
Mwadzidzidzi Saulo anaona kuwala

MUTU 96

Yesu Anasankha Saulo

Saulo anali nzika ya Roma ndipo anabadwira ku Tariso. Iye anali Mfarisi ndipo ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose koma ankadana kwambiri ndi Akhristu. Ankagwira Akhristu n’kupita nawo kundende. Iye analiponso pamene anthu olusa ankagenda Sitefano ndi miyaya mpaka kumupha.

Koma Saulo sanakhutire ndi kumanga Akhristu ku Yerusalemu. Choncho anapempha chilolezo kwa mkulu wa ansembe kuti akagwirenso Akhristu a mumzinda wa Damasiko. Koma atatsala pang’ono kufika mumzindawo, mwadzidzidzi anaona kuwala ndipo anagwa pansi. Kenako anamva mawu akuti: ‘Saulo, kodi ukundizunziranji?’ Iye anafunsa kuti: ‘Ndinu ndani?’ Mawu aja anamvekanso kuti: ‘Ndine Yesu. Pita ku Damasiko ndipo ukauzidwa zoyenera kuchita.’ Nthawi yomweyo Saulo anasiya kuona moti anachita kumugwira dzanja n’kumamutsogolera.

Ku Damasiko kunali Mkhristu wina wokhulupirika dzina lake Hananiya. Yesu anauza Hananiya kuti: ‘Pita ku Msewu Wowongoka ndipo ukafike panyumba ya Yudasi n’kukafunsa za munthu wotchedwa Saulo.’ Koma Hananiya anati: ‘Ambuye, munthu ameneyo ndikumudziwa bwino. Akumagwira ophunzira n’kumawatsekera m’ndende.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Pita. Ndasankha Saulo kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yambiri.’

Saulo anakhala wakhungu ataona kuwala

Hananiya anapitadi ndipo atapeza Saulo anamuuza kuti: ‘M’bale wanga Saulo, Yesu wandituma kuti ndidzatsegule maso ako.’ Nthawi yomweyo Saulo anayamba kuona. Anaphunzira za Yesu ndipo anakhala wophunzira wake. Atabatizidwa anayamba kulalikira m’masunagoge. Ayuda anadabwa kwambiri ataona kuti Saulo wayamba kuphunzitsa anthu za Yesu. Iwo anati: ‘Si munthu amene ankagwira ophunzira a Yesu uja uyu?’

Saulo anaphunzitsa anthu a ku Damasiko kwa zaka zitatu. Koma Ayuda ankadana naye kwambiri ndipo anakonza zoti amuphe. Abale atamva zimenezi anamuika m’dengu n’kumutulutsira pawindo la mpanda.

Saulo atafika ku Yerusalemu, ankafuna kuti azikhala limodzi ndi abale. Koma abalewo ankamuopa. Kenako wophunzira wina wotchedwa Baranaba anamukomera mtima ndipo anapita naye kwa atumwi n’kuwafotokozera kuti Sauloyo anasintha kwambiri ndipo tsopano ndi Mkhristu. Saulo anayamba kulalikira molimba mtima limodzi ndi mpingo wa ku Yerusalemu. Kenako anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Paulo.

“Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa . . . Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.”​—1 Timoteyo 1:15

Mafunso: N’chifukwa chiyani Akhristu ankaopa Saulo? N’chiyani chinachititsa kuti iye asinthe n’kukhala Mkhristu?

Machitidwe 7:54-60; 8:1-3; 9:1-28; 13:9; 21:40; 22:1-15; Aroma 1:1; Agalatiya 1:11-18

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena